Genesis 36 (BOGWICC)
1 Nazi zidzukulu za Esau amene ankatchedwanso Edomu: 2 Esau anakwatira akazi atatu a ku Kanaani. Iwowa ndiwo Ada mwana wa Eloni Mhiti; Oholibama mwana wa Ana amene anali mwana wa Zibeoni Mhivi 3 ndi Basemati mwana wa Ismaeli, amenenso anali mlongo wa Nabayoti. 4 Ada anaberekera Esau, Elifazi; Basemati anabereka Reueli; 5 ndipo Oholibama anabereka Yeusi, Yolamu ndi Kora. Amenewa anali ana a Esau amene anabadwira ku Kanaani. 6 Esau anatenga akazi ake, ana ake aamuna ndi aakazi ndi ena onse a pa banja pake. Anatenganso ziweto zake ndi ziweto zake zonse pamodzi ndi katundu wake yense amene anamupata ku Kanaani, ndipo anachoka ku dziko la Kanaani kupatukana ndi mʼbale wake Yakobo. 7 Iwo anatero chifukwa dziko limene ankakhalamo silikanakwanira awiriwo. Iwowa anali ndi ziweto zochuluka motero kuti sakanatha kukhala pamodzi. 8 Choncho Esau (amene ndi Edomu) anakakhazikika ku dziko la mapiri ku Seiri. 9 Nazi zidzukulu za Esau, kholo la Aedomu amene ankakhala ku Seiri. 10 Awa ndi mayina a ana aamuna a Esau:Elifazi, mwana wa Ada, mkazi wa Esau, ndi Reueli, mwana wamwamuna wa Basemati, mkazi wa Esau. 11 Awa ndi mayina a ana a Elifazi:Temani, Omari, Zefo, Gatamu ndi Kenazi. 12 Timna anali mzikazi wa Elifazi, mwana wa Esau. Iyeyo anaberekera Elifazi mwana dzina lake Amaleki. Amenewa ndiwo zidzukulu za Ada, mkazi wa Esau. 13 Awa ndi ana a Reueli:Nahati, Zera, Sama ndi Miza. Amenewa ndi ana a Basemati, mkazi wa Esau. 14 Ana aamuna a Oholibama, mkazi wa Esau, mwana wa Ana ndi mdzukulu wa Zebeoni ndi awa:Yeusi, Yolamu ndi Kora. 15 Nawa mafumu a zidzukulu za Esau:Mwa ana a Elifazi, mwana woyamba wa Esau panali mafumu awa:Temani, Omari, Zefo, ndi Kenazi, 16 Kora, Gatamu, ndi Amaleki. Awa anali mafumu mwa ana a Elifazi ku Edomu ndipo onsewa anali zidzukulu za Ada. 17 Mwa ana a Reueli, mwana wa Esau munali mafumu awa:Nahati, Zera, Sama ndi Miza. Awa anali mafumu mwa ana a Reueli ku Edomu. Iwowa anali zidzukulu za Basemati mkazi wa Esau. 18 Mwa ana a Oholibama, mkazi wa Esau munali mafumu awa:Yeusi, Yolamu, ndi Kora. Amenewa anali mafumu mwa ana a mkazi wa Esau, Oholibama, mwana wa Ana. 19 Amenewa ndiwo zidzukulu za Esau (amene ndi Edomu) ndiponso mafumu awo. 20 Awa ndi ana a Seiri Mhori, amene ankakhala mʼdzikomo:Lotani, Sobala, Zibeoni, Ana, 21 Disoni, Ezeri ndi Disani. Amenewa ndiwo ana a Seiri a ku Edomu ndipo analinso mafumu a Ahori. 22 Ana aamuna a Lotani anali awa:Hori ndi Homamu. Timna anali mlongo wake wa Lotani. 23 Ana aamuna a Sobala anali awa:Alivani, Manahati, Ebala, Sefo ndi Onamu. 24 Ana aamuna a Zibeoni anali awa:Ayiwa ndi Ana. Uyu ndi Ana amene anapeza akasupe a madzi amoto mʼchipululu pamene ankadyetsa abulu abambo wake Zibeoni. 25 Ana a Ana anali:Disoni ndi Oholibama mwana wake wamkazi. 26 Ana aamuna a Disoni anali awa:Hemudani, Esibani, Itirani ndi Kerani. 27 Ana aamuna a Ezeri anali awa:Bilihani, Zaavani ndi Akani. 28 Ana aamuna a Disani anali awa:Uzi ndi Arani. 29 Mafumu a Ahori anali awa:Lotani, Sobala, Zibeoni, Ana, 30 Disoni, Ezeri ndi Disani. Amenewa ndiwo mafumu a Ahori, monga mwa mafuko awo, mʼdziko la Seiri. 31 Awa ndi mafumu amene ankalamulira dziko la Edomu, mfumu iliyonse ya Israeli isanayambe kulamulira kumeneko: 32 Bela mwana wa Beori anakhala mfumu ya ku Edomu. Mzinda wake ankawutcha Dinihaba. 33 Bela atamwalira, Yobabu mwana wa Zera wochokera ku Bozira analowa ufumu mʼmalo mwake. 34 Atafa Yobabu, Husamu wochokera ku dziko la Atemani, analowa mʼmalo mwake ngati mfumu. 35 Husamu atamwalira, Hadadi mwana wa Bedadi, amene anagonjetsa Amidiyani mʼdziko la Mowabu, analowa ufumu mʼmalo mwake. Mzinda wake unkatchedwa Aviti. 36 Hadadi atamwalira, Samila wochokera ku Masireka, analowa ufumu mʼmalo mwake. 37 Samila atamwalira, Sauli wochokera ku Rehoboti wa ku Mtsinje, analowa ufumu mʼmalo mwake. 38 Sauli atamwalira, Baala-Hanani, mwana wa Akibori analowa ufumu mʼmalo mwake. 39 Pamene Baala-Hanani mwana wa Akibori anamwalira, Hadari analowa ufumu mʼmalo mwake. Mzinda wake unkatchedwa Pau, ndipo dzina la mkazi wake linali Mehatabeli, mwana wamkazi wa Matiredi, mwana wamkazi wa Me-Zahabu. 40 Mayina a mafumu ochokera mwa zidzukulu za Esau malingana ndi mafuko awo ndi malo a fuko lililonse anali awa:Timna, Aliva, Yeteti, 41 Oholibama, Ela, Pinoni, 42 Kenazi, Temani, Mibezari, 43 Magidieli ndi Iramu. Awa anali mafumu a ku Edomu molingana ndi malo awo okhala mʼdzikomo. Umenewu ndi mndandanda wa mʼbado wa Esau, kholo la Aedomu.