Genesis 39 (BOGWICC)
1 Tsopano Yosefe anatengedwa kupita ku Igupto. Potifara Mwigupto amene anali mmodzi wa akuluakulu a Farao ndiponso mkulu wa asilikali olonda ku nyumba kwa Farao, anagula Yosefe kwa Aismaeli amene anapita naye kumeneko. 2 Koma Yehova anali ndi Yosefe ndipo zake zonse zimayenda bwino. Iye ankakhala mʼnyumba ya mbuye wake wa ku Igupto. 3 Mbuye wake anaona kuti Yehova anali naye Yosefe ndi kuti pa chilichonse chimene anachita Yehova ankaonetsetsa kuti achite bwino. 4 Potifara anakondwera ndi Yosefe chifukwa cha matumikiridwe ake. Choncho anamusandutsa woyangʼanira nyumba yake ndi zonse za mʼnyumba yake. 5 Kuchokera pa nthawi imene anamuyika kukhala woyangʼanira wa nyumbayo ndi zonse za mʼnyumbamo, Yehova anadalitsa nyumba ya Mwiguptoyo chifukwa cha Yosefe. Madalitso a Yehova anali pa chilichonse chimene Potifara anali nacho, za mʼnyumba komanso za ku munda. 6 Choncho anasiyira mʼmanja mwa Yosefe chilichonse chomwe anali nacho, kotero kuti samadandaula ndi chilichonse kupatula chakudya chimene ankadya.Tsopano Yosefe anali wa thupi labwino ndi wokongola. 7 Patapita kanthawi, mkazi wa mbuye wake anayamba kusirira Yosefe nati, “Bwanji ugone nane!” 8 Koma iye anakana namuwuza kuti, “Inu mukuona kuti mbuye wanga sadandaula ndi kena kalikonse mʼnyumba muno, ndipo chawo chilichonse anachiyika mʼmanja mwanga. 9 Motero kuti palibe wina wamkulu kuposa ine mʼnyumba muno. Ndipo palibe chilichonse chimene mbuye wanga sanachipereke kwa ine kupatula inuyo, chifukwa ndinu mkazi wake. Tsono ndingachite bwanji choyipa choterechi ndi kuchimwira Mulungu?” 10 Ndipo ngakhale kuti iye anayankhula mawu omwewa ndi Yosefe tsiku ndi tsiku, Yosefe sanalole kugona naye ngakhale kukhala naye pafupi. 11 Tsiku lina Yosefe analowa mʼnyumbamo kukagwira ntchito zake, ndipo munalibe wina aliyense wantchito mʼnyumbamo. 12 Mkazi uja anamugwira mkanjo Yosefe nati, “Tiye ugone nane!” Koma Yosefe anasiya mkanjo wake mʼmanja mwa mkaziyo nathawira kunja kwa nyumba. 13 Pamene mkazi uja anaona kuti Yosefe wamusiyira mkanjo wake mʼmanja mwake nathawira kunja kwa nyumba, 14 iye anayitana antchito ake a mʼnyumba nati, “Taonani mwamuna wanga anabwera ndi Mhebri uyu mʼnyumba muno kuti adzagone nane. Iyeyu analowa ku chipinda kwanga kuti adzagone nane ndipo ine ndinakuwa kwambiri. 15 Atandimva ndikukuwa, anandisiyira mkanjo wakewu nʼkuthawira kunja.” 16 Tsono mkazi wa Potifara uja anasunga mkanjowo mpaka mbuye wake wa Yosefe atabwera ku nyumba. 17 Tsono anamuwuza nkhaniyi nati: “Wantchito Wachihebri amene munatibweretsera uja anabwera kuti adzagone nane. 18 Koma pamene ndinakuwa, iye anandisiyira mkanjo wake nathawira kunja.” 19 Mbuye wake wa Yosefe atamva nkhani imene mkazi wake anamuwuza kuti, “Ndi zimene anandichitira wantchito wanu,” anapsa mtima kwambiri. 20 Tsono iye anatenga Yosefe namuyika mʼndende mmene ankasungiramo amʼndende a mfumu.Ndipo Yosefe anakhala mʼndendemo 21 koma Yehova anali naye, ndipo anamuonetsa kukoma mtima kwake, kotero kuti woyangʼanira ndende anakondwera ndi Yosefe. 22 Choncho woyangʼanira ndende uja anamuyika Yosefe kukhala woyangʼanira onse amene anayikidwa mʼndende. Ndiponso anamupatsa udindo woyangʼanira zonse zochitika mʼndendemo. 23 Woyangʼanira ndende uja sankayangʼaniranso china chilichonse chimene chinali mu ulamuliro wa Yosefe, chifukwa Yehova anali ndi Yosefe. Ndipo Yehova anaonetsetsa kuti chilichonse chimene Yosefe ankachita chimuyendere bwino.
In Other Versions
Genesis 39 in the ANGEFD
Genesis 39 in the ANTPNG2D
Genesis 39 in the AS21
Genesis 39 in the BAGH
Genesis 39 in the BBPNG
Genesis 39 in the BBT1E
Genesis 39 in the BDS
Genesis 39 in the BEV
Genesis 39 in the BHAD
Genesis 39 in the BIB
Genesis 39 in the BLPT
Genesis 39 in the BNT
Genesis 39 in the BNTABOOT
Genesis 39 in the BNTLV
Genesis 39 in the BOATCB
Genesis 39 in the BOATCB2
Genesis 39 in the BOBCV
Genesis 39 in the BOCNT
Genesis 39 in the BOECS
Genesis 39 in the BOHCB
Genesis 39 in the BOHCV
Genesis 39 in the BOHLNT
Genesis 39 in the BOHNTLTAL
Genesis 39 in the BOICB
Genesis 39 in the BOILNTAP
Genesis 39 in the BOITCV
Genesis 39 in the BOKCV
Genesis 39 in the BOKCV2
Genesis 39 in the BOKHWOG
Genesis 39 in the BOKSSV
Genesis 39 in the BOLCB
Genesis 39 in the BOLCB2
Genesis 39 in the BOMCV
Genesis 39 in the BONAV
Genesis 39 in the BONCB
Genesis 39 in the BONLT
Genesis 39 in the BONUT2
Genesis 39 in the BOPLNT
Genesis 39 in the BOSCB
Genesis 39 in the BOSNC
Genesis 39 in the BOTLNT
Genesis 39 in the BOVCB
Genesis 39 in the BOYCB
Genesis 39 in the BPBB
Genesis 39 in the BPH
Genesis 39 in the BSB
Genesis 39 in the CCB
Genesis 39 in the CUV
Genesis 39 in the CUVS
Genesis 39 in the DBT
Genesis 39 in the DGDNT
Genesis 39 in the DHNT
Genesis 39 in the DNT
Genesis 39 in the ELBE
Genesis 39 in the EMTV
Genesis 39 in the ESV
Genesis 39 in the FBV
Genesis 39 in the FEB
Genesis 39 in the GGMNT
Genesis 39 in the GNT
Genesis 39 in the HARY
Genesis 39 in the HNT
Genesis 39 in the IRVA
Genesis 39 in the IRVB
Genesis 39 in the IRVG
Genesis 39 in the IRVH
Genesis 39 in the IRVK
Genesis 39 in the IRVM
Genesis 39 in the IRVM2
Genesis 39 in the IRVO
Genesis 39 in the IRVP
Genesis 39 in the IRVT
Genesis 39 in the IRVT2
Genesis 39 in the IRVU
Genesis 39 in the ISVN
Genesis 39 in the JSNT
Genesis 39 in the KAPI
Genesis 39 in the KBT1ETNIK
Genesis 39 in the KBV
Genesis 39 in the KJV
Genesis 39 in the KNFD
Genesis 39 in the LBA
Genesis 39 in the LBLA
Genesis 39 in the LNT
Genesis 39 in the LSV
Genesis 39 in the MAAL
Genesis 39 in the MBV
Genesis 39 in the MBV2
Genesis 39 in the MHNT
Genesis 39 in the MKNFD
Genesis 39 in the MNG
Genesis 39 in the MNT
Genesis 39 in the MNT2
Genesis 39 in the MRS1T
Genesis 39 in the NAA
Genesis 39 in the NASB
Genesis 39 in the NBLA
Genesis 39 in the NBS
Genesis 39 in the NBVTP
Genesis 39 in the NET2
Genesis 39 in the NIV11
Genesis 39 in the NNT
Genesis 39 in the NNT2
Genesis 39 in the NNT3
Genesis 39 in the PDDPT
Genesis 39 in the PFNT
Genesis 39 in the RMNT
Genesis 39 in the SBIAS
Genesis 39 in the SBIBS
Genesis 39 in the SBIBS2
Genesis 39 in the SBICS
Genesis 39 in the SBIDS
Genesis 39 in the SBIGS
Genesis 39 in the SBIHS
Genesis 39 in the SBIIS
Genesis 39 in the SBIIS2
Genesis 39 in the SBIIS3
Genesis 39 in the SBIKS
Genesis 39 in the SBIKS2
Genesis 39 in the SBIMS
Genesis 39 in the SBIOS
Genesis 39 in the SBIPS
Genesis 39 in the SBISS
Genesis 39 in the SBITS
Genesis 39 in the SBITS2
Genesis 39 in the SBITS3
Genesis 39 in the SBITS4
Genesis 39 in the SBIUS
Genesis 39 in the SBIVS
Genesis 39 in the SBT
Genesis 39 in the SBT1E
Genesis 39 in the SCHL
Genesis 39 in the SNT
Genesis 39 in the SUSU
Genesis 39 in the SUSU2
Genesis 39 in the SYNO
Genesis 39 in the TBIAOTANT
Genesis 39 in the TBT1E
Genesis 39 in the TBT1E2
Genesis 39 in the TFTIP
Genesis 39 in the TFTU
Genesis 39 in the TGNTATF3T
Genesis 39 in the THAI
Genesis 39 in the TNFD
Genesis 39 in the TNT
Genesis 39 in the TNTIK
Genesis 39 in the TNTIL
Genesis 39 in the TNTIN
Genesis 39 in the TNTIP
Genesis 39 in the TNTIZ
Genesis 39 in the TOMA
Genesis 39 in the TTENT
Genesis 39 in the UBG
Genesis 39 in the UGV
Genesis 39 in the UGV2
Genesis 39 in the UGV3
Genesis 39 in the VBL
Genesis 39 in the VDCC
Genesis 39 in the YALU
Genesis 39 in the YAPE
Genesis 39 in the YBVTP
Genesis 39 in the ZBP