Ezekiel 24 (BOGWICC)

1 Pa tsiku lakhumi la mwezi wakhumi chaka chachisanu ndi chinayi, Yehova anandiyankhula kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu lemba dzina la tsiku lalero, lero lomwe lino, chifukwa mfumu ya Babuloni yazungulira Yerusalemu lero lino. 3 Uwaphere mwambi anthu owukirawa ndi kuwawuza kuti: ‘Ambuye Yehova akuti,“ ‘Ikani mʼphika pa moto,ndipo mu mʼphikamo muthiremo madzi. 4 Mu mʼphikamo muyikemo nthuli za nyama,nthuli zonse zabwino kwambiri za mwendo wathako ndi mwendo wamwamba.Mudzadzemo mafupa abwino kwambiri. 5 Pa gulu la nkhosa musankhepo nkhosa yabwino kwambiri.Muyike nkhuni pansi pa mʼphikawo.Madzi awire.Kenaka muphike nyamayo pamodzi ndi mafupa omwe.’ 6 “ ‘Nʼchifukwa chake, Ambuye Yehova akuti,“ ‘Tsoka kwa mzinda wokhetsa magazi,tsoka kwa mʼphika wadzimbiri;dzimbiri lake losachoka!Mutulutsemo nthuli imodzimodziosasankhulapo. 7 “ ‘Paja magazi amene anakhetsa akanali pakati pake mu mzindamo.Iye awakhuthulira pa thanthwe losalala.Sanawakhutulire pa dothikuopa kuti fumbi lingawafotsere. 8 Ndinasiya magaziwo pa mwala wosalalakuti asafotseredwe ndi fumbichifukwa ndinafuna kuonetsa mkwiyo wanga ndi kulipsira. 9 “ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti:“ ‘Tsoka kwa mzinda wokhetsa magazi!Inenso, ndidzawunjika mulu waukulu wa nkhuni. 10 Choncho wonjeza nkhunindipo muyatse moto.Phikani nyamayo bwinobwino,muthiremo zokometsera,mutsanule msuzi, ndipo mupsereze mafupawo. 11 Tsono muyike pa makala mʼphika wopanda kanthuwompaka utenthe kuchita kuti psuukuti zonyansa zake zisungunukendi kuti dzimbiri lake lichoke. 12 Koma mʼphikawo walephereka kuyeretsedwa.Dzimbiri lake linalowerera silingatheke kuchokangakhale ndi moto womwe. 13 “ ‘Tsono dzimbiri limeneli ndi zilakolako za dama lako. Pakuti ine ndinayesa kukutsuka koma iwe sunayere, ndipo sudzayeranso mpaka ukali wanga utakwaniratu pa iwe. 14 “ ‘Ine Yehova ndayankhula. Zimenezi zikubwera ndipo ndidzazichitadi. Sindidzabwerera mʼmbuyo. Sindidzakulekerera kapena kukuchitira chifundo. Ndidzakulanga molingana ndi makhalidwe ndi machitidwe ako, akutero Ambuye Yehova.’ ” 15 Yehova anandiyankhula kuti: 16 “Iwe mwana wa munthu, Ine ndikulanda mwadzidzidzi mkazi amene amakukomera mʼmaso kwambiri. Koma usadandaule, usalire kapena kukhetsa misozi. 17 Ubuwule koma mwakachetechete. Usamulire wakufayo. Uvale nduwira yako ndithu, nsapato zakonso usavule. Usaphimbe nkhope kapena kudya chakudya cha anamfedwa.” 18 Choncho ndinayankhula ndi anthu mmawa, ndipo madzulo mkazi wanga anamwalira. Mmawa mwake ndinachita monga momwe anandilamulira. 19 Ndipo anthu anandifunsa kuti, “Kodi sutifotokozera tanthauzo la zimene ukuchitazi?” 20 Ndinawayankha kuti, “Yehova anandipatsa uthenga wakuti, 21 ‘Awuze Aisraeli kuti: Ine Ambuye Yehova ndikuti: ndidzayipitsa Nyumba yanga yopatulika, nyumba imene mwakhala mukuyinyadira. Mumakondwa kwambiri poyiona, ndipo mumayikonda ndi mtima onse. Ana aamuna ndi aakazi amene munawasiya mʼmbuyo adzaphedwa ndi lupanga. 22 Ndipo mudzachita monga ndachitira inemu. Inu simudzaphimba nkhope zanu kapena kudya chakudya cha anamfedwa. 23 Mudzavala nduwira zanu kumutu ndi nsapato zanu ku mapazi anu. Simudzabuma maliro kapena kukhetsa misozi koma mudzavutika kwambiri chifukwa cha machimo anu ndipo mudzabuwula pakati panu. 24 Ine Ezekieli ndidzakhala chitsanzo chanu. Mudzachita monga momwe ndachitira. Izi zikadzachitika, akutero Yehova, ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Wamphamvuzonse.’ 25 “Ndipo Yehova anandiyankhula nati: Iwe mwana wa munthu, tsiku lina ndidzawachotsera anthuwa linga lawo limene ankakondwerera kukongola kwake, limene linkawakomera mʼmaso mwawo, limenenso anayikapo mtima wawo kwambiri. Ndidzawachotsera ana awo aamuna ndi aakazi. 26 Pa tsiku limenelo wothawa nkhondo adzabwera kudzakuwuzani zimenezo. 27 Pa tsiku limenelo pakamwa pako padzatsekuka. Udzatha kuyankhula naye ndipo sudzakhalanso chete. Motero udzakhala chizindikiro kwa iwo, ndipo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”

In Other Versions

Ezekiel 24 in the ANGEFD

Ezekiel 24 in the ANTPNG2D

Ezekiel 24 in the AS21

Ezekiel 24 in the BAGH

Ezekiel 24 in the BBPNG

Ezekiel 24 in the BBT1E

Ezekiel 24 in the BDS

Ezekiel 24 in the BEV

Ezekiel 24 in the BHAD

Ezekiel 24 in the BIB

Ezekiel 24 in the BLPT

Ezekiel 24 in the BNT

Ezekiel 24 in the BNTABOOT

Ezekiel 24 in the BNTLV

Ezekiel 24 in the BOATCB

Ezekiel 24 in the BOATCB2

Ezekiel 24 in the BOBCV

Ezekiel 24 in the BOCNT

Ezekiel 24 in the BOECS

Ezekiel 24 in the BOHCB

Ezekiel 24 in the BOHCV

Ezekiel 24 in the BOHLNT

Ezekiel 24 in the BOHNTLTAL

Ezekiel 24 in the BOICB

Ezekiel 24 in the BOILNTAP

Ezekiel 24 in the BOITCV

Ezekiel 24 in the BOKCV

Ezekiel 24 in the BOKCV2

Ezekiel 24 in the BOKHWOG

Ezekiel 24 in the BOKSSV

Ezekiel 24 in the BOLCB

Ezekiel 24 in the BOLCB2

Ezekiel 24 in the BOMCV

Ezekiel 24 in the BONAV

Ezekiel 24 in the BONCB

Ezekiel 24 in the BONLT

Ezekiel 24 in the BONUT2

Ezekiel 24 in the BOPLNT

Ezekiel 24 in the BOSCB

Ezekiel 24 in the BOSNC

Ezekiel 24 in the BOTLNT

Ezekiel 24 in the BOVCB

Ezekiel 24 in the BOYCB

Ezekiel 24 in the BPBB

Ezekiel 24 in the BPH

Ezekiel 24 in the BSB

Ezekiel 24 in the CCB

Ezekiel 24 in the CUV

Ezekiel 24 in the CUVS

Ezekiel 24 in the DBT

Ezekiel 24 in the DGDNT

Ezekiel 24 in the DHNT

Ezekiel 24 in the DNT

Ezekiel 24 in the ELBE

Ezekiel 24 in the EMTV

Ezekiel 24 in the ESV

Ezekiel 24 in the FBV

Ezekiel 24 in the FEB

Ezekiel 24 in the GGMNT

Ezekiel 24 in the GNT

Ezekiel 24 in the HARY

Ezekiel 24 in the HNT

Ezekiel 24 in the IRVA

Ezekiel 24 in the IRVB

Ezekiel 24 in the IRVG

Ezekiel 24 in the IRVH

Ezekiel 24 in the IRVK

Ezekiel 24 in the IRVM

Ezekiel 24 in the IRVM2

Ezekiel 24 in the IRVO

Ezekiel 24 in the IRVP

Ezekiel 24 in the IRVT

Ezekiel 24 in the IRVT2

Ezekiel 24 in the IRVU

Ezekiel 24 in the ISVN

Ezekiel 24 in the JSNT

Ezekiel 24 in the KAPI

Ezekiel 24 in the KBT1ETNIK

Ezekiel 24 in the KBV

Ezekiel 24 in the KJV

Ezekiel 24 in the KNFD

Ezekiel 24 in the LBA

Ezekiel 24 in the LBLA

Ezekiel 24 in the LNT

Ezekiel 24 in the LSV

Ezekiel 24 in the MAAL

Ezekiel 24 in the MBV

Ezekiel 24 in the MBV2

Ezekiel 24 in the MHNT

Ezekiel 24 in the MKNFD

Ezekiel 24 in the MNG

Ezekiel 24 in the MNT

Ezekiel 24 in the MNT2

Ezekiel 24 in the MRS1T

Ezekiel 24 in the NAA

Ezekiel 24 in the NASB

Ezekiel 24 in the NBLA

Ezekiel 24 in the NBS

Ezekiel 24 in the NBVTP

Ezekiel 24 in the NET2

Ezekiel 24 in the NIV11

Ezekiel 24 in the NNT

Ezekiel 24 in the NNT2

Ezekiel 24 in the NNT3

Ezekiel 24 in the PDDPT

Ezekiel 24 in the PFNT

Ezekiel 24 in the RMNT

Ezekiel 24 in the SBIAS

Ezekiel 24 in the SBIBS

Ezekiel 24 in the SBIBS2

Ezekiel 24 in the SBICS

Ezekiel 24 in the SBIDS

Ezekiel 24 in the SBIGS

Ezekiel 24 in the SBIHS

Ezekiel 24 in the SBIIS

Ezekiel 24 in the SBIIS2

Ezekiel 24 in the SBIIS3

Ezekiel 24 in the SBIKS

Ezekiel 24 in the SBIKS2

Ezekiel 24 in the SBIMS

Ezekiel 24 in the SBIOS

Ezekiel 24 in the SBIPS

Ezekiel 24 in the SBISS

Ezekiel 24 in the SBITS

Ezekiel 24 in the SBITS2

Ezekiel 24 in the SBITS3

Ezekiel 24 in the SBITS4

Ezekiel 24 in the SBIUS

Ezekiel 24 in the SBIVS

Ezekiel 24 in the SBT

Ezekiel 24 in the SBT1E

Ezekiel 24 in the SCHL

Ezekiel 24 in the SNT

Ezekiel 24 in the SUSU

Ezekiel 24 in the SUSU2

Ezekiel 24 in the SYNO

Ezekiel 24 in the TBIAOTANT

Ezekiel 24 in the TBT1E

Ezekiel 24 in the TBT1E2

Ezekiel 24 in the TFTIP

Ezekiel 24 in the TFTU

Ezekiel 24 in the TGNTATF3T

Ezekiel 24 in the THAI

Ezekiel 24 in the TNFD

Ezekiel 24 in the TNT

Ezekiel 24 in the TNTIK

Ezekiel 24 in the TNTIL

Ezekiel 24 in the TNTIN

Ezekiel 24 in the TNTIP

Ezekiel 24 in the TNTIZ

Ezekiel 24 in the TOMA

Ezekiel 24 in the TTENT

Ezekiel 24 in the UBG

Ezekiel 24 in the UGV

Ezekiel 24 in the UGV2

Ezekiel 24 in the UGV3

Ezekiel 24 in the VBL

Ezekiel 24 in the VDCC

Ezekiel 24 in the YALU

Ezekiel 24 in the YAPE

Ezekiel 24 in the YBVTP

Ezekiel 24 in the ZBP