Genesis 45 (BOGWICC)

1 Tsono Yosefe sanathenso kuwugwira mtima kuti asalire pamaso pa antchito ake ndipo anafuwula kuti, “Aliyense achoke pamaso panga!” Motero panalibe wina aliyense pamene Yosefe anadziwulula kwa abale ake. 2 Ndipo analira mokweza mwakuti Aigupto anamva. Onse a ku nyumba kwa Farao anamvanso za zimenezi. 3 Yosefe anati kwa abale ake, “Ine ndine Yosefe! Kodi abambo anga akanali ndi moyo?” Koma abale ake sanathe kumuyankha chifukwa anali ndi mantha kwambiri pamaso pake. 4 Ndipo Yosefe anati kwa abale ake, “Senderani pafupi nane.” Atasendera iye anati, “Ine ndine mʼbale wanu Yosefe amene munamugulitsa ku Igupto! 5 Ndipo tsopano, musawawidwe mtima kapena kudzipsera mtima chifukwa choti munandigulitsa ine kuno, popeza Mulungu ananditsogoza ine kuti adzapulumutse miyoyo yanu. 6 Kwa zaka ziwiri tsopano, kwakhala kuli njala mʼdziko muno, ndipo kwa zaka zisanu zikubwerazi, anthu sadzalima kapena kukolola. 7 Koma Mulungu ananditsogoza kuti adzakusungeni ndi moyo ndi kuti mudzakhale ndi zidzukulu pa dziko lapansi. 8 “Motero, si inu amene munanditumiza kuno koma Mulungu. Iye anandisandutsa kukhala nduna yayikulu ya Farao, ndipo zonse za mʼnyumba mwake zili mʼmanja mwangamu. Komanso amene akulamulira dziko lonse la Igupto ndi ine. 9 Tsono fulumirani mubwerere kwa abambo anga ndi kuwawuza kuti, ‘Mwana wanu Yosefe akuti, Mulungu anandisandutsa kukhala mbuye wa dziko lonse la Igupto. Ndiye bwerani kuno musachedwe. 10 Ndipo inu, ana anu, zidzukulu zanu, pamodzi ndi nkhosa ndi ngʼombe zanu ndi antchito anu amene muli nawo muzidzakhala mʼdziko la Goseni pafupi ndi ine. 11 Ine ndizidzakupatsani zakudya kumeneko chifukwa zaka zisanu za njala zikubwera ndithu. Kupanda kutero, inu ndi mabanja anu pamodzi ndi anthu anu onse mudzasowa chakudya.’ 12 “Tsono inu nonse pamodzi ndi mʼbale wangayu Benjamini, mukuona kuti ndi inedi amene ndikuyankhula nanu. 13 Mukawawuze abambo anga kuti ndili pa ulemerero ku dziko la Igupto kuno ndi zonse zimene mwaziona. Tsopano fulumirani kuti mukabwere nawo kuno abambo anga.” 14 Kenaka Yosefe anakhumbatira Benjamini, mngʼono wake uja nayamba kulira. Nayenso Benjamini anayamba kulira atamukumbatira. 15 Atatero, Yosefe anapsompsona abale ake onse aja, akulira. Pambuyo pake abale ake aja anacheza ndi Yosefe. 16 Akunyumba kwa Farao atamva kuti abale ake a Yosefe abwera, Farao pamodzi ndi nduna zake zonse anakondwera. 17 Farao anati kwa Yosefe, “Uwawuze abale ako kuti, ‘Senzetsani nyama zanu katundu ndi kubwerera ku dziko la Kanaani. 18 Mukabwere nawo abambo anu ndi mabanja anu kuno, ndipo ine ndidzakupatsani dera lachonde kwambiri mʼdziko la Igupto. Mudzadya zokoma za mʼdzikoli.’ ” 19 “Uwawuzenso kuti, ‘Tengani ngolo zingapo za kuno ku Igupto kuti mukakwezepo ana anu, akazi anu pamodzi ndi abambo ako ndi kubwera nawo kuno. 20 Musadandaule zosiya katundu komweko chifukwa dziko lachonde la kuno ku Igupto lidzakhala lanu.’ ” 21 Choncho ana a Israeli anachita zimenezo. Yosefe anawapatsa ngolo monga Farao analamulira, ndipo anawapatsanso chakudya cha paulendo wawo. 22 Anaperekanso kwa aliyense zovala zatsopano, koma kwa Benjamini anapereka siliva wolemera pafupifupi makilogalamu anayi ndi zovala zisanu. 23 Ndipo abambo ake anawatumizira izi: abulu khumi osenza zinthu zabwino kwambiri za ku Igupto, ndi abulu aakazi khumi osenza tirigu, buledi ndi zakudya zina za pa ulendo wake. 24 Kenaka anawalola abale ake aja kuti azipita, ndipo akunyamuka, iye anawawuza kuti, “Osakangana mʼnjira!” 25 Ndipo anachoka ku Igupto nafika kwa abambo awo Yakobo mʼdziko la Kanaani. 26 Iwo anawuza abambo awo kuti, “Yosefe akanali ndi moyo! Ndiponsotu, ndiye akulamulira dziko la Igupto.” Yakobo anangoti kakasi osankhulupirira. 27 Komabe atamufotokozera zonse zimene Yosefe anawawuza ndipo ataona ngolo zimene Yosefe anatumiza kuti adzakweremo popita ku Igupto, mtima wa Yakobo, abambo awo unatsitsimuka. 28 Ndipo Israeli anati, “Ndatsimikizadi! Mwana wanga Yosefe akanali ndi moyodi. Ndipita ndikamuone ndisanafe.”

In Other Versions

Genesis 45 in the ANGEFD

Genesis 45 in the ANTPNG2D

Genesis 45 in the AS21

Genesis 45 in the BAGH

Genesis 45 in the BBPNG

Genesis 45 in the BBT1E

Genesis 45 in the BDS

Genesis 45 in the BEV

Genesis 45 in the BHAD

Genesis 45 in the BIB

Genesis 45 in the BLPT

Genesis 45 in the BNT

Genesis 45 in the BNTABOOT

Genesis 45 in the BNTLV

Genesis 45 in the BOATCB

Genesis 45 in the BOATCB2

Genesis 45 in the BOBCV

Genesis 45 in the BOCNT

Genesis 45 in the BOECS

Genesis 45 in the BOHCB

Genesis 45 in the BOHCV

Genesis 45 in the BOHLNT

Genesis 45 in the BOHNTLTAL

Genesis 45 in the BOICB

Genesis 45 in the BOILNTAP

Genesis 45 in the BOITCV

Genesis 45 in the BOKCV

Genesis 45 in the BOKCV2

Genesis 45 in the BOKHWOG

Genesis 45 in the BOKSSV

Genesis 45 in the BOLCB

Genesis 45 in the BOLCB2

Genesis 45 in the BOMCV

Genesis 45 in the BONAV

Genesis 45 in the BONCB

Genesis 45 in the BONLT

Genesis 45 in the BONUT2

Genesis 45 in the BOPLNT

Genesis 45 in the BOSCB

Genesis 45 in the BOSNC

Genesis 45 in the BOTLNT

Genesis 45 in the BOVCB

Genesis 45 in the BOYCB

Genesis 45 in the BPBB

Genesis 45 in the BPH

Genesis 45 in the BSB

Genesis 45 in the CCB

Genesis 45 in the CUV

Genesis 45 in the CUVS

Genesis 45 in the DBT

Genesis 45 in the DGDNT

Genesis 45 in the DHNT

Genesis 45 in the DNT

Genesis 45 in the ELBE

Genesis 45 in the EMTV

Genesis 45 in the ESV

Genesis 45 in the FBV

Genesis 45 in the FEB

Genesis 45 in the GGMNT

Genesis 45 in the GNT

Genesis 45 in the HARY

Genesis 45 in the HNT

Genesis 45 in the IRVA

Genesis 45 in the IRVB

Genesis 45 in the IRVG

Genesis 45 in the IRVH

Genesis 45 in the IRVK

Genesis 45 in the IRVM

Genesis 45 in the IRVM2

Genesis 45 in the IRVO

Genesis 45 in the IRVP

Genesis 45 in the IRVT

Genesis 45 in the IRVT2

Genesis 45 in the IRVU

Genesis 45 in the ISVN

Genesis 45 in the JSNT

Genesis 45 in the KAPI

Genesis 45 in the KBT1ETNIK

Genesis 45 in the KBV

Genesis 45 in the KJV

Genesis 45 in the KNFD

Genesis 45 in the LBA

Genesis 45 in the LBLA

Genesis 45 in the LNT

Genesis 45 in the LSV

Genesis 45 in the MAAL

Genesis 45 in the MBV

Genesis 45 in the MBV2

Genesis 45 in the MHNT

Genesis 45 in the MKNFD

Genesis 45 in the MNG

Genesis 45 in the MNT

Genesis 45 in the MNT2

Genesis 45 in the MRS1T

Genesis 45 in the NAA

Genesis 45 in the NASB

Genesis 45 in the NBLA

Genesis 45 in the NBS

Genesis 45 in the NBVTP

Genesis 45 in the NET2

Genesis 45 in the NIV11

Genesis 45 in the NNT

Genesis 45 in the NNT2

Genesis 45 in the NNT3

Genesis 45 in the PDDPT

Genesis 45 in the PFNT

Genesis 45 in the RMNT

Genesis 45 in the SBIAS

Genesis 45 in the SBIBS

Genesis 45 in the SBIBS2

Genesis 45 in the SBICS

Genesis 45 in the SBIDS

Genesis 45 in the SBIGS

Genesis 45 in the SBIHS

Genesis 45 in the SBIIS

Genesis 45 in the SBIIS2

Genesis 45 in the SBIIS3

Genesis 45 in the SBIKS

Genesis 45 in the SBIKS2

Genesis 45 in the SBIMS

Genesis 45 in the SBIOS

Genesis 45 in the SBIPS

Genesis 45 in the SBISS

Genesis 45 in the SBITS

Genesis 45 in the SBITS2

Genesis 45 in the SBITS3

Genesis 45 in the SBITS4

Genesis 45 in the SBIUS

Genesis 45 in the SBIVS

Genesis 45 in the SBT

Genesis 45 in the SBT1E

Genesis 45 in the SCHL

Genesis 45 in the SNT

Genesis 45 in the SUSU

Genesis 45 in the SUSU2

Genesis 45 in the SYNO

Genesis 45 in the TBIAOTANT

Genesis 45 in the TBT1E

Genesis 45 in the TBT1E2

Genesis 45 in the TFTIP

Genesis 45 in the TFTU

Genesis 45 in the TGNTATF3T

Genesis 45 in the THAI

Genesis 45 in the TNFD

Genesis 45 in the TNT

Genesis 45 in the TNTIK

Genesis 45 in the TNTIL

Genesis 45 in the TNTIN

Genesis 45 in the TNTIP

Genesis 45 in the TNTIZ

Genesis 45 in the TOMA

Genesis 45 in the TTENT

Genesis 45 in the UBG

Genesis 45 in the UGV

Genesis 45 in the UGV2

Genesis 45 in the UGV3

Genesis 45 in the VBL

Genesis 45 in the VDCC

Genesis 45 in the YALU

Genesis 45 in the YAPE

Genesis 45 in the YBVTP

Genesis 45 in the ZBP