Exodus 2 (BOGWICC)
1 Ndipo munthu wina wa fuko la Levi anakwatira mkazi wa fuko lomwelo. 2 Mkaziyo anatenga pathupi ndipo anabereka mwana wamwamuna. Ataona kuti mwanayo anali wokongola, anamubisa kwa miyezi itatu. 3 Koma mwanayo atafika pa msinkhu woti sakanathanso kubisidwa, amayi ake anatenga kadengu kopangidwa ndi bango nakamata phula. Kenaka anayika mwanayo mʼmenemo ndi kukamuyika pa mabango mu mtsinje wa Nailo. 4 Mlongo wake wa mwanayo anayima pataliko kuti aone chimene chidzamuchitikira mwanayo. 5 Mwana wamkazi wa Farao anapita ku mtsinje wa Nailo kukasamba ndipo adzakazi ake ankayenda mʼmbali mwa mtsinjewo. Tsono mwana wa Farao uja anaona kadenguko pakati pa mabango ndipo anatuma mdzakazi wake kuti akakatenge. 6 Iye atavundukula anaona mwana wamwamuna akungolira. Iye anamva naye chisoni mwana uja, nati, “Ameneyu ndi mmodzi mwa ana a Chihebri.” 7 Kenaka mlongo wake wa mwanayo anafunsa mwana wa Farao kuti, “Ndingapite kukakupezerani mmodzi mwa amayi a Chihebri kuti azikakulererani mwanayu?” 8 Iye anayankha kuti, “Inde, pita.” Ndipo mtsikanayo anapita nakayitana amayi a mwanayo. 9 Mwana wa Farao anati, “Tengani mwanayu mukandilerere, ndidzakulipirani.” Mayiyo anatenga mwanayo kukamulera. 10 Mwanayo atakula anakamupereka kwa mwana wa Farao ndipo anakhala mwana wake. Iye anamutcha dzina lake Mose, popeza anati, “Ndinamuvuwula mʼmadzi.” 11 Tsiku lina, Mose atakula, anapita kumene kunali anthu a mtundu wake ndipo anawaona akugwira ntchito yowawa. Iye anaona Mwigupto akumenya Mhebri, mmodzi mwa anthu a mtundu wake. 12 Atayangʼana uku ndi uku, naona kuti panalibe wina aliyense, Mose anamupha Mwiguptoyo ndipo anamukwirira mu mchenga. 13 Mmawa mwake Mose anapita ndipo anaona anthu awiri a Chihebri akumenyana. Iye anafunsa amene anali wolakwa kuti, “Chifukwa chiyani ukumenya Mhebri mnzako?” 14 Munthu uja anati, “Kodi ndani anakuyika kuti ukhale wotilamulira ndi wotiweruza? Kodi ukufuna kundipha monga momwe unaphera Mwigupto uja?” Mose anachita mantha ndipo anati mu mtima mwake, “Chimene ndinachita chija chadziwika.” 15 Farao atamva zimenezi anafuna kuti aphe Mose, koma Mose anathawa ndipo anapita kukakhala ku Midiyani. Ali kumeneko, tsiku lina anakhala pansi pafupi ndi chitsime. 16 Wansembe wa ku Midiyaniko anali ndi ana aakazi asanu ndi awiri. Iwowa anabwera kudzatunga madzi ndi kudzaza mu zomwera kuti amwetse nkhosa za abambo awo. 17 Koma kunabwera abusa ena amene anathamangitsa atsikana aja. Ndiye Mose anayimirira nawathandiza atsikana aja ndi kumwetsa nkhosa zawo. 18 Atsikana aja atabwerera kwa abambo awo Reueli, iye anawafunsa kuti, “Chifukwa chiyani lero mwabwera msanga?” 19 Atsikanawo anayankha kuti, “Mwigupto wina ndiye watilanditsa kwa abusa. Ndiponso anatitungira madzi ndi kumwetsa ziweto zathu.” 20 Tsono Reueli anafunsa ana ake kuti, “Ndiye ali kuti munthuyo? Chifukwa chiyani mwamusiya? Kamuyitaneni kuti adzadye.” 21 Mose anavomera kukhala ndi Reueli, ndipo anamupatsa Zipora kuti akhale mkazi wake. 22 Zipora anabereka mwana wa mwamuna amene Mose anamutcha Geresomu, popeza anati, “Ndakhala mlendo mʼdziko la eni.” 23 Nthawi yonseyo nʼkuti ana a Israeli akulira chifukwa cha ukapolo wawo uja. Iwo anafuwula kupempha thandizo, ndipo kulira kwawoko kunafika kwa Mulungu. 24 Mulungu anamva kubuwula kwawo ndipo anakumbukira pangano lake ndi Abrahamu, Isake ndi Yakobo. 25 Mulungu ataona Aisraeli aja ndi masautso awo, Iye anawamvera chifundo.
In Other Versions
Exodus 2 in the ANGEFD
Exodus 2 in the ANTPNG2D
Exodus 2 in the AS21
Exodus 2 in the BAGH
Exodus 2 in the BBPNG
Exodus 2 in the BBT1E
Exodus 2 in the BDS
Exodus 2 in the BEV
Exodus 2 in the BHAD
Exodus 2 in the BIB
Exodus 2 in the BLPT
Exodus 2 in the BNT
Exodus 2 in the BNTABOOT
Exodus 2 in the BNTLV
Exodus 2 in the BOATCB
Exodus 2 in the BOATCB2
Exodus 2 in the BOBCV
Exodus 2 in the BOCNT
Exodus 2 in the BOECS
Exodus 2 in the BOHCB
Exodus 2 in the BOHCV
Exodus 2 in the BOHLNT
Exodus 2 in the BOHNTLTAL
Exodus 2 in the BOICB
Exodus 2 in the BOILNTAP
Exodus 2 in the BOITCV
Exodus 2 in the BOKCV
Exodus 2 in the BOKCV2
Exodus 2 in the BOKHWOG
Exodus 2 in the BOKSSV
Exodus 2 in the BOLCB
Exodus 2 in the BOLCB2
Exodus 2 in the BOMCV
Exodus 2 in the BONAV
Exodus 2 in the BONCB
Exodus 2 in the BONLT
Exodus 2 in the BONUT2
Exodus 2 in the BOPLNT
Exodus 2 in the BOSCB
Exodus 2 in the BOSNC
Exodus 2 in the BOTLNT
Exodus 2 in the BOVCB
Exodus 2 in the BOYCB
Exodus 2 in the BPBB
Exodus 2 in the BPH
Exodus 2 in the BSB
Exodus 2 in the CCB
Exodus 2 in the CUV
Exodus 2 in the CUVS
Exodus 2 in the DBT
Exodus 2 in the DGDNT
Exodus 2 in the DHNT
Exodus 2 in the DNT
Exodus 2 in the ELBE
Exodus 2 in the EMTV
Exodus 2 in the ESV
Exodus 2 in the FBV
Exodus 2 in the FEB
Exodus 2 in the GGMNT
Exodus 2 in the GNT
Exodus 2 in the HARY
Exodus 2 in the HNT
Exodus 2 in the IRVA
Exodus 2 in the IRVB
Exodus 2 in the IRVG
Exodus 2 in the IRVH
Exodus 2 in the IRVK
Exodus 2 in the IRVM
Exodus 2 in the IRVM2
Exodus 2 in the IRVO
Exodus 2 in the IRVP
Exodus 2 in the IRVT
Exodus 2 in the IRVT2
Exodus 2 in the IRVU
Exodus 2 in the ISVN
Exodus 2 in the JSNT
Exodus 2 in the KAPI
Exodus 2 in the KBT1ETNIK
Exodus 2 in the KBV
Exodus 2 in the KJV
Exodus 2 in the KNFD
Exodus 2 in the LBA
Exodus 2 in the LBLA
Exodus 2 in the LNT
Exodus 2 in the LSV
Exodus 2 in the MAAL
Exodus 2 in the MBV
Exodus 2 in the MBV2
Exodus 2 in the MHNT
Exodus 2 in the MKNFD
Exodus 2 in the MNG
Exodus 2 in the MNT
Exodus 2 in the MNT2
Exodus 2 in the MRS1T
Exodus 2 in the NAA
Exodus 2 in the NASB
Exodus 2 in the NBLA
Exodus 2 in the NBS
Exodus 2 in the NBVTP
Exodus 2 in the NET2
Exodus 2 in the NIV11
Exodus 2 in the NNT
Exodus 2 in the NNT2
Exodus 2 in the NNT3
Exodus 2 in the PDDPT
Exodus 2 in the PFNT
Exodus 2 in the RMNT
Exodus 2 in the SBIAS
Exodus 2 in the SBIBS
Exodus 2 in the SBIBS2
Exodus 2 in the SBICS
Exodus 2 in the SBIDS
Exodus 2 in the SBIGS
Exodus 2 in the SBIHS
Exodus 2 in the SBIIS
Exodus 2 in the SBIIS2
Exodus 2 in the SBIIS3
Exodus 2 in the SBIKS
Exodus 2 in the SBIKS2
Exodus 2 in the SBIMS
Exodus 2 in the SBIOS
Exodus 2 in the SBIPS
Exodus 2 in the SBISS
Exodus 2 in the SBITS
Exodus 2 in the SBITS2
Exodus 2 in the SBITS3
Exodus 2 in the SBITS4
Exodus 2 in the SBIUS
Exodus 2 in the SBIVS
Exodus 2 in the SBT
Exodus 2 in the SBT1E
Exodus 2 in the SCHL
Exodus 2 in the SNT
Exodus 2 in the SUSU
Exodus 2 in the SUSU2
Exodus 2 in the SYNO
Exodus 2 in the TBIAOTANT
Exodus 2 in the TBT1E
Exodus 2 in the TBT1E2
Exodus 2 in the TFTIP
Exodus 2 in the TFTU
Exodus 2 in the TGNTATF3T
Exodus 2 in the THAI
Exodus 2 in the TNFD
Exodus 2 in the TNT
Exodus 2 in the TNTIK
Exodus 2 in the TNTIL
Exodus 2 in the TNTIN
Exodus 2 in the TNTIP
Exodus 2 in the TNTIZ
Exodus 2 in the TOMA
Exodus 2 in the TTENT
Exodus 2 in the UBG
Exodus 2 in the UGV
Exodus 2 in the UGV2
Exodus 2 in the UGV3
Exodus 2 in the VBL
Exodus 2 in the VDCC
Exodus 2 in the YALU
Exodus 2 in the YAPE
Exodus 2 in the YBVTP
Exodus 2 in the ZBP