Exodus 36 (BOGWICC)

1 Choncho Bezaleli, Oholiabu pamodzi ndi anthu aluso onse amene Yehova anawapatsa luso ndi nzeru zodziwira kupanga zofunika zonse zomangira malo opatulika, adzapanga zonse iwowo, monga momwe Yehova analamulira.” 2 Ndipo Mose anayitana Bezaleli ndi Oholiabu ndiponso munthu aliyense waluso amene Yehova anamupatsa luso ndiponso amene anali ndi mtima wofuna kugwira ntchito. 3 Iwo analandira kuchokera kwa Mose zopereka zonse Aisraeli anabweretsa kuti agwirire ntchito yomanga malo wopatulika. Ndipo anthu anapitirira kupereka zopereka zaufulu mmawa uliwonse. 4 Kotero amisiri onse amene amagwira ntchito yonse ya malo wopatulika anasiya ntchitoyo 5 ndipo anati kwa Mose, “Anthu akubweretsa kuposa zimene zikufunika kugwirira ntchito imene Yehova analamulira kuti ichitike.” 6 Choncho Mose analamulira ndipo analengeza mu msasa onse, “Mwamuna kapena mayi aliyense asaperekenso chopereka chilichonse cha ku malo wopatulika.” Choncho anthu analetsedwa kubweretsa zambiri, 7 chifukwa zimene anali nazo zinali zoposera zimene zimafunika kugwirira ntchito yonse. 8 Anthu onse aluso pakati pa anthu ogwira ntchitoyo anapanga chihema pogwiritsa ntchito nsalu khumi zofewa, zosalala ndi zolukidwa bwino, zobiriwira, zapepo ndi zofiira. Ndipo anthu aluso anapeta pa nsaluzo Akerubi. 9 Nsalu zonse zinali zofanana. Mulitali mwake zinali mamita khumi ndi atatu, mulifupi mamita awiri. 10 Iwo analumikiza nsalu zisanu, kuti ikhale nsalu imodzi ndipo anachita chimodzimodzi ndi nsalu zisanu zinazo. 11 Kenaka anapanga zokolowekamo za nsalu yobiriwira mʼmphepete mwa nsalu imodzi yotsiriza ya mbali ina. Ndipo anachita chimodzimodzi ndi nsalu yotsiriza ya mbali inayo. 12 Iwo anasokerera zokolowekamo makumi asanu pa nsalu yoyamba ndi zokolowekamo makumi asanu zinanso pa nsalu inayo. Anapanga kuti zokolowekamozo ziziyangʼanana. 13 Kenaka anapanga ngowe zagolide 50 zolumikizira nsalu ziwirizo kotero kuti zinapanga chihema chimodzi. 14 Iwo anapanga nsalu za ubweya wambuzi zophimba pamwamba pa chihemacho. Nsalu zonse pamodzi zinalipo khumi ndi imodzi. 15 Nsalu zonse khumi ndi imodzi zinali zofanana. Mulitali mwake munali mamita khumi ndi anayi ndipo mulifupi mwake munali mamita awiri. 16 Iwo analumikiza nsalu zisanu kukhala nsalu imodzi ndipo nsalu zinazo zisanu ndi imodzi, analumikizanso kukhala nsalu imodzinso. 17 Kenaka anasokerera zokolowekamo makumi asanu mʼmphepete mwa nsalu imodzi yotsirizira ya nsalu yoyamba yolumikiza ija ndiponso anapanga zokolowekamo zina makumi asanu mʼmphepete mwa nsalu yotsirizira ya nsalu inanso yolumikiza ija. 18 Iwo anapanga ngowe 50 zamkuwa zolowetsa mu zokolowekazo ndipo anaphatikiza nsalu ziwirizo kuti tentiyo ikhale imodzi. 19 Ndipo anapanga chikopa cha nkhosa zazimuna cha utoto wofiira chophimbira tentiyo ndipo pamwamba pake anapanganso chophimbira china cha zikopa za akatumbu. 20 Iwo anapanga maferemu amatabwa amtengo wa mkesha oyimikira chihemacho. 21 Feremu iliyonse inali yotalika mamita anayi ndipo mulifupi mwake munali masentimita 69. 22 Thabwa lililonse linali ndi zolumikizira ziwiri. Iwo anapanga maferemu onse a chihemacho ndi matabwa otere. 23 Anapanga maferemu makumi awiri a mbali yakummwera kwa chihemacho, 24 ndiponso anapanga matsinde 40 asiliva ndipo anawayika pansi pa maferemuwo. Pansi pa feremu iliyonse anayika matsinde awiri ogwiriziza zolumikizira ziwiri zija. 25 Iwo anapanganso maferemu makumi awiri a mbali yakumpoto ya chihemacho, 26 ndiponso matsinde makumi anayi asiliva, awiri pansi pa feremu iliyonse. 27 Anapanganso maferemu asanu ndi imodzi a kumbuyo kwa tenti, kumbali yakumadzulo, 28 ndiponso maferemu awiri a pa ngodya yakumbuyo kwenikweni kwa tenti. 29 Pa ngodya ziwirizi panali maferemu awiri, kuyambira pansi mpaka pamwamba atalumikizidwa pa ngowe imodzi. Maferemu onse anali ofanana. 30 Choncho panali maferemu asanu ndi atatu ndiponso matsinde 16 asiliva, awiri anali pansi pa feremu iliyonse. 31 Iwo anapanganso mitanda ya matabwa amtengo wa mkesha. Mitanda isanu inali ya maferemu a mbali imodzi ya chihema, 32 mitanda isanu inanso inali ya maferemu a mbali inayo ndipo mitanda ina isanu ya mbali yakumadzulo, kumapeto kwenikweni kwa chihema. 33 Anapanga mtanda wapakati omwe umachokera pa maferemu a mbali ina mpaka mbali inanso. 34 Iwo anakuta maferemuwo ndi golide ndiponso anapanga mphete zagolide zogwiriziza mitandayo. Ndipo mitandayonso anayikuta ndi golide. 35 Anapanga nsalu yokhala ndi mtundu wamtambo, wapepo ndi ofiira ndipo nsaluyo inali yolukidwa bwino, yofewa ndi yosalala. Ndipo anthu aluso anapetapo zithunzi za Akerubi. 36 Iwo anapanga nsanamira zinayi zamtengo wa mkesha zokutidwa ndi golide. Anapanganso ngowe zagolide za nsanamirazo ndi matsinde asiliva anayi. 37 Anapanga nsalu ya pa chipata cholowera mu chihema, yamtundu wamtambo, wapepo ndi ofiira yomwe inali yofewa ndi yosalala, yopetedwa bwino ndi amisiri aluso. 38 Anapanga nsanamira zisanu ndi ngowe zake. Anakuta pamwamba pa nsanamirazo ndi zomangira zake ndi golide, ndipo anapanganso matsinde asanu amkuwa.

In Other Versions

Exodus 36 in the ANGEFD

Exodus 36 in the ANTPNG2D

Exodus 36 in the AS21

Exodus 36 in the BAGH

Exodus 36 in the BBPNG

Exodus 36 in the BBT1E

Exodus 36 in the BDS

Exodus 36 in the BEV

Exodus 36 in the BHAD

Exodus 36 in the BIB

Exodus 36 in the BLPT

Exodus 36 in the BNT

Exodus 36 in the BNTABOOT

Exodus 36 in the BNTLV

Exodus 36 in the BOATCB

Exodus 36 in the BOATCB2

Exodus 36 in the BOBCV

Exodus 36 in the BOCNT

Exodus 36 in the BOECS

Exodus 36 in the BOHCB

Exodus 36 in the BOHCV

Exodus 36 in the BOHLNT

Exodus 36 in the BOHNTLTAL

Exodus 36 in the BOICB

Exodus 36 in the BOILNTAP

Exodus 36 in the BOITCV

Exodus 36 in the BOKCV

Exodus 36 in the BOKCV2

Exodus 36 in the BOKHWOG

Exodus 36 in the BOKSSV

Exodus 36 in the BOLCB

Exodus 36 in the BOLCB2

Exodus 36 in the BOMCV

Exodus 36 in the BONAV

Exodus 36 in the BONCB

Exodus 36 in the BONLT

Exodus 36 in the BONUT2

Exodus 36 in the BOPLNT

Exodus 36 in the BOSCB

Exodus 36 in the BOSNC

Exodus 36 in the BOTLNT

Exodus 36 in the BOVCB

Exodus 36 in the BOYCB

Exodus 36 in the BPBB

Exodus 36 in the BPH

Exodus 36 in the BSB

Exodus 36 in the CCB

Exodus 36 in the CUV

Exodus 36 in the CUVS

Exodus 36 in the DBT

Exodus 36 in the DGDNT

Exodus 36 in the DHNT

Exodus 36 in the DNT

Exodus 36 in the ELBE

Exodus 36 in the EMTV

Exodus 36 in the ESV

Exodus 36 in the FBV

Exodus 36 in the FEB

Exodus 36 in the GGMNT

Exodus 36 in the GNT

Exodus 36 in the HARY

Exodus 36 in the HNT

Exodus 36 in the IRVA

Exodus 36 in the IRVB

Exodus 36 in the IRVG

Exodus 36 in the IRVH

Exodus 36 in the IRVK

Exodus 36 in the IRVM

Exodus 36 in the IRVM2

Exodus 36 in the IRVO

Exodus 36 in the IRVP

Exodus 36 in the IRVT

Exodus 36 in the IRVT2

Exodus 36 in the IRVU

Exodus 36 in the ISVN

Exodus 36 in the JSNT

Exodus 36 in the KAPI

Exodus 36 in the KBT1ETNIK

Exodus 36 in the KBV

Exodus 36 in the KJV

Exodus 36 in the KNFD

Exodus 36 in the LBA

Exodus 36 in the LBLA

Exodus 36 in the LNT

Exodus 36 in the LSV

Exodus 36 in the MAAL

Exodus 36 in the MBV

Exodus 36 in the MBV2

Exodus 36 in the MHNT

Exodus 36 in the MKNFD

Exodus 36 in the MNG

Exodus 36 in the MNT

Exodus 36 in the MNT2

Exodus 36 in the MRS1T

Exodus 36 in the NAA

Exodus 36 in the NASB

Exodus 36 in the NBLA

Exodus 36 in the NBS

Exodus 36 in the NBVTP

Exodus 36 in the NET2

Exodus 36 in the NIV11

Exodus 36 in the NNT

Exodus 36 in the NNT2

Exodus 36 in the NNT3

Exodus 36 in the PDDPT

Exodus 36 in the PFNT

Exodus 36 in the RMNT

Exodus 36 in the SBIAS

Exodus 36 in the SBIBS

Exodus 36 in the SBIBS2

Exodus 36 in the SBICS

Exodus 36 in the SBIDS

Exodus 36 in the SBIGS

Exodus 36 in the SBIHS

Exodus 36 in the SBIIS

Exodus 36 in the SBIIS2

Exodus 36 in the SBIIS3

Exodus 36 in the SBIKS

Exodus 36 in the SBIKS2

Exodus 36 in the SBIMS

Exodus 36 in the SBIOS

Exodus 36 in the SBIPS

Exodus 36 in the SBISS

Exodus 36 in the SBITS

Exodus 36 in the SBITS2

Exodus 36 in the SBITS3

Exodus 36 in the SBITS4

Exodus 36 in the SBIUS

Exodus 36 in the SBIVS

Exodus 36 in the SBT

Exodus 36 in the SBT1E

Exodus 36 in the SCHL

Exodus 36 in the SNT

Exodus 36 in the SUSU

Exodus 36 in the SUSU2

Exodus 36 in the SYNO

Exodus 36 in the TBIAOTANT

Exodus 36 in the TBT1E

Exodus 36 in the TBT1E2

Exodus 36 in the TFTIP

Exodus 36 in the TFTU

Exodus 36 in the TGNTATF3T

Exodus 36 in the THAI

Exodus 36 in the TNFD

Exodus 36 in the TNT

Exodus 36 in the TNTIK

Exodus 36 in the TNTIL

Exodus 36 in the TNTIN

Exodus 36 in the TNTIP

Exodus 36 in the TNTIZ

Exodus 36 in the TOMA

Exodus 36 in the TTENT

Exodus 36 in the UBG

Exodus 36 in the UGV

Exodus 36 in the UGV2

Exodus 36 in the UGV3

Exodus 36 in the VBL

Exodus 36 in the VDCC

Exodus 36 in the YALU

Exodus 36 in the YAPE

Exodus 36 in the YBVTP

Exodus 36 in the ZBP