Galatians 2 (BOGWICC)

1 Kenaka, patatha zaka khumi ndi zinayi, ndinapitanso ku Yerusalemu, nthawi iyi ndinapita ndi Barnaba. Ndinatenganso Tito kuti apite nafe. 2 Ine ndinapita chifukwa Mulungu anachita kundionetsera kuti ndipite ndipo ndinakakumana ndi atsogoleri mu msonkhano mwamseri ndi kuwafotokozera Uthenga Wabwino umene ndimalalikira pakati pa anthu a mitundu ina. Ndinachita zimenezi kuti ndikhale ndi chitsimikizo kuopa kuti mwina ndinathamanga kapena ndimathamanga liwiro pachabe. 3 Komatu ngakhale Tito, amene anali nane sanakakamizidwe kuti achite mdulidwe, ngakhale iyeyo anali Mgriki. 4 Nkhani iyi inayambika chifukwa abale ena achinyengo amene analowerera pakati pathu kuti adzaone za ufulu umene tili nawo mwa Khristu Yesu ndikuti atisandutse akapolo. 5 Ife sitinawagonjere ndi pangʼono pomwe, nʼcholinga chakuti choonadi cha Uthenga Wabwino chikhalebe ndi ife. 6 Koma kunena za aja ankaoneka ngati ofunika kwambiri, chimene iwo anali sichisintha kanthu kwa ine; chifukwa Mulungu alibe tsankho, iwowo sanawonjezepo kanthu pa uthenga wanga. 7 Makamaka anaona kuti ine ndinapatsidwa ntchito yolalikira Uthenga Wabwino kwa anthu a mitundu ina monga momwe Petro anapatsidwa ntchito yolalikira Uthenga Wabwino kwa Ayuda. 8 Pakuti Mulungu, amene amagwira ntchito mu utumiki wa Petro monga mtumwi kwa Ayuda, amagwiranso ntchito mu utumiki wanga monga mtumiki kwa anthu a mitundu ina. 9 Yakobo, Petro ndi Yohane, amene ankatengedwa ngati mizati, atazindikira chisomo chimene chinapatsidwa kwa ine, anagwirana chanza ndi ine ndi Barnaba kusonyeza chiyanjano chathu. Iwo anavomereza kuti ife tipite kwa anthu a mitundu ina ndipo iwo apite kwa Ayuda. 10 Chimene iwo anapempha ndi chakuti ife tipitirize kukumbukira osauka, chinthu chimene ine ndinali okonzeka kuchichita. 11 Petro atafika ku Antiokeya, ine ndinamudzudzula pa gulu chifukwa anapezeka wolakwa. 12 Pakuti asanafike anthu otumidwa ndi Yakobo, iye ankadya pamodzi ndi anthu a mitundu ina. Koma atafika, iyeyo anachoka pakati pa anthuwo nakakhala pa yekha chifukwa ankaopa anthu a mʼgulu la mdulidwe. 13 Ayuda enanso anamutsata pochita zachinyengozi, kotero kuti ngakhale Barnaba anasocheretsedwa chifukwa cha chinyengo chawocho. 14 Koma nditaona kuti iwo sankachita molingana ndi choonadi cha Uthenga Wabwino, ndinawuza Petro pamaso pa anthu onse kuti, “Iwe ndiwe Myuda koma ukukhala ngati munthu wa mtundu wina, osati Myuda. Nanga nʼchifukwa chiyani ukukakamiza anthu a mitundu ina kuti akhale ngati Ayuda? 15 “Ife amene ndife Ayuda mwachibadwa, osati anthu a mitundu ina ochimwa, 16 tikudziwa kuti munthu salungamitsidwa pochita ntchito za lamulo koma ndi chikhulupiriro mwa Yesu Khristu. Chomwecho, ifenso tinakhulupirira Khristu Yesu kuti tilungamitsidwe mwachikhulupiriro mwa Khristu ndipo osati pochita ntchito za lamulo, chifukwa palibe amene adzalungamitsidwa pochita ntchito za lamulo. 17 “Tsono ngati ife, pamene tikufuna kulungamitsidwa mwa Khristu, zikuonekeratu poyera kuti ndifenso ochimwa, kodi zikutanthauza kuti Khristu amalimbikitsa uchimo? Ayi. Nʼkosatheka! 18 Ngati ine ndimanganso chimene ndinachigumula, ndikuonetsa kuti ndine wophwanya lamulo. 19 “Pakuti pamene ndinayesera kutsatira lamulo, lamulolo linandionetsa kuti ndine wochimwa. Choncho ndinasiya kutsatira lamulo kuti ndikhale ndi moyo kwa Mulungu. 20 Ndinapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kotero kuti sindinenso amene ndili ndi moyo, koma ndi Khristu amene ali ndi moyo mwa ine. Moyo umene ndili nawo tsopano mʼthupi lino, ndi moyo mwachikhulupiriro mwa Mwana wa Mulungu, amene anandikonda nadzipereka yekha chifukwa cha ine. 21 Ine sindikukankhira kumbali chisomo cha Mulungu, chifukwa ngati chilungamo chikanapezeka pochita ntchito za lamulo, ndiye kuti Khristu anafa pachabe.”

In Other Versions

Galatians 2 in the ANGEFD

Galatians 2 in the ANTPNG2D

Galatians 2 in the AS21

Galatians 2 in the BAGH

Galatians 2 in the BBPNG

Galatians 2 in the BBT1E

Galatians 2 in the BDS

Galatians 2 in the BEV

Galatians 2 in the BHAD

Galatians 2 in the BIB

Galatians 2 in the BLPT

Galatians 2 in the BNT

Galatians 2 in the BNTABOOT

Galatians 2 in the BNTLV

Galatians 2 in the BOATCB

Galatians 2 in the BOATCB2

Galatians 2 in the BOBCV

Galatians 2 in the BOCNT

Galatians 2 in the BOECS

Galatians 2 in the BOHCB

Galatians 2 in the BOHCV

Galatians 2 in the BOHLNT

Galatians 2 in the BOHNTLTAL

Galatians 2 in the BOICB

Galatians 2 in the BOILNTAP

Galatians 2 in the BOITCV

Galatians 2 in the BOKCV

Galatians 2 in the BOKCV2

Galatians 2 in the BOKHWOG

Galatians 2 in the BOKSSV

Galatians 2 in the BOLCB

Galatians 2 in the BOLCB2

Galatians 2 in the BOMCV

Galatians 2 in the BONAV

Galatians 2 in the BONCB

Galatians 2 in the BONLT

Galatians 2 in the BONUT2

Galatians 2 in the BOPLNT

Galatians 2 in the BOSCB

Galatians 2 in the BOSNC

Galatians 2 in the BOTLNT

Galatians 2 in the BOVCB

Galatians 2 in the BOYCB

Galatians 2 in the BPBB

Galatians 2 in the BPH

Galatians 2 in the BSB

Galatians 2 in the CCB

Galatians 2 in the CUV

Galatians 2 in the CUVS

Galatians 2 in the DBT

Galatians 2 in the DGDNT

Galatians 2 in the DHNT

Galatians 2 in the DNT

Galatians 2 in the ELBE

Galatians 2 in the EMTV

Galatians 2 in the ESV

Galatians 2 in the FBV

Galatians 2 in the FEB

Galatians 2 in the GGMNT

Galatians 2 in the GNT

Galatians 2 in the HARY

Galatians 2 in the HNT

Galatians 2 in the IRVA

Galatians 2 in the IRVB

Galatians 2 in the IRVG

Galatians 2 in the IRVH

Galatians 2 in the IRVK

Galatians 2 in the IRVM

Galatians 2 in the IRVM2

Galatians 2 in the IRVO

Galatians 2 in the IRVP

Galatians 2 in the IRVT

Galatians 2 in the IRVT2

Galatians 2 in the IRVU

Galatians 2 in the ISVN

Galatians 2 in the JSNT

Galatians 2 in the KAPI

Galatians 2 in the KBT1ETNIK

Galatians 2 in the KBV

Galatians 2 in the KJV

Galatians 2 in the KNFD

Galatians 2 in the LBA

Galatians 2 in the LBLA

Galatians 2 in the LNT

Galatians 2 in the LSV

Galatians 2 in the MAAL

Galatians 2 in the MBV

Galatians 2 in the MBV2

Galatians 2 in the MHNT

Galatians 2 in the MKNFD

Galatians 2 in the MNG

Galatians 2 in the MNT

Galatians 2 in the MNT2

Galatians 2 in the MRS1T

Galatians 2 in the NAA

Galatians 2 in the NASB

Galatians 2 in the NBLA

Galatians 2 in the NBS

Galatians 2 in the NBVTP

Galatians 2 in the NET2

Galatians 2 in the NIV11

Galatians 2 in the NNT

Galatians 2 in the NNT2

Galatians 2 in the NNT3

Galatians 2 in the PDDPT

Galatians 2 in the PFNT

Galatians 2 in the RMNT

Galatians 2 in the SBIAS

Galatians 2 in the SBIBS

Galatians 2 in the SBIBS2

Galatians 2 in the SBICS

Galatians 2 in the SBIDS

Galatians 2 in the SBIGS

Galatians 2 in the SBIHS

Galatians 2 in the SBIIS

Galatians 2 in the SBIIS2

Galatians 2 in the SBIIS3

Galatians 2 in the SBIKS

Galatians 2 in the SBIKS2

Galatians 2 in the SBIMS

Galatians 2 in the SBIOS

Galatians 2 in the SBIPS

Galatians 2 in the SBISS

Galatians 2 in the SBITS

Galatians 2 in the SBITS2

Galatians 2 in the SBITS3

Galatians 2 in the SBITS4

Galatians 2 in the SBIUS

Galatians 2 in the SBIVS

Galatians 2 in the SBT

Galatians 2 in the SBT1E

Galatians 2 in the SCHL

Galatians 2 in the SNT

Galatians 2 in the SUSU

Galatians 2 in the SUSU2

Galatians 2 in the SYNO

Galatians 2 in the TBIAOTANT

Galatians 2 in the TBT1E

Galatians 2 in the TBT1E2

Galatians 2 in the TFTIP

Galatians 2 in the TFTU

Galatians 2 in the TGNTATF3T

Galatians 2 in the THAI

Galatians 2 in the TNFD

Galatians 2 in the TNT

Galatians 2 in the TNTIK

Galatians 2 in the TNTIL

Galatians 2 in the TNTIN

Galatians 2 in the TNTIP

Galatians 2 in the TNTIZ

Galatians 2 in the TOMA

Galatians 2 in the TTENT

Galatians 2 in the UBG

Galatians 2 in the UGV

Galatians 2 in the UGV2

Galatians 2 in the UGV3

Galatians 2 in the VBL

Galatians 2 in the VDCC

Galatians 2 in the YALU

Galatians 2 in the YAPE

Galatians 2 in the YBVTP

Galatians 2 in the ZBP