Daniel 10 (BOGWICC)
1 Chaka chachitatu cha Koresi mfumu ya Aperezi, Danieli amene ankatchedwa Belitesezara analandira mawu a vumbulutso. Uthenga wake unali woona ndipo anawumvetsa movutikira. Uthengawu anawumva kudzera mʼmasomphenya. 2 Pa nthawi imeneyi, ine Danieli ndinalira kwa masabata atatu. 3 Sindinadye chakudya chokoma; nyama ndi vinyo sizinakhudze milomo yanga ndi pangʼono pomwe; ndipo sindinadzole mafuta aliwonse mpaka patatha masabata atatu. 4 Pa tsiku la 24 la mwezi woyamba, nditayima mʼmbali mwa mtsinje waukulu wa Tigirisi, 5 ndinakweza maso ndipo ndinaona kuti pafupi ndi ine panali munthu wochokera ku Ufazi atavala zovala zosalala ndi lamba wa golide woyengeka bwino mʼchiwuno mwake. 6 Thupi lake linali ngati mwala wonyezimira, nkhope yake ngati chiphaliwali, maso ake ngati muni wowala, manja ndi miyendo yake ngati mkuwa wowala, ndipo mawu ake ngati liwu la chikhamu cha anthu. 7 Ine Danieli ndinali ndekha pamene ndinaona masomphenyawa; anthu amene anali ndi ine sanawaone, koma anadzazidwa ndi mantha kotero kuti anathawa ndi kukabisala. 8 Choncho ndinatsala ndekha, ndikuonetsetsa masomphenya a ulemererowa. Ndiye nkhope yanga inasinthika, ndinalefuka, ndipo ndinalibenso mphamvu. 9 Kenaka ndinamva iye akuyankhula, ndipo pamene ndinkamvetsera, ndinagwa chafufumimba ndi kugona tulo tofa nato. 10 Dzanja linandikhudza ndi kundinyamula ndipo ndinachita ngati kuwerama pa mawondo manja atagwira pansi. 11 Iye anati, “Danieli, iwe wokondedwa kwambiri, imirira ndipo uganizire mosamala mawu ndiyankhule kwa iwe, popeza tsopano ndatumidwa kwa iwe.” Atanena izi kwa ine ndinayimirira monjenjemera. 12 Ndipo iye anapitiriza nati, “Usachite mantha Danieli. Kuyambira tsiku loyamba pamene unatsimikiza mtima kuti umvetse zinthuzi ndi kudzichepetsa pamaso pa Mulungu wako, pempho lako linamveka ndipo ndabwera kudzayankha mapemphero akowo. 13 Koma mtsogoleri wa ufumu wa Peresiya ananditchingira pa masiku 21, kenaka Mikayeli, mmodzi mwa angelo akuluakulu anadza kudzandithandiza chifukwa ndinakhala komweko ndi mafumu a ku Peresiya. 14 Tsopano ndafika kuti ndidzakufotokozere zimene zidzachitika kwa anthu a mtundu wako kutsogolo. Ndipo pali masomphenya enanso okhudza nthawi imene ikudza.” 15 Pa nthawi yomwe ankanena izi kwa ine, ndinazolika nkhope yanga pansi kusowa chonena. 16 Kenaka wina wa maonekedwe ngati munthu anakhudza milomo yanga, ndipo ndinatsekula pakamwa panga ndi kuyamba kuyankhula. Ndinati kwa amene anayima patsogolo panga, “Ine ndasweka mtima chifukwa cha masomphenyawa mbuye wanga, ndipo ndalefuka. 17 Kodi ine mtumiki wamba wa mbuye wanga ndingathe bwanji kuyankhula ndi inu mbuye wanga? Mphamvu zanga zatha, ndipo ndikulephera kupuma.” 18 Kenaka wooneka ngati munthu uja anandikhudzanso ndipo anandipatsa mphamvu. 19 Iye anati, “Usachite mantha, munthu wokondedwa kwambiriwe. Mtendere ukhale ndi Iwe ndipo ukhale wolimba.”Atayankhula nane, ndinalimbikitsidwa ndipo ndinati, “Yankhulani Mbuye wanga, popeza mwandipatsa mphamvu.” 20 Ndipo iye anati, “Kodi ukudziwa chifukwa chimene ndabwerera kwa iwe? Ndiyamba ndabwerera kukamenyana ndi mtsogoleri wa ufumu wa Peresiya, ndipo ndikakanthana naye, kenaka mtsogoleri wa ufumu wa Grisi adzabwera. 21 Koma ndikuwuza zimene zalembedwa mʼbuku la zoona koma palibe wondithandiza kulimbana nawo kupatula Mikayeli, kalonga wako.”
In Other Versions
Daniel 10 in the ANGEFD
Daniel 10 in the ANTPNG2D
Daniel 10 in the AS21
Daniel 10 in the BAGH
Daniel 10 in the BBPNG
Daniel 10 in the BBT1E
Daniel 10 in the BDS
Daniel 10 in the BEV
Daniel 10 in the BHAD
Daniel 10 in the BIB
Daniel 10 in the BLPT
Daniel 10 in the BNT
Daniel 10 in the BNTABOOT
Daniel 10 in the BNTLV
Daniel 10 in the BOATCB
Daniel 10 in the BOATCB2
Daniel 10 in the BOBCV
Daniel 10 in the BOCNT
Daniel 10 in the BOECS
Daniel 10 in the BOHCB
Daniel 10 in the BOHCV
Daniel 10 in the BOHLNT
Daniel 10 in the BOHNTLTAL
Daniel 10 in the BOICB
Daniel 10 in the BOILNTAP
Daniel 10 in the BOITCV
Daniel 10 in the BOKCV
Daniel 10 in the BOKCV2
Daniel 10 in the BOKHWOG
Daniel 10 in the BOKSSV
Daniel 10 in the BOLCB
Daniel 10 in the BOLCB2
Daniel 10 in the BOMCV
Daniel 10 in the BONAV
Daniel 10 in the BONCB
Daniel 10 in the BONLT
Daniel 10 in the BONUT2
Daniel 10 in the BOPLNT
Daniel 10 in the BOSCB
Daniel 10 in the BOSNC
Daniel 10 in the BOTLNT
Daniel 10 in the BOVCB
Daniel 10 in the BOYCB
Daniel 10 in the BPBB
Daniel 10 in the BPH
Daniel 10 in the BSB
Daniel 10 in the CCB
Daniel 10 in the CUV
Daniel 10 in the CUVS
Daniel 10 in the DBT
Daniel 10 in the DGDNT
Daniel 10 in the DHNT
Daniel 10 in the DNT
Daniel 10 in the ELBE
Daniel 10 in the EMTV
Daniel 10 in the ESV
Daniel 10 in the FBV
Daniel 10 in the FEB
Daniel 10 in the GGMNT
Daniel 10 in the GNT
Daniel 10 in the HARY
Daniel 10 in the HNT
Daniel 10 in the IRVA
Daniel 10 in the IRVB
Daniel 10 in the IRVG
Daniel 10 in the IRVH
Daniel 10 in the IRVK
Daniel 10 in the IRVM
Daniel 10 in the IRVM2
Daniel 10 in the IRVO
Daniel 10 in the IRVP
Daniel 10 in the IRVT
Daniel 10 in the IRVT2
Daniel 10 in the IRVU
Daniel 10 in the ISVN
Daniel 10 in the JSNT
Daniel 10 in the KAPI
Daniel 10 in the KBT1ETNIK
Daniel 10 in the KBV
Daniel 10 in the KJV
Daniel 10 in the KNFD
Daniel 10 in the LBA
Daniel 10 in the LBLA
Daniel 10 in the LNT
Daniel 10 in the LSV
Daniel 10 in the MAAL
Daniel 10 in the MBV
Daniel 10 in the MBV2
Daniel 10 in the MHNT
Daniel 10 in the MKNFD
Daniel 10 in the MNG
Daniel 10 in the MNT
Daniel 10 in the MNT2
Daniel 10 in the MRS1T
Daniel 10 in the NAA
Daniel 10 in the NASB
Daniel 10 in the NBLA
Daniel 10 in the NBS
Daniel 10 in the NBVTP
Daniel 10 in the NET2
Daniel 10 in the NIV11
Daniel 10 in the NNT
Daniel 10 in the NNT2
Daniel 10 in the NNT3
Daniel 10 in the PDDPT
Daniel 10 in the PFNT
Daniel 10 in the RMNT
Daniel 10 in the SBIAS
Daniel 10 in the SBIBS
Daniel 10 in the SBIBS2
Daniel 10 in the SBICS
Daniel 10 in the SBIDS
Daniel 10 in the SBIGS
Daniel 10 in the SBIHS
Daniel 10 in the SBIIS
Daniel 10 in the SBIIS2
Daniel 10 in the SBIIS3
Daniel 10 in the SBIKS
Daniel 10 in the SBIKS2
Daniel 10 in the SBIMS
Daniel 10 in the SBIOS
Daniel 10 in the SBIPS
Daniel 10 in the SBISS
Daniel 10 in the SBITS
Daniel 10 in the SBITS2
Daniel 10 in the SBITS3
Daniel 10 in the SBITS4
Daniel 10 in the SBIUS
Daniel 10 in the SBIVS
Daniel 10 in the SBT
Daniel 10 in the SBT1E
Daniel 10 in the SCHL
Daniel 10 in the SNT
Daniel 10 in the SUSU
Daniel 10 in the SUSU2
Daniel 10 in the SYNO
Daniel 10 in the TBIAOTANT
Daniel 10 in the TBT1E
Daniel 10 in the TBT1E2
Daniel 10 in the TFTIP
Daniel 10 in the TFTU
Daniel 10 in the TGNTATF3T
Daniel 10 in the THAI
Daniel 10 in the TNFD
Daniel 10 in the TNT
Daniel 10 in the TNTIK
Daniel 10 in the TNTIL
Daniel 10 in the TNTIN
Daniel 10 in the TNTIP
Daniel 10 in the TNTIZ
Daniel 10 in the TOMA
Daniel 10 in the TTENT
Daniel 10 in the UBG
Daniel 10 in the UGV
Daniel 10 in the UGV2
Daniel 10 in the UGV3
Daniel 10 in the VBL
Daniel 10 in the VDCC
Daniel 10 in the YALU
Daniel 10 in the YAPE
Daniel 10 in the YBVTP
Daniel 10 in the ZBP