Acts 9 (BOGWICC)

1 Pa nthawi imeneyi, Saulo ankaopsezabe okhulupirira Ambuye nafuna kuwapha. Iye anapita kwa mkulu wa ansembe, 2 ndi kukapempha makalata a chilolezo kuti apite nawo ku masunagoge a ku Damasiko, kuti ngati atakapezeka ena kumeneko otsata Njirayo, kaya ndi amuna kapena amayi, akawamange ndi kuwatenga kubwera nawo ku Yerusalemu. 3 Akuyandikira ku Damasikoku paulendo wake, mwadzidzidzi kuwala kochokera kumwamba kunamuzungulira iye. 4 Iye anagwa pansi ndipo anamva mawu akuti, “Saulo, Saulo ukundizunziranji Ine?” 5 Saulo anafunsa kuti, “Ndinu yani Ambuye?”Ambuye anayankha kuti, “Ndine Yesu amene iwe ukumuzunza.” 6 “Tsopano dzuka, lowa mu mzindamo, ndipo udzawuzidwa zoyenera kuchita.” 7 Anthu amene anali naye paulendo, anasowa chonena; iwo anamva mawu koma sanaone wina aliyense. 8 Saulo anayimirira, ndipo pamene anatsekula maso ake sanathe kuona. Kotero anamugwira dzanja ndi kulowa naye mu Damasiko. 9 Anakhala wosaona kwa masiku atatu ndiponso sanadye kapena kumwa kanthu kalikonse. 10 Ku Damasiko kunali wophunzira wina dzina lake Hananiya. Ambuye anamuyitana mʼmasomphenya kuti, “Hananiya!”Iye anayankha kuti, “Ine Ambuye.” 11 Ambuye anamuwuza iye kuti, “Nyamuka, pita ku nyumba ya Yudasi imene ili pa Njira Yolunjika ndipo ukafunse za munthu wochokera ku Tarisisi dzina lake Saulo, pakuti akupemphera. 12 Ndipo waona mʼmasomphenya munthu, dzina lake Hananiya atabwera ndi kumusanjika manja kuti aonenso.” 13 Hananiya anayankha kuti, “Ambuye, ndinamva zambiri za munthu uyu ndi zonse zoyipa anachitira oyera mtima a ku Yerusalemu. 14 Ndipo wabwera kuno ndi ulamuliro wa akulu ansembe kuti adzamange onse amene amayitana pa dzina lanu.” 15 Koma Ambuye anati kwa Hananiya, “Pita! Munthu uyu ndi chida changa chosankhika chonyamulira dzina langa pamaso pa anthu a mitundu ina ndi mafumu awo ndiponso kwa anthu a Israeli. 16 Ine ndidzamuonetsa zowawa zonse zimene ayenera kumva chifukwa cha dzina langa.” 17 Pamenepo Hananiya ananyamuka ndi kukalowa mʼnyumbayo. Anamusanjika manja Sauloyo ndipo anati, “Mʼbale Saulo, Ambuye Yesu, amene anakuonekera pa msewu pamene umabwera kuno wandituma kuti uwonenso ndi kudzazidwa ndi Mzimu Woyera.” 18 Nthawi yomweyo mʼmaso mwa Saulo munachoka zinthu zokhala ngati mamba ansomba, ndipo anayambanso kuona. Iye anayimirira nabatizidwa, 19 ndipo atadya chakudya, anapezanso mphamvu.Saulo anakhala masiku angapo ndi ophunzira a ku Damasiko. 20 Posakhalitsa anayamba kulalikira mʼsunagoge kuti Yesu ndiye Mwana wa Mulungu. 21 Onse amene anamva iye akulalikira anadabwa ndipo anafunsa kuti, “Kodi uyu si munthu amene anayambitsa kuzunza okhulupirira ku mpingo wa ku Yerusalemu? Kodi siwabwera kuno kuti awamange ndi kuwapereka kwa akulu a ansembe?” 22 Koma mphamvu za Saulo zinali kukulirakulira ndipo anathetsa nzeru Ayuda okhala ku Damasiko powatsimikizira kuti Yesu ndi Mpulumutsi. 23 Patapita masiku ambiri, Ayuda anapangana zoti aphe Saulo, 24 koma iye anadziwa za chiwembucho. Anthu ankadikirira usana ndi usiku pa zipata za mzindawo kuti amuphe. 25 Koma ophunzira ake anamutenga usiku, namutsitsira kunja kwa mpandawo mʼdengu. 26 Saulo atafika ku Yerusalemu, anayesetsa kulowa mʼgulu la ophunzira koma onse anamuopa chifukwa sanakhulupirire kuti anali wophunziradi. 27 Koma Barnaba anamutenga napita naye kwa atumwi. Iye anawafotokozera iwo za mmene Saulo anaonera Ambuye pa njira paja, ndi kuti Ambuye anamuyankhula, ndi momwe analalikira ku Damasiko mʼdzina la Yesu mosaopa. 28 Kotero Saulo anakhala nawo nayendayenda mwaufulu mu Yerusalemu akulalikira molimba mtima mʼdzina la Ambuye. 29 Anayankhula ndi kutsutsana ndi Ayuda a Chihelene, koma iwo ankafuna kumupha. 30 Abale atadziwa zimenezi, anamutenga Saulo ndi kupita naye ku Kaisareya, ndipo anamutumiza ku Tarisisi. 31 Pamenepo mpingo wa ku Yudeya konse, ku Galileya ndi ku Samariya unakhala pamtendere, unalimbikitsidwa; ndi kupatsidwa mphamvu ndi Mzimu Woyera, unakula mʼchiwerengero, ndi kukhala moopa Ambuye. 32 Pamene Petro amayendera mpingo, anapita kukachezera oyera mtima a ku Luda. 33 Kumeneko anakapeza munthu dzina lake Eneya, wofa ziwalo amene anagona pa mphasa kwa zaka zisanu ndi zitatu. 34 Petro anati kwa iye, “Eneya, Yesu Khristu akukuchiritsa iwe, dzuka ndipo yalula mphasa yako.” Nthawi yomweyo Eneya anayimirira. 35 Anthu onse amene anakhala ku Luda ndi ku Sharoni anamuona ndipo anatembenukira kwa Ambuye. 36 Ku Yopa kunali wophunzira wina dzina lake Tabita (mʼChigriki amati Dorika) amene nthawi zonse ankachita zachifundo ndiponso kuthandiza osauka. 37 Nthawi imeneyi anadwala ndipo anamwalira, anasambitsa thupi lake, namugoneka mʼchipinda chammwamba. 38 Popeza ku Yopa kunali pafupi ndi Luda; pamene ophunzira anamva kuti Petro anali ku Luda, anatuma anthu awiri kuti akamudandaulire kuti, “Chonde bwerani kuno msanga!” 39 Petro ananyamuka, napita nawo, ndipo atafika anamutengera ku chipinda chammwamba. Amasiye onse anayima momuzungulira akulira ndi kumuonetsa mwinjiro ndi zovala zina zimene Dorika ankapanga akanali moyo. 40 Petro anatulutsa anthu onse mʼchipindamo; ndipo anagwada pansi ndi kupemphera. Anatembenukira mtembo uja nati, “Tabita, dzuka,” Tabita anatsekula maso ake, ndipo ataona Petro anakhala pansi. 41 Petro anamugwira dzanja, namuyimiritsa. Ndipo anayitana okhulupirira ndi amasiye namupereka wamoyo. 42 Zimenezi zinadziwika ku Yopa konse, ndipo anthu ambiri anakhulupirira Ambuye. 43 Petro anakhala ku Yopa kwa masiku ambiri kwa munthu wina, dzina lake Simoni, mmisiri wa zikopa.

In Other Versions

Acts 9 in the ANGEFD

Acts 9 in the ANTPNG2D

Acts 9 in the AS21

Acts 9 in the BAGH

Acts 9 in the BBPNG

Acts 9 in the BBT1E

Acts 9 in the BDS

Acts 9 in the BEV

Acts 9 in the BHAD

Acts 9 in the BIB

Acts 9 in the BLPT

Acts 9 in the BNT

Acts 9 in the BNTABOOT

Acts 9 in the BNTLV

Acts 9 in the BOATCB

Acts 9 in the BOATCB2

Acts 9 in the BOBCV

Acts 9 in the BOCNT

Acts 9 in the BOECS

Acts 9 in the BOHCB

Acts 9 in the BOHCV

Acts 9 in the BOHLNT

Acts 9 in the BOHNTLTAL

Acts 9 in the BOICB

Acts 9 in the BOILNTAP

Acts 9 in the BOITCV

Acts 9 in the BOKCV

Acts 9 in the BOKCV2

Acts 9 in the BOKHWOG

Acts 9 in the BOKSSV

Acts 9 in the BOLCB

Acts 9 in the BOLCB2

Acts 9 in the BOMCV

Acts 9 in the BONAV

Acts 9 in the BONCB

Acts 9 in the BONLT

Acts 9 in the BONUT2

Acts 9 in the BOPLNT

Acts 9 in the BOSCB

Acts 9 in the BOSNC

Acts 9 in the BOTLNT

Acts 9 in the BOVCB

Acts 9 in the BOYCB

Acts 9 in the BPBB

Acts 9 in the BPH

Acts 9 in the BSB

Acts 9 in the CCB

Acts 9 in the CUV

Acts 9 in the CUVS

Acts 9 in the DBT

Acts 9 in the DGDNT

Acts 9 in the DHNT

Acts 9 in the DNT

Acts 9 in the ELBE

Acts 9 in the EMTV

Acts 9 in the ESV

Acts 9 in the FBV

Acts 9 in the FEB

Acts 9 in the GGMNT

Acts 9 in the GNT

Acts 9 in the HARY

Acts 9 in the HNT

Acts 9 in the IRVA

Acts 9 in the IRVB

Acts 9 in the IRVG

Acts 9 in the IRVH

Acts 9 in the IRVK

Acts 9 in the IRVM

Acts 9 in the IRVM2

Acts 9 in the IRVO

Acts 9 in the IRVP

Acts 9 in the IRVT

Acts 9 in the IRVT2

Acts 9 in the IRVU

Acts 9 in the ISVN

Acts 9 in the JSNT

Acts 9 in the KAPI

Acts 9 in the KBT1ETNIK

Acts 9 in the KBV

Acts 9 in the KJV

Acts 9 in the KNFD

Acts 9 in the LBA

Acts 9 in the LBLA

Acts 9 in the LNT

Acts 9 in the LSV

Acts 9 in the MAAL

Acts 9 in the MBV

Acts 9 in the MBV2

Acts 9 in the MHNT

Acts 9 in the MKNFD

Acts 9 in the MNG

Acts 9 in the MNT

Acts 9 in the MNT2

Acts 9 in the MRS1T

Acts 9 in the NAA

Acts 9 in the NASB

Acts 9 in the NBLA

Acts 9 in the NBS

Acts 9 in the NBVTP

Acts 9 in the NET2

Acts 9 in the NIV11

Acts 9 in the NNT

Acts 9 in the NNT2

Acts 9 in the NNT3

Acts 9 in the PDDPT

Acts 9 in the PFNT

Acts 9 in the RMNT

Acts 9 in the SBIAS

Acts 9 in the SBIBS

Acts 9 in the SBIBS2

Acts 9 in the SBICS

Acts 9 in the SBIDS

Acts 9 in the SBIGS

Acts 9 in the SBIHS

Acts 9 in the SBIIS

Acts 9 in the SBIIS2

Acts 9 in the SBIIS3

Acts 9 in the SBIKS

Acts 9 in the SBIKS2

Acts 9 in the SBIMS

Acts 9 in the SBIOS

Acts 9 in the SBIPS

Acts 9 in the SBISS

Acts 9 in the SBITS

Acts 9 in the SBITS2

Acts 9 in the SBITS3

Acts 9 in the SBITS4

Acts 9 in the SBIUS

Acts 9 in the SBIVS

Acts 9 in the SBT

Acts 9 in the SBT1E

Acts 9 in the SCHL

Acts 9 in the SNT

Acts 9 in the SUSU

Acts 9 in the SUSU2

Acts 9 in the SYNO

Acts 9 in the TBIAOTANT

Acts 9 in the TBT1E

Acts 9 in the TBT1E2

Acts 9 in the TFTIP

Acts 9 in the TFTU

Acts 9 in the TGNTATF3T

Acts 9 in the THAI

Acts 9 in the TNFD

Acts 9 in the TNT

Acts 9 in the TNTIK

Acts 9 in the TNTIL

Acts 9 in the TNTIN

Acts 9 in the TNTIP

Acts 9 in the TNTIZ

Acts 9 in the TOMA

Acts 9 in the TTENT

Acts 9 in the UBG

Acts 9 in the UGV

Acts 9 in the UGV2

Acts 9 in the UGV3

Acts 9 in the VBL

Acts 9 in the VDCC

Acts 9 in the YALU

Acts 9 in the YAPE

Acts 9 in the YBVTP

Acts 9 in the ZBP