Deuteronomy 9 (BOGWICC)

1 Mvera Israeli. Watsala pangʼono kuwoloka Yorodani ndi kukathamangitsa mitundu ikuluikulu ndi yamphamvu kuposa iweyo, imene mizinda yake ndi ikuluikulu yokhala ndi makoma ofika mpaka kumwamba. 2 Anthuwo ndi ataliatali, Aanaki! Ukudziwa za iwo ndipo unamvapo zikunenedwa kuti, “Ndani amene angalimbane ndi Aanaki?” 3 Koma khulupirira lero kuti Yehova Mulungu wako amene ali patsogolo pako ali ngati moto wonyeketsa. Adzawononga iwowo ndipo adzawagonjetsa iweyo ukuona. Pamenepo udzawathamangitsa ndi kuwakantha mwamsanga, monga momwe Yehova wakulonjezera. 4 Yehova Mulungu wako akadzawapirikitsa pamaso pako, usadzanene mu mtima mwako kuti, “Yehova wandibweretsa kuno kudzalanda dziko lino chifukwa cha kulungama kwanga.” Ayi, koma ndi chifukwa cha kuyipa kwa anthu amene Yehova ati awapirikitse pamaso pako. 5 Sukalowa ndi kutenga dziko lawolo chifukwa cha kulungama kwako kapena kukhulupirika kwako koma chifukwa cha kuyipa kwa anthuwo. Yehova Mulungu wako awapirikitsa pamaso pako kuti akwaniritse zimene analumbira kwa makolo ako Abrahamu, Isake ndi Yakobo. 6 Tsono zindikira kuti si chifukwa cha kulungama kwako kuti Yehova Mulungu wako akukupatsa dziko labwinoli kuti ulitenge popeza ndiwe wokanika. 7 Kumbukirani izi ndipo musayiwale mmene munaputira mkwiyo wa Yehova Mulungu mʼchipululu muja. Kuyambira tsiku limene munatuluka mu Igupto mpaka pamene munafika kuno, mwakhala owukira Yehova. 8 Ku Horebu munaputa mkwiyo wa Yehova, kotero kuti anakwiya kwambiri nafuna kukuwonongani. 9 Nditakwera ku phiri kuti ndikalandire miyala iwiri ya malamulo, ya pangano limene Yehova anachita ndi inu, ndinakhala ku phiriko kwa masiku makumi anayi usiku ndi usana, sindinadye buledi kapena kumwa madzi. 10 Yehova anandipatsa miyala iwiri yolembedwa ndi chala chake. Pa miyalapo panali malamulo onse amene Yehova analengeza kwa inu pa phiri kuchokera mʼmoto pa tsiku la msonkhano. 11 Pakutha pa masiku makumi anayi usiku ndi usana, Yehova anandipatsa miyala iwiri, miyala ya pangano. 12 Tsono Yehova anandiwuza, “Tsikako kuno msanga, chifukwa anthu ako aja unawatulutsa ku Iguptowa adziyipitsa. Iwo apatukapo mofulumira pa zimene ndinawalamulira ndipo adzipangira fano lachitsulo.” 13 Ndipo Yehova anati kwa ine, “Anthu awa ndawaona ndipo ndi anthu okanikadi! 14 Ndilekeni ndiwawononge ndi kufafaniza mayina awo pa dziko lapansi. Ndipo ndidzakuyesa iwe mtundu wa anthu wamphamvu ndi wochuluka kuposa iwo.” 15 Choncho ndinatembenuka ndi kutsika phiri moto ukanayakabe. Ndipo miyala iwiri ya pangano inali mʼmanja mwanga. 16 Ine poyangʼana ndinaona kuti inu munachimwira Yehova Mulungu wanu. Munadzipangira fano lowumbidwa ngati mwana wangʼombe. Inuyo munapatuka msanga kuchoka pa njira imene Yehova anakulamulirani. 17 Motero ine ndinaponya pansi miyala imene inali mʼmanja mwanga, ndi kuyiphwanya inu mukuona. 18 Tsono nthawi yomweyo ndinagwa chafufumimba pamaso pa Yehova kwa masiku makumi anayi usiku ndi usana. Sindinadye buledi kapena kumwa madzi chifukwa cha machimo onse amene munawachita, kuchita zoyipa pamaso pa Yehova ndi kumukwiyitsa kwambiri. 19 Ine ndinachita mantha ndi mkwiyo ndi ukali wa Yehova chifukwa anakwiya nanu kokwanira kukuwonongani. Koma Yehova anandimveranso. 20 Ndipo Yehova anakwiya ndi Aaroni ndipo akanamuwononga, koma ine ndinamupemphereranso Aaroniyo. 21 Ndiponso ndinatenga chinthu chanu choyipacho, mwana wangʼombe amene munapangayo, ndi kumuwotcha pa moto. Kenaka ndinamuphwanya ndi kumuperapera ndikukhala ngati fumbi ndipo ndinawaza fumbilo mu mtsinje umene unkayenda kuchokera mʼphiri. 22 Inu munamukwiyitsanso Yehova ku Tabera, ku Masa ndi ku Kibiroti Hatava. 23 Ndipo Yehova atakutulutsani ku Kadesi Barinea anati, “Pitani mukatenge dziko limene ndakupatsani.” Koma munawukira ulamuliro wa Yehova Mulungu wanu. Inu simunamukhulupirire kapena kumumvera. 24 Kuyambira pamene ndinakudziwani, mwakhala owukira Yehova. 25 Ine ndinagwa chafufumimba pamaso pa Yehova kwa masiku makumi anayi usana ndi usiku chifukwa Yehova ananena kuti akuwonongani. 26 Ndinapemphera kwa Ambuye ndi kuti, “Haa Yehova Wamkulukulu, musawawononge anthu anu, chuma chanuchanu chimene munachipulumutsa ndi mphamvu yanu yayikulu ku Igupto ndi dzanja lanu la mphamvu. 27 Kumbukirani atumiki anu Abrahamu, Isake ndi Yakobo. Musatengere kupulupudza, kuyipa ndi kuchimwa kwawo anthuwa. 28 Kupanda kutero, ndiye kuti anthu a ku dziko lija munatitulutsaku adzati, ‘Yehova anawatulutsa kuti akawaphe mʼchipululu popeza sanathe kukawalowetsa mʼdziko limene anawalonjeza ndipo anadana nawo.’ 29 Koma iwowa ndi anthu anu, chuma chanu chimene munachitulutsa ndi mphamvu yanu yayikulu ndi mkono wanu wotambasuka.”

In Other Versions

Deuteronomy 9 in the ANGEFD

Deuteronomy 9 in the ANTPNG2D

Deuteronomy 9 in the AS21

Deuteronomy 9 in the BAGH

Deuteronomy 9 in the BBPNG

Deuteronomy 9 in the BBT1E

Deuteronomy 9 in the BDS

Deuteronomy 9 in the BEV

Deuteronomy 9 in the BHAD

Deuteronomy 9 in the BIB

Deuteronomy 9 in the BLPT

Deuteronomy 9 in the BNT

Deuteronomy 9 in the BNTABOOT

Deuteronomy 9 in the BNTLV

Deuteronomy 9 in the BOATCB

Deuteronomy 9 in the BOATCB2

Deuteronomy 9 in the BOBCV

Deuteronomy 9 in the BOCNT

Deuteronomy 9 in the BOECS

Deuteronomy 9 in the BOHCB

Deuteronomy 9 in the BOHCV

Deuteronomy 9 in the BOHLNT

Deuteronomy 9 in the BOHNTLTAL

Deuteronomy 9 in the BOICB

Deuteronomy 9 in the BOILNTAP

Deuteronomy 9 in the BOITCV

Deuteronomy 9 in the BOKCV

Deuteronomy 9 in the BOKCV2

Deuteronomy 9 in the BOKHWOG

Deuteronomy 9 in the BOKSSV

Deuteronomy 9 in the BOLCB

Deuteronomy 9 in the BOLCB2

Deuteronomy 9 in the BOMCV

Deuteronomy 9 in the BONAV

Deuteronomy 9 in the BONCB

Deuteronomy 9 in the BONLT

Deuteronomy 9 in the BONUT2

Deuteronomy 9 in the BOPLNT

Deuteronomy 9 in the BOSCB

Deuteronomy 9 in the BOSNC

Deuteronomy 9 in the BOTLNT

Deuteronomy 9 in the BOVCB

Deuteronomy 9 in the BOYCB

Deuteronomy 9 in the BPBB

Deuteronomy 9 in the BPH

Deuteronomy 9 in the BSB

Deuteronomy 9 in the CCB

Deuteronomy 9 in the CUV

Deuteronomy 9 in the CUVS

Deuteronomy 9 in the DBT

Deuteronomy 9 in the DGDNT

Deuteronomy 9 in the DHNT

Deuteronomy 9 in the DNT

Deuteronomy 9 in the ELBE

Deuteronomy 9 in the EMTV

Deuteronomy 9 in the ESV

Deuteronomy 9 in the FBV

Deuteronomy 9 in the FEB

Deuteronomy 9 in the GGMNT

Deuteronomy 9 in the GNT

Deuteronomy 9 in the HARY

Deuteronomy 9 in the HNT

Deuteronomy 9 in the IRVA

Deuteronomy 9 in the IRVB

Deuteronomy 9 in the IRVG

Deuteronomy 9 in the IRVH

Deuteronomy 9 in the IRVK

Deuteronomy 9 in the IRVM

Deuteronomy 9 in the IRVM2

Deuteronomy 9 in the IRVO

Deuteronomy 9 in the IRVP

Deuteronomy 9 in the IRVT

Deuteronomy 9 in the IRVT2

Deuteronomy 9 in the IRVU

Deuteronomy 9 in the ISVN

Deuteronomy 9 in the JSNT

Deuteronomy 9 in the KAPI

Deuteronomy 9 in the KBT1ETNIK

Deuteronomy 9 in the KBV

Deuteronomy 9 in the KJV

Deuteronomy 9 in the KNFD

Deuteronomy 9 in the LBA

Deuteronomy 9 in the LBLA

Deuteronomy 9 in the LNT

Deuteronomy 9 in the LSV

Deuteronomy 9 in the MAAL

Deuteronomy 9 in the MBV

Deuteronomy 9 in the MBV2

Deuteronomy 9 in the MHNT

Deuteronomy 9 in the MKNFD

Deuteronomy 9 in the MNG

Deuteronomy 9 in the MNT

Deuteronomy 9 in the MNT2

Deuteronomy 9 in the MRS1T

Deuteronomy 9 in the NAA

Deuteronomy 9 in the NASB

Deuteronomy 9 in the NBLA

Deuteronomy 9 in the NBS

Deuteronomy 9 in the NBVTP

Deuteronomy 9 in the NET2

Deuteronomy 9 in the NIV11

Deuteronomy 9 in the NNT

Deuteronomy 9 in the NNT2

Deuteronomy 9 in the NNT3

Deuteronomy 9 in the PDDPT

Deuteronomy 9 in the PFNT

Deuteronomy 9 in the RMNT

Deuteronomy 9 in the SBIAS

Deuteronomy 9 in the SBIBS

Deuteronomy 9 in the SBIBS2

Deuteronomy 9 in the SBICS

Deuteronomy 9 in the SBIDS

Deuteronomy 9 in the SBIGS

Deuteronomy 9 in the SBIHS

Deuteronomy 9 in the SBIIS

Deuteronomy 9 in the SBIIS2

Deuteronomy 9 in the SBIIS3

Deuteronomy 9 in the SBIKS

Deuteronomy 9 in the SBIKS2

Deuteronomy 9 in the SBIMS

Deuteronomy 9 in the SBIOS

Deuteronomy 9 in the SBIPS

Deuteronomy 9 in the SBISS

Deuteronomy 9 in the SBITS

Deuteronomy 9 in the SBITS2

Deuteronomy 9 in the SBITS3

Deuteronomy 9 in the SBITS4

Deuteronomy 9 in the SBIUS

Deuteronomy 9 in the SBIVS

Deuteronomy 9 in the SBT

Deuteronomy 9 in the SBT1E

Deuteronomy 9 in the SCHL

Deuteronomy 9 in the SNT

Deuteronomy 9 in the SUSU

Deuteronomy 9 in the SUSU2

Deuteronomy 9 in the SYNO

Deuteronomy 9 in the TBIAOTANT

Deuteronomy 9 in the TBT1E

Deuteronomy 9 in the TBT1E2

Deuteronomy 9 in the TFTIP

Deuteronomy 9 in the TFTU

Deuteronomy 9 in the TGNTATF3T

Deuteronomy 9 in the THAI

Deuteronomy 9 in the TNFD

Deuteronomy 9 in the TNT

Deuteronomy 9 in the TNTIK

Deuteronomy 9 in the TNTIL

Deuteronomy 9 in the TNTIN

Deuteronomy 9 in the TNTIP

Deuteronomy 9 in the TNTIZ

Deuteronomy 9 in the TOMA

Deuteronomy 9 in the TTENT

Deuteronomy 9 in the UBG

Deuteronomy 9 in the UGV

Deuteronomy 9 in the UGV2

Deuteronomy 9 in the UGV3

Deuteronomy 9 in the VBL

Deuteronomy 9 in the VDCC

Deuteronomy 9 in the YALU

Deuteronomy 9 in the YAPE

Deuteronomy 9 in the YBVTP

Deuteronomy 9 in the ZBP