Exodus 37 (BOGWICC)

1 Bezaleli anapanga Bokosi la Chipangano lamatabwa amtengo wa mkesha. Kutalika kwake kunali masentimita 114, mulifupi mwake munali masentimita 69, msinkhu wake masentimita 69. 2 Iye analikuta bokosilo ndi golide wabwino kwambiri mʼkati mwake ndi kunja komwe. Anapanganso mkombero wagolide kuzungulira bokosilo. 3 Iye anapanga mphete zinayi zagolide ndi kuzimangirira ku miyendo yake inayi ija, mbali ina ziwiri ndi mbali inanso ziwiri. 4 Kenaka anapanga mizati yamtengo wa mkesha ndi kuzikuta ndi golide. 5 Ndipo analowetsa nsichizo mʼmphete zija za mbali zonse ziwiri za bokosilo kuti azinyamulira. 6 Iye anapanga chivundikiro cha bokosilo cha golide wabwino kwambiri, kutalika kwake masentimita 114, mulifupi mwake masentimita 69. 7 Ndipo anapanga Akerubi awiri agolide osula ndi nyundo ndi kuwayika mbali ziwiri za chivundikirocho. 8 Iye anapanga kerubi mmodzi mbali ina ndi wina mbali inayo. Akerubiwa anawapangira limodzi ndi chivundikirocho mʼmapeto mwa mbali ziwirizo. 9 Mapiko a Akerubiwo anatambasukira pamwamba pa chivundikiro cha bokosilo kuti achiphimbe. Akerubiwo anakhala choyangʼanana, aliyense kuyangʼana chivundikirocho. 10 Iwo anapanga tebulo la matabwa amtengo wa mkesha, mulitali mwake masentimita 91, mulifupi mwake masentimita 46, msinkhu wake masentimita 69. 11 Kenaka analikuta ndi golide wabwino kwambiri, ndipo anapanga mkombero wagolide mʼmbali mwake. 12 Iwo anapanga feremu yozungulira tebulo, mulifupi mwake ngati chikhatho cha dzanja, ndipo anayika mkombero wagolide kuzungulira feremuyo. 13 Iwo anapanga mphete zinayi zagolide ndipo anazilumikiza ku ngodya zake zinayi, kumene kunali miyendo yake inayi. 14 Mphetezo anaziyika kufupi ndi feremu kuti azikolowekamo nsichi zonyamulira tebuloyo. 15 Anapanga nsichi zamtengo wa mkesha ndi kuzikuta ndi golide kuti azinyamulira tebulolo. 16 Ndipo anapanga ziwiya za pa tebulolo zagolide wabwino, mbale ndi zipande, mitsuko ndi mabeseni zogwiritsa ntchito popereka nsembe za chakumwa. 17 Iwo anapanga choyikapo nyale chagolide wabwino kwambiri. Tsinde lake ndi mphanda zake zinasulidwa ndi nyundo. Zikho zake zokhala ndi mphukira ndi maluwa ake zinapangidwa kumodzi. 18 Mʼmbali mwake munali mphanda zisanu ndi imodzi, zitatu mbali iliyonse. 19 Zikho zitatu zokhala ngati za maluwa amtowo, mphukira ndi duwa zinali pa mphanda yoyamba. Pa mphanda yachiwiri panalinso zikho zitatu zokhala ngati za maluwa amtowo, mphukira ndi duwa. Ndipo mphanda zonse zisanu ndi imodzi zinali chimodzimodzi ndipo zinatuluka mʼchoyikapo nyalecho. 20 Pa choyikapo nyalecho panali zikho zinayi zokhala ngati maluwa amtowo, mphukira ndi maluwa ake. 21 Mphukira yoyamba inali mʼmunsi mwa nthambi ziwiri zoyamba za pa choyikapo nyale. Mphukira yachiwiri inali mʼmunsi mwa nthambi ziwiri zinazo. Mphukira yachitatu inali mʼmunsi mwa nthambi zina ziwirinso. Zonse pamodzi zinali nthambi zisanu ndi imodzi 22 Mphukira ndi nthambi zonse zinasulidwa kumodzi ndi choyikapo nyalecho ndi golide wabwino kwambiri. 23 Iwo anapanga nyale zisanu ndi ziwiri, mbaniro ndi zowolera phulusa, zonse zinali zagolide wabwino kwambiri. 24 Iwo anapanga choyikapo nyale ndi zipangizo zake zonse zagolide wabwino kwambiri wolemera makilogalamu 34. 25 Iwo anapanga guwa lamatabwa amtengo wa mkesha lofukizirapo lubani. Linali lofanana mbali zonse, mulitali masentimita 46, mulifupi masentimita 46, ndipo msinkhu masentimita 91, ndipo nyanga zake zinapangidwa kumodzi ndi guwalo. 26 Iwo anakuta guwa lonse ndi golide wabwino kwambiri, pamwamba pake, mbali zonse ndi nyanga zake, ndipo anapanga mkombero wagolide kuzungulira guwalo. 27 Anapanga mphete ziwiri pansi pa mkomberowo ndi kulumikiza ku mbali zonse ziwiri kuti apisemo nsichi zonyamulira. 28 Anapanga mizati yamtengo wa mkesha ndipo anayikuta ndi golide. 29 Iwo anapanganso mafuta opatulika odzozera ndi zofukiza za fungo lokoma kwambiri. Iyi inali ntchito ya mʼmisiri waluso lopanga zonunkhiritsa.

In Other Versions

Exodus 37 in the ANGEFD

Exodus 37 in the ANTPNG2D

Exodus 37 in the AS21

Exodus 37 in the BAGH

Exodus 37 in the BBPNG

Exodus 37 in the BBT1E

Exodus 37 in the BDS

Exodus 37 in the BEV

Exodus 37 in the BHAD

Exodus 37 in the BIB

Exodus 37 in the BLPT

Exodus 37 in the BNT

Exodus 37 in the BNTABOOT

Exodus 37 in the BNTLV

Exodus 37 in the BOATCB

Exodus 37 in the BOATCB2

Exodus 37 in the BOBCV

Exodus 37 in the BOCNT

Exodus 37 in the BOECS

Exodus 37 in the BOHCB

Exodus 37 in the BOHCV

Exodus 37 in the BOHLNT

Exodus 37 in the BOHNTLTAL

Exodus 37 in the BOICB

Exodus 37 in the BOILNTAP

Exodus 37 in the BOITCV

Exodus 37 in the BOKCV

Exodus 37 in the BOKCV2

Exodus 37 in the BOKHWOG

Exodus 37 in the BOKSSV

Exodus 37 in the BOLCB

Exodus 37 in the BOLCB2

Exodus 37 in the BOMCV

Exodus 37 in the BONAV

Exodus 37 in the BONCB

Exodus 37 in the BONLT

Exodus 37 in the BONUT2

Exodus 37 in the BOPLNT

Exodus 37 in the BOSCB

Exodus 37 in the BOSNC

Exodus 37 in the BOTLNT

Exodus 37 in the BOVCB

Exodus 37 in the BOYCB

Exodus 37 in the BPBB

Exodus 37 in the BPH

Exodus 37 in the BSB

Exodus 37 in the CCB

Exodus 37 in the CUV

Exodus 37 in the CUVS

Exodus 37 in the DBT

Exodus 37 in the DGDNT

Exodus 37 in the DHNT

Exodus 37 in the DNT

Exodus 37 in the ELBE

Exodus 37 in the EMTV

Exodus 37 in the ESV

Exodus 37 in the FBV

Exodus 37 in the FEB

Exodus 37 in the GGMNT

Exodus 37 in the GNT

Exodus 37 in the HARY

Exodus 37 in the HNT

Exodus 37 in the IRVA

Exodus 37 in the IRVB

Exodus 37 in the IRVG

Exodus 37 in the IRVH

Exodus 37 in the IRVK

Exodus 37 in the IRVM

Exodus 37 in the IRVM2

Exodus 37 in the IRVO

Exodus 37 in the IRVP

Exodus 37 in the IRVT

Exodus 37 in the IRVT2

Exodus 37 in the IRVU

Exodus 37 in the ISVN

Exodus 37 in the JSNT

Exodus 37 in the KAPI

Exodus 37 in the KBT1ETNIK

Exodus 37 in the KBV

Exodus 37 in the KJV

Exodus 37 in the KNFD

Exodus 37 in the LBA

Exodus 37 in the LBLA

Exodus 37 in the LNT

Exodus 37 in the LSV

Exodus 37 in the MAAL

Exodus 37 in the MBV

Exodus 37 in the MBV2

Exodus 37 in the MHNT

Exodus 37 in the MKNFD

Exodus 37 in the MNG

Exodus 37 in the MNT

Exodus 37 in the MNT2

Exodus 37 in the MRS1T

Exodus 37 in the NAA

Exodus 37 in the NASB

Exodus 37 in the NBLA

Exodus 37 in the NBS

Exodus 37 in the NBVTP

Exodus 37 in the NET2

Exodus 37 in the NIV11

Exodus 37 in the NNT

Exodus 37 in the NNT2

Exodus 37 in the NNT3

Exodus 37 in the PDDPT

Exodus 37 in the PFNT

Exodus 37 in the RMNT

Exodus 37 in the SBIAS

Exodus 37 in the SBIBS

Exodus 37 in the SBIBS2

Exodus 37 in the SBICS

Exodus 37 in the SBIDS

Exodus 37 in the SBIGS

Exodus 37 in the SBIHS

Exodus 37 in the SBIIS

Exodus 37 in the SBIIS2

Exodus 37 in the SBIIS3

Exodus 37 in the SBIKS

Exodus 37 in the SBIKS2

Exodus 37 in the SBIMS

Exodus 37 in the SBIOS

Exodus 37 in the SBIPS

Exodus 37 in the SBISS

Exodus 37 in the SBITS

Exodus 37 in the SBITS2

Exodus 37 in the SBITS3

Exodus 37 in the SBITS4

Exodus 37 in the SBIUS

Exodus 37 in the SBIVS

Exodus 37 in the SBT

Exodus 37 in the SBT1E

Exodus 37 in the SCHL

Exodus 37 in the SNT

Exodus 37 in the SUSU

Exodus 37 in the SUSU2

Exodus 37 in the SYNO

Exodus 37 in the TBIAOTANT

Exodus 37 in the TBT1E

Exodus 37 in the TBT1E2

Exodus 37 in the TFTIP

Exodus 37 in the TFTU

Exodus 37 in the TGNTATF3T

Exodus 37 in the THAI

Exodus 37 in the TNFD

Exodus 37 in the TNT

Exodus 37 in the TNTIK

Exodus 37 in the TNTIL

Exodus 37 in the TNTIN

Exodus 37 in the TNTIP

Exodus 37 in the TNTIZ

Exodus 37 in the TOMA

Exodus 37 in the TTENT

Exodus 37 in the UBG

Exodus 37 in the UGV

Exodus 37 in the UGV2

Exodus 37 in the UGV3

Exodus 37 in the VBL

Exodus 37 in the VDCC

Exodus 37 in the YALU

Exodus 37 in the YAPE

Exodus 37 in the YBVTP

Exodus 37 in the ZBP