Exodus 18 (BOGWICC)

1 Yetero wansembe wa ku Midiyani amenenso anali mpongozi wa Mose, anamva zonse zimene Mulungu anachitira Mose ndi anthu ake a Aisraeli ndi mmene Yehova anawatulutsira mʼdziko la Igupto. 2 Mose atamubweza Zipora, mkazi wake, Yetero, mpongozi wake anamulandira 3 mwana wake wamkaziyo pamodzi ndi ana ake aamuna awiri. Mose anamupatsa mwana wachisamba dzina loti Geresomu popeza anati, “Ndakhala mlendo mʼdziko lachilendo.” 4 Ndipo mwana wake wachiwiri anamupatsa dzina loti Eliezara, pakuti anati, “Mulungu wa makolo anga anali thandizo langa. Iye anandipulumutsa ku lupanga la Farao.” 5 Yetero, mpongozi wa Mose pamodzi ndi ana a Mose aamuna awiri ndi mkazi wake anabwera kwa Mose ku chipululu pa phiri la Mulungu kumene Mose anamanga misasa. 6 Yetero anali atatumiza uthenga kwa Mose kuti, “Ine Yetero, mpongozi wako, ndikubwera ndi mkazi wako ndi ana ake awiri.” 7 Kotero Mose anatuluka kukakumana ndi mpongozi wake ndipo anawerama ndi kupsompsona. Atalonjerana anakalowa mu tenti 8 Mose anafotokozera mpongozi wake zonse zimene Yehova anamuchita Farao ndi Aigupto chifukwa cha Israeli komanso zowawa zonse anakumana nazo mʼnjira. Mose anafotokozanso momwe Yehova anawapulumutsira. 9 Yetero anakondwa kwambiri atamva zabwino zonse zimene Yehova anachitira Aisraeli powapulumutsa mʼdzanja la Aigupto. 10 Iye anati, “Alemekezeke Yehova amene wakupulumutsani mʼdzanja la Aigupto ndi Farao. Wapulumutsanso anthuwa mʼdzanja la Aigupto. 11 Tsopano ndikudziwa kuti Yehova ndi wopambana milungu ina yonse, pakuti anachita izi kwa amene ananyoza Israeli.” 12 Ndipo Yetero, mpongozi wa Mose anapereka nsembe yopsereza ndi nsembe zina kwa Mulungu. Aaroni ndi akuluakulu onse a Israeli anabwera kudzadya chakudya pamodzi ndi mpongozi wa Mose pamaso pa Mulungu. 13 Mmawa mwake, Mose anakhala pa mpando kuti aweruze milandu ya anthu. Anthu anayima momuzungulira kuyambira mmawa mpaka madzulo. 14 Mpongozi wa Mose ataona zonse zimene iye amawachitira anthu anati, “Nʼchiyani chimene mukuwachitira anthuwa? Nʼchifukwa chiyani mulipo nokha woweruza, pamene anthu onsewa ayimirira kuyambira mmawa mpaka madzulo?” 15 Mose anamuyankha kuti, “Chifukwa anthuwa anabwera kwa ine kudzafunsa zimene Mulungu akufuna. 16 Ngati munthu akangana ndi mʼbale wake, onse awiri amabwera kwa ine, ndipo ine ndimawaweruza. Ndimawawuzanso malamulo a Mulungu ndi malangizo ake.” 17 Mpongozi wa Mose anayankha kuti, “Zimene mukuchitazi si zabwino. 18 Ntchitoyi ndi yayikulu kuposa mphamvu zanu. Inu simungathe kuyigwira nokha. Inu pamodzi ndi anthuwa amene amabwera kwa inu mudzatopa. 19 Tsono tamverani ndikulangizeni, ndipo Mulungu akhale nanu. Inu muziwayimirira anthuwa pamaso pa Mulungu, ndipo mikangano yawo muzibwera nayo kwa Iye. 20 Aphunzitseni mawu ndi malangizo a Mulungu. Aphunzitseni mmene ayenera kukhalira ndi zimene ayenera kuchita. 21 Koma sankhani amuna odziwa ntchito yawo, anthu owopa Mulungu, anthu odalirika amene amadana ndi kupeza phindu mwachinyengo. Tsono muwayike kuti akhale oyangʼanira anthu motere: atsogoleri a anthu 1,000, ena a anthu 100, ena a anthu 50 ndi ena a anthu khumi. 22 Tsono amenewa aziweruza anthu nthawi zonse. Mlandu uliwonse waukulu azibwera nawo kwa inu, koma mlandu waungʼono aziweruza okha. Izi zidzachititsa kuti ntchito yanu ipepuke, popeza mudzagwira ntchito mothandizana. 23 Ngati mutsatira malangizowa monga mmene Mulungu wakulamulirani ndiye kuti simudzafowoka ndipo anthu onsewa adzapita kwawo mu mtendere.” 24 Mose anamvera mpongozi wake ndi kuchita zonse zimene iye ananena. 25 Iye anasankha amuna odziwa bwino ntchito zawo ndipo anawayika kuti akhale atsogoleri, oyangʼanira anthu motere: atsogoleri a anthu 1,000, ena a anthu 500, ena a anthu makumi asanu ndi ena a anthu khumi. 26 Iwowa ankaweruza anthu nthawi zonse. Milandu yovuta ankabwera nayo kwa Mose, koma yosavuta ankayiweruza okha. 27 Kenaka Mose analola kuti mpongozi wake, Yetero anyamuke kubwerera ku dziko la kwawo.

In Other Versions

Exodus 18 in the ANGEFD

Exodus 18 in the ANTPNG2D

Exodus 18 in the AS21

Exodus 18 in the BAGH

Exodus 18 in the BBPNG

Exodus 18 in the BBT1E

Exodus 18 in the BDS

Exodus 18 in the BEV

Exodus 18 in the BHAD

Exodus 18 in the BIB

Exodus 18 in the BLPT

Exodus 18 in the BNT

Exodus 18 in the BNTABOOT

Exodus 18 in the BNTLV

Exodus 18 in the BOATCB

Exodus 18 in the BOATCB2

Exodus 18 in the BOBCV

Exodus 18 in the BOCNT

Exodus 18 in the BOECS

Exodus 18 in the BOHCB

Exodus 18 in the BOHCV

Exodus 18 in the BOHLNT

Exodus 18 in the BOHNTLTAL

Exodus 18 in the BOICB

Exodus 18 in the BOILNTAP

Exodus 18 in the BOITCV

Exodus 18 in the BOKCV

Exodus 18 in the BOKCV2

Exodus 18 in the BOKHWOG

Exodus 18 in the BOKSSV

Exodus 18 in the BOLCB

Exodus 18 in the BOLCB2

Exodus 18 in the BOMCV

Exodus 18 in the BONAV

Exodus 18 in the BONCB

Exodus 18 in the BONLT

Exodus 18 in the BONUT2

Exodus 18 in the BOPLNT

Exodus 18 in the BOSCB

Exodus 18 in the BOSNC

Exodus 18 in the BOTLNT

Exodus 18 in the BOVCB

Exodus 18 in the BOYCB

Exodus 18 in the BPBB

Exodus 18 in the BPH

Exodus 18 in the BSB

Exodus 18 in the CCB

Exodus 18 in the CUV

Exodus 18 in the CUVS

Exodus 18 in the DBT

Exodus 18 in the DGDNT

Exodus 18 in the DHNT

Exodus 18 in the DNT

Exodus 18 in the ELBE

Exodus 18 in the EMTV

Exodus 18 in the ESV

Exodus 18 in the FBV

Exodus 18 in the FEB

Exodus 18 in the GGMNT

Exodus 18 in the GNT

Exodus 18 in the HARY

Exodus 18 in the HNT

Exodus 18 in the IRVA

Exodus 18 in the IRVB

Exodus 18 in the IRVG

Exodus 18 in the IRVH

Exodus 18 in the IRVK

Exodus 18 in the IRVM

Exodus 18 in the IRVM2

Exodus 18 in the IRVO

Exodus 18 in the IRVP

Exodus 18 in the IRVT

Exodus 18 in the IRVT2

Exodus 18 in the IRVU

Exodus 18 in the ISVN

Exodus 18 in the JSNT

Exodus 18 in the KAPI

Exodus 18 in the KBT1ETNIK

Exodus 18 in the KBV

Exodus 18 in the KJV

Exodus 18 in the KNFD

Exodus 18 in the LBA

Exodus 18 in the LBLA

Exodus 18 in the LNT

Exodus 18 in the LSV

Exodus 18 in the MAAL

Exodus 18 in the MBV

Exodus 18 in the MBV2

Exodus 18 in the MHNT

Exodus 18 in the MKNFD

Exodus 18 in the MNG

Exodus 18 in the MNT

Exodus 18 in the MNT2

Exodus 18 in the MRS1T

Exodus 18 in the NAA

Exodus 18 in the NASB

Exodus 18 in the NBLA

Exodus 18 in the NBS

Exodus 18 in the NBVTP

Exodus 18 in the NET2

Exodus 18 in the NIV11

Exodus 18 in the NNT

Exodus 18 in the NNT2

Exodus 18 in the NNT3

Exodus 18 in the PDDPT

Exodus 18 in the PFNT

Exodus 18 in the RMNT

Exodus 18 in the SBIAS

Exodus 18 in the SBIBS

Exodus 18 in the SBIBS2

Exodus 18 in the SBICS

Exodus 18 in the SBIDS

Exodus 18 in the SBIGS

Exodus 18 in the SBIHS

Exodus 18 in the SBIIS

Exodus 18 in the SBIIS2

Exodus 18 in the SBIIS3

Exodus 18 in the SBIKS

Exodus 18 in the SBIKS2

Exodus 18 in the SBIMS

Exodus 18 in the SBIOS

Exodus 18 in the SBIPS

Exodus 18 in the SBISS

Exodus 18 in the SBITS

Exodus 18 in the SBITS2

Exodus 18 in the SBITS3

Exodus 18 in the SBITS4

Exodus 18 in the SBIUS

Exodus 18 in the SBIVS

Exodus 18 in the SBT

Exodus 18 in the SBT1E

Exodus 18 in the SCHL

Exodus 18 in the SNT

Exodus 18 in the SUSU

Exodus 18 in the SUSU2

Exodus 18 in the SYNO

Exodus 18 in the TBIAOTANT

Exodus 18 in the TBT1E

Exodus 18 in the TBT1E2

Exodus 18 in the TFTIP

Exodus 18 in the TFTU

Exodus 18 in the TGNTATF3T

Exodus 18 in the THAI

Exodus 18 in the TNFD

Exodus 18 in the TNT

Exodus 18 in the TNTIK

Exodus 18 in the TNTIL

Exodus 18 in the TNTIN

Exodus 18 in the TNTIP

Exodus 18 in the TNTIZ

Exodus 18 in the TOMA

Exodus 18 in the TTENT

Exodus 18 in the UBG

Exodus 18 in the UGV

Exodus 18 in the UGV2

Exodus 18 in the UGV3

Exodus 18 in the VBL

Exodus 18 in the VDCC

Exodus 18 in the YALU

Exodus 18 in the YAPE

Exodus 18 in the YBVTP

Exodus 18 in the ZBP