Ezekiel 29 (BOGWICC)
1 Pa tsiku lakhumi ndi chiwiri la mwezi wakhumi, chaka chakhumi, Yehova anandiyankhula kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, tembenukira kwa Farao, mfumu ya Igupto, ndipo unenere modzudzula mfumuyo pamodzi ndi dziko lake. 3 Uyiwuze mfumuyo kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti,“ ‘Ndine mdani wako, iwe Farao mfumu ya Igupto,iwe ngʼona yayikulu yogona pakati pa mitsinje yako.Umanena kuti, ‘Mtsinje wa Nailo ndi wanga;ndinadzipangira ndekha.’ 4 Koma ndidzakukola ndi mbedza mʼkamwa mwakondipo nsomba za mʼmitsinje yako zidzakangamira ku mamba ako.Tsono ndidzakutulutsa mu mtsinje mwakomopamodzi ndi nsomba zimene zakangamira ku mamba ako. 5 Ndidzakutaya ku chipululu,iwe pamodzi ndi nsomba zonse za mʼmitsinje yako.Udzagwera pamtetete kuthengopopanda munthu woti akutole kuti akayike maliro ako.Ndidzakusandutsa chakudyacha zirombo za pa dziko lapansi ndi mbalame za mlengalenga. 6 Motero aliyense amene amakhala mu Igupto adzadziwa kuti Ine ndine Yehova. “ ‘Iwe unakhala ngati ndodo yabango ku Aisraeli. 7 Pamene anakugwira unathethekera mʼmanja mwawo ndi kucheka mapewa awo. Pamene anakutsamira, unathyoka ndipo misana yawo inagwedezeka. 8 “ ‘Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti, ndikubweretsera lupanga kuti lidzaphe anthu pamodzi ndi nyama zomwe. 9 Dziko la Igupto lidzasanduka lopanda anthu. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.“ ‘Popeza iwe unati, ‘Mtsinje wa Nailo ndi wanga; ndinawupanga ndine,’ 10 nʼchifukwa chake Ine ndikudana nawe pamodzi ndi mitsinje yakoyo, ndipo ndidzasandutsa dziko la Igupto bwinja kuyambira chipululu cha Migidoli mpaka ku mzinda wa Asiwani, kukafika ku malire a Kusi. 11 Palibe phazi la munthu kapena la nyama limene lidzapondepo. Kudzakhala kopanda anthu kwa zaka makumi anayi. 12 Ndidzasandutsa dziko la Igupto kukhala chipululu ngati zipululu za mayiko ena. Kwa zaka makumi anayi mizinda yakenso idzakhala yopasuka pakati pa mizinda yopasuka. Ndipo ndidzathamangitsira Aigupto pakati pa mitundu ya anthu ndi kuwabalalitsira mʼmayiko. 13 “ ‘Komabe Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pakutha pa zaka makumi anayi ndidzasonkhanitsa Aigupto onse kuchokera ku mayiko amene ndinawabalalitsirako. 14 Ndidzachotsa Aiguptowo ku ukapolo ndipo ndidzawabwezera ku Patirosi kumene anachokera. Kumeneko iwo adzakhala ufumu wotsika. 15 Udzakhala ufumu wotsika kwambiri kupambana maufumu ena onse ndipo sudzadzitukumula pakati pa mitundu ina. Ndidzawufowoketsa kwambiri kotero kuti sudzathanso kulamulira mitundu ya anthu. 16 Aisraeli sadzadaliranso Aigupto. Koma kuti chilango chawo chidzawakumbutsa tchimo lawo lija lofunafuna thandizo kuchokera ku Igupto. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.’ ” 17 Pa tsiku loyamba la mwezi woyamba, chaka cha 27, Yehova anandiyankhula kuti: 18 “Iwe mwana wa munthu, kale Nebukadinezara mfumu ya Babuloni inagwiritsa ntchito ankhondo ake kukathira nkhondo mzinda wa Turo, mpaka munthu aliyense anachita dazi chifukwa chosenza katundu, ndipo ananyuka pa phewa. Komabe ngakhale iyeyo, kapena gulu lake lankhondo sanaphulepo kanthu pa ntchito yonse imene anayigwira polimbana ndi mzindawo. 19 Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti, Ine ndidzapereka Igupto kwa Nebukadinezara mfumu ya Babuloni, ndipo iyo idzatenga chuma chake ndi kuchifunkha ngati malipiro a gulu lake lankhondo. 20 Ndamupatsa Nebukadinezara Igupto ngati mphotho ya kulimbika kwake chifukwa iyo ndi gulu lake lankhondo anandigwirira ntchito, akutero Ambuye Yehova. 21 “Pa nthawi imeneyo ndidzapereka mphamvu yatsopano pa Aisraeli, ndipo ndidzatsekula pakamwa pako, iwe, Ezekieli kuti uthe kuyankhula pakati pawo. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”
In Other Versions
Ezekiel 29 in the ANGEFD
Ezekiel 29 in the ANTPNG2D
Ezekiel 29 in the AS21
Ezekiel 29 in the BAGH
Ezekiel 29 in the BBPNG
Ezekiel 29 in the BBT1E
Ezekiel 29 in the BDS
Ezekiel 29 in the BEV
Ezekiel 29 in the BHAD
Ezekiel 29 in the BIB
Ezekiel 29 in the BLPT
Ezekiel 29 in the BNT
Ezekiel 29 in the BNTABOOT
Ezekiel 29 in the BNTLV
Ezekiel 29 in the BOATCB
Ezekiel 29 in the BOATCB2
Ezekiel 29 in the BOBCV
Ezekiel 29 in the BOCNT
Ezekiel 29 in the BOECS
Ezekiel 29 in the BOHCB
Ezekiel 29 in the BOHCV
Ezekiel 29 in the BOHLNT
Ezekiel 29 in the BOHNTLTAL
Ezekiel 29 in the BOICB
Ezekiel 29 in the BOILNTAP
Ezekiel 29 in the BOITCV
Ezekiel 29 in the BOKCV
Ezekiel 29 in the BOKCV2
Ezekiel 29 in the BOKHWOG
Ezekiel 29 in the BOKSSV
Ezekiel 29 in the BOLCB
Ezekiel 29 in the BOLCB2
Ezekiel 29 in the BOMCV
Ezekiel 29 in the BONAV
Ezekiel 29 in the BONCB
Ezekiel 29 in the BONLT
Ezekiel 29 in the BONUT2
Ezekiel 29 in the BOPLNT
Ezekiel 29 in the BOSCB
Ezekiel 29 in the BOSNC
Ezekiel 29 in the BOTLNT
Ezekiel 29 in the BOVCB
Ezekiel 29 in the BOYCB
Ezekiel 29 in the BPBB
Ezekiel 29 in the BPH
Ezekiel 29 in the BSB
Ezekiel 29 in the CCB
Ezekiel 29 in the CUV
Ezekiel 29 in the CUVS
Ezekiel 29 in the DBT
Ezekiel 29 in the DGDNT
Ezekiel 29 in the DHNT
Ezekiel 29 in the DNT
Ezekiel 29 in the ELBE
Ezekiel 29 in the EMTV
Ezekiel 29 in the ESV
Ezekiel 29 in the FBV
Ezekiel 29 in the FEB
Ezekiel 29 in the GGMNT
Ezekiel 29 in the GNT
Ezekiel 29 in the HARY
Ezekiel 29 in the HNT
Ezekiel 29 in the IRVA
Ezekiel 29 in the IRVB
Ezekiel 29 in the IRVG
Ezekiel 29 in the IRVH
Ezekiel 29 in the IRVK
Ezekiel 29 in the IRVM
Ezekiel 29 in the IRVM2
Ezekiel 29 in the IRVO
Ezekiel 29 in the IRVP
Ezekiel 29 in the IRVT
Ezekiel 29 in the IRVT2
Ezekiel 29 in the IRVU
Ezekiel 29 in the ISVN
Ezekiel 29 in the JSNT
Ezekiel 29 in the KAPI
Ezekiel 29 in the KBT1ETNIK
Ezekiel 29 in the KBV
Ezekiel 29 in the KJV
Ezekiel 29 in the KNFD
Ezekiel 29 in the LBA
Ezekiel 29 in the LBLA
Ezekiel 29 in the LNT
Ezekiel 29 in the LSV
Ezekiel 29 in the MAAL
Ezekiel 29 in the MBV
Ezekiel 29 in the MBV2
Ezekiel 29 in the MHNT
Ezekiel 29 in the MKNFD
Ezekiel 29 in the MNG
Ezekiel 29 in the MNT
Ezekiel 29 in the MNT2
Ezekiel 29 in the MRS1T
Ezekiel 29 in the NAA
Ezekiel 29 in the NASB
Ezekiel 29 in the NBLA
Ezekiel 29 in the NBS
Ezekiel 29 in the NBVTP
Ezekiel 29 in the NET2
Ezekiel 29 in the NIV11
Ezekiel 29 in the NNT
Ezekiel 29 in the NNT2
Ezekiel 29 in the NNT3
Ezekiel 29 in the PDDPT
Ezekiel 29 in the PFNT
Ezekiel 29 in the RMNT
Ezekiel 29 in the SBIAS
Ezekiel 29 in the SBIBS
Ezekiel 29 in the SBIBS2
Ezekiel 29 in the SBICS
Ezekiel 29 in the SBIDS
Ezekiel 29 in the SBIGS
Ezekiel 29 in the SBIHS
Ezekiel 29 in the SBIIS
Ezekiel 29 in the SBIIS2
Ezekiel 29 in the SBIIS3
Ezekiel 29 in the SBIKS
Ezekiel 29 in the SBIKS2
Ezekiel 29 in the SBIMS
Ezekiel 29 in the SBIOS
Ezekiel 29 in the SBIPS
Ezekiel 29 in the SBISS
Ezekiel 29 in the SBITS
Ezekiel 29 in the SBITS2
Ezekiel 29 in the SBITS3
Ezekiel 29 in the SBITS4
Ezekiel 29 in the SBIUS
Ezekiel 29 in the SBIVS
Ezekiel 29 in the SBT
Ezekiel 29 in the SBT1E
Ezekiel 29 in the SCHL
Ezekiel 29 in the SNT
Ezekiel 29 in the SUSU
Ezekiel 29 in the SUSU2
Ezekiel 29 in the SYNO
Ezekiel 29 in the TBIAOTANT
Ezekiel 29 in the TBT1E
Ezekiel 29 in the TBT1E2
Ezekiel 29 in the TFTIP
Ezekiel 29 in the TFTU
Ezekiel 29 in the TGNTATF3T
Ezekiel 29 in the THAI
Ezekiel 29 in the TNFD
Ezekiel 29 in the TNT
Ezekiel 29 in the TNTIK
Ezekiel 29 in the TNTIL
Ezekiel 29 in the TNTIN
Ezekiel 29 in the TNTIP
Ezekiel 29 in the TNTIZ
Ezekiel 29 in the TOMA
Ezekiel 29 in the TTENT
Ezekiel 29 in the UBG
Ezekiel 29 in the UGV
Ezekiel 29 in the UGV2
Ezekiel 29 in the UGV3
Ezekiel 29 in the VBL
Ezekiel 29 in the VDCC
Ezekiel 29 in the YALU
Ezekiel 29 in the YAPE
Ezekiel 29 in the YBVTP
Ezekiel 29 in the ZBP