Deuteronomy 14 (BOGWICC)
1 Inu ndinu ana a Yehova Mulungu wanu. Osamadzichekacheka kapena kudzimeta pamphumi chifukwa cha abale anu amene amwalira, 2 pakuti ndinu anthu opatulika a Yehova Mulungu wanu. Pakati pa anthu onse pa dziko lonse lapansi, Yehova wasankha inu kuti chikhale chuma chake chamtengo wapatali. 3 Musamadye chinthu chilichonse chonyansa. 4 Nyama zomwe mukhoza kudya ndi izi: ngʼombe, nkhosa, mbuzi, 5 mbawala, gwape, mphoyo, mphalapala, ngoma, nyumbu ndi mbalale. 6 Nyama iliyonse imene ili ndi chipondero chogawikana pakati ndi yobzikula mukhoza kudya. 7 Komabe pakati pa nyama zimene zimabzikula kapena zogawikana zipondero, zimene simukuyenera kudya ndi ngamira, kalulu ndi mbira. Zimenezi ngakhale zimabzikula, zipondero zake sizogawikana, choncho ndi zodetsedwa, musadye. 8 Nkhumba simabzikula ndi yodetsedwanso ngakhale ili ndi zipondero zogawikana. Musamadye nyama yake kapena kukhudza imene yafa. 9 Mwa zamoyo zonse zimene zimakhala mʼmadzi, mukhoza kudya chilichonse chimene chili ndi minga ya pa msana ndi mamba. 10 Koma chilichonse chimene chilibe minga ya pa msana ndi mamba musadye pakuti nʼchodetsedwa. 11 Mukhoza kudya mbalame iliyonse yoyenera kudya. 12 Koma simukuyenera kudya izi: mphungu, nkhwazi, mwimba, 13 nankapakapa, akamtema, akhungubwi a mitundu yonse, ndi mtundu uliwonse wa miphamba, 14 mtundu uliwonse wa khwangwala, 15 kadzidzi wamphondo, kadzidzi wodzuma, chipudo, mtundu uliwonse wa akabawi, 16 kadzidzi wamngʼono, chiswankhono ndi mantchichi, 17 tsekwe, vuwo, dembo, 18 indwa, zimeza za mitundu yonse, nsadzu ndi mleme. 19 Zowuluka zonse za miyendo inayi ndi zodetsedwa. Musamadye zimenezi. 20 Koma chowuluka chilichonse choyenera kudya mukhoza kudya. 21 Musamadye chilichonse chimene mwachipeza chofaifa. Mukhoza kupatsa mlendo amene akukhala mu mzinda wina uliwonse wa mizinda yanu. Iyeyo akhoza kudya kapena mukhoza kugulitsa kwa wina aliyense amene sali wa mtundu wanu. Koma inu ndinu anthu opatulika a Yehova Mulungu wanu.Musamaphike mwana wambuzi mu mkaka wa mayi wake. 22 Muzionetsetsa kuti mukupatula chakhumi pa zokolola zanu chaka chilichonse. 23 Muzidyera chakhumi cha tirigu wanu, vinyo wanu watsopano ndi mafuta, ndi ana oyamba kubadwa a ngʼombe zanu pamaso pa Yehova Mulungu wanu pa malo amene adzasankhe ngati kokhalako dzina lake, kuti muphunzire kuopa Yehova Mulungu wanu. 24 Koma ngati malo amenewa ali kutali kwambiri ndipo kuti inu mwadalitsidwa ndi Yehova Mulungu wanu, ndipo simungathe kunyamula chakhumi chanu (chifukwa chakuti malo amene Yehova adzasankha kukayikako dzina lake ali kutali kwambiri), 25 ndiye musinthitse chakhumi chanucho ndi siliva, ndipo mutenge silivayo ndi kupita naye kumalo kumene Yehova Mulungu wanu adzasankhe. 26 Gwiritsani ntchito silivayo kugula chilichonse chimene muchifuna monga ngʼombe, nkhosa, vinyo kapena zakumwa zina zosasitsa, kapena china chilichonse chimene muchifuna. Ndipo inu ndi anthu a pa banja panu mudzazidyera komweko pamaso pa Yehova Mulungu wanu ndi kukondwera. 27 Alevi okhala mʼmizinda yanu musaleke kuwathandiza popeza alibe gawo lawo la chuma kapena cholowa chawochawo. 28 Kumapeto kwa zaka zitatu zilizonse muzibweretsa zakhumi zonse pa zokolola za chaka chimenecho ndi kuzisunga mʼmidzi yanu, 29 kuti Alevi (amene alibe gawo lawo la chuma kapena cholowa chawochawo), alendo, ana ndi akazi amasiye, amene akukhala mʼmizinda yanu akhoza kubwera kudzadya ndi kukhuta. Ndipo kuti akutero Yehova Mulungu wanu akudalitseni pa ntchito zanu zonse.
In Other Versions
Deuteronomy 14 in the ANGEFD
Deuteronomy 14 in the ANTPNG2D
Deuteronomy 14 in the AS21
Deuteronomy 14 in the BAGH
Deuteronomy 14 in the BBPNG
Deuteronomy 14 in the BBT1E
Deuteronomy 14 in the BDS
Deuteronomy 14 in the BEV
Deuteronomy 14 in the BHAD
Deuteronomy 14 in the BIB
Deuteronomy 14 in the BLPT
Deuteronomy 14 in the BNT
Deuteronomy 14 in the BNTABOOT
Deuteronomy 14 in the BNTLV
Deuteronomy 14 in the BOATCB
Deuteronomy 14 in the BOATCB2
Deuteronomy 14 in the BOBCV
Deuteronomy 14 in the BOCNT
Deuteronomy 14 in the BOECS
Deuteronomy 14 in the BOHCB
Deuteronomy 14 in the BOHCV
Deuteronomy 14 in the BOHLNT
Deuteronomy 14 in the BOHNTLTAL
Deuteronomy 14 in the BOICB
Deuteronomy 14 in the BOILNTAP
Deuteronomy 14 in the BOITCV
Deuteronomy 14 in the BOKCV
Deuteronomy 14 in the BOKCV2
Deuteronomy 14 in the BOKHWOG
Deuteronomy 14 in the BOKSSV
Deuteronomy 14 in the BOLCB
Deuteronomy 14 in the BOLCB2
Deuteronomy 14 in the BOMCV
Deuteronomy 14 in the BONAV
Deuteronomy 14 in the BONCB
Deuteronomy 14 in the BONLT
Deuteronomy 14 in the BONUT2
Deuteronomy 14 in the BOPLNT
Deuteronomy 14 in the BOSCB
Deuteronomy 14 in the BOSNC
Deuteronomy 14 in the BOTLNT
Deuteronomy 14 in the BOVCB
Deuteronomy 14 in the BOYCB
Deuteronomy 14 in the BPBB
Deuteronomy 14 in the BPH
Deuteronomy 14 in the BSB
Deuteronomy 14 in the CCB
Deuteronomy 14 in the CUV
Deuteronomy 14 in the CUVS
Deuteronomy 14 in the DBT
Deuteronomy 14 in the DGDNT
Deuteronomy 14 in the DHNT
Deuteronomy 14 in the DNT
Deuteronomy 14 in the ELBE
Deuteronomy 14 in the EMTV
Deuteronomy 14 in the ESV
Deuteronomy 14 in the FBV
Deuteronomy 14 in the FEB
Deuteronomy 14 in the GGMNT
Deuteronomy 14 in the GNT
Deuteronomy 14 in the HARY
Deuteronomy 14 in the HNT
Deuteronomy 14 in the IRVA
Deuteronomy 14 in the IRVB
Deuteronomy 14 in the IRVG
Deuteronomy 14 in the IRVH
Deuteronomy 14 in the IRVK
Deuteronomy 14 in the IRVM
Deuteronomy 14 in the IRVM2
Deuteronomy 14 in the IRVO
Deuteronomy 14 in the IRVP
Deuteronomy 14 in the IRVT
Deuteronomy 14 in the IRVT2
Deuteronomy 14 in the IRVU
Deuteronomy 14 in the ISVN
Deuteronomy 14 in the JSNT
Deuteronomy 14 in the KAPI
Deuteronomy 14 in the KBT1ETNIK
Deuteronomy 14 in the KBV
Deuteronomy 14 in the KJV
Deuteronomy 14 in the KNFD
Deuteronomy 14 in the LBA
Deuteronomy 14 in the LBLA
Deuteronomy 14 in the LNT
Deuteronomy 14 in the LSV
Deuteronomy 14 in the MAAL
Deuteronomy 14 in the MBV
Deuteronomy 14 in the MBV2
Deuteronomy 14 in the MHNT
Deuteronomy 14 in the MKNFD
Deuteronomy 14 in the MNG
Deuteronomy 14 in the MNT
Deuteronomy 14 in the MNT2
Deuteronomy 14 in the MRS1T
Deuteronomy 14 in the NAA
Deuteronomy 14 in the NASB
Deuteronomy 14 in the NBLA
Deuteronomy 14 in the NBS
Deuteronomy 14 in the NBVTP
Deuteronomy 14 in the NET2
Deuteronomy 14 in the NIV11
Deuteronomy 14 in the NNT
Deuteronomy 14 in the NNT2
Deuteronomy 14 in the NNT3
Deuteronomy 14 in the PDDPT
Deuteronomy 14 in the PFNT
Deuteronomy 14 in the RMNT
Deuteronomy 14 in the SBIAS
Deuteronomy 14 in the SBIBS
Deuteronomy 14 in the SBIBS2
Deuteronomy 14 in the SBICS
Deuteronomy 14 in the SBIDS
Deuteronomy 14 in the SBIGS
Deuteronomy 14 in the SBIHS
Deuteronomy 14 in the SBIIS
Deuteronomy 14 in the SBIIS2
Deuteronomy 14 in the SBIIS3
Deuteronomy 14 in the SBIKS
Deuteronomy 14 in the SBIKS2
Deuteronomy 14 in the SBIMS
Deuteronomy 14 in the SBIOS
Deuteronomy 14 in the SBIPS
Deuteronomy 14 in the SBISS
Deuteronomy 14 in the SBITS
Deuteronomy 14 in the SBITS2
Deuteronomy 14 in the SBITS3
Deuteronomy 14 in the SBITS4
Deuteronomy 14 in the SBIUS
Deuteronomy 14 in the SBIVS
Deuteronomy 14 in the SBT
Deuteronomy 14 in the SBT1E
Deuteronomy 14 in the SCHL
Deuteronomy 14 in the SNT
Deuteronomy 14 in the SUSU
Deuteronomy 14 in the SUSU2
Deuteronomy 14 in the SYNO
Deuteronomy 14 in the TBIAOTANT
Deuteronomy 14 in the TBT1E
Deuteronomy 14 in the TBT1E2
Deuteronomy 14 in the TFTIP
Deuteronomy 14 in the TFTU
Deuteronomy 14 in the TGNTATF3T
Deuteronomy 14 in the THAI
Deuteronomy 14 in the TNFD
Deuteronomy 14 in the TNT
Deuteronomy 14 in the TNTIK
Deuteronomy 14 in the TNTIL
Deuteronomy 14 in the TNTIN
Deuteronomy 14 in the TNTIP
Deuteronomy 14 in the TNTIZ
Deuteronomy 14 in the TOMA
Deuteronomy 14 in the TTENT
Deuteronomy 14 in the UBG
Deuteronomy 14 in the UGV
Deuteronomy 14 in the UGV2
Deuteronomy 14 in the UGV3
Deuteronomy 14 in the VBL
Deuteronomy 14 in the VDCC
Deuteronomy 14 in the YALU
Deuteronomy 14 in the YAPE
Deuteronomy 14 in the YBVTP
Deuteronomy 14 in the ZBP