Ezekiel 38 (BOGWICC)

1 Yehova anandiyankhula kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, tembenukira kwa Gogi, wa ku dziko la Magogi, amene ali kalonga wamkulu wa mzinda wa Mesaki ndi Tubala. Umuyimbe mlandu. 3 Umuwuze mawu a Ine Ambuye Yehova akuti, ‘Ine ndikudana nawe, iwe Gogi, kalonga wamkulu wa ku Mesaki ndi Tubala. 4 Ndidzakuzunguza, ndidzakukola ndi mbedza mʼkamwa mwako. Ndidzakutulutsa iweyo pamodzi ndi gulu lako lonse la nkhondo, akavalo ako ndi okwerapo ake. Onse adzakhala atanyamula zida za nkhondo, zishango ndi malihawo ndipo malupanga awo adzakhala osolola. 5 Pamodzi ndi iwowo, padzakhalanso ankhondo a ku Perisiya, ku Kusi, ndi ku Puti. Onsewa adzakhala atanyamula zishango ndi kuvala zipewa zankhondo. 6 Padzakhalanso Gomeri pamodzi ndi ankhondo ake onse ndiponso banja la Togarima ndi gulu lake lonse lankhondo lochokera kutali kumpoto. Padzakhaladi mitundu yambiri ya anthu pamodzi ndi iwe. 7 “ ‘Konzekani! Mukhaledi okonzeka, iweyo pamodzi ndi gulu lonse la nkhondo limene lakusonkhanira. Iweyo udzawatsogolera pokamenya nkhondo. 8 Pakapita masiku ambiri ndidzakuyitana. Zaka zikubwerazi ndidzakulowetsa mʼdziko limene lapulumuka ku nkhondo. Anthu ake anasonkhanitsidwa kuchokera ku mitundu ya anthu ambiri nʼkukakhazikika pa mapiri a Israeli amene kwa nthawi yayitali anali ngati chipululu. Anthu onsewa tsopano akukhala mwa mtendere. 9 Tsono iwe pamodzi ndi ankhondo ako onse ndiponso mitundu yambiri ya anthu imene ili nawe mudzabwera ngati mphepo yamkuntho. Mudzaphimba dziko lonse ngati mitambo. 10 “Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pa tsiku limenelo mu mtima mwako mudzabwera maganizo ofuna kukonzekera kuchita zoyipa. 11 Iwe udzanena kuti, ‘Ndikukathira nkhondo dziko la midzi yopanda mipanda; ndikathira nkhondo anthu okhala mwamtendere, anthu amene satchinjirizidwa ndi mipanda, zipata kapena mipiringidzo. 12 Ndipita kukalanda chuma chawo ndi kukafunkha zinthu zawo. Ndidzalimbana ndi midzi imene kale inali mabwinja. Ndikathira nkhondo anthu amene anasonkhanitsidwa kuchokera kwa anthu a mitundu ina. Iwowa ali ndi ziweto zambiri, katundu wochuluka ndiponso amakhala pakatikati pa dziko lapansi.’ 13 Anthu a ku Seba, a ku Dedani ndiponso amalonda a ku Tarisisi pamodzi ndi midzi yake yonse adzakufunsa kuti, ‘Kodi wabwera kudzafunkha? Kodi wasonkhanitsa gulu lako la nkhondo kudzalanda chuma, kudzatenga siliva ndi golide, ziweto ndi katundu kuti zikhale zofunkha zochuluka?’ ” 14 “Nʼchifukwa chake, iwe mwana wa munthu, nenera ndipo uwuze Gogi kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pa nthawi imene anthu anga adzakhala pa mtendere, iwe udzanyamuka. 15 Udzabwera kuchokera ku dziko lako kutali kumpoto, iwe pamodzi ndi mitundu yambiri ya anthu imene ili nawe, onse okwera akavalo, gulu lankhondo lalikulu ndi lamphamvu. 16 Udzabwera kudzalimbana ndi anthu anga Aisraeli ngati mtambo wophimba dziko. Masiku amenewo, iwe Gogi, ndidzabwera nawe kuti ulimbane ndi dziko langa, kuti anthu a mitundu ina andidziwe Ine, pamene ndidzaonetsa kuyera kwanga pa zimene ndidzakuchite iweyo. 17 “ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Kodi iwe si amene ndinayankhula za iwe masiku amakedzana kudzera mwa atumiki anga aneneri a Israeli? Pa zaka zambiri iwo ankalengeza kuti ndidzawutsa iwe kuti udzalimbane ndi Israeli. 18 Zimene chidzachitika pa tsiku limenelo ndi izi: Gogi akadzathira nkhondo dziko la Israeli, mkwiyo wanga woopsa udzayaka. Ndikutero Ine Ambuye Wamphamvuzonse. 19 Chifukwa cha mkwiyo ndi ukali wanga woyakawo Ine ndikunenetsa kuti pa nthawi imeneyo padzakhala chivomerezi chachikulu mʼdziko la Israeli. 20 Nsomba za mʼnyanja, mbalame zamumlengalenga, zirombo zakuthengo, cholengedwa chilichonse chimene chimakwawa pansi, ndiponso anthu onse okhala pa dziko lapansi, adzanjenjemera pamaso panga. Mapiri adzangʼambika, malo okwera kwambiri adzagumuka ndipo khoma lililonse lidzagwa pansi. 21 Ndidzawutsira Gogi nkhondo kuchokera ku mapiri anga. Ndikutero Ine Ambuye Yehova. Anthu a Gogiyo adzaphana okhaokha ndi malupanga. 22 Ine ndidzamulanga ndi mliri ndi imfa. Ndidzagwetsa mvula yoopsa ya matalala, ndiponso sulufule ndi miyala ya moto pa iye ndi pa asilikali ake ndiponso pa mitundu yambiri ya anthu imene ili naye. 23 Motero ndidzadzionetsa kuti ndine wamphamvu ndi woyera. Ndiponso ndidzadziwika pamaso pa anthu a mitundu ina yambiri. Momwemo adzadziwadi kuti Ine ndine Yehova.’ ”

In Other Versions

Ezekiel 38 in the ANGEFD

Ezekiel 38 in the ANTPNG2D

Ezekiel 38 in the AS21

Ezekiel 38 in the BAGH

Ezekiel 38 in the BBPNG

Ezekiel 38 in the BBT1E

Ezekiel 38 in the BDS

Ezekiel 38 in the BEV

Ezekiel 38 in the BHAD

Ezekiel 38 in the BIB

Ezekiel 38 in the BLPT

Ezekiel 38 in the BNT

Ezekiel 38 in the BNTABOOT

Ezekiel 38 in the BNTLV

Ezekiel 38 in the BOATCB

Ezekiel 38 in the BOATCB2

Ezekiel 38 in the BOBCV

Ezekiel 38 in the BOCNT

Ezekiel 38 in the BOECS

Ezekiel 38 in the BOHCB

Ezekiel 38 in the BOHCV

Ezekiel 38 in the BOHLNT

Ezekiel 38 in the BOHNTLTAL

Ezekiel 38 in the BOICB

Ezekiel 38 in the BOILNTAP

Ezekiel 38 in the BOITCV

Ezekiel 38 in the BOKCV

Ezekiel 38 in the BOKCV2

Ezekiel 38 in the BOKHWOG

Ezekiel 38 in the BOKSSV

Ezekiel 38 in the BOLCB

Ezekiel 38 in the BOLCB2

Ezekiel 38 in the BOMCV

Ezekiel 38 in the BONAV

Ezekiel 38 in the BONCB

Ezekiel 38 in the BONLT

Ezekiel 38 in the BONUT2

Ezekiel 38 in the BOPLNT

Ezekiel 38 in the BOSCB

Ezekiel 38 in the BOSNC

Ezekiel 38 in the BOTLNT

Ezekiel 38 in the BOVCB

Ezekiel 38 in the BOYCB

Ezekiel 38 in the BPBB

Ezekiel 38 in the BPH

Ezekiel 38 in the BSB

Ezekiel 38 in the CCB

Ezekiel 38 in the CUV

Ezekiel 38 in the CUVS

Ezekiel 38 in the DBT

Ezekiel 38 in the DGDNT

Ezekiel 38 in the DHNT

Ezekiel 38 in the DNT

Ezekiel 38 in the ELBE

Ezekiel 38 in the EMTV

Ezekiel 38 in the ESV

Ezekiel 38 in the FBV

Ezekiel 38 in the FEB

Ezekiel 38 in the GGMNT

Ezekiel 38 in the GNT

Ezekiel 38 in the HARY

Ezekiel 38 in the HNT

Ezekiel 38 in the IRVA

Ezekiel 38 in the IRVB

Ezekiel 38 in the IRVG

Ezekiel 38 in the IRVH

Ezekiel 38 in the IRVK

Ezekiel 38 in the IRVM

Ezekiel 38 in the IRVM2

Ezekiel 38 in the IRVO

Ezekiel 38 in the IRVP

Ezekiel 38 in the IRVT

Ezekiel 38 in the IRVT2

Ezekiel 38 in the IRVU

Ezekiel 38 in the ISVN

Ezekiel 38 in the JSNT

Ezekiel 38 in the KAPI

Ezekiel 38 in the KBT1ETNIK

Ezekiel 38 in the KBV

Ezekiel 38 in the KJV

Ezekiel 38 in the KNFD

Ezekiel 38 in the LBA

Ezekiel 38 in the LBLA

Ezekiel 38 in the LNT

Ezekiel 38 in the LSV

Ezekiel 38 in the MAAL

Ezekiel 38 in the MBV

Ezekiel 38 in the MBV2

Ezekiel 38 in the MHNT

Ezekiel 38 in the MKNFD

Ezekiel 38 in the MNG

Ezekiel 38 in the MNT

Ezekiel 38 in the MNT2

Ezekiel 38 in the MRS1T

Ezekiel 38 in the NAA

Ezekiel 38 in the NASB

Ezekiel 38 in the NBLA

Ezekiel 38 in the NBS

Ezekiel 38 in the NBVTP

Ezekiel 38 in the NET2

Ezekiel 38 in the NIV11

Ezekiel 38 in the NNT

Ezekiel 38 in the NNT2

Ezekiel 38 in the NNT3

Ezekiel 38 in the PDDPT

Ezekiel 38 in the PFNT

Ezekiel 38 in the RMNT

Ezekiel 38 in the SBIAS

Ezekiel 38 in the SBIBS

Ezekiel 38 in the SBIBS2

Ezekiel 38 in the SBICS

Ezekiel 38 in the SBIDS

Ezekiel 38 in the SBIGS

Ezekiel 38 in the SBIHS

Ezekiel 38 in the SBIIS

Ezekiel 38 in the SBIIS2

Ezekiel 38 in the SBIIS3

Ezekiel 38 in the SBIKS

Ezekiel 38 in the SBIKS2

Ezekiel 38 in the SBIMS

Ezekiel 38 in the SBIOS

Ezekiel 38 in the SBIPS

Ezekiel 38 in the SBISS

Ezekiel 38 in the SBITS

Ezekiel 38 in the SBITS2

Ezekiel 38 in the SBITS3

Ezekiel 38 in the SBITS4

Ezekiel 38 in the SBIUS

Ezekiel 38 in the SBIVS

Ezekiel 38 in the SBT

Ezekiel 38 in the SBT1E

Ezekiel 38 in the SCHL

Ezekiel 38 in the SNT

Ezekiel 38 in the SUSU

Ezekiel 38 in the SUSU2

Ezekiel 38 in the SYNO

Ezekiel 38 in the TBIAOTANT

Ezekiel 38 in the TBT1E

Ezekiel 38 in the TBT1E2

Ezekiel 38 in the TFTIP

Ezekiel 38 in the TFTU

Ezekiel 38 in the TGNTATF3T

Ezekiel 38 in the THAI

Ezekiel 38 in the TNFD

Ezekiel 38 in the TNT

Ezekiel 38 in the TNTIK

Ezekiel 38 in the TNTIL

Ezekiel 38 in the TNTIN

Ezekiel 38 in the TNTIP

Ezekiel 38 in the TNTIZ

Ezekiel 38 in the TOMA

Ezekiel 38 in the TTENT

Ezekiel 38 in the UBG

Ezekiel 38 in the UGV

Ezekiel 38 in the UGV2

Ezekiel 38 in the UGV3

Ezekiel 38 in the VBL

Ezekiel 38 in the VDCC

Ezekiel 38 in the YALU

Ezekiel 38 in the YAPE

Ezekiel 38 in the YBVTP

Ezekiel 38 in the ZBP