Genesis 33 (BOGWICC)
1 Yakobo atakweza maso ake anaona Esau akubwera ndi anthu ake 400. Choncho ana ake anawagawira Leya, Rakele ndi antchito awiri aja. 2 Anayika antchito ndi ana awo patsogolo, kenaka nʼkubwera Leya ndi ana ake, ndipo pambuyo pawo Rakele ndi Yosefe. 3 Iye mwini anakhala patsogolo nawerama mpaka kukhudza pansi kasanu ndi kawiri pamene amayandikira mʼbale wake. 4 Koma Esau anathamanga kukakumana ndi Yakobo ndipo anamukupatira namupsompsona. Onse awiri ankangolira. 5 Kenaka Esau ataona amayi ndi ana awo anamufunsa Yakobo kuti, “Kodi anthu amene uli nawowa ndi a ndani?”Yakobo anayankha kuti, “Awa ndi ana amene Mulungu, mwa kukoma mtima kwake, wapereka kwa mtumiki wanune.” 6 Tsono antchito aja anayandikira naweramitsa mitu pansi. 7 Kenaka, Leya ndi ana ake anabwera. Nawonso anaweramitsa mitu pansi. Potsiriza pa onse anabwera Yosefe ndi Rakele naweramitsanso mitu yawo pansi. 8 Esau anafunsa kuti, “Kodi gulu la ziweto ndakumana nalo lija ndi layani?”Yakobo anayankha nati, “Mbuye wanga, gulu lija ndi lanu kuti mundikomere mtima.” 9 Koma Esau anati, “Mʼbale wanga, ine ndili nazo kale zambiri. Zinthu zakozi sunga.” 10 Yakobo anati, “Chonde musatero. Ngati mwandikomera mtima, landirani mphatso yangayi kuchokera kwa ine. Pakuti ndi mmene mwandirandira bwinomu, ine ndikamaona nkhope yanu ndikuchita ngati ndikuona nkhope ya Mulungu. 11 Chonde, landirani mphatso imene ndakutengeraniyi, popeza Mulungu wandikomera mtima kwambiri moti ndili ndi zonse zimene ndizifuna.” Ndipo popeza kuti Yakobo anamuwumiriza, Esau analandira. 12 Ndipo Esau anati, “Tiyeni tizipita; nditsagana nanu.” 13 Koma Yakobo anati kwa iye, “Mbuye wanga, inu mudziwa kuti anawa ndi a nthete ndiponso ndiyenera kusamalira nkhosa ndi ngʼombe zimene zikuyamwitsa ana awo. Ngati ndizimenya kuti zifulumire, tsiku limodzi lokha nyamazo zidzafa. 14 Choncho, mbuye wanga lolani kuti mutsogole. Ine ndiziyenda pangʼonopangʼono pambuyo pa ziwetozi ndi anawa mpaka ndikafika ku Seiri.” 15 Esau anati, “Ndiye bwanji ndikusiyireko ena mwa anthu anga.”Koma Yakobo anati, “Koma muchitiranji zimenezi? Chachikulu nʼkuti mwandilandira bwino, mbuye wanga.” 16 Choncho tsiku limenelo Esau anayamba ulendo wobwerera ku Seiri. 17 Komabe Yakobo anapita ku Sukoti. Kumeneko anamanga nyumba yake ndi makola a ziweto zake. Nʼchifukwa chake malowa amatchedwa Sukoti. 18 Mmene ankabwerera kuchokera ku Padanaramu, Yakobo anafika ku Salemu, mzinda wa Sekemu ku Kanaani. Anamanga msasa pamalopo moyangʼanana ndi mzindawo. 19 Malo amenewo anagula kwa zidzukulu za Hamori, abambo a Sekemu ndi ndalama 100 zasiliva. 20 Pamalopo anamanganso guwa lansembe, nalitcha Eli Elohe Israeli.
In Other Versions
Genesis 33 in the ANGEFD
Genesis 33 in the ANTPNG2D
Genesis 33 in the AS21
Genesis 33 in the BAGH
Genesis 33 in the BBPNG
Genesis 33 in the BBT1E
Genesis 33 in the BDS
Genesis 33 in the BEV
Genesis 33 in the BHAD
Genesis 33 in the BIB
Genesis 33 in the BLPT
Genesis 33 in the BNT
Genesis 33 in the BNTABOOT
Genesis 33 in the BNTLV
Genesis 33 in the BOATCB
Genesis 33 in the BOATCB2
Genesis 33 in the BOBCV
Genesis 33 in the BOCNT
Genesis 33 in the BOECS
Genesis 33 in the BOHCB
Genesis 33 in the BOHCV
Genesis 33 in the BOHLNT
Genesis 33 in the BOHNTLTAL
Genesis 33 in the BOICB
Genesis 33 in the BOILNTAP
Genesis 33 in the BOITCV
Genesis 33 in the BOKCV
Genesis 33 in the BOKCV2
Genesis 33 in the BOKHWOG
Genesis 33 in the BOKSSV
Genesis 33 in the BOLCB
Genesis 33 in the BOLCB2
Genesis 33 in the BOMCV
Genesis 33 in the BONAV
Genesis 33 in the BONCB
Genesis 33 in the BONLT
Genesis 33 in the BONUT2
Genesis 33 in the BOPLNT
Genesis 33 in the BOSCB
Genesis 33 in the BOSNC
Genesis 33 in the BOTLNT
Genesis 33 in the BOVCB
Genesis 33 in the BOYCB
Genesis 33 in the BPBB
Genesis 33 in the BPH
Genesis 33 in the BSB
Genesis 33 in the CCB
Genesis 33 in the CUV
Genesis 33 in the CUVS
Genesis 33 in the DBT
Genesis 33 in the DGDNT
Genesis 33 in the DHNT
Genesis 33 in the DNT
Genesis 33 in the ELBE
Genesis 33 in the EMTV
Genesis 33 in the ESV
Genesis 33 in the FBV
Genesis 33 in the FEB
Genesis 33 in the GGMNT
Genesis 33 in the GNT
Genesis 33 in the HARY
Genesis 33 in the HNT
Genesis 33 in the IRVA
Genesis 33 in the IRVB
Genesis 33 in the IRVG
Genesis 33 in the IRVH
Genesis 33 in the IRVK
Genesis 33 in the IRVM
Genesis 33 in the IRVM2
Genesis 33 in the IRVO
Genesis 33 in the IRVP
Genesis 33 in the IRVT
Genesis 33 in the IRVT2
Genesis 33 in the IRVU
Genesis 33 in the ISVN
Genesis 33 in the JSNT
Genesis 33 in the KAPI
Genesis 33 in the KBT1ETNIK
Genesis 33 in the KBV
Genesis 33 in the KJV
Genesis 33 in the KNFD
Genesis 33 in the LBA
Genesis 33 in the LBLA
Genesis 33 in the LNT
Genesis 33 in the LSV
Genesis 33 in the MAAL
Genesis 33 in the MBV
Genesis 33 in the MBV2
Genesis 33 in the MHNT
Genesis 33 in the MKNFD
Genesis 33 in the MNG
Genesis 33 in the MNT
Genesis 33 in the MNT2
Genesis 33 in the MRS1T
Genesis 33 in the NAA
Genesis 33 in the NASB
Genesis 33 in the NBLA
Genesis 33 in the NBS
Genesis 33 in the NBVTP
Genesis 33 in the NET2
Genesis 33 in the NIV11
Genesis 33 in the NNT
Genesis 33 in the NNT2
Genesis 33 in the NNT3
Genesis 33 in the PDDPT
Genesis 33 in the PFNT
Genesis 33 in the RMNT
Genesis 33 in the SBIAS
Genesis 33 in the SBIBS
Genesis 33 in the SBIBS2
Genesis 33 in the SBICS
Genesis 33 in the SBIDS
Genesis 33 in the SBIGS
Genesis 33 in the SBIHS
Genesis 33 in the SBIIS
Genesis 33 in the SBIIS2
Genesis 33 in the SBIIS3
Genesis 33 in the SBIKS
Genesis 33 in the SBIKS2
Genesis 33 in the SBIMS
Genesis 33 in the SBIOS
Genesis 33 in the SBIPS
Genesis 33 in the SBISS
Genesis 33 in the SBITS
Genesis 33 in the SBITS2
Genesis 33 in the SBITS3
Genesis 33 in the SBITS4
Genesis 33 in the SBIUS
Genesis 33 in the SBIVS
Genesis 33 in the SBT
Genesis 33 in the SBT1E
Genesis 33 in the SCHL
Genesis 33 in the SNT
Genesis 33 in the SUSU
Genesis 33 in the SUSU2
Genesis 33 in the SYNO
Genesis 33 in the TBIAOTANT
Genesis 33 in the TBT1E
Genesis 33 in the TBT1E2
Genesis 33 in the TFTIP
Genesis 33 in the TFTU
Genesis 33 in the TGNTATF3T
Genesis 33 in the THAI
Genesis 33 in the TNFD
Genesis 33 in the TNT
Genesis 33 in the TNTIK
Genesis 33 in the TNTIL
Genesis 33 in the TNTIN
Genesis 33 in the TNTIP
Genesis 33 in the TNTIZ
Genesis 33 in the TOMA
Genesis 33 in the TTENT
Genesis 33 in the UBG
Genesis 33 in the UGV
Genesis 33 in the UGV2
Genesis 33 in the UGV3
Genesis 33 in the VBL
Genesis 33 in the VDCC
Genesis 33 in the YALU
Genesis 33 in the YAPE
Genesis 33 in the YBVTP
Genesis 33 in the ZBP