Ezekiel 33 (BOGWICC)

1 Yehova anandiyankhula nati: 2 “Iwe mwana wa munthu awuze anthu a mtundu wako kuti, ‘Paja zimati ndikatumiza nkhondo mʼdziko anthu a mʼdzikomo amasankha munthu mmodzi pakati pawo kuti akhale mlonda. 3 Tsono iyeyo amati akaona nkhondo ikubwera amaliza lipenga kuti achenjeze anthuwo. 4 Wina aliyense akamva lipenga koma osasamala, mdani uja akabwera nʼkumupha, ndiye kuti wadziphetsa yekha. 5 Iye anamva kulira kwa lipenga koma sanalabadire. Ndiye kuti wadziphetsa yekha. Akanasamala kuchenjeza kwa mlonda akanapulumuka. 6 Koma ngati mlondayo aona lupanga likubwera ndipo osawomba lipengalo kuchenjeza anthu, ndipo lupanga libwera ndi kuchotsa moyo wa mmodzi mwa iwo, munthu ameneyo adzafa chifukwa cha tchimo lake, koma ndidzamuyimba mlandu mlondayo chifukwa cha imfa ya mnzakeyo.’ 7 “Tsono iwe mwana wa munthu, ndakuyika kuti ukhale mlonda wa Aisraeli. Choncho imva mawu amene ndikuyankhula ndipo uwachenjeze. 8 Ndikawuza munthu woyipa kuti, ‘Iwe munthu woyipa, udzafa ndithu,’ ndipo iwe osayankhula kumuchenjeza kuti aleke njira zake, munthu wochimwayo adzafa chifukwa cha tchimo lake, koma Ine ndidzakuyimba mlandu chifukwa cha imfa yake. 9 Koma ngati uchenjeza munthu woyipa kuti aleke njira zake, ndipo iye osatero, adzafa chifukwa cha tchimo lake, koma iwe udzapulumutsa moyo wako. 10 “Iwe mwana wa munthu, akumbutse Aisraeli mawu awo akuti, ‘Ife talemedwa ndi zolakwa zathu ndi machimo athu, ndipo tikuwonda chifukwa cha zimene tachita. Kodi tingakhale ndi moyo bwanji?’ ” 11 Uwawuze kuti, Ine Ambuye Yehova ndikuti: “Pali Ine wamoyo, sindikondwera ndi imfa ya munthu woyipa. Ndimakondwera ndikamaona munthu woyipa akuleka zoyipa zake kuti akhale ndi moyo. Tembenukani! Tembenukani, siyani makhalidwe anu oyipa! Muferanji, Inu Aisraeli? 12 “Tsono iwe mwana wa munthu, awuze anthu a mtundu wako kuti, ‘Ngati munthu wolungama achimwa, ndiye kuti ntchito zake zabwino zija sizidzamupulutsa. Koma wochimwa akaleka ntchito zake zoyipazo, sadzalangidwa konse. Ndithu ngati munthu wolungama ayamba kuchimwa sadzatha kukhala ndi moyo chifukwa cha ntchito zake zabwino zija.’ 13 Ngati ndiwuza munthu wolungama kuti adzafa ndithu, koma iyeyo nʼkumadalira ntchito zake zabwino zimene anachita kale ndi kuyamba kuchimwa, ndiye kuti ntchito zake zabwinozo zidzayiwalika. Iye adzafa chifukwa cha machimo ake. 14 Ndipo ngati ndiwuza munthu woyipa kuti, ‘Udzafa ndithu,’ tsono iye nʼkutembenuka kuleka machimo ake ndi kuyamba kuchita zimene Yehova afuna, 15 monga kubweza chimene anatenga ngati chikole cha ngongole, kubweza chimene anaba, kutsatira malamulo omwe amapereka moyo ndi kuleka kuchita zoyipa, iye adzakhala ndithu ndi moyo; sadzafa. 16 Ndidzakhululuka machimo ake onse anachita. Iye wachita zimene ndi zolungama ndi zoyenera ndipo iye adzakhala ndi moyo ndithu. 17 “Komabe anthu a mtundu wako akunena kuti, ‘Zimene Ambuye amachita ndi zopanda chilungamo.’ Ayi, koma makhalidwe awo ndiwo ali osalungama. 18 Ngati munthu wolungama atembenuka ndi kuleka ntchito zake zolungama ndi kuyamba kuchita zoyipa, adzafa nazo. 19 Ndipo ngati munthu woyipa atembenuka ndi kuleka ntchito zake zoyipa ndi kuyamba kuchita zolungama ndi zoyenera, iye adzakhala ndi moyo pochita zimenezo. 20 Koma Inu Aisraeli, mukunena kuti, ‘Zimene Ambuye amachita ndi zopanda chilungamo.’ Ayi, inu Aisraeli, Ine ndidzaweruza aliyense wa inu potsata ntchito zake.” 21 Pa tsiku lachisanu la mwezi wakhumi, chaka chakhumi ndi chiwiri cha ukapolo wathu, munthu wina amene anapulumuka ku Yerusalemu anabwera kudzandiwuza kuti, “Mzinda wagwa!” 22 Tsono madzulo ake munthuyo asanafike, dzanja la Yehova linali pa ine. Koma mmawa mwake munthuyo atabwera Yehova anatsekula pakamwa panga, motero kuti sindinakhalenso wosayankhula. 23 Ndipo Yehova anandiyankhula kuti: 24 “Iwe mwana wa munthu, anthu amene akukhala mʼmizinda ya mabwinja ya dziko la Israeli akunena kuti, ‘Abrahamu anali munthu mmodzi yekha, ndipo anamupatsa dziko lonse. Koma ife tilipo ambiri, motero tsono dzikolo ndi lathu.’ 25 Choncho iwe uwawuze kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti, ‘Inu mumadya nyama ili ndi magazi ake, ndipo mumapembedza mafano ndi kukhetsa magazi, kodi tsono inu nʼkulandira dzikoli? 26 Mumadalira lupanga lanu, mumachita zinthu zonyansa, ndipo aliyense wa inu amachita chigololo ndi mkazi wa mnzake. Kodi inu nʼkulandira dzikoli?’ 27 “Uwawuze kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti, ‘Ndithu pali Ine wamoyo, anthu amene anatsala mʼmizinda ya mabwinja adzaphedwa ndi lupanga, amene ali ku midzi ndidzawapereka kuti adzadyedwe ndi zirombo zakuthengo, ndipo amene ali mʼmalinga ndi mʼmapanga adzafa ndi mliri. 28 Ndidzalisandutsa chipululu dzikolo, ndipo mphamvu zake zimene amanyadira zidzatheratu, ndipo mapiri a Yerusalemu adzasanduka chipululu, kotero kuti palibe amene adzatha kudutsako. 29 Ndikadzasandutsa dzikolo chipululu chifukwa cha zonyansa zimene ankachita, pamenepo ndiye adzadziwa kuti ndine Yehova.’ 30 “Koma kunena za iwe, mwana wa munthu, anthu a mtundu wako akumayankhula za iwe akakhala pa makoma a mzinda ndi pa makomo a nyumba zawo. Akumawuzana kuti, ‘Tiyeni tikamve uthenga umene wachokera kwa Yehova.’ 31 Anthu anga amabwera kwa iwe, monga momwe amachitira nthawi zonse anthu anga, ndipo amakhala pansi pamaso pako kumvetsera mawu ako. Koma zimene akumvazo sazichita. Zokamba zawo zimaonetsa chikondi, koma mitima yawo imakhala pa phindu lawo. 32 Kunena zoona, kwa iwowo sindiwe kanthu konse, ndiwe munthu wamba chabe womangoyimba nyimbo zachikondi ndi liwu lokoma poyimba zeze. Kumva amamva mawu ako koma sawagwiritsa ntchito. 33 “Koma zonsezi zikadzachitika, ndipo zidzachitika ndithu, pamenepo adzadziwa kuti mneneri anali pakati pawo.”

In Other Versions

Ezekiel 33 in the ANGEFD

Ezekiel 33 in the ANTPNG2D

Ezekiel 33 in the AS21

Ezekiel 33 in the BAGH

Ezekiel 33 in the BBPNG

Ezekiel 33 in the BBT1E

Ezekiel 33 in the BDS

Ezekiel 33 in the BEV

Ezekiel 33 in the BHAD

Ezekiel 33 in the BIB

Ezekiel 33 in the BLPT

Ezekiel 33 in the BNT

Ezekiel 33 in the BNTABOOT

Ezekiel 33 in the BNTLV

Ezekiel 33 in the BOATCB

Ezekiel 33 in the BOATCB2

Ezekiel 33 in the BOBCV

Ezekiel 33 in the BOCNT

Ezekiel 33 in the BOECS

Ezekiel 33 in the BOHCB

Ezekiel 33 in the BOHCV

Ezekiel 33 in the BOHLNT

Ezekiel 33 in the BOHNTLTAL

Ezekiel 33 in the BOICB

Ezekiel 33 in the BOILNTAP

Ezekiel 33 in the BOITCV

Ezekiel 33 in the BOKCV

Ezekiel 33 in the BOKCV2

Ezekiel 33 in the BOKHWOG

Ezekiel 33 in the BOKSSV

Ezekiel 33 in the BOLCB

Ezekiel 33 in the BOLCB2

Ezekiel 33 in the BOMCV

Ezekiel 33 in the BONAV

Ezekiel 33 in the BONCB

Ezekiel 33 in the BONLT

Ezekiel 33 in the BONUT2

Ezekiel 33 in the BOPLNT

Ezekiel 33 in the BOSCB

Ezekiel 33 in the BOSNC

Ezekiel 33 in the BOTLNT

Ezekiel 33 in the BOVCB

Ezekiel 33 in the BOYCB

Ezekiel 33 in the BPBB

Ezekiel 33 in the BPH

Ezekiel 33 in the BSB

Ezekiel 33 in the CCB

Ezekiel 33 in the CUV

Ezekiel 33 in the CUVS

Ezekiel 33 in the DBT

Ezekiel 33 in the DGDNT

Ezekiel 33 in the DHNT

Ezekiel 33 in the DNT

Ezekiel 33 in the ELBE

Ezekiel 33 in the EMTV

Ezekiel 33 in the ESV

Ezekiel 33 in the FBV

Ezekiel 33 in the FEB

Ezekiel 33 in the GGMNT

Ezekiel 33 in the GNT

Ezekiel 33 in the HARY

Ezekiel 33 in the HNT

Ezekiel 33 in the IRVA

Ezekiel 33 in the IRVB

Ezekiel 33 in the IRVG

Ezekiel 33 in the IRVH

Ezekiel 33 in the IRVK

Ezekiel 33 in the IRVM

Ezekiel 33 in the IRVM2

Ezekiel 33 in the IRVO

Ezekiel 33 in the IRVP

Ezekiel 33 in the IRVT

Ezekiel 33 in the IRVT2

Ezekiel 33 in the IRVU

Ezekiel 33 in the ISVN

Ezekiel 33 in the JSNT

Ezekiel 33 in the KAPI

Ezekiel 33 in the KBT1ETNIK

Ezekiel 33 in the KBV

Ezekiel 33 in the KJV

Ezekiel 33 in the KNFD

Ezekiel 33 in the LBA

Ezekiel 33 in the LBLA

Ezekiel 33 in the LNT

Ezekiel 33 in the LSV

Ezekiel 33 in the MAAL

Ezekiel 33 in the MBV

Ezekiel 33 in the MBV2

Ezekiel 33 in the MHNT

Ezekiel 33 in the MKNFD

Ezekiel 33 in the MNG

Ezekiel 33 in the MNT

Ezekiel 33 in the MNT2

Ezekiel 33 in the MRS1T

Ezekiel 33 in the NAA

Ezekiel 33 in the NASB

Ezekiel 33 in the NBLA

Ezekiel 33 in the NBS

Ezekiel 33 in the NBVTP

Ezekiel 33 in the NET2

Ezekiel 33 in the NIV11

Ezekiel 33 in the NNT

Ezekiel 33 in the NNT2

Ezekiel 33 in the NNT3

Ezekiel 33 in the PDDPT

Ezekiel 33 in the PFNT

Ezekiel 33 in the RMNT

Ezekiel 33 in the SBIAS

Ezekiel 33 in the SBIBS

Ezekiel 33 in the SBIBS2

Ezekiel 33 in the SBICS

Ezekiel 33 in the SBIDS

Ezekiel 33 in the SBIGS

Ezekiel 33 in the SBIHS

Ezekiel 33 in the SBIIS

Ezekiel 33 in the SBIIS2

Ezekiel 33 in the SBIIS3

Ezekiel 33 in the SBIKS

Ezekiel 33 in the SBIKS2

Ezekiel 33 in the SBIMS

Ezekiel 33 in the SBIOS

Ezekiel 33 in the SBIPS

Ezekiel 33 in the SBISS

Ezekiel 33 in the SBITS

Ezekiel 33 in the SBITS2

Ezekiel 33 in the SBITS3

Ezekiel 33 in the SBITS4

Ezekiel 33 in the SBIUS

Ezekiel 33 in the SBIVS

Ezekiel 33 in the SBT

Ezekiel 33 in the SBT1E

Ezekiel 33 in the SCHL

Ezekiel 33 in the SNT

Ezekiel 33 in the SUSU

Ezekiel 33 in the SUSU2

Ezekiel 33 in the SYNO

Ezekiel 33 in the TBIAOTANT

Ezekiel 33 in the TBT1E

Ezekiel 33 in the TBT1E2

Ezekiel 33 in the TFTIP

Ezekiel 33 in the TFTU

Ezekiel 33 in the TGNTATF3T

Ezekiel 33 in the THAI

Ezekiel 33 in the TNFD

Ezekiel 33 in the TNT

Ezekiel 33 in the TNTIK

Ezekiel 33 in the TNTIL

Ezekiel 33 in the TNTIN

Ezekiel 33 in the TNTIP

Ezekiel 33 in the TNTIZ

Ezekiel 33 in the TOMA

Ezekiel 33 in the TTENT

Ezekiel 33 in the UBG

Ezekiel 33 in the UGV

Ezekiel 33 in the UGV2

Ezekiel 33 in the UGV3

Ezekiel 33 in the VBL

Ezekiel 33 in the VDCC

Ezekiel 33 in the YALU

Ezekiel 33 in the YAPE

Ezekiel 33 in the YBVTP

Ezekiel 33 in the ZBP