Genesis 40 (BOGWICC)
1 Patapita nthawi, woperekera zakumwa ndi wopanga buledi a ku nyumba kwa mfumu ya ku Igupto analakwira mbuye wawoyo. 2 Farao anapsa mtima ndi akuluakulu awiriwa, 3 ndipo anakawatsekera mʼndende, nakawayika mʼmanja mwa mkulu wa asilikali olonda ku nyumba kwa mfumu kuja, mʼndende momwe Yosefe ankasungidwamo. 4 Mkulu wa alonda aja anawapereka mʼmanja mwa Yosefe, ndipo iye anawasamalira.Iwo anakhala mʼndendemo kwa kanthawi. 5 Usiku wina, aliyense wa anthu awiriwa, wopereka zakumwa pamodzi ndi wopanga buledi wa ku nyumba ya mfumu ya ku Igupto aja, amene ankasungidwa mʼndende, analota maloto. Malotowo anali ndi tanthauzo lake. 6 Mmawa wake, Yosefe atabwera, anaona kuti nkhope zawo zinali zakugwa. 7 Choncho anafunsa akuluakulu a kwa Farao amene anali naye mʼndende muja kuti, “Bwanji nkhope zanu zili zachisoni lero?” 8 Iwo anayankha, “Tonse awiri talota maloto, koma palibe wotitanthauzira malotowo.”Pamenepo Yosefe anawawuza kuti, “Ndi Mulungu yekha amene amapereka matanthauzo a maloto. Uzeni ine maloto anu.” 9 Choncho mkulu wa operekera zakumwa uja anamuwuza Yosefe maloto ake. Anati, “Mʼmaloto anga ndinaona mtengo wa mpesa, 10 unali ndi nthambi zitatu. Mpesawo utangophukira, unachita maluwa ndipo maphava ake anabereka mphesa zakupsa. 11 Chikho cha Farao chinali mʼmanja mwanga, ndipo ndinatenga mphesa, kupsinyira mu chikho cha Farao ndi kuchipereka mʼmanja mwake.” 12 Yosefe anati kwa iye, “Tanthauzo lake ndi ili: Nthambi zitatuzo ndi masiku atatu. 13 Pakangopita masiku atatu, Farao adzakutulutsa muno. Udzaperekera zakumwa kwa Farao monga momwe umachitira poyamba. 14 Koma zako zikakuyendera bwino, udzandikumbukire ndi kundikomera mtima. Chonde ukandipepesere kwa Farao kuti anditulutse muno. 15 Popezatu ine anangochita mondiba kubwera nane kuno kuchokera ku dziko la Ahebri, ndipo ngakhale kunoko, ine sindinalakwe kali konse kuti ndizipezeka mʼdzenje muno.” 16 Mkulu wa opanga buledi ataona kuti Yosefe wapereka tanthauzo labwino, anati kwa Yosefe, “Inenso ndinalota nditasenza nsengwa zitatu za buledi. 17 Mu nsengwa yapamwamba munali zakudya zamitundumitundu za Farao, koma mbalame zimadya zakudyazo.” 18 Yosefe anati, “Tanthauzo lake ndi ili: nsengwa zitatuzo ndi masiku atatu. 19 Pakangotha masiku atatu Farao adzakutulutsa muno koma adzakupachika. Ndipo mbalame zidzadya mnofu wako.” 20 Tsono tsiku lachitatulo linali lokumbukira kubadwa kwa Farao, ndipo anawakonzera phwando akuluakulu ake onse. Anatulutsa mʼndende mkulu wa operekera zakumwa ndi mkulu wa ophika buledi, ndipo anawayimiritsa pamaso pa nduna zake. 21 Tsono Farao anamubwezera mkulu wa operekera zakumwa uja pa udindo wake, kotero kuti anayamba kuperekeranso zakumwa kwa Farao, 22 koma mkulu wa ophika buledi anamupachika, mofanana ndi mmene Yosefe anatanthauzira maloto. 23 Koma mkulu wa operekera zakumwa uja sanamukumbukire Yosefe ndipo anamuyiwaliratu.
In Other Versions
Genesis 40 in the ANGEFD
Genesis 40 in the ANTPNG2D
Genesis 40 in the AS21
Genesis 40 in the BAGH
Genesis 40 in the BBPNG
Genesis 40 in the BBT1E
Genesis 40 in the BDS
Genesis 40 in the BEV
Genesis 40 in the BHAD
Genesis 40 in the BIB
Genesis 40 in the BLPT
Genesis 40 in the BNT
Genesis 40 in the BNTABOOT
Genesis 40 in the BNTLV
Genesis 40 in the BOATCB
Genesis 40 in the BOATCB2
Genesis 40 in the BOBCV
Genesis 40 in the BOCNT
Genesis 40 in the BOECS
Genesis 40 in the BOHCB
Genesis 40 in the BOHCV
Genesis 40 in the BOHLNT
Genesis 40 in the BOHNTLTAL
Genesis 40 in the BOICB
Genesis 40 in the BOILNTAP
Genesis 40 in the BOITCV
Genesis 40 in the BOKCV
Genesis 40 in the BOKCV2
Genesis 40 in the BOKHWOG
Genesis 40 in the BOKSSV
Genesis 40 in the BOLCB
Genesis 40 in the BOLCB2
Genesis 40 in the BOMCV
Genesis 40 in the BONAV
Genesis 40 in the BONCB
Genesis 40 in the BONLT
Genesis 40 in the BONUT2
Genesis 40 in the BOPLNT
Genesis 40 in the BOSCB
Genesis 40 in the BOSNC
Genesis 40 in the BOTLNT
Genesis 40 in the BOVCB
Genesis 40 in the BOYCB
Genesis 40 in the BPBB
Genesis 40 in the BPH
Genesis 40 in the BSB
Genesis 40 in the CCB
Genesis 40 in the CUV
Genesis 40 in the CUVS
Genesis 40 in the DBT
Genesis 40 in the DGDNT
Genesis 40 in the DHNT
Genesis 40 in the DNT
Genesis 40 in the ELBE
Genesis 40 in the EMTV
Genesis 40 in the ESV
Genesis 40 in the FBV
Genesis 40 in the FEB
Genesis 40 in the GGMNT
Genesis 40 in the GNT
Genesis 40 in the HARY
Genesis 40 in the HNT
Genesis 40 in the IRVA
Genesis 40 in the IRVB
Genesis 40 in the IRVG
Genesis 40 in the IRVH
Genesis 40 in the IRVK
Genesis 40 in the IRVM
Genesis 40 in the IRVM2
Genesis 40 in the IRVO
Genesis 40 in the IRVP
Genesis 40 in the IRVT
Genesis 40 in the IRVT2
Genesis 40 in the IRVU
Genesis 40 in the ISVN
Genesis 40 in the JSNT
Genesis 40 in the KAPI
Genesis 40 in the KBT1ETNIK
Genesis 40 in the KBV
Genesis 40 in the KJV
Genesis 40 in the KNFD
Genesis 40 in the LBA
Genesis 40 in the LBLA
Genesis 40 in the LNT
Genesis 40 in the LSV
Genesis 40 in the MAAL
Genesis 40 in the MBV
Genesis 40 in the MBV2
Genesis 40 in the MHNT
Genesis 40 in the MKNFD
Genesis 40 in the MNG
Genesis 40 in the MNT
Genesis 40 in the MNT2
Genesis 40 in the MRS1T
Genesis 40 in the NAA
Genesis 40 in the NASB
Genesis 40 in the NBLA
Genesis 40 in the NBS
Genesis 40 in the NBVTP
Genesis 40 in the NET2
Genesis 40 in the NIV11
Genesis 40 in the NNT
Genesis 40 in the NNT2
Genesis 40 in the NNT3
Genesis 40 in the PDDPT
Genesis 40 in the PFNT
Genesis 40 in the RMNT
Genesis 40 in the SBIAS
Genesis 40 in the SBIBS
Genesis 40 in the SBIBS2
Genesis 40 in the SBICS
Genesis 40 in the SBIDS
Genesis 40 in the SBIGS
Genesis 40 in the SBIHS
Genesis 40 in the SBIIS
Genesis 40 in the SBIIS2
Genesis 40 in the SBIIS3
Genesis 40 in the SBIKS
Genesis 40 in the SBIKS2
Genesis 40 in the SBIMS
Genesis 40 in the SBIOS
Genesis 40 in the SBIPS
Genesis 40 in the SBISS
Genesis 40 in the SBITS
Genesis 40 in the SBITS2
Genesis 40 in the SBITS3
Genesis 40 in the SBITS4
Genesis 40 in the SBIUS
Genesis 40 in the SBIVS
Genesis 40 in the SBT
Genesis 40 in the SBT1E
Genesis 40 in the SCHL
Genesis 40 in the SNT
Genesis 40 in the SUSU
Genesis 40 in the SUSU2
Genesis 40 in the SYNO
Genesis 40 in the TBIAOTANT
Genesis 40 in the TBT1E
Genesis 40 in the TBT1E2
Genesis 40 in the TFTIP
Genesis 40 in the TFTU
Genesis 40 in the TGNTATF3T
Genesis 40 in the THAI
Genesis 40 in the TNFD
Genesis 40 in the TNT
Genesis 40 in the TNTIK
Genesis 40 in the TNTIL
Genesis 40 in the TNTIN
Genesis 40 in the TNTIP
Genesis 40 in the TNTIZ
Genesis 40 in the TOMA
Genesis 40 in the TTENT
Genesis 40 in the UBG
Genesis 40 in the UGV
Genesis 40 in the UGV2
Genesis 40 in the UGV3
Genesis 40 in the VBL
Genesis 40 in the VDCC
Genesis 40 in the YALU
Genesis 40 in the YAPE
Genesis 40 in the YBVTP
Genesis 40 in the ZBP