Ephesians 6 (BOGWICC)
1 Inu ana, mverani makolo anu mwa Ambuye, pakuti zimenezi ndi zoyenera. 2 “Lemekeza abambo ndi amayi ako.” Limeneli ndi lamulo loyamba lokhala ndi lonjezo. 3 Ngati ulemekeza abambo ako ndi amayi ako, “zinthu zidzakuyendera bwino ndipo udzasangalala ndi moyo wautali pa dziko lapansi.” 4 Abambo musakwiyitse ana anu; mʼmalo mwake, muwalere mʼchiphunzitso ndi mʼchilangizo cha Ambuye. 5 Inu antchito, mverani mabwana anu mwaulemu ndi mwamantha ndi moona mtima, monga momwe mungamvere Khristu. 6 Musawamvere pamene akukuonani kuti akukomereni mtima, koma ngati akapolo a Khristu ochita chifuniro cha Mulungu kuchokera mu mtima mwanu. 7 Tumikirani ndi mtima wonse, ngati kuti mukutumikira Ambuye, osati anthu. 8 Inu mukudziwa kuti Ambuye adzamupatsa munthu aliyense mphotho chifukwa cha ntchito yake yabwino imene anagwira, kaya munthuyo ndi kapolo kapena mfulu. 9 Ndipo inu mabwana, muziwachitiranso chimodzimodzi antchito anu. Musamawaopseze, popeza mukudziwa kuti Mbuye wawo ndi wanunso, nonse Mbuye wanu ali kumwamba, ndipo Iyeyo alibe tsankho. 10 Potsiriza ndikuti, dzilimbitseni mwa Ambuye ndi mwa mphamvu zake zazikulu. 11 Valani zida zonse za Mulungu kuti muthe kuyima ndi kukana machenjerero a Satana. 12 Pakuti sitikulimbana ndi thupi ndi magazi, koma tikulimbana ndi maufumu, maulamuliro, mphamvu za dziko la mdima, ndi mphamvu zoyipa kwambiri zauzimu zamlengalenga. 13 Choncho valani zida zonse za Mulungu, kuti pamene tsiku loyipa kwambiri lifika, mudzathe kuyima chilili, ndipo mutatha kuchita zonse, mudzayimabe mwamphamvu. 14 Tsono imani mwamphamvu, mutamangira choonadi ngati lamba mʼchiwuno mwanu, mutavala chilungamo ngati chitsulo chotchinjiriza pa chifuwa. 15 Valani Uthenga Wabwino wamtendere ku mapazi anu ngati nsapato. 16 Kuwonjezera pa zonsezi, nyamulani chishango cha chikhulupiriro, ndipo ndi chimenechi mudzatha kuzimitsa mivi yonse yoyaka moto ya oyipayo. 17 Valani chipewa cha chipulumutso ndi kutenga lupanga la mzimu, limene ndi Mawu a Mulungu. 18 Ndipo mupemphere mwa Mzimu nthawi zonse, mʼmitundu yonse ya mapemphero ndi zopempha. Ndipo pozindikira izi, khalani achangu kupempherera oyera mtima nthawi zonse. 19 Mundipempherere inenso, kuti nthawi iliyonse pamene nditsekula pakamwa panga, andipatse mawu kuti ndiwulule zinsinsi za Uthenga Wabwino mopanda mantha. 20 Ndine kazembe wa Uthenga Wabwinowu ngakhale ndili womangidwa mʼndende. Pempherani kuti ndilalikire mopanda mantha, monga ndiyenera. 21 Tukiko, mʼbale wanga wokondedwa ndi mtumiki wokhulupirika mwa Ambuye, adzakuwuzani zonse kuti inunso mudziwe mmene ndilili ndi zimene ndikuchita. 22 Ine ndikumutumiza kwa inu, kuti mudziwe za moyo wathu, ndi kuti akulimbikitseni. 23 Mtendere, chikondi pamodzi ndi chikhulupiriro kuchokera kwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu zikhale ndi abale onse. 24 Chisomo kwa onse amene amakonda Ambuye athu Yesu Khristu ndi chikondi chosatha.
In Other Versions
Ephesians 6 in the ANGEFD
Ephesians 6 in the ANTPNG2D
Ephesians 6 in the AS21
Ephesians 6 in the BAGH
Ephesians 6 in the BBPNG
Ephesians 6 in the BBT1E
Ephesians 6 in the BDS
Ephesians 6 in the BEV
Ephesians 6 in the BHAD
Ephesians 6 in the BIB
Ephesians 6 in the BLPT
Ephesians 6 in the BNT
Ephesians 6 in the BNTABOOT
Ephesians 6 in the BNTLV
Ephesians 6 in the BOATCB
Ephesians 6 in the BOATCB2
Ephesians 6 in the BOBCV
Ephesians 6 in the BOCNT
Ephesians 6 in the BOECS
Ephesians 6 in the BOHCB
Ephesians 6 in the BOHCV
Ephesians 6 in the BOHLNT
Ephesians 6 in the BOHNTLTAL
Ephesians 6 in the BOICB
Ephesians 6 in the BOILNTAP
Ephesians 6 in the BOITCV
Ephesians 6 in the BOKCV
Ephesians 6 in the BOKCV2
Ephesians 6 in the BOKHWOG
Ephesians 6 in the BOKSSV
Ephesians 6 in the BOLCB
Ephesians 6 in the BOLCB2
Ephesians 6 in the BOMCV
Ephesians 6 in the BONAV
Ephesians 6 in the BONCB
Ephesians 6 in the BONLT
Ephesians 6 in the BONUT2
Ephesians 6 in the BOPLNT
Ephesians 6 in the BOSCB
Ephesians 6 in the BOSNC
Ephesians 6 in the BOTLNT
Ephesians 6 in the BOVCB
Ephesians 6 in the BOYCB
Ephesians 6 in the BPBB
Ephesians 6 in the BPH
Ephesians 6 in the BSB
Ephesians 6 in the CCB
Ephesians 6 in the CUV
Ephesians 6 in the CUVS
Ephesians 6 in the DBT
Ephesians 6 in the DGDNT
Ephesians 6 in the DHNT
Ephesians 6 in the DNT
Ephesians 6 in the ELBE
Ephesians 6 in the EMTV
Ephesians 6 in the ESV
Ephesians 6 in the FBV
Ephesians 6 in the FEB
Ephesians 6 in the GGMNT
Ephesians 6 in the GNT
Ephesians 6 in the HARY
Ephesians 6 in the HNT
Ephesians 6 in the IRVA
Ephesians 6 in the IRVB
Ephesians 6 in the IRVG
Ephesians 6 in the IRVH
Ephesians 6 in the IRVK
Ephesians 6 in the IRVM
Ephesians 6 in the IRVM2
Ephesians 6 in the IRVO
Ephesians 6 in the IRVP
Ephesians 6 in the IRVT
Ephesians 6 in the IRVT2
Ephesians 6 in the IRVU
Ephesians 6 in the ISVN
Ephesians 6 in the JSNT
Ephesians 6 in the KAPI
Ephesians 6 in the KBT1ETNIK
Ephesians 6 in the KBV
Ephesians 6 in the KJV
Ephesians 6 in the KNFD
Ephesians 6 in the LBA
Ephesians 6 in the LBLA
Ephesians 6 in the LNT
Ephesians 6 in the LSV
Ephesians 6 in the MAAL
Ephesians 6 in the MBV
Ephesians 6 in the MBV2
Ephesians 6 in the MHNT
Ephesians 6 in the MKNFD
Ephesians 6 in the MNG
Ephesians 6 in the MNT
Ephesians 6 in the MNT2
Ephesians 6 in the MRS1T
Ephesians 6 in the NAA
Ephesians 6 in the NASB
Ephesians 6 in the NBLA
Ephesians 6 in the NBS
Ephesians 6 in the NBVTP
Ephesians 6 in the NET2
Ephesians 6 in the NIV11
Ephesians 6 in the NNT
Ephesians 6 in the NNT2
Ephesians 6 in the NNT3
Ephesians 6 in the PDDPT
Ephesians 6 in the PFNT
Ephesians 6 in the RMNT
Ephesians 6 in the SBIAS
Ephesians 6 in the SBIBS
Ephesians 6 in the SBIBS2
Ephesians 6 in the SBICS
Ephesians 6 in the SBIDS
Ephesians 6 in the SBIGS
Ephesians 6 in the SBIHS
Ephesians 6 in the SBIIS
Ephesians 6 in the SBIIS2
Ephesians 6 in the SBIIS3
Ephesians 6 in the SBIKS
Ephesians 6 in the SBIKS2
Ephesians 6 in the SBIMS
Ephesians 6 in the SBIOS
Ephesians 6 in the SBIPS
Ephesians 6 in the SBISS
Ephesians 6 in the SBITS
Ephesians 6 in the SBITS2
Ephesians 6 in the SBITS3
Ephesians 6 in the SBITS4
Ephesians 6 in the SBIUS
Ephesians 6 in the SBIVS
Ephesians 6 in the SBT
Ephesians 6 in the SBT1E
Ephesians 6 in the SCHL
Ephesians 6 in the SNT
Ephesians 6 in the SUSU
Ephesians 6 in the SUSU2
Ephesians 6 in the SYNO
Ephesians 6 in the TBIAOTANT
Ephesians 6 in the TBT1E
Ephesians 6 in the TBT1E2
Ephesians 6 in the TFTIP
Ephesians 6 in the TFTU
Ephesians 6 in the TGNTATF3T
Ephesians 6 in the THAI
Ephesians 6 in the TNFD
Ephesians 6 in the TNT
Ephesians 6 in the TNTIK
Ephesians 6 in the TNTIL
Ephesians 6 in the TNTIN
Ephesians 6 in the TNTIP
Ephesians 6 in the TNTIZ
Ephesians 6 in the TOMA
Ephesians 6 in the TTENT
Ephesians 6 in the UBG
Ephesians 6 in the UGV
Ephesians 6 in the UGV2
Ephesians 6 in the UGV3
Ephesians 6 in the VBL
Ephesians 6 in the VDCC
Ephesians 6 in the YALU
Ephesians 6 in the YAPE
Ephesians 6 in the YBVTP
Ephesians 6 in the ZBP