Deuteronomy 21 (BOGWICC)
1 Ngati munthu apezeka ataphedwa mʼmunda mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kukhala lanu koma inu osadziwa amene wamupha, 2 akuluakulu anu ndi oweruza adzapite ndi kuyeza kutalikirana kuchokera pamene pali mtembowo ndi mizinda yoyandikira. 3 Kenaka akuluakulu a mzinda wapafupi kwambiri ndi mtembowo adzatenge ngʼombe imene sinagwirepo ntchito kapena kuvalapo goli 4 ndi kuyikusira ku chigwa chimene sichinalimidwepo ndiponso kumene kuli mtsinje woyenda. Ku chigwa kumeneko ayenera kukayithyola khosi ngʼombeyo. 5 Ansembe, ana a Aaroni, adzapite patsogolo pangʼono, popeza ndiwo amene Yehova Mulungu wanu anawasankha kuti azitumikira, kupereka mdalitso mʼdzina la Yehova ndi kugamula milandu yonse yamikangano ndi yovulazana. 6 Kenaka akuluakulu a mzinda wapafupi kwambiri ndi mtembowo adzasamba mʼmanja pamwamba pa ngʼombe yothyoledwa khosi ija, 7 nadzatsimikiza kuti, “Manja athu sanakhetse magazi awa ndipo sitinaonerere kuphedwako. 8 Yehova, landirani nsembe yopepesa ya anthu anu Aisraeli amene munawapulumutsa, ndipo muwakhululukire tchimo la kupha munthu wosalakwa.” Mukatero ndiye kuti adzapezeka kuti ndi osalakwa. 9 Kotero mudzadzichotsera nokha tchimo lokhetsa magazi wosalakwa, popeza mwachita zoyenera pamaso pa Yehova. 10 Mukapita kukachita nkhondo ndi adani anu, Yehova Mulungu wanu nawapereka adani anuwo mʼmanja mwanu muwagwira ukapolo, 11 ndiye ngati muona mkazi wokongola pakati pa ogwidwawo nakutengani mtima, mukhoza kumutenga kuti akhale mkazi wanu. 12 Mumutengere ku nyumba kwanu, kumumeta tsitsi lake, mumuwenge zikhadabo zake 13 ndipo avulidwe zovala zimene anagwidwa nazo. Atakhala mʼnyumba mwanu nalira maliro a abambo ndi amayi ake kwa mwezi wathunthu, ndiye mukhoza kupita kwa iye ndi kukhala mwamuna wake ndipo iyeyo adzakhala mkazi wanu. 14 Ngati simukukondweretsedwa naye, muloleni kuti apite kumene afuna. Musamugulitse kapena kumuzunza ngati kapolo, popeza mwamuchotsa ulemu. 15 Ngati munthu ali ndi akazi awiri, nakonda wina koposa mnzake, onsewa ndikubereka ana aamuna koma woyamba nakhala mwana wa mkazi amene samukondayo, 16 akamagawa chuma chake akanali moyo kwa ana akewo, asapereke ufulu wa mwana woyamba kubadwa kwa mwana wamwamuna wa mkazi amene amamukonda mʼmalo mwa mwana wake woyamba kubadwa weniweni amene ndi mwana wamkazi amene samukonda. 17 Iye ayenera kuonetsa kuti mwana wake wamwamuna wa mkazi wosakondedwayo ndiye woyamba kubadwa pomupatsa miyeso iwiri ya zonse zimene ali nazo. Mwana wamwamuna ameneyo ndiye chizindikiro cha mphamvu za abambo ake. Ufulu wokhala mwana wamwamuna woyamba ndi wake. 18 Ngati munthu ali ndi mwana wamwamuna wosamvera ndi wowukira amene samvera a abambo ake ndi amayi ake akamuweruza, 19 abambo ndi amayi ake amugwire ndi kupita naye kwa akuluakulu ku chipata cha mzinda wake ndipo 20 akawawuze akuluakuluwo kuti, “Mwana wathu wamwamunayu ndi wosamva ndi wowukira. Iyeyu satimvera. Ndi mwana wadyera komanso ndi chidakwa.” 21 Pamenepo anthu onse a mu mzinda wake adzamuphe ndi miyala. Muyenera kuchotsa zoyipa pakati panu. Aisraeli onse adzamva zimenezi ndipo adzachita mantha. 22 Ngati munthu wopezeka ndi mlandu wopha mnzake waphedwa ndipo mtembo wake wapachikidwa pamtengo, 23 musasiye mtembowo pa mtengopo usiku wonse. Muonetsetse kuti mwakawukwirira tsiku lomwelo, chifukwa aliyense wopachikidwa pamtengo ndi wotembereredwa ndi Mulungu. Musayipitse dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani ngati cholowa chanu.
In Other Versions
Deuteronomy 21 in the ANGEFD
Deuteronomy 21 in the ANTPNG2D
Deuteronomy 21 in the AS21
Deuteronomy 21 in the BAGH
Deuteronomy 21 in the BBPNG
Deuteronomy 21 in the BBT1E
Deuteronomy 21 in the BDS
Deuteronomy 21 in the BEV
Deuteronomy 21 in the BHAD
Deuteronomy 21 in the BIB
Deuteronomy 21 in the BLPT
Deuteronomy 21 in the BNT
Deuteronomy 21 in the BNTABOOT
Deuteronomy 21 in the BNTLV
Deuteronomy 21 in the BOATCB
Deuteronomy 21 in the BOATCB2
Deuteronomy 21 in the BOBCV
Deuteronomy 21 in the BOCNT
Deuteronomy 21 in the BOECS
Deuteronomy 21 in the BOHCB
Deuteronomy 21 in the BOHCV
Deuteronomy 21 in the BOHLNT
Deuteronomy 21 in the BOHNTLTAL
Deuteronomy 21 in the BOICB
Deuteronomy 21 in the BOILNTAP
Deuteronomy 21 in the BOITCV
Deuteronomy 21 in the BOKCV
Deuteronomy 21 in the BOKCV2
Deuteronomy 21 in the BOKHWOG
Deuteronomy 21 in the BOKSSV
Deuteronomy 21 in the BOLCB
Deuteronomy 21 in the BOLCB2
Deuteronomy 21 in the BOMCV
Deuteronomy 21 in the BONAV
Deuteronomy 21 in the BONCB
Deuteronomy 21 in the BONLT
Deuteronomy 21 in the BONUT2
Deuteronomy 21 in the BOPLNT
Deuteronomy 21 in the BOSCB
Deuteronomy 21 in the BOSNC
Deuteronomy 21 in the BOTLNT
Deuteronomy 21 in the BOVCB
Deuteronomy 21 in the BOYCB
Deuteronomy 21 in the BPBB
Deuteronomy 21 in the BPH
Deuteronomy 21 in the BSB
Deuteronomy 21 in the CCB
Deuteronomy 21 in the CUV
Deuteronomy 21 in the CUVS
Deuteronomy 21 in the DBT
Deuteronomy 21 in the DGDNT
Deuteronomy 21 in the DHNT
Deuteronomy 21 in the DNT
Deuteronomy 21 in the ELBE
Deuteronomy 21 in the EMTV
Deuteronomy 21 in the ESV
Deuteronomy 21 in the FBV
Deuteronomy 21 in the FEB
Deuteronomy 21 in the GGMNT
Deuteronomy 21 in the GNT
Deuteronomy 21 in the HARY
Deuteronomy 21 in the HNT
Deuteronomy 21 in the IRVA
Deuteronomy 21 in the IRVB
Deuteronomy 21 in the IRVG
Deuteronomy 21 in the IRVH
Deuteronomy 21 in the IRVK
Deuteronomy 21 in the IRVM
Deuteronomy 21 in the IRVM2
Deuteronomy 21 in the IRVO
Deuteronomy 21 in the IRVP
Deuteronomy 21 in the IRVT
Deuteronomy 21 in the IRVT2
Deuteronomy 21 in the IRVU
Deuteronomy 21 in the ISVN
Deuteronomy 21 in the JSNT
Deuteronomy 21 in the KAPI
Deuteronomy 21 in the KBT1ETNIK
Deuteronomy 21 in the KBV
Deuteronomy 21 in the KJV
Deuteronomy 21 in the KNFD
Deuteronomy 21 in the LBA
Deuteronomy 21 in the LBLA
Deuteronomy 21 in the LNT
Deuteronomy 21 in the LSV
Deuteronomy 21 in the MAAL
Deuteronomy 21 in the MBV
Deuteronomy 21 in the MBV2
Deuteronomy 21 in the MHNT
Deuteronomy 21 in the MKNFD
Deuteronomy 21 in the MNG
Deuteronomy 21 in the MNT
Deuteronomy 21 in the MNT2
Deuteronomy 21 in the MRS1T
Deuteronomy 21 in the NAA
Deuteronomy 21 in the NASB
Deuteronomy 21 in the NBLA
Deuteronomy 21 in the NBS
Deuteronomy 21 in the NBVTP
Deuteronomy 21 in the NET2
Deuteronomy 21 in the NIV11
Deuteronomy 21 in the NNT
Deuteronomy 21 in the NNT2
Deuteronomy 21 in the NNT3
Deuteronomy 21 in the PDDPT
Deuteronomy 21 in the PFNT
Deuteronomy 21 in the RMNT
Deuteronomy 21 in the SBIAS
Deuteronomy 21 in the SBIBS
Deuteronomy 21 in the SBIBS2
Deuteronomy 21 in the SBICS
Deuteronomy 21 in the SBIDS
Deuteronomy 21 in the SBIGS
Deuteronomy 21 in the SBIHS
Deuteronomy 21 in the SBIIS
Deuteronomy 21 in the SBIIS2
Deuteronomy 21 in the SBIIS3
Deuteronomy 21 in the SBIKS
Deuteronomy 21 in the SBIKS2
Deuteronomy 21 in the SBIMS
Deuteronomy 21 in the SBIOS
Deuteronomy 21 in the SBIPS
Deuteronomy 21 in the SBISS
Deuteronomy 21 in the SBITS
Deuteronomy 21 in the SBITS2
Deuteronomy 21 in the SBITS3
Deuteronomy 21 in the SBITS4
Deuteronomy 21 in the SBIUS
Deuteronomy 21 in the SBIVS
Deuteronomy 21 in the SBT
Deuteronomy 21 in the SBT1E
Deuteronomy 21 in the SCHL
Deuteronomy 21 in the SNT
Deuteronomy 21 in the SUSU
Deuteronomy 21 in the SUSU2
Deuteronomy 21 in the SYNO
Deuteronomy 21 in the TBIAOTANT
Deuteronomy 21 in the TBT1E
Deuteronomy 21 in the TBT1E2
Deuteronomy 21 in the TFTIP
Deuteronomy 21 in the TFTU
Deuteronomy 21 in the TGNTATF3T
Deuteronomy 21 in the THAI
Deuteronomy 21 in the TNFD
Deuteronomy 21 in the TNT
Deuteronomy 21 in the TNTIK
Deuteronomy 21 in the TNTIL
Deuteronomy 21 in the TNTIN
Deuteronomy 21 in the TNTIP
Deuteronomy 21 in the TNTIZ
Deuteronomy 21 in the TOMA
Deuteronomy 21 in the TTENT
Deuteronomy 21 in the UBG
Deuteronomy 21 in the UGV
Deuteronomy 21 in the UGV2
Deuteronomy 21 in the UGV3
Deuteronomy 21 in the VBL
Deuteronomy 21 in the VDCC
Deuteronomy 21 in the YALU
Deuteronomy 21 in the YAPE
Deuteronomy 21 in the YBVTP
Deuteronomy 21 in the ZBP