Galatians 4 (BOGWICC)
1 Chimene ndikunena ndi chakuti, ngati mlowamʼmalo akali wamngʼono, sasiyana ndi kapolo, ngakhale kuti chuma chonse ndi chake. 2 Mwanayo ayenera kumvera omulera ndiponso anthu oyangʼanira chuma mpaka nthawi imene abambo ake anakhazikitsa. 3 Chomwechonso, ife pamene tinali ana, tinali akapolo a miyambo ya dziko lapansi. 4 Koma nthawi itakwana, Mulungu anatumiza Mwana wake, wobadwa mwa mayi, wobadwa pansi pa lamulo, 5 kudzawombola amene anali pansi pa lamulo, kuti tilandiridwe monga ana. 6 Ndipo popeza ndinu ana, Mulungu anatumiza Mzimu wa Mwana wake kuti alowe mʼmitima mwathu, Mzimu amene amafuwula kuti, “Abba, Atate.” 7 Choncho sindiwenso kapolo, koma mwana wa Mulungu. Tsono popeza ndiwe mwana wake, Mulungu wakusandutsanso mlowamʼmalo. 8 Koma poyamba pamene simunkamudziwa Mulungu, munali akapolo a zimene mwachilengedwe si milungu. 9 Koma tsopano pakuti mukumudziwa Mulungu, kapena ndinene kuti Mulungu akukudziwani, nʼchifukwa chiyani mukubwereranso ku miyambo yofowoka ndi yomvetsa chisoni? Kodi mukufuna musandukenso akapolo? 10 Mumasunga masiku, miyezi ndi nyengo ndi zaka. 11 Ine ndikuopa kuti mwina ntchito zanga pa inu ndinagwira pachabe. 12 Abale, ndikukudandaulirani, mukhale ngati ine, popeza ine ndinakhala ngati inu. Inu simunandilakwire. 13 Monga inu mukudziwa ndinkakulalikirani Uthenga Wabwino ndili wofowoka. 14 Ngakhale kuti matendawo anali ngati mayesero kwa inu, simunandinyoze kapena kunyansidwa nane. Komatu inu munandilandira ngati kuti ndinali mngelo wa Mulungu, ngati kuti ndinali Khristu Yesu mwini. 15 Kodi chimwemwe chanu chonse chija chili kuti? Ine nditha kuchitira umboni kuti, ngati kukanatheka, inu mukanakolowola maso anu ndi kundipatsa. 16 Kodi tsopano ine ndasanduka mdani wanu chifukwa ndakuwuzani choonadi? 17 Anthu amenewo akuchita changu kuti akukopeni, koma changu chawocho sichabwino. Chimene iwo akufuna ndi chakuti akuchotseni inu kwa ife, kuti mukachite changu powathandiza iwowo. 18 Nʼkwabwino kuchita changu, ngati cholingacho chili chabwino ndi kukhala otero nthawi zonse osati pokhapo pamene ine ndili ndi inu. 19 Ana anga okondedwa, inu amene ine ndikukumveraninso zowawa za kubereka kufikira Khristu atawumbidwa mwa inu, 20 ine ndikanakonda ndikanakhala nanu tsopano kuti ndisinthe mawu anga, chifukwa ndathedwa nanu nzeru. 21 Tandiwuzani, inu, abale amene mukufuna kukhala pansi pa lamulo, kodi simukudziwa chimene lamulo limanena? 22 Pakuti zinalembedwa kuti Abrahamu anali ndi ana aamuna awiri, wina mayi wake anali kapolo ndipo wina mayi wake anali mfulu. 23 Mwana wake wobadwa mwa kapolo anabadwa mwathupi; koma mwana wake wobadwa mwa mfulu anabadwa monga mwa lonjezo. 24 Zinthu izi zinali ngati fanizo, pakuti amayi awiriwa akuyimira mapangano awiri. Pangano limodzi ndi lochokera mʼPhiri la Sinai, ndiye Hagara, ndipo amabereka ana amene ndi akapolo. 25 Tsono Hagara, akuyimira Phiri la Sinai ku Arabiya amene afanizidwa ndi mzinda wa Yerusalemu wa lero, chifukwa ali mu ukapolo pamodzi ndi ana ake. 26 Koma Yerusalemu wakumwamba ndiye mfulu, ndipo ndiye mayi wathu. 27 Pakuti kwalembedwa kuti,“Sangalala, iwe mayi wosabala,amene sunabalepo mwana;imba nthungululu ndi kufuwula mwachimwemwe,iwe amene sunamvepo ululu wa pobereka;chifukwa mkazi wosiyidwa adzakhala ndi ana ambirikuposa mkazi wokwatiwa.” 28 Tsono inu abale, ndinu ana alonjezo ngati Isake. 29 Nthawi imeneyo mwana wobadwa mwathupi anazunza mwana wobadwa mwamphamvu za Mzimu. Zili chimodzimodzinso lero. 30 Kodi Malemba akuti chiyani? “Muchotse kapoloyo pamodzi ndi mwana wake, chifukwa mwana wa kapolo sadzagawana chuma ndi mwana wamfulu.” 31 Chifukwa chake, abale, ife sindife ana akapolo, koma ana a mfulu.
In Other Versions
Galatians 4 in the ANGEFD
Galatians 4 in the ANTPNG2D
Galatians 4 in the AS21
Galatians 4 in the BAGH
Galatians 4 in the BBPNG
Galatians 4 in the BBT1E
Galatians 4 in the BDS
Galatians 4 in the BEV
Galatians 4 in the BHAD
Galatians 4 in the BIB
Galatians 4 in the BLPT
Galatians 4 in the BNT
Galatians 4 in the BNTABOOT
Galatians 4 in the BNTLV
Galatians 4 in the BOATCB
Galatians 4 in the BOATCB2
Galatians 4 in the BOBCV
Galatians 4 in the BOCNT
Galatians 4 in the BOECS
Galatians 4 in the BOHCB
Galatians 4 in the BOHCV
Galatians 4 in the BOHLNT
Galatians 4 in the BOHNTLTAL
Galatians 4 in the BOICB
Galatians 4 in the BOILNTAP
Galatians 4 in the BOITCV
Galatians 4 in the BOKCV
Galatians 4 in the BOKCV2
Galatians 4 in the BOKHWOG
Galatians 4 in the BOKSSV
Galatians 4 in the BOLCB
Galatians 4 in the BOLCB2
Galatians 4 in the BOMCV
Galatians 4 in the BONAV
Galatians 4 in the BONCB
Galatians 4 in the BONLT
Galatians 4 in the BONUT2
Galatians 4 in the BOPLNT
Galatians 4 in the BOSCB
Galatians 4 in the BOSNC
Galatians 4 in the BOTLNT
Galatians 4 in the BOVCB
Galatians 4 in the BOYCB
Galatians 4 in the BPBB
Galatians 4 in the BPH
Galatians 4 in the BSB
Galatians 4 in the CCB
Galatians 4 in the CUV
Galatians 4 in the CUVS
Galatians 4 in the DBT
Galatians 4 in the DGDNT
Galatians 4 in the DHNT
Galatians 4 in the DNT
Galatians 4 in the ELBE
Galatians 4 in the EMTV
Galatians 4 in the ESV
Galatians 4 in the FBV
Galatians 4 in the FEB
Galatians 4 in the GGMNT
Galatians 4 in the GNT
Galatians 4 in the HARY
Galatians 4 in the HNT
Galatians 4 in the IRVA
Galatians 4 in the IRVB
Galatians 4 in the IRVG
Galatians 4 in the IRVH
Galatians 4 in the IRVK
Galatians 4 in the IRVM
Galatians 4 in the IRVM2
Galatians 4 in the IRVO
Galatians 4 in the IRVP
Galatians 4 in the IRVT
Galatians 4 in the IRVT2
Galatians 4 in the IRVU
Galatians 4 in the ISVN
Galatians 4 in the JSNT
Galatians 4 in the KAPI
Galatians 4 in the KBT1ETNIK
Galatians 4 in the KBV
Galatians 4 in the KJV
Galatians 4 in the KNFD
Galatians 4 in the LBA
Galatians 4 in the LBLA
Galatians 4 in the LNT
Galatians 4 in the LSV
Galatians 4 in the MAAL
Galatians 4 in the MBV
Galatians 4 in the MBV2
Galatians 4 in the MHNT
Galatians 4 in the MKNFD
Galatians 4 in the MNG
Galatians 4 in the MNT
Galatians 4 in the MNT2
Galatians 4 in the MRS1T
Galatians 4 in the NAA
Galatians 4 in the NASB
Galatians 4 in the NBLA
Galatians 4 in the NBS
Galatians 4 in the NBVTP
Galatians 4 in the NET2
Galatians 4 in the NIV11
Galatians 4 in the NNT
Galatians 4 in the NNT2
Galatians 4 in the NNT3
Galatians 4 in the PDDPT
Galatians 4 in the PFNT
Galatians 4 in the RMNT
Galatians 4 in the SBIAS
Galatians 4 in the SBIBS
Galatians 4 in the SBIBS2
Galatians 4 in the SBICS
Galatians 4 in the SBIDS
Galatians 4 in the SBIGS
Galatians 4 in the SBIHS
Galatians 4 in the SBIIS
Galatians 4 in the SBIIS2
Galatians 4 in the SBIIS3
Galatians 4 in the SBIKS
Galatians 4 in the SBIKS2
Galatians 4 in the SBIMS
Galatians 4 in the SBIOS
Galatians 4 in the SBIPS
Galatians 4 in the SBISS
Galatians 4 in the SBITS
Galatians 4 in the SBITS2
Galatians 4 in the SBITS3
Galatians 4 in the SBITS4
Galatians 4 in the SBIUS
Galatians 4 in the SBIVS
Galatians 4 in the SBT
Galatians 4 in the SBT1E
Galatians 4 in the SCHL
Galatians 4 in the SNT
Galatians 4 in the SUSU
Galatians 4 in the SUSU2
Galatians 4 in the SYNO
Galatians 4 in the TBIAOTANT
Galatians 4 in the TBT1E
Galatians 4 in the TBT1E2
Galatians 4 in the TFTIP
Galatians 4 in the TFTU
Galatians 4 in the TGNTATF3T
Galatians 4 in the THAI
Galatians 4 in the TNFD
Galatians 4 in the TNT
Galatians 4 in the TNTIK
Galatians 4 in the TNTIL
Galatians 4 in the TNTIN
Galatians 4 in the TNTIP
Galatians 4 in the TNTIZ
Galatians 4 in the TOMA
Galatians 4 in the TTENT
Galatians 4 in the UBG
Galatians 4 in the UGV
Galatians 4 in the UGV2
Galatians 4 in the UGV3
Galatians 4 in the VBL
Galatians 4 in the VDCC
Galatians 4 in the YALU
Galatians 4 in the YAPE
Galatians 4 in the YBVTP
Galatians 4 in the ZBP