Ezekiel 13 (BOGWICC)
1 Yehova anayankhulanso nane kuti, 2 “Iwe mwana wa munthu unenere modzudzula aneneri a Israeli amene akunenera za kukhosi kwawo. Uwawuze iwowa kuti, ‘Imvani mawu a Yehova!’ 3 Ambuye Yehova akuti, ‘Tsoka kwa aneneri opusa amene amangonenera zopeka ngakhale kuti sanaone kanthu konse!’ 4 Iwe Israeli, aneneri ako ali ngati nkhandwe pa mabwinja. 5 Simunakwere khoma kuti mukakonze mʼmene munagumuka, kuti Aisraeli adziteteze kolimba pa nkhondo pa tsiku la Yehova. 6 Masomphenya awo ndi achabe ndipo kuwombeza kwawo ndi kwabodza. Iwo amati, ‘Yehova akutero,’ pomwe Yehova sanawatume. Komabe iwo amayembekezera kuti zimene ayankhulazo zichitikadi. 7 Koma Ine ndikuti masomphenya anu ngachabechabe ndi zimene mwawombedzazo nʼzabodza. Mumanena kuti, ‘Akutero Yehova,’ pamene sindinayankhule nʼkomwe. 8 “Tsono Ine Ambuye Wamphamvuzonse ndikukutsutsani chifukwa cha zoyankhula zanu zonama ndi masomphenya anu abodzawo. Ndikutero Ine Yehova. 9 Ndidzalanga aneneri amene amanenera zabodza za zinthu zimene amati anaziona mʼmasomphenya. Sadzakhala nawo mʼbwalo la anthu anga ndipo mayina awo sadzalembedwa mu kawundula wa nzika za Israeli. Sadzalowa nawo mʼdziko la Israeli. Pamenepo mudzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova. 10 “Popeza kuti aneneri asocheretsa anthu anga pomanena kuti, ‘Kuli mtendere’ pamene mtendere palibe; ndiponso anthu akamanga khoma iwo nʼkumalipaka njereza, 11 choncho ufotokozere amene alipaka njerezawo kuti khomalo lidzagwa. Mvula idzagwa mwamphamvu, kudzagwa matalala akuluakulu, ndipo kudzawomba mphepo yamkuntho. 12 Pamene khomalo lagwa, kodi anthu sadzakufunsani kuti, ‘Kodi njereza yemwe munapaka uja ali kuti?’ 13 “Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti: Mwa ukali ndidzakunthitsa mphepo ya mkuntho. Ndidzagwetsa matalala akuluakulu ndili ndi ukali ndipo ndidzavumbwitsa mvula yamphamvu ndi mkwiyo mpaka khomalo litawonongeka kotheratu. 14 Ndidzagwetsa khoma limene munalipaka njerezalo. Ndidzaligumuliratu mpaka pansi kotero kuti maziko ake adzaoneka. Khomalo likadzagwa, inu mudzawonongekamo; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova. 15 Kotero ndidzagwiritsa ntchito mkwiyo wanga pa khomali ndi pa amene analipaka njereza. Pambuyo pake ndidzakuwuzani kuti, ‘Khoma lagwa pamodzi ndi amene analipaka njereza. 16 Agwanso aneneri a Yerusalemu amene ankalosa za Yerusalemu nʼkumati anaona mʼmasomphenya za mtendere wa Yerusalemu pamene mtendere kunalibe konse, akutero Ambuye Wamphamvuzonse.’ 17 “Tsono iwe mwana wa munthu, yankhulapo pa nkhani za akazi amene ali pakati pa anthu ako. Iwo amanenera zopeka za mʼmutu mwawo. Tsono adzudzule. 18 Uwawuze kuti, ‘Ambuye Yehova akuti: Tsoka kwa akazi amene amasoka zithumwa zapamkono, amenenso amasoka nsalu za kumutu za anthu. Kodi mufuna kukola mitima ya anthu anga, inuyo nʼkupulumutsa moyo wanu? 19 Ponamiza anthu anga amene amamva za mabodza anu, inu mwapha anthu amene sanayenera kufa ndipo mwasiya ndi moyo amene sanayenera kukhala ndi moyo. 20 “ ‘Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ine ndikudana ndi zithumwa zanu zimene mumakokera nazo mitima ya anthu ngati mbalame. Ndidzazingʼamba kudzichotsa pa mikono yanu. Choncho ndidzapulumutsa miyoyo ya anthu amene munawakola ngati mbalame. 21 Ndidzangʼamba nsalu zanu za matsengazo ndi kupulumutsa anthu anga mʼmanja mwanu, ndipo simudzakhalanso ndi mphamvu yowakolera. Pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova. 22 Popeza kuti munatayitsa mtima anthu olungama ngakhale sindinafune kuti ataye mtima; ndipo munalimbitsa anthu oyipa kuti asaleka machimo awo motero sakutha kupulumutsa moyo wawo, 23 choncho inu simudzaonanso masomphenya abodza kapena kuwombeza. Ine ndidzapulumutsa anthu anga mʼmanja mwanu. Ndipo pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’ ”
In Other Versions
Ezekiel 13 in the ANGEFD
Ezekiel 13 in the ANTPNG2D
Ezekiel 13 in the AS21
Ezekiel 13 in the BAGH
Ezekiel 13 in the BBPNG
Ezekiel 13 in the BBT1E
Ezekiel 13 in the BDS
Ezekiel 13 in the BEV
Ezekiel 13 in the BHAD
Ezekiel 13 in the BIB
Ezekiel 13 in the BLPT
Ezekiel 13 in the BNT
Ezekiel 13 in the BNTABOOT
Ezekiel 13 in the BNTLV
Ezekiel 13 in the BOATCB
Ezekiel 13 in the BOATCB2
Ezekiel 13 in the BOBCV
Ezekiel 13 in the BOCNT
Ezekiel 13 in the BOECS
Ezekiel 13 in the BOHCB
Ezekiel 13 in the BOHCV
Ezekiel 13 in the BOHLNT
Ezekiel 13 in the BOHNTLTAL
Ezekiel 13 in the BOICB
Ezekiel 13 in the BOILNTAP
Ezekiel 13 in the BOITCV
Ezekiel 13 in the BOKCV
Ezekiel 13 in the BOKCV2
Ezekiel 13 in the BOKHWOG
Ezekiel 13 in the BOKSSV
Ezekiel 13 in the BOLCB
Ezekiel 13 in the BOLCB2
Ezekiel 13 in the BOMCV
Ezekiel 13 in the BONAV
Ezekiel 13 in the BONCB
Ezekiel 13 in the BONLT
Ezekiel 13 in the BONUT2
Ezekiel 13 in the BOPLNT
Ezekiel 13 in the BOSCB
Ezekiel 13 in the BOSNC
Ezekiel 13 in the BOTLNT
Ezekiel 13 in the BOVCB
Ezekiel 13 in the BOYCB
Ezekiel 13 in the BPBB
Ezekiel 13 in the BPH
Ezekiel 13 in the BSB
Ezekiel 13 in the CCB
Ezekiel 13 in the CUV
Ezekiel 13 in the CUVS
Ezekiel 13 in the DBT
Ezekiel 13 in the DGDNT
Ezekiel 13 in the DHNT
Ezekiel 13 in the DNT
Ezekiel 13 in the ELBE
Ezekiel 13 in the EMTV
Ezekiel 13 in the ESV
Ezekiel 13 in the FBV
Ezekiel 13 in the FEB
Ezekiel 13 in the GGMNT
Ezekiel 13 in the GNT
Ezekiel 13 in the HARY
Ezekiel 13 in the HNT
Ezekiel 13 in the IRVA
Ezekiel 13 in the IRVB
Ezekiel 13 in the IRVG
Ezekiel 13 in the IRVH
Ezekiel 13 in the IRVK
Ezekiel 13 in the IRVM
Ezekiel 13 in the IRVM2
Ezekiel 13 in the IRVO
Ezekiel 13 in the IRVP
Ezekiel 13 in the IRVT
Ezekiel 13 in the IRVT2
Ezekiel 13 in the IRVU
Ezekiel 13 in the ISVN
Ezekiel 13 in the JSNT
Ezekiel 13 in the KAPI
Ezekiel 13 in the KBT1ETNIK
Ezekiel 13 in the KBV
Ezekiel 13 in the KJV
Ezekiel 13 in the KNFD
Ezekiel 13 in the LBA
Ezekiel 13 in the LBLA
Ezekiel 13 in the LNT
Ezekiel 13 in the LSV
Ezekiel 13 in the MAAL
Ezekiel 13 in the MBV
Ezekiel 13 in the MBV2
Ezekiel 13 in the MHNT
Ezekiel 13 in the MKNFD
Ezekiel 13 in the MNG
Ezekiel 13 in the MNT
Ezekiel 13 in the MNT2
Ezekiel 13 in the MRS1T
Ezekiel 13 in the NAA
Ezekiel 13 in the NASB
Ezekiel 13 in the NBLA
Ezekiel 13 in the NBS
Ezekiel 13 in the NBVTP
Ezekiel 13 in the NET2
Ezekiel 13 in the NIV11
Ezekiel 13 in the NNT
Ezekiel 13 in the NNT2
Ezekiel 13 in the NNT3
Ezekiel 13 in the PDDPT
Ezekiel 13 in the PFNT
Ezekiel 13 in the RMNT
Ezekiel 13 in the SBIAS
Ezekiel 13 in the SBIBS
Ezekiel 13 in the SBIBS2
Ezekiel 13 in the SBICS
Ezekiel 13 in the SBIDS
Ezekiel 13 in the SBIGS
Ezekiel 13 in the SBIHS
Ezekiel 13 in the SBIIS
Ezekiel 13 in the SBIIS2
Ezekiel 13 in the SBIIS3
Ezekiel 13 in the SBIKS
Ezekiel 13 in the SBIKS2
Ezekiel 13 in the SBIMS
Ezekiel 13 in the SBIOS
Ezekiel 13 in the SBIPS
Ezekiel 13 in the SBISS
Ezekiel 13 in the SBITS
Ezekiel 13 in the SBITS2
Ezekiel 13 in the SBITS3
Ezekiel 13 in the SBITS4
Ezekiel 13 in the SBIUS
Ezekiel 13 in the SBIVS
Ezekiel 13 in the SBT
Ezekiel 13 in the SBT1E
Ezekiel 13 in the SCHL
Ezekiel 13 in the SNT
Ezekiel 13 in the SUSU
Ezekiel 13 in the SUSU2
Ezekiel 13 in the SYNO
Ezekiel 13 in the TBIAOTANT
Ezekiel 13 in the TBT1E
Ezekiel 13 in the TBT1E2
Ezekiel 13 in the TFTIP
Ezekiel 13 in the TFTU
Ezekiel 13 in the TGNTATF3T
Ezekiel 13 in the THAI
Ezekiel 13 in the TNFD
Ezekiel 13 in the TNT
Ezekiel 13 in the TNTIK
Ezekiel 13 in the TNTIL
Ezekiel 13 in the TNTIN
Ezekiel 13 in the TNTIP
Ezekiel 13 in the TNTIZ
Ezekiel 13 in the TOMA
Ezekiel 13 in the TTENT
Ezekiel 13 in the UBG
Ezekiel 13 in the UGV
Ezekiel 13 in the UGV2
Ezekiel 13 in the UGV3
Ezekiel 13 in the VBL
Ezekiel 13 in the VDCC
Ezekiel 13 in the YALU
Ezekiel 13 in the YAPE
Ezekiel 13 in the YBVTP
Ezekiel 13 in the ZBP