Esther 8 (BOGWICC)

1 Tsiku lomwelo mfumu Ahasiwero anamupatsa mfumukazi Estere nyumba ya Hamani, mdani wa Ayuda. Ndipo Mordekai anafika pamaso pa mfumu, popeza Estere anamuwuza ubale wawo. 2 Mfumu inavula mphete yake yodindira imene analanda kwa Hamani ndipo Estere anamusankha Mordekai kukhala woyangʼanira nyumba ya Hamani. 3 Estere anayankhulanso ndi mfumu ndipo anadzigwetsa pa mapazi ake. Uku akulira iye anapempha mfumu kuti iletse choyipa, makamaka chiwembu chimene Hamani Mwagagi anakonza kuti awononge a Yuda. 4 Ndipo mfumu inamuloza Estere ndi ndodo yake yagolide ndipo Estere anadzuka ndi kuyima pamaso pake. 5 Iye anati, “Ngati chikomera mfumu ndi kukukondweretsani, ngati pempho langa muliona kuti ndi loyenera ndi kuti mukondwera nane tsono mfumu ilole kuti lamulo lilembedwe kusintha mawu a mʼmakalata amene Hamani mwana wa Hamedata, Mwagagi, anatumiza ku zigawo zonse za mfumu. Paja Hamani analemba kuti Ayuda onse awonongedwe. 6 Kodi ndingapirire bwanji pamene ndi kuona tsoka likugwera anthu a mtundu wanga? Ndingapirire bwanji pamene abale anga akuwonongedwa?” 7 Mfumu Ahasiwero anamuyankha mfumukazi Estere ndi Mordekai Myuda kuti, “Ndapereka nyumba ya Hamani kwa Estere ndipo Hamaniyo amupachika kale pa mtanda chifukwa anafuna kuwononga Ayuda. 8 Tsono inu awiri, lembani za Ayudawo monga mufunira. Mulembe mʼdzina la mfumu ndipo musindikize chizindikiro cha mphete ya mfumu popeza kuti cholembedwa mʼdzina la mfumu ndi kusindikizidwa ndi chizindikiro cha mphete ya mfumu sichingasinthidwe.” 9 Nthawi yomweyo, pa tsiku la 23 la mwezi wachitatu wa Sivani, mfumu inayitana alembi ake. Analemba zonse zokhudza Ayuda monga ananenera Mordekai. Analembera akazembe, abwanamkubwa ndi nduna za zigawo 127 kuyambira ku India mpaka ku Kusi. Zimene analamula Mordekai zinalembedwa mʼzilembo za chigawo chilichonse ndi chiyankhulo cha mtundu uliwonse wa anthu. Ayudanso anawalembera mʼmalemba awo ndi chiyankhulo chawo. 10 Mordekai analemba makalatawo mʼdzina la mfumu Ahasiwero, nawadinda ndi chizindikiro cha mphete ya mfumu. Ndipo anawatumiza ndi anthu amithenga amene anakwera pa akavalo a ufumu othamanga kwambiri obadwa mu khola la ufumu. 11 Mʼmakalata amenewa mfumu inalola kuti Ayuda okhala mu mzinda uliwonse akhale ndi ufulu wokumana ndi kudzitchinjiriza komanso kuwononga, kupha ndi kufafaniziratu gulu lililonse la nkhondo la anthu a mtundu uliwonse kapena chigawo chimene chingawathire nkhondo. Ayudawo analoledwa kuwononga gulu lankhondo lija, ana awo ndi akazi awo komanso kuti afunkhe katundu wawo. 12 Ayuda analoledwa kuchita zimenezi mʼzigawo zonse za Mfumu Ahasiwero pa tsiku limodzi lokha la 13 la mwezi wa 12, mwezi wa Adara. 13 Mawu a mʼmakalatawo anayenera kudziwitsidwa kwa anthu a mtundu uliwonse mu chigawo chilichonse kuti ndi lamulo ndithu kwa anthu a mtundu uliwonse ndi kuti Ayuda adzakhale okonzeka pa tsikulo kulipsira kwa adani awo. 14 Atawalamulira a mfumu, amithenga aja anapita nawo makalata mwachangu, atakwera pa akavalo a mfumu. Ndipo lamulolo analiperekanso ku likulu la mzinda wa Susa. 15 Mordekai anachoka pamaso pa mfumu atavala zovala zaufumu zooneka ngati mtambo ndi zofewa zoyera, chipewa chachikulu cha golide ndi mkanjo wapepo. Ndipo mzinda wa Susa unafuwula mokondwa. 16 Kwa Ayuda inali nthawi ya nkhope zowala ndi za chimwemwe, chikondwerero ndi ulemu. 17 Mʼchigawo chilichonse ndi mu mzinda uliwonse, kumene mawu a mfumu onena za lamulo lake anafika, kunali chimwemwe ndi chikondwerero pakati pa Ayuda. Linali tsiku la phwando ndi chikondwerero. Ndipo anthu ambiri a mitundu ina anazitcha Ayuda chifukwa anachita mantha ndi Ayudawo.

In Other Versions

Esther 8 in the ANGEFD

Esther 8 in the ANTPNG2D

Esther 8 in the AS21

Esther 8 in the BAGH

Esther 8 in the BBPNG

Esther 8 in the BBT1E

Esther 8 in the BDS

Esther 8 in the BEV

Esther 8 in the BHAD

Esther 8 in the BIB

Esther 8 in the BLPT

Esther 8 in the BNT

Esther 8 in the BNTABOOT

Esther 8 in the BNTLV

Esther 8 in the BOATCB

Esther 8 in the BOATCB2

Esther 8 in the BOBCV

Esther 8 in the BOCNT

Esther 8 in the BOECS

Esther 8 in the BOHCB

Esther 8 in the BOHCV

Esther 8 in the BOHLNT

Esther 8 in the BOHNTLTAL

Esther 8 in the BOICB

Esther 8 in the BOILNTAP

Esther 8 in the BOITCV

Esther 8 in the BOKCV

Esther 8 in the BOKCV2

Esther 8 in the BOKHWOG

Esther 8 in the BOKSSV

Esther 8 in the BOLCB

Esther 8 in the BOLCB2

Esther 8 in the BOMCV

Esther 8 in the BONAV

Esther 8 in the BONCB

Esther 8 in the BONLT

Esther 8 in the BONUT2

Esther 8 in the BOPLNT

Esther 8 in the BOSCB

Esther 8 in the BOSNC

Esther 8 in the BOTLNT

Esther 8 in the BOVCB

Esther 8 in the BOYCB

Esther 8 in the BPBB

Esther 8 in the BPH

Esther 8 in the BSB

Esther 8 in the CCB

Esther 8 in the CUV

Esther 8 in the CUVS

Esther 8 in the DBT

Esther 8 in the DGDNT

Esther 8 in the DHNT

Esther 8 in the DNT

Esther 8 in the ELBE

Esther 8 in the EMTV

Esther 8 in the ESV

Esther 8 in the FBV

Esther 8 in the FEB

Esther 8 in the GGMNT

Esther 8 in the GNT

Esther 8 in the HARY

Esther 8 in the HNT

Esther 8 in the IRVA

Esther 8 in the IRVB

Esther 8 in the IRVG

Esther 8 in the IRVH

Esther 8 in the IRVK

Esther 8 in the IRVM

Esther 8 in the IRVM2

Esther 8 in the IRVO

Esther 8 in the IRVP

Esther 8 in the IRVT

Esther 8 in the IRVT2

Esther 8 in the IRVU

Esther 8 in the ISVN

Esther 8 in the JSNT

Esther 8 in the KAPI

Esther 8 in the KBT1ETNIK

Esther 8 in the KBV

Esther 8 in the KJV

Esther 8 in the KNFD

Esther 8 in the LBA

Esther 8 in the LBLA

Esther 8 in the LNT

Esther 8 in the LSV

Esther 8 in the MAAL

Esther 8 in the MBV

Esther 8 in the MBV2

Esther 8 in the MHNT

Esther 8 in the MKNFD

Esther 8 in the MNG

Esther 8 in the MNT

Esther 8 in the MNT2

Esther 8 in the MRS1T

Esther 8 in the NAA

Esther 8 in the NASB

Esther 8 in the NBLA

Esther 8 in the NBS

Esther 8 in the NBVTP

Esther 8 in the NET2

Esther 8 in the NIV11

Esther 8 in the NNT

Esther 8 in the NNT2

Esther 8 in the NNT3

Esther 8 in the PDDPT

Esther 8 in the PFNT

Esther 8 in the RMNT

Esther 8 in the SBIAS

Esther 8 in the SBIBS

Esther 8 in the SBIBS2

Esther 8 in the SBICS

Esther 8 in the SBIDS

Esther 8 in the SBIGS

Esther 8 in the SBIHS

Esther 8 in the SBIIS

Esther 8 in the SBIIS2

Esther 8 in the SBIIS3

Esther 8 in the SBIKS

Esther 8 in the SBIKS2

Esther 8 in the SBIMS

Esther 8 in the SBIOS

Esther 8 in the SBIPS

Esther 8 in the SBISS

Esther 8 in the SBITS

Esther 8 in the SBITS2

Esther 8 in the SBITS3

Esther 8 in the SBITS4

Esther 8 in the SBIUS

Esther 8 in the SBIVS

Esther 8 in the SBT

Esther 8 in the SBT1E

Esther 8 in the SCHL

Esther 8 in the SNT

Esther 8 in the SUSU

Esther 8 in the SUSU2

Esther 8 in the SYNO

Esther 8 in the TBIAOTANT

Esther 8 in the TBT1E

Esther 8 in the TBT1E2

Esther 8 in the TFTIP

Esther 8 in the TFTU

Esther 8 in the TGNTATF3T

Esther 8 in the THAI

Esther 8 in the TNFD

Esther 8 in the TNT

Esther 8 in the TNTIK

Esther 8 in the TNTIL

Esther 8 in the TNTIN

Esther 8 in the TNTIP

Esther 8 in the TNTIZ

Esther 8 in the TOMA

Esther 8 in the TTENT

Esther 8 in the UBG

Esther 8 in the UGV

Esther 8 in the UGV2

Esther 8 in the UGV3

Esther 8 in the VBL

Esther 8 in the VDCC

Esther 8 in the YALU

Esther 8 in the YAPE

Esther 8 in the YBVTP

Esther 8 in the ZBP