Ecclesiastes 2 (BOGWICC)

1 Ine ndinaganiza mu mtima mwanga, “Tsopano ndiyese zosangalatsa kuti ndipeze zomwe ndi zabwino.” Koma izi zinaonekanso kuti ndi zopandapake. 2 “Kuseka,” ndinati, “imeneyo ndi misala. Ndipo kodi chisangalalo chimabweretsa phindu lanji?” 3 Ndinayesa kudzisangalatsa ndi vinyo, koma umenewu unali uchitsiru, pamenepo nʼkuti maganizo anga akutsogozedwa ndi nzeru. Ine ndinkati mwina kapena njira yotero nʼkukhala yopambana, imene anthu amatsata pofuna kusangalala pa masiku owerengeka a moyo wawo. 4 Ndinagwira ntchito zikuluzikulu: Ndinadzimangira nyumba ndi kuwoka mipesa. 5 Ndinalima madimba ndi minda yamitengo; ndipo ndinadzalamo mitengo ya zipatso za mitundu yonse. 6 Ndinakumba mayiwe osungiramo madzi woti ndizithirira minda ya mitengo yodzalidwa ija. 7 Ndinagula akapolo aamuna ndi akapolo aakazi, ndiponso ndinali ndi akapolo ena omwe anabadwira mʼnyumba mwanga. Ndinalinso ndi ngʼombe ndi nkhosa zambiri kupambana aliyense mu Yerusalemu amene analipo ndisanabadwe. 8 Ndinadzikundikira siliva ndi golide, ndiponso chuma chochokera kwa mafumu ndi madera awo. Ndinali ndi amuna ndi akazi oyimba ndiponso azikazi; zinthu zokondweretsa mtima wa munthu. 9 Ndinali munthu wotchuka kupambana wina aliyense mu Yerusalemu amene analipo ndisanabadwe. Mu zonsezi nzeru zanga zinali nane. 10 Sindinadzimane chilichonse chimene maso anga anachifuna;mtima wanga sindinawumane zokondweretsa.Mtima wanga unakondwera ndi ntchito yanga yonse,ndipo iyi ndiyo inali mphotho ya ntchito zanga zonse zolemetsa. 11 Koma pamene ndinayamba kuyangʼanayangʼana zonse zimene ndinachita ndi manja anga,ndi zimene ndinazivutikira kuti ndizipeze,zonsezi zinali zopandapake; kungodzivuta chabe,palibe chomwe ndinapindula pansi pano. 12 Kenaka maganizo anga anayamba kulingalira zakuti nzeru nʼchiyani,komanso kuti misala ndi uchitsiru nʼchiyani.Kodi munthu wodzalowa ufumu tsopanoyo angachite chiyanichoposa chimene chinachitidwa kale? 13 Ndinaona kuti nzeru ndi yopambana uchitsiru,monga momwe kuwala kumapambanira mdima. 14 Munthu wanzeru amayenda maso ali patsogolo,pamene chitsiru chimayenda mʼchimbulimbuli;koma ndinazindikira kuti chomwechimawachitikira onsewo ndi chimodzi. 15 Pamenepo ndinalingalira mu mtima mwanga,“Zochitikira chitsiru zidzandichitikiranso ine.Nanga tsono phindu langa nʼchiyani pakukhala wanzeru?”Ndinati mu mtima mwanga,“Ichinso ndi chopandapake.” 16 Pakuti munthu wanzeru, pamodzinso ndi chitsiru sadzakumbukiridwa nthawi yayitali;mʼmasiku amʼtsogolo awiriwo adzayiwalika.Mmene chimafera chitsiru ndi mmenenso amafera wanzeru! 17 Kotero ndinadana nawo moyo chifukwa ntchito zimene zimagwiridwa pansi pano ndi zosautsa kwa ine. Ntchito zonsezo ndi zopandapake, nʼkungodzivuta chabe. 18 Ine ndinadana nazo ntchito zonse zimene ndinazigwira pansi pano, chifukwa ndinayenera kudzazisiyira wina amene adzalowa mʼmalo mwanga. 19 Ndipo ndani amadziwa kuti munthu ameneyo adzakhala wanzeru kapena chitsiru? Komabe munthuyo adzakhala wolamulira zonse zimene ndinazichita pansi pano mwa nzeru zanga. Izinso ndi zopandapake. 20 Motero ndinayamba kutaya mtima chifukwa cha ntchito zonse zimene ndinazivutikira pansi pano. 21 Pakuti munthu atha kugwira ntchito yake mwanzeru, chidziwitso ndi luntha, ndipo kenaka nʼkusiyira wina amene sanakhetserepo thukuta. Izinso ndi zopandapake ndiponso tsoka lalikulu. 22 Kodi munthu amapindulanji pa ntchito zonse zolemetsa ndi zodetsa nkhawa zimene amazichita pansi pano? 23 Masiku ake onse amakhala achisoni, ntchito yake imakhala yovuta; ngakhale usiku womwe, mtima wake supumula. Izinso ndi zopandapake. 24 Kwa munthu palibe chabwino china kuposa kudya, kumwa ndi kukondwerera ntchito zake. Izinso ndaona kuti ndi zochokera kwa Mulungu, 25 pakuti popanda Iye, ndani angadye ndi kupeza chisangalalo? 26 Munthu amene amakondweretsa Mulungu, Mulunguyo amamusandutsa wanzeru, wozindikira ndi wachisangalalo, koma wochimwa, Mulungu amamupatsa ntchito yosonkhanitsa ndi kusunga chuma kuti adzachipereke kwa amene Mulunguyo amakondwera naye. Izinso ndi zopandapake, nʼkungodzivuta chabe.

In Other Versions

Ecclesiastes 2 in the ANGEFD

Ecclesiastes 2 in the ANTPNG2D

Ecclesiastes 2 in the AS21

Ecclesiastes 2 in the BAGH

Ecclesiastes 2 in the BBPNG

Ecclesiastes 2 in the BBT1E

Ecclesiastes 2 in the BDS

Ecclesiastes 2 in the BEV

Ecclesiastes 2 in the BHAD

Ecclesiastes 2 in the BIB

Ecclesiastes 2 in the BLPT

Ecclesiastes 2 in the BNT

Ecclesiastes 2 in the BNTABOOT

Ecclesiastes 2 in the BNTLV

Ecclesiastes 2 in the BOATCB

Ecclesiastes 2 in the BOATCB2

Ecclesiastes 2 in the BOBCV

Ecclesiastes 2 in the BOCNT

Ecclesiastes 2 in the BOECS

Ecclesiastes 2 in the BOHCB

Ecclesiastes 2 in the BOHCV

Ecclesiastes 2 in the BOHLNT

Ecclesiastes 2 in the BOHNTLTAL

Ecclesiastes 2 in the BOICB

Ecclesiastes 2 in the BOILNTAP

Ecclesiastes 2 in the BOITCV

Ecclesiastes 2 in the BOKCV

Ecclesiastes 2 in the BOKCV2

Ecclesiastes 2 in the BOKHWOG

Ecclesiastes 2 in the BOKSSV

Ecclesiastes 2 in the BOLCB

Ecclesiastes 2 in the BOLCB2

Ecclesiastes 2 in the BOMCV

Ecclesiastes 2 in the BONAV

Ecclesiastes 2 in the BONCB

Ecclesiastes 2 in the BONLT

Ecclesiastes 2 in the BONUT2

Ecclesiastes 2 in the BOPLNT

Ecclesiastes 2 in the BOSCB

Ecclesiastes 2 in the BOSNC

Ecclesiastes 2 in the BOTLNT

Ecclesiastes 2 in the BOVCB

Ecclesiastes 2 in the BOYCB

Ecclesiastes 2 in the BPBB

Ecclesiastes 2 in the BPH

Ecclesiastes 2 in the BSB

Ecclesiastes 2 in the CCB

Ecclesiastes 2 in the CUV

Ecclesiastes 2 in the CUVS

Ecclesiastes 2 in the DBT

Ecclesiastes 2 in the DGDNT

Ecclesiastes 2 in the DHNT

Ecclesiastes 2 in the DNT

Ecclesiastes 2 in the ELBE

Ecclesiastes 2 in the EMTV

Ecclesiastes 2 in the ESV

Ecclesiastes 2 in the FBV

Ecclesiastes 2 in the FEB

Ecclesiastes 2 in the GGMNT

Ecclesiastes 2 in the GNT

Ecclesiastes 2 in the HARY

Ecclesiastes 2 in the HNT

Ecclesiastes 2 in the IRVA

Ecclesiastes 2 in the IRVB

Ecclesiastes 2 in the IRVG

Ecclesiastes 2 in the IRVH

Ecclesiastes 2 in the IRVK

Ecclesiastes 2 in the IRVM

Ecclesiastes 2 in the IRVM2

Ecclesiastes 2 in the IRVO

Ecclesiastes 2 in the IRVP

Ecclesiastes 2 in the IRVT

Ecclesiastes 2 in the IRVT2

Ecclesiastes 2 in the IRVU

Ecclesiastes 2 in the ISVN

Ecclesiastes 2 in the JSNT

Ecclesiastes 2 in the KAPI

Ecclesiastes 2 in the KBT1ETNIK

Ecclesiastes 2 in the KBV

Ecclesiastes 2 in the KJV

Ecclesiastes 2 in the KNFD

Ecclesiastes 2 in the LBA

Ecclesiastes 2 in the LBLA

Ecclesiastes 2 in the LNT

Ecclesiastes 2 in the LSV

Ecclesiastes 2 in the MAAL

Ecclesiastes 2 in the MBV

Ecclesiastes 2 in the MBV2

Ecclesiastes 2 in the MHNT

Ecclesiastes 2 in the MKNFD

Ecclesiastes 2 in the MNG

Ecclesiastes 2 in the MNT

Ecclesiastes 2 in the MNT2

Ecclesiastes 2 in the MRS1T

Ecclesiastes 2 in the NAA

Ecclesiastes 2 in the NASB

Ecclesiastes 2 in the NBLA

Ecclesiastes 2 in the NBS

Ecclesiastes 2 in the NBVTP

Ecclesiastes 2 in the NET2

Ecclesiastes 2 in the NIV11

Ecclesiastes 2 in the NNT

Ecclesiastes 2 in the NNT2

Ecclesiastes 2 in the NNT3

Ecclesiastes 2 in the PDDPT

Ecclesiastes 2 in the PFNT

Ecclesiastes 2 in the RMNT

Ecclesiastes 2 in the SBIAS

Ecclesiastes 2 in the SBIBS

Ecclesiastes 2 in the SBIBS2

Ecclesiastes 2 in the SBICS

Ecclesiastes 2 in the SBIDS

Ecclesiastes 2 in the SBIGS

Ecclesiastes 2 in the SBIHS

Ecclesiastes 2 in the SBIIS

Ecclesiastes 2 in the SBIIS2

Ecclesiastes 2 in the SBIIS3

Ecclesiastes 2 in the SBIKS

Ecclesiastes 2 in the SBIKS2

Ecclesiastes 2 in the SBIMS

Ecclesiastes 2 in the SBIOS

Ecclesiastes 2 in the SBIPS

Ecclesiastes 2 in the SBISS

Ecclesiastes 2 in the SBITS

Ecclesiastes 2 in the SBITS2

Ecclesiastes 2 in the SBITS3

Ecclesiastes 2 in the SBITS4

Ecclesiastes 2 in the SBIUS

Ecclesiastes 2 in the SBIVS

Ecclesiastes 2 in the SBT

Ecclesiastes 2 in the SBT1E

Ecclesiastes 2 in the SCHL

Ecclesiastes 2 in the SNT

Ecclesiastes 2 in the SUSU

Ecclesiastes 2 in the SUSU2

Ecclesiastes 2 in the SYNO

Ecclesiastes 2 in the TBIAOTANT

Ecclesiastes 2 in the TBT1E

Ecclesiastes 2 in the TBT1E2

Ecclesiastes 2 in the TFTIP

Ecclesiastes 2 in the TFTU

Ecclesiastes 2 in the TGNTATF3T

Ecclesiastes 2 in the THAI

Ecclesiastes 2 in the TNFD

Ecclesiastes 2 in the TNT

Ecclesiastes 2 in the TNTIK

Ecclesiastes 2 in the TNTIL

Ecclesiastes 2 in the TNTIN

Ecclesiastes 2 in the TNTIP

Ecclesiastes 2 in the TNTIZ

Ecclesiastes 2 in the TOMA

Ecclesiastes 2 in the TTENT

Ecclesiastes 2 in the UBG

Ecclesiastes 2 in the UGV

Ecclesiastes 2 in the UGV2

Ecclesiastes 2 in the UGV3

Ecclesiastes 2 in the VBL

Ecclesiastes 2 in the VDCC

Ecclesiastes 2 in the YALU

Ecclesiastes 2 in the YAPE

Ecclesiastes 2 in the YBVTP

Ecclesiastes 2 in the ZBP