Deuteronomy 15 (BOGWICC)
1 Kumapeto kwa zaka zisanu ndi ziwiri zilizonse, muzikhululukirana ngongole. 2 Zimenezi muzichita motere: wobwereketsa aliyense adzakhululukira ngongole imene anabwereketsa kwa Mwisraeli mnzake. Iye asadzafunenso kuti Mwisraeli mnzakeyo kapena mʼbale wake amubwezere chifukwa nthawi ya Ambuye yokhululukirana ngongole yalengezedwa. 3 Mukhoza kulonjerera ngongole kwa mlendo, koma mukhululukire ngongole ina iliyonse imene mʼbale wanu ali nayo. 4 Komabe pasadzakhale wosauka pakati panu chifukwa Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani kwambiri mʼdziko limene adzakupatsani kuti likhale lanu ngati cholowa chanu. 5 Adzakudalitsani pokhapokha ngati mudzamveradi Yehova Mulungu wanu posunga ndi kutsatira malamulo onse amene ndikukupatsani lero. 6 Pakuti Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani monga analonjeza, ndipo inu mudzabwereketsa chuma kwa mitundu yambiri ya anthu koma inu simudzabwereka kwa aliyense. Mudzalamulira mitundu yambiri ya anthu koma inuyo palibe amene adzakulamulireni. 7 Ngati pali mʼbale wanu wina wosauka mu mzinda wanu wina uliwonse mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, musawumitse mitima yanu kapena kuchita kaligwiritsa kwa mʼbale wanu wosaukayo. 8 Koma mukhale ofewa manja ndipo mumukongoze mʼbale wanu momasuka pa chilichonse chimene akufuna. 9 Musayesere ndi pangʼono pomwe kusunga maganizo oyipa awa mu mtima mwanu: “Chaka chachisanu ndi chiwiri, chaka chokhululukirana ngongole, chayandikira,” kuti musaonetse mtima woyipa kwa mʼbale wanu wosauka nʼkusamupatsa chilichonse. Iye angadzakunenereni inu mlandu kwa Ambuye, ndipo mudzapezeka wochimwa. 10 Mumupatse iye mowolowamanja ndipo muchite zimenezi mosasungira kanthu kumtima. Tsono chifukwa cha zimenezi, Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani pa ntchito zanu zonse ndi pa chilichonse chimene mukhudza. 11 Anthu osauka sadzatha mʼdziko lanu. Chomwecho ndikukulamulani kuti mukhale ofewa manja kwa abale anu ndi kwa osauka, osowa mʼdziko mwanu. 12 Ngati mʼbale wanu wamwamuna kapena wamkazi adzigulitsa yekha kwa inu, nakugwirirani ntchito zaka zisanu ndi chimodzi, muzimumasula mʼchaka cha chisanu ndi chiwiri. 13 Ndipo pamene mumumasula, musangomulola apite chimanjamanja. 14 Mumupatse mowolowamanja zochokera pa ziweto zanu, kopunthira tirigu ndi kopsinyira vinyo. Inu mumupatse iye monga Yehova Mulungu wanu wakudalitsirani. 15 Kumbukirani kuti munali akapolo mʼdziko la Igupto ndipo Yehova Mulungu wanu anakupulumutsani. Nʼchifukwa chake ndikukupatsani lamulo ili lero lino. 16 Koma ngati kapoloyo akuwuzani kuti, “Ine sindikufuna kumasulidwa,” chifukwa choti wakukondani inuyo pamodzi ndi banja lanu ndiponso kuti kwamukomera iyeyo kuti azikhalabe nanu, 17 pamenepo muzitenga chobowolera chachitsulo ndi kubowola khutu lake pa chitseko, ndipo mukatero adzakhala kapolo wanu moyo wake wonse. Mdzakazi wanu muzimuchitanso chimodzimodzi. 18 Musaone ngati chopweteka kumasula wantchito wanu, chifukwa ntchito imene wayigwira pa zaka zisanu ndi chimodzi zimenezi ndi yopindula kawiri pa ntchito imene akanagwira waganyu chabe. Ndipo Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani pa chilichonse chimene mukuchita. 19 Mumupatulire Yehova Mulungu wanu choyamba kubadwa chachimuna chilichonse pa ngʼombe ndi nkhosa zanu. Musamazigwiritse ntchito ngʼombe zoyamba kubadwa kapena kumeta nkhosa zoyamba kubadwa. 20 Inuyo ndi banja lanu, chaka chilichonse muzizidya zimenezi pamaso pa Yehova Mulungu wanu pa malo amene Iye adzasankhe. 21 Ngati chiweto chili ndi chilema monga kulumala kapena chosaona, kapena ngati chili ndi cholakwika chachikulu chilichonse, musachipereke nsembe kwa Yehova Mulungu wanu. 22 Muzichidya mʼmizinda yanuyanu. Onse odetsedwa monga mwa mwambo ndi oyeretsedwa omwe akhoza kuchidya monga akudya gwape kapena mbawala. 23 Koma musadye magazi ake. Muwathire pansi ngati madzi.
In Other Versions
Deuteronomy 15 in the ANGEFD
Deuteronomy 15 in the ANTPNG2D
Deuteronomy 15 in the AS21
Deuteronomy 15 in the BAGH
Deuteronomy 15 in the BBPNG
Deuteronomy 15 in the BBT1E
Deuteronomy 15 in the BDS
Deuteronomy 15 in the BEV
Deuteronomy 15 in the BHAD
Deuteronomy 15 in the BIB
Deuteronomy 15 in the BLPT
Deuteronomy 15 in the BNT
Deuteronomy 15 in the BNTABOOT
Deuteronomy 15 in the BNTLV
Deuteronomy 15 in the BOATCB
Deuteronomy 15 in the BOATCB2
Deuteronomy 15 in the BOBCV
Deuteronomy 15 in the BOCNT
Deuteronomy 15 in the BOECS
Deuteronomy 15 in the BOHCB
Deuteronomy 15 in the BOHCV
Deuteronomy 15 in the BOHLNT
Deuteronomy 15 in the BOHNTLTAL
Deuteronomy 15 in the BOICB
Deuteronomy 15 in the BOILNTAP
Deuteronomy 15 in the BOITCV
Deuteronomy 15 in the BOKCV
Deuteronomy 15 in the BOKCV2
Deuteronomy 15 in the BOKHWOG
Deuteronomy 15 in the BOKSSV
Deuteronomy 15 in the BOLCB
Deuteronomy 15 in the BOLCB2
Deuteronomy 15 in the BOMCV
Deuteronomy 15 in the BONAV
Deuteronomy 15 in the BONCB
Deuteronomy 15 in the BONLT
Deuteronomy 15 in the BONUT2
Deuteronomy 15 in the BOPLNT
Deuteronomy 15 in the BOSCB
Deuteronomy 15 in the BOSNC
Deuteronomy 15 in the BOTLNT
Deuteronomy 15 in the BOVCB
Deuteronomy 15 in the BOYCB
Deuteronomy 15 in the BPBB
Deuteronomy 15 in the BPH
Deuteronomy 15 in the BSB
Deuteronomy 15 in the CCB
Deuteronomy 15 in the CUV
Deuteronomy 15 in the CUVS
Deuteronomy 15 in the DBT
Deuteronomy 15 in the DGDNT
Deuteronomy 15 in the DHNT
Deuteronomy 15 in the DNT
Deuteronomy 15 in the ELBE
Deuteronomy 15 in the EMTV
Deuteronomy 15 in the ESV
Deuteronomy 15 in the FBV
Deuteronomy 15 in the FEB
Deuteronomy 15 in the GGMNT
Deuteronomy 15 in the GNT
Deuteronomy 15 in the HARY
Deuteronomy 15 in the HNT
Deuteronomy 15 in the IRVA
Deuteronomy 15 in the IRVB
Deuteronomy 15 in the IRVG
Deuteronomy 15 in the IRVH
Deuteronomy 15 in the IRVK
Deuteronomy 15 in the IRVM
Deuteronomy 15 in the IRVM2
Deuteronomy 15 in the IRVO
Deuteronomy 15 in the IRVP
Deuteronomy 15 in the IRVT
Deuteronomy 15 in the IRVT2
Deuteronomy 15 in the IRVU
Deuteronomy 15 in the ISVN
Deuteronomy 15 in the JSNT
Deuteronomy 15 in the KAPI
Deuteronomy 15 in the KBT1ETNIK
Deuteronomy 15 in the KBV
Deuteronomy 15 in the KJV
Deuteronomy 15 in the KNFD
Deuteronomy 15 in the LBA
Deuteronomy 15 in the LBLA
Deuteronomy 15 in the LNT
Deuteronomy 15 in the LSV
Deuteronomy 15 in the MAAL
Deuteronomy 15 in the MBV
Deuteronomy 15 in the MBV2
Deuteronomy 15 in the MHNT
Deuteronomy 15 in the MKNFD
Deuteronomy 15 in the MNG
Deuteronomy 15 in the MNT
Deuteronomy 15 in the MNT2
Deuteronomy 15 in the MRS1T
Deuteronomy 15 in the NAA
Deuteronomy 15 in the NASB
Deuteronomy 15 in the NBLA
Deuteronomy 15 in the NBS
Deuteronomy 15 in the NBVTP
Deuteronomy 15 in the NET2
Deuteronomy 15 in the NIV11
Deuteronomy 15 in the NNT
Deuteronomy 15 in the NNT2
Deuteronomy 15 in the NNT3
Deuteronomy 15 in the PDDPT
Deuteronomy 15 in the PFNT
Deuteronomy 15 in the RMNT
Deuteronomy 15 in the SBIAS
Deuteronomy 15 in the SBIBS
Deuteronomy 15 in the SBIBS2
Deuteronomy 15 in the SBICS
Deuteronomy 15 in the SBIDS
Deuteronomy 15 in the SBIGS
Deuteronomy 15 in the SBIHS
Deuteronomy 15 in the SBIIS
Deuteronomy 15 in the SBIIS2
Deuteronomy 15 in the SBIIS3
Deuteronomy 15 in the SBIKS
Deuteronomy 15 in the SBIKS2
Deuteronomy 15 in the SBIMS
Deuteronomy 15 in the SBIOS
Deuteronomy 15 in the SBIPS
Deuteronomy 15 in the SBISS
Deuteronomy 15 in the SBITS
Deuteronomy 15 in the SBITS2
Deuteronomy 15 in the SBITS3
Deuteronomy 15 in the SBITS4
Deuteronomy 15 in the SBIUS
Deuteronomy 15 in the SBIVS
Deuteronomy 15 in the SBT
Deuteronomy 15 in the SBT1E
Deuteronomy 15 in the SCHL
Deuteronomy 15 in the SNT
Deuteronomy 15 in the SUSU
Deuteronomy 15 in the SUSU2
Deuteronomy 15 in the SYNO
Deuteronomy 15 in the TBIAOTANT
Deuteronomy 15 in the TBT1E
Deuteronomy 15 in the TBT1E2
Deuteronomy 15 in the TFTIP
Deuteronomy 15 in the TFTU
Deuteronomy 15 in the TGNTATF3T
Deuteronomy 15 in the THAI
Deuteronomy 15 in the TNFD
Deuteronomy 15 in the TNT
Deuteronomy 15 in the TNTIK
Deuteronomy 15 in the TNTIL
Deuteronomy 15 in the TNTIN
Deuteronomy 15 in the TNTIP
Deuteronomy 15 in the TNTIZ
Deuteronomy 15 in the TOMA
Deuteronomy 15 in the TTENT
Deuteronomy 15 in the UBG
Deuteronomy 15 in the UGV
Deuteronomy 15 in the UGV2
Deuteronomy 15 in the UGV3
Deuteronomy 15 in the VBL
Deuteronomy 15 in the VDCC
Deuteronomy 15 in the YALU
Deuteronomy 15 in the YAPE
Deuteronomy 15 in the YBVTP
Deuteronomy 15 in the ZBP