Galatians 5 (BOGWICC)
1 Khristu anatimasula kuti tikhale mfulu. Tsono chirimikani, ndipo musakodwenso mʼgoli la ukapolo. 2 Chonde mvetsetsani! Ine Paulo, ndikukuwuzani kuti mukalola kuchita mdulidwe, Khristu simupindula nayenso konse. 3 Ndikubwerezanso kuwuza munthu aliyense wovomereza kuchita mdulidwe kuti ayeneranso kutsata Malamulo onse. 4 Inu amene mukufuna kulungamitsidwa ndi lamulo mwachotsedwa mwa Khristu; munagwa kusiyana nacho chisomo. 5 Koma mwachikhulupiriro, ife tikudikira mwachidwi kudzera mwa Mzimu, chilungamo chimene tikuyembekeza. 6 Pakuti mwa Khristu Yesu mdulidwe kapena kusachita mdulidwe zilibe phindu. Chinthu chokhacho chimene chimafunika ndi chikhulupiriro chogwira ntchito mwachikondi. 7 Inu munkathamanga mpikisano wanu wabwino. Anakuletsani ndani kuti musamverenso choonadi? 8 Kukopeka kwanu kumeneku sikuchokera kwa Iye amene anakuyitanani. 9 “Yisiti wapangʼono amagwira ntchito mu buledi yense.” 10 Ine ndikutsimikiza mwa Ambuye kuti inu simudzasiyana nane maganizo. Iye amene akukusokonezani adzalangidwa, kaya iyeyo ndiye ndani. 11 Abale, ngati ine ndikulalikirabe za mdulidwe, nʼchifukwa chiyani ndikusautsidwabe? Ngati ndikanakhala kuti sindikulalikira chipulumutso cha mtanda, palibe amene akanakhumudwa. 12 Kunena za amene akukuvutani, ndikanakonda akanangodzithena okha! 13 Inu abale, Mulungu anakuyitanani kuti mukhale mfulu. Koma musagwiritse ntchito ufulu wanuwo kuchita zoyipa zachikhalidwe cha uchimo cha thupi lanu, koma mutumikirane wina ndi mnzake mwachikondi. 14 Pakuti malamulo onse akuphatikizidwa mu lamulo ili, “Konda mnansi wako monga iwe mwini.” 15 Ngati mupitiriza kulumana ndi kukhadzulana, samalani kuti mungawonongane. 16 Choncho ine ndikuti, mulole kuti Mzimu akutsogolereni ndipo simudzachita zofuna za thupi lanu la uchimo. 17 Pakuti thupi lanu la uchimo limalakalaka zimene ndi zotsutsana ndi Mzimu, ndi Mzimu zimene ndi zotsutsana ndi thupi lanu la uchimo. Ziwirizi zimadana, kotero kuti simungachite zimene mukufuna. 18 Koma ngati Mzimu akutsogolerani, ndiye kuti simuli pansi pa lamulo. 19 Ntchito za thupi lanu la uchimo zimaonekera poyera ndi izi: dama, zodetsa ndi kuchita zonyansa; 20 kupembedza mafano ndi ufiti; kudana, kukangana, kupsa mtima, kudzikonda, kugawikana, mipatuko 21 ndi nsanje, kuledzera, mchezo ndi zina zotere. Ine ndikukuchenjezani monga ndinachita poyamba paja kuti amene amachita zimenezi sadzalandira ufumu wa Mulungu. 22 Koma chipatso cha Mzimu Woyera ndi chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, 23 kufatsa ndi kudziretsa. Palibe lamulo loletsa zimenezi. 24 Amene ali ake a Khristu Yesu anapachika pa mtanda thupi lawo la uchimo pamodzi ndi zokhumba zawo ndi zolakalaka zawo. 25 Popeza timakhala ndi moyo mwa Mzimu Woyera, tiyeni tiyende pamodzi ndi Mzimu Woyera. 26 Tisakhale odzitukumula, oputana ndi ochitirana nsanje.
In Other Versions
Galatians 5 in the ANGEFD
Galatians 5 in the ANTPNG2D
Galatians 5 in the AS21
Galatians 5 in the BAGH
Galatians 5 in the BBPNG
Galatians 5 in the BBT1E
Galatians 5 in the BDS
Galatians 5 in the BEV
Galatians 5 in the BHAD
Galatians 5 in the BIB
Galatians 5 in the BLPT
Galatians 5 in the BNT
Galatians 5 in the BNTABOOT
Galatians 5 in the BNTLV
Galatians 5 in the BOATCB
Galatians 5 in the BOATCB2
Galatians 5 in the BOBCV
Galatians 5 in the BOCNT
Galatians 5 in the BOECS
Galatians 5 in the BOHCB
Galatians 5 in the BOHCV
Galatians 5 in the BOHLNT
Galatians 5 in the BOHNTLTAL
Galatians 5 in the BOICB
Galatians 5 in the BOILNTAP
Galatians 5 in the BOITCV
Galatians 5 in the BOKCV
Galatians 5 in the BOKCV2
Galatians 5 in the BOKHWOG
Galatians 5 in the BOKSSV
Galatians 5 in the BOLCB
Galatians 5 in the BOLCB2
Galatians 5 in the BOMCV
Galatians 5 in the BONAV
Galatians 5 in the BONCB
Galatians 5 in the BONLT
Galatians 5 in the BONUT2
Galatians 5 in the BOPLNT
Galatians 5 in the BOSCB
Galatians 5 in the BOSNC
Galatians 5 in the BOTLNT
Galatians 5 in the BOVCB
Galatians 5 in the BOYCB
Galatians 5 in the BPBB
Galatians 5 in the BPH
Galatians 5 in the BSB
Galatians 5 in the CCB
Galatians 5 in the CUV
Galatians 5 in the CUVS
Galatians 5 in the DBT
Galatians 5 in the DGDNT
Galatians 5 in the DHNT
Galatians 5 in the DNT
Galatians 5 in the ELBE
Galatians 5 in the EMTV
Galatians 5 in the ESV
Galatians 5 in the FBV
Galatians 5 in the FEB
Galatians 5 in the GGMNT
Galatians 5 in the GNT
Galatians 5 in the HARY
Galatians 5 in the HNT
Galatians 5 in the IRVA
Galatians 5 in the IRVB
Galatians 5 in the IRVG
Galatians 5 in the IRVH
Galatians 5 in the IRVK
Galatians 5 in the IRVM
Galatians 5 in the IRVM2
Galatians 5 in the IRVO
Galatians 5 in the IRVP
Galatians 5 in the IRVT
Galatians 5 in the IRVT2
Galatians 5 in the IRVU
Galatians 5 in the ISVN
Galatians 5 in the JSNT
Galatians 5 in the KAPI
Galatians 5 in the KBT1ETNIK
Galatians 5 in the KBV
Galatians 5 in the KJV
Galatians 5 in the KNFD
Galatians 5 in the LBA
Galatians 5 in the LBLA
Galatians 5 in the LNT
Galatians 5 in the LSV
Galatians 5 in the MAAL
Galatians 5 in the MBV
Galatians 5 in the MBV2
Galatians 5 in the MHNT
Galatians 5 in the MKNFD
Galatians 5 in the MNG
Galatians 5 in the MNT
Galatians 5 in the MNT2
Galatians 5 in the MRS1T
Galatians 5 in the NAA
Galatians 5 in the NASB
Galatians 5 in the NBLA
Galatians 5 in the NBS
Galatians 5 in the NBVTP
Galatians 5 in the NET2
Galatians 5 in the NIV11
Galatians 5 in the NNT
Galatians 5 in the NNT2
Galatians 5 in the NNT3
Galatians 5 in the PDDPT
Galatians 5 in the PFNT
Galatians 5 in the RMNT
Galatians 5 in the SBIAS
Galatians 5 in the SBIBS
Galatians 5 in the SBIBS2
Galatians 5 in the SBICS
Galatians 5 in the SBIDS
Galatians 5 in the SBIGS
Galatians 5 in the SBIHS
Galatians 5 in the SBIIS
Galatians 5 in the SBIIS2
Galatians 5 in the SBIIS3
Galatians 5 in the SBIKS
Galatians 5 in the SBIKS2
Galatians 5 in the SBIMS
Galatians 5 in the SBIOS
Galatians 5 in the SBIPS
Galatians 5 in the SBISS
Galatians 5 in the SBITS
Galatians 5 in the SBITS2
Galatians 5 in the SBITS3
Galatians 5 in the SBITS4
Galatians 5 in the SBIUS
Galatians 5 in the SBIVS
Galatians 5 in the SBT
Galatians 5 in the SBT1E
Galatians 5 in the SCHL
Galatians 5 in the SNT
Galatians 5 in the SUSU
Galatians 5 in the SUSU2
Galatians 5 in the SYNO
Galatians 5 in the TBIAOTANT
Galatians 5 in the TBT1E
Galatians 5 in the TBT1E2
Galatians 5 in the TFTIP
Galatians 5 in the TFTU
Galatians 5 in the TGNTATF3T
Galatians 5 in the THAI
Galatians 5 in the TNFD
Galatians 5 in the TNT
Galatians 5 in the TNTIK
Galatians 5 in the TNTIL
Galatians 5 in the TNTIN
Galatians 5 in the TNTIP
Galatians 5 in the TNTIZ
Galatians 5 in the TOMA
Galatians 5 in the TTENT
Galatians 5 in the UBG
Galatians 5 in the UGV
Galatians 5 in the UGV2
Galatians 5 in the UGV3
Galatians 5 in the VBL
Galatians 5 in the VDCC
Galatians 5 in the YALU
Galatians 5 in the YAPE
Galatians 5 in the YBVTP
Galatians 5 in the ZBP