Exodus 19 (BOGWICC)
1 Ana a Israeli aja anafika ku chipululu cha Sinai pa tsiku loyamba la mwezi wachitatu chichokere mʼdziko la Igupto. 2 Atachoka ku Refidimu, anafika ku Sinai, ndipo Aisraeli anamangako misasa yawo moyangʼanana ndi phirilo. 3 Mose anakwera ku phiri kukakumana ndi Mulungu ndipo Yehova anamuyitana nati, “Ukawuze zidzukulu za Yakobo, ana onse a Israeli kuti, 4 ‘Inu eni munaona zimene ndinawachitira Aigupto ndiponso mmene ndinakunyamulirani, monga mmene chiwombankhanga chimanyamulira ana ake pa mapiko,’ ndikukubweretsani kwa Ine. 5 Tsopano, ngati mumveradi mawu anga ndi kusunga pangano langa, mudzakhala chuma changa chapamtima pakati pa mitundu yonse. Ngakhale kuti dziko lonse lapansi ndi langa, 6 inu mudzakhala ansembe achifumu ndi mtundu woyera mtima. Awa ndi mawu amene uyenera kuwawuza Aisraeli.” 7 Ndipo Mose anabwerera ndi kuyitanitsa akuluakulu. Atabwera anawafotokozera mawu amene Yehova anamulamulira kuti adzanene. 8 Anthu onse anayankha pamodzi kuti, “Ife tidzachita zonse zimene Yehova wanena.” Choncho Mose anabweza yankho lawo kwa Yehova. 9 Yehova anati kwa Mose, “Ine ndibwera kwa iwe mu mtambo wakuda kuti anthu adzandimve ndikuyankhula ndi iwe. Choncho adzakukhulupirira nthawi zonse.” Kenaka Mose anawuza Yehova zimene anthu ananena. 10 Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Pita kwa anthu onse ndi kuwayeretsa lero ndi mawa. Achape zovala zawo 11 ndipo akhale atakonzeka pofika tsiku lachitatu, chifukwa tsiku limenelo Yehova adzatsika pa phiri la Sinai anthu onse akuona. 12 Uwalembere malire anthuwo kuzungulira phirilo ndipo uwawuze kuti, ‘Samalani musakwere phirilo kapena kukhudza tsinde lake. Aliyense wokhudza phiri adzaphedwa ndithu. 13 Aliyense wokhudza phiri adzaphedwa ndi miyala kapena kumulasa ndi mivi. Palibe amene adzamukhudze. Palibe munthu amene adzaloledwa kukhala ndi moyo ngakhale nyama. Iwo adzayenera kuphedwa.’ Koma anthu adzapita ku phirilo akadzamva kulira kwa lipenga la nyanga yankhosa.” 14 Tsono Mose anatsika phiri lija nafika kwa anthu aja ndi kuwayeretsa. Iwo anachapa zovala zawo. 15 Kenaka iye anati kwa anthu, “Konzekerani tsiku lachitatu, musagone pamodzi ndi mkazi.” 16 Mʼmamawa wa tsiku lachitatu kunali mabingu, ziphaliwali ndi mtambo wakuda umene unaphimba phiri, ndiponso lipenga lolira kwambiri. Aliyense ku misasa kuja ananjenjemera ndi mantha. 17 Ndipo Mose anatsogolera anthu kutuluka mʼmisasa kukakumana ndi Mulungu, ndipo anayima mʼmunsi mwa phiri. 18 Phiri la Sinai linakutidwa ndi utsi, chifukwa Yehova anatsika ndi moto pa phiripo. Utsi unakwera ngati wochokera mʼngʼanjo yamoto ndipo phiri lonse linagwedezeka kwambiri. 19 Liwu la lipenga linkakulirakulira. Tsono Mose anayankhula ndipo Yehova anamuyankha ndi mabingu. 20 Yehova anatsika nafika pamwamba pa phiri la Sinai, ndipo anayitana Mose kuti apite pa phiripo. Choncho Mose anakwera, 21 ndipo Yehova anati kwa iye, “Tsika ukawachenjeze anthu kuti asayesere kudutsa malire kuti adzandione chifukwa ambiri a iwo adzafa. 22 Ngakhale ansembe amene amatumikira pamaso pa Yehova ayenera kudziyeretsa kuopa kuti ndingadzawalange.” 23 Mose anati kwa Yehova, “Anthu sangakwere phiri la Sinai chifukwa inu munatichenjeza. Lembani malire kuzungulira phiri ndipo mulipatule kuti likhale loyera.” 24 Yehova anayankha, “Tsika ukamutenge Aaroni. Koma ansembe ndi anthu asayesere kubzola malire kuti abwere kwa Yehova chifukwa Iye adzawalanga.” 25 Ndipo Mose anatsika ndi kukawawuza anthuwo.
In Other Versions
Exodus 19 in the ANGEFD
Exodus 19 in the ANTPNG2D
Exodus 19 in the AS21
Exodus 19 in the BAGH
Exodus 19 in the BBPNG
Exodus 19 in the BBT1E
Exodus 19 in the BDS
Exodus 19 in the BEV
Exodus 19 in the BHAD
Exodus 19 in the BIB
Exodus 19 in the BLPT
Exodus 19 in the BNT
Exodus 19 in the BNTABOOT
Exodus 19 in the BNTLV
Exodus 19 in the BOATCB
Exodus 19 in the BOATCB2
Exodus 19 in the BOBCV
Exodus 19 in the BOCNT
Exodus 19 in the BOECS
Exodus 19 in the BOHCB
Exodus 19 in the BOHCV
Exodus 19 in the BOHLNT
Exodus 19 in the BOHNTLTAL
Exodus 19 in the BOICB
Exodus 19 in the BOILNTAP
Exodus 19 in the BOITCV
Exodus 19 in the BOKCV
Exodus 19 in the BOKCV2
Exodus 19 in the BOKHWOG
Exodus 19 in the BOKSSV
Exodus 19 in the BOLCB
Exodus 19 in the BOLCB2
Exodus 19 in the BOMCV
Exodus 19 in the BONAV
Exodus 19 in the BONCB
Exodus 19 in the BONLT
Exodus 19 in the BONUT2
Exodus 19 in the BOPLNT
Exodus 19 in the BOSCB
Exodus 19 in the BOSNC
Exodus 19 in the BOTLNT
Exodus 19 in the BOVCB
Exodus 19 in the BOYCB
Exodus 19 in the BPBB
Exodus 19 in the BPH
Exodus 19 in the BSB
Exodus 19 in the CCB
Exodus 19 in the CUV
Exodus 19 in the CUVS
Exodus 19 in the DBT
Exodus 19 in the DGDNT
Exodus 19 in the DHNT
Exodus 19 in the DNT
Exodus 19 in the ELBE
Exodus 19 in the EMTV
Exodus 19 in the ESV
Exodus 19 in the FBV
Exodus 19 in the FEB
Exodus 19 in the GGMNT
Exodus 19 in the GNT
Exodus 19 in the HARY
Exodus 19 in the HNT
Exodus 19 in the IRVA
Exodus 19 in the IRVB
Exodus 19 in the IRVG
Exodus 19 in the IRVH
Exodus 19 in the IRVK
Exodus 19 in the IRVM
Exodus 19 in the IRVM2
Exodus 19 in the IRVO
Exodus 19 in the IRVP
Exodus 19 in the IRVT
Exodus 19 in the IRVT2
Exodus 19 in the IRVU
Exodus 19 in the ISVN
Exodus 19 in the JSNT
Exodus 19 in the KAPI
Exodus 19 in the KBT1ETNIK
Exodus 19 in the KBV
Exodus 19 in the KJV
Exodus 19 in the KNFD
Exodus 19 in the LBA
Exodus 19 in the LBLA
Exodus 19 in the LNT
Exodus 19 in the LSV
Exodus 19 in the MAAL
Exodus 19 in the MBV
Exodus 19 in the MBV2
Exodus 19 in the MHNT
Exodus 19 in the MKNFD
Exodus 19 in the MNG
Exodus 19 in the MNT
Exodus 19 in the MNT2
Exodus 19 in the MRS1T
Exodus 19 in the NAA
Exodus 19 in the NASB
Exodus 19 in the NBLA
Exodus 19 in the NBS
Exodus 19 in the NBVTP
Exodus 19 in the NET2
Exodus 19 in the NIV11
Exodus 19 in the NNT
Exodus 19 in the NNT2
Exodus 19 in the NNT3
Exodus 19 in the PDDPT
Exodus 19 in the PFNT
Exodus 19 in the RMNT
Exodus 19 in the SBIAS
Exodus 19 in the SBIBS
Exodus 19 in the SBIBS2
Exodus 19 in the SBICS
Exodus 19 in the SBIDS
Exodus 19 in the SBIGS
Exodus 19 in the SBIHS
Exodus 19 in the SBIIS
Exodus 19 in the SBIIS2
Exodus 19 in the SBIIS3
Exodus 19 in the SBIKS
Exodus 19 in the SBIKS2
Exodus 19 in the SBIMS
Exodus 19 in the SBIOS
Exodus 19 in the SBIPS
Exodus 19 in the SBISS
Exodus 19 in the SBITS
Exodus 19 in the SBITS2
Exodus 19 in the SBITS3
Exodus 19 in the SBITS4
Exodus 19 in the SBIUS
Exodus 19 in the SBIVS
Exodus 19 in the SBT
Exodus 19 in the SBT1E
Exodus 19 in the SCHL
Exodus 19 in the SNT
Exodus 19 in the SUSU
Exodus 19 in the SUSU2
Exodus 19 in the SYNO
Exodus 19 in the TBIAOTANT
Exodus 19 in the TBT1E
Exodus 19 in the TBT1E2
Exodus 19 in the TFTIP
Exodus 19 in the TFTU
Exodus 19 in the TGNTATF3T
Exodus 19 in the THAI
Exodus 19 in the TNFD
Exodus 19 in the TNT
Exodus 19 in the TNTIK
Exodus 19 in the TNTIL
Exodus 19 in the TNTIN
Exodus 19 in the TNTIP
Exodus 19 in the TNTIZ
Exodus 19 in the TOMA
Exodus 19 in the TTENT
Exodus 19 in the UBG
Exodus 19 in the UGV
Exodus 19 in the UGV2
Exodus 19 in the UGV3
Exodus 19 in the VBL
Exodus 19 in the VDCC
Exodus 19 in the YALU
Exodus 19 in the YAPE
Exodus 19 in the YBVTP
Exodus 19 in the ZBP