Deuteronomy 6 (BOGWICC)

1 Awa ndi malamulo, malangizo ndi ziphunzitso zimene Yehova Mulungu wanu anandilamula kuti ndikuphunzitseni kuti mukawatsatire mʼdziko limene mukuwolokera Yorodani kuti mukalitenge, 2 kuti inuyo, ana anu, ndi zidzukulu zanu mʼtsogolomo mudzaope Yehova Mulungu wanu moyo wanu wonse posunga malangizo ndi malamulo ake onse amene ndinakupatsani inu kuti musangalale ndi moyo wautali. 3 Mvera Israeli ndipo usamalitse kuchita malamulowa kuti zinthu zikuyendere bwino mʼdziko ndi kuti muchuluke kwambiri mʼdziko loyenda mkaka ndi uchi monga momwe Yehova Mulungu wa makolo anu anakulonjezerani. 4 Tamvani inu Aisraeli, Yehova Mulungu wathu, Yehova ndi mmodzi. 5 Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse. 6 Malamulo amene ndakupatsani lero ayenera kukhala mu mtima mwanu. 7 Muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu. Muzikamba za malamulowa pamene muli mʼnyumba zanu, pamene mukuyenda mʼnjira, pamene mukugona ndi pamene mukudzuka. 8 Muwamange ngati zizindikiro pa manja anu ndi kuwamangirira pa zipumi zanu. 9 Muwalembe pa mphuthu za nyumba zanu ndi pa zipata zanu. 10 Pamene Yehova Mulungu wanu akukulowetsani ndi kukupatsani dziko limene analumbirira makolo anu Abrahamu, Isake ndi Yakobo, dziko lokhala ndi mizinda ikuluikulu imene inu simunamange, 11 nyumba zodzaza ndi zinthu za mitundu yonse zimene inu simunayikemo, zitsime zimene inu simunakumbe, minda ya mpesa ndi mitengo ya olivi zimene inuyo simunadzale, tsono mukadya ndi kukhuta, 12 samalani kuti mungayiwale Yehova amene anakutulutsani ku Igupto, kukuchotsani mu ukapolo. 13 Muziopa Yehova Mulungu wanu ndi kumutumikira Iye yekha, ndipo muzilumbira pa dzina lake. 14 Musamatsatire milungu ina, milungu ya anthu ena okuzungulirani, 15 pakuti Yehova Mulungu wanu amene ali pakati panu, ndi Mulungu wansanje ndipo adzakukwiyirani kwambiri ndi kukuwonongani, kukufafanizani mʼdziko. 16 Musamuyese Yehova Mulungu wanu monga munachitira ku Masa. 17 Onetsetsani kuti mukusunga malamulo a Yehova Mulungu wanu, malangizo ake ndi zikhazikitso zake zimene anakulamulirani. 18 Chitani zoyenera ndi zabwino pamaso pa Yehova, kuti zikuyendereni bwino ndi kuti mukhoza kukalowa ndi kulanda dziko labwinolo limene Yehova analonjeza molumbira kwa makolo anu, 19 kupirikitsiratu adani anu onse, monga Yehova wanenera. 20 Mʼtsogolo muno, ana anu akadzakufunsani kuti, “Kodi tanthauzo la ndondomeko, malangizo, zikhazikitso ndi malamulo amene Yehova Mulungu wathu anakulamulani nʼchiyani?” 21 Inu mudzawawuze kuti, “Ife tinali akapolo a Farao ku Igupto, koma Yehova anatitulutsa ku Igupto ndi dzanja lamphamvu. 22 Ifeyo tikuona Yehova anatumiza zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa, zazikulu ndi zoopsa, pa Aigupto ndi Farao pamodzi ndi banja lake lonse. 23 Koma anatitulutsa kumeneko ndi kutilowetsa kuno natipatsa dziko limene analonjeza mwa lumbiro kwa makolo athu. 24 Yehova anatilamula kuti tizimvera malamulo onsewa, kuti tizimuopa kuti zinthu zizitiyendera bwino pa moyo wathu monga momwe zilili leromu. 25 Ndipo ngati tisamala kumvera malamulo onsewa pamaso pa Yehova Mulungu wathu monga momwe anatilamulira ife, chimenecho chidzakhala chilungamo chathu.”

In Other Versions

Deuteronomy 6 in the ANGEFD

Deuteronomy 6 in the ANTPNG2D

Deuteronomy 6 in the AS21

Deuteronomy 6 in the BAGH

Deuteronomy 6 in the BBPNG

Deuteronomy 6 in the BBT1E

Deuteronomy 6 in the BDS

Deuteronomy 6 in the BEV

Deuteronomy 6 in the BHAD

Deuteronomy 6 in the BIB

Deuteronomy 6 in the BLPT

Deuteronomy 6 in the BNT

Deuteronomy 6 in the BNTABOOT

Deuteronomy 6 in the BNTLV

Deuteronomy 6 in the BOATCB

Deuteronomy 6 in the BOATCB2

Deuteronomy 6 in the BOBCV

Deuteronomy 6 in the BOCNT

Deuteronomy 6 in the BOECS

Deuteronomy 6 in the BOHCB

Deuteronomy 6 in the BOHCV

Deuteronomy 6 in the BOHLNT

Deuteronomy 6 in the BOHNTLTAL

Deuteronomy 6 in the BOICB

Deuteronomy 6 in the BOILNTAP

Deuteronomy 6 in the BOITCV

Deuteronomy 6 in the BOKCV

Deuteronomy 6 in the BOKCV2

Deuteronomy 6 in the BOKHWOG

Deuteronomy 6 in the BOKSSV

Deuteronomy 6 in the BOLCB

Deuteronomy 6 in the BOLCB2

Deuteronomy 6 in the BOMCV

Deuteronomy 6 in the BONAV

Deuteronomy 6 in the BONCB

Deuteronomy 6 in the BONLT

Deuteronomy 6 in the BONUT2

Deuteronomy 6 in the BOPLNT

Deuteronomy 6 in the BOSCB

Deuteronomy 6 in the BOSNC

Deuteronomy 6 in the BOTLNT

Deuteronomy 6 in the BOVCB

Deuteronomy 6 in the BOYCB

Deuteronomy 6 in the BPBB

Deuteronomy 6 in the BPH

Deuteronomy 6 in the BSB

Deuteronomy 6 in the CCB

Deuteronomy 6 in the CUV

Deuteronomy 6 in the CUVS

Deuteronomy 6 in the DBT

Deuteronomy 6 in the DGDNT

Deuteronomy 6 in the DHNT

Deuteronomy 6 in the DNT

Deuteronomy 6 in the ELBE

Deuteronomy 6 in the EMTV

Deuteronomy 6 in the ESV

Deuteronomy 6 in the FBV

Deuteronomy 6 in the FEB

Deuteronomy 6 in the GGMNT

Deuteronomy 6 in the GNT

Deuteronomy 6 in the HARY

Deuteronomy 6 in the HNT

Deuteronomy 6 in the IRVA

Deuteronomy 6 in the IRVB

Deuteronomy 6 in the IRVG

Deuteronomy 6 in the IRVH

Deuteronomy 6 in the IRVK

Deuteronomy 6 in the IRVM

Deuteronomy 6 in the IRVM2

Deuteronomy 6 in the IRVO

Deuteronomy 6 in the IRVP

Deuteronomy 6 in the IRVT

Deuteronomy 6 in the IRVT2

Deuteronomy 6 in the IRVU

Deuteronomy 6 in the ISVN

Deuteronomy 6 in the JSNT

Deuteronomy 6 in the KAPI

Deuteronomy 6 in the KBT1ETNIK

Deuteronomy 6 in the KBV

Deuteronomy 6 in the KJV

Deuteronomy 6 in the KNFD

Deuteronomy 6 in the LBA

Deuteronomy 6 in the LBLA

Deuteronomy 6 in the LNT

Deuteronomy 6 in the LSV

Deuteronomy 6 in the MAAL

Deuteronomy 6 in the MBV

Deuteronomy 6 in the MBV2

Deuteronomy 6 in the MHNT

Deuteronomy 6 in the MKNFD

Deuteronomy 6 in the MNG

Deuteronomy 6 in the MNT

Deuteronomy 6 in the MNT2

Deuteronomy 6 in the MRS1T

Deuteronomy 6 in the NAA

Deuteronomy 6 in the NASB

Deuteronomy 6 in the NBLA

Deuteronomy 6 in the NBS

Deuteronomy 6 in the NBVTP

Deuteronomy 6 in the NET2

Deuteronomy 6 in the NIV11

Deuteronomy 6 in the NNT

Deuteronomy 6 in the NNT2

Deuteronomy 6 in the NNT3

Deuteronomy 6 in the PDDPT

Deuteronomy 6 in the PFNT

Deuteronomy 6 in the RMNT

Deuteronomy 6 in the SBIAS

Deuteronomy 6 in the SBIBS

Deuteronomy 6 in the SBIBS2

Deuteronomy 6 in the SBICS

Deuteronomy 6 in the SBIDS

Deuteronomy 6 in the SBIGS

Deuteronomy 6 in the SBIHS

Deuteronomy 6 in the SBIIS

Deuteronomy 6 in the SBIIS2

Deuteronomy 6 in the SBIIS3

Deuteronomy 6 in the SBIKS

Deuteronomy 6 in the SBIKS2

Deuteronomy 6 in the SBIMS

Deuteronomy 6 in the SBIOS

Deuteronomy 6 in the SBIPS

Deuteronomy 6 in the SBISS

Deuteronomy 6 in the SBITS

Deuteronomy 6 in the SBITS2

Deuteronomy 6 in the SBITS3

Deuteronomy 6 in the SBITS4

Deuteronomy 6 in the SBIUS

Deuteronomy 6 in the SBIVS

Deuteronomy 6 in the SBT

Deuteronomy 6 in the SBT1E

Deuteronomy 6 in the SCHL

Deuteronomy 6 in the SNT

Deuteronomy 6 in the SUSU

Deuteronomy 6 in the SUSU2

Deuteronomy 6 in the SYNO

Deuteronomy 6 in the TBIAOTANT

Deuteronomy 6 in the TBT1E

Deuteronomy 6 in the TBT1E2

Deuteronomy 6 in the TFTIP

Deuteronomy 6 in the TFTU

Deuteronomy 6 in the TGNTATF3T

Deuteronomy 6 in the THAI

Deuteronomy 6 in the TNFD

Deuteronomy 6 in the TNT

Deuteronomy 6 in the TNTIK

Deuteronomy 6 in the TNTIL

Deuteronomy 6 in the TNTIN

Deuteronomy 6 in the TNTIP

Deuteronomy 6 in the TNTIZ

Deuteronomy 6 in the TOMA

Deuteronomy 6 in the TTENT

Deuteronomy 6 in the UBG

Deuteronomy 6 in the UGV

Deuteronomy 6 in the UGV2

Deuteronomy 6 in the UGV3

Deuteronomy 6 in the VBL

Deuteronomy 6 in the VDCC

Deuteronomy 6 in the YALU

Deuteronomy 6 in the YAPE

Deuteronomy 6 in the YBVTP

Deuteronomy 6 in the ZBP