Haggai 2 (BOGWICC)

1 Pa tsiku la 21 la mwezi wachisanu ndi chiwiri, Yehova anayankhula kudzera mwa mneneri Hagai kuti: 2 “Yankhula kwa Zerubabeli mwana wa Sealatieli, bwanamkubwa wa Yuda, kwa Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, ndi kwa anthu onse otsala. Afunse kuti, 3 ‘Kodi alipo amene watsala pakati panu amene anaona ulemerero wakale wa Nyumba iyi? Nanga tsopano ikuoneka motani kwa inu? Kodi sikuoneka ngati yopanda pake kwa inu? 4 Iwe Zerubabeli, limba mtima tsopano,’ akutero Yehova. ‘Limba mtima, iwe Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe. Limbani mtima, anthu nonse a mʼdziko,’ akutero Yehova, ‘ndipo gwirani ntchito. Pakuti ine ndili nanu,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse. 5 ‘Izi ndi zimene ndinapangana nanu pamene munkatuluka ku Igupto. Ndipo Mzimu wanga uli pakati panu. Musachite mantha.’ 6 “Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Pakapita nthawi pangʼono ndidzagwedezanso thambo ndi dziko lapansi, nyanja ndi mtunda. 7 Ndidzagwedeza mitundu yonse ya anthu, ndipo chimene mitundu yonse ya anthu imachifuna chidzabwera, ndipo ndidzaza Nyumba ino ndi ulemerero,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse. 8 ‘Siliva yense ndi wanga, golide yense ndi wanganso,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse. 9 ‘Ulemerero wa nyumba iyi udzaposa ulemerero wa nyumba yoyamba ija,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse. ‘Ndipo pamalo pano ndidzakhazikitsapo mtendere,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse.” 10 Chaka chachiwiri cha Dariyo, pa tsiku la 24 la mwezi wachisanu ndi chinayi, Yehova anayankhula ndi mneneri Hagai kuti: 11 “Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Funsa ansembe za zimene lamulo likunena: 12 Ngati munthu wakulunga nyama yopatulika mu mkanjo wake, ndipo mkanjowo nʼkukhudza buledi kapena msuzi, kapena vinyo, mafuta kapena chakudya cha mtundu wina uliwonse, kodi zimenezo zimasanduka zopatulika?’ ”Ansembe anayankha kuti, “Ayi.” 13 Pamenepo Hagai anati, “Ngati munthu amene anayipitsidwa pokhudza mtembo akhudza chimodzi cha zinthu zimenezi, kodi chinthucho chimayipitsidwa?”Ansembe anayankha kuti, “Inde, chimayipitsidwa.” 14 Pamenepo Hagai anati, “ ‘Ndi mmene zilili ndi anthu awa ndi dziko ili pamaso panga,’ akutero Yehova. ‘Chilichonse amachita ndiponso chilichonse chimene amapereka nʼchodetsedwa. 15 “ ‘Tsopano muganizire zimenezi kuyambira lero mpaka mʼtsogolo. Ganizirani momwe zinthu zinalili asanayambe kumanga nyumba ya Yehova. 16 Pamene munthu ankayembekezera miyeso ya tirigu makumi awiri ankangopeza khumi yokha. Munthu akapita kuti akatunge miyeso makumi asanu ya vinyo mu mtsuko, ankangopeza miyeso makumi awiri yokha. 17 Ndinawononga ntchito yonse ya manja anu ndi chinsikwi, chiwawu ndi matalala, komabe inu simunatembenukire kwa Ine,’ akutero Yehova 18 ‘Kuyambira lero tsiku la 24 la mwezi wachisanu ndi chinayi mpaka mʼtsogolo, chonde ganizirani bwino tsiku limene munayika maziko a nyumba ya Yehova. Ganizirani bwino. 19 Kodi mʼnkhokwe mwatsala mbewu? Mpaka lero, mpesa ndi mtengo wa mkuyu, makangadza ndi mtengo wa olivi sizinabereke zipatso.“ ‘Kuyambira lero mpaka mʼtsogolo ndidzakudalitsani.’ ” 20 Yehova anayankhula ndi Hagai kachiwiri, pa tsiku la 24 la mwezi kuti: 21 “Uza Zerubabeli, bwanamkubwa wa Yuda, kuti ndidzagwedeza thambo ndi dziko lapansi. 22 Ndidzagwetsa mipando yaufumu ndi kuwononga mphamvu za maufumu achilendo. Ndidzagubuduza magaleta ndi okwerapo ake; akavalo ndi okwerapo ake adzagwa, aliyense adzaphedwa ndi lupanga la mʼbale wake. 23 “ ‘Tsiku limenelo,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse, ‘ndidzakutenga, iwe mtumiki wanga Zerubabeli mwana wa Sealatieli,’ akutero Yehova, ‘ndipo ndidzakusandutsa kukhala mphete yanga yolamulira, pakuti ndasankha iwe,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse.”

In Other Versions

Haggai 2 in the ANGEFD

Haggai 2 in the ANTPNG2D

Haggai 2 in the AS21

Haggai 2 in the BAGH

Haggai 2 in the BBPNG

Haggai 2 in the BBT1E

Haggai 2 in the BDS

Haggai 2 in the BEV

Haggai 2 in the BHAD

Haggai 2 in the BIB

Haggai 2 in the BLPT

Haggai 2 in the BNT

Haggai 2 in the BNTABOOT

Haggai 2 in the BNTLV

Haggai 2 in the BOATCB

Haggai 2 in the BOATCB2

Haggai 2 in the BOBCV

Haggai 2 in the BOCNT

Haggai 2 in the BOECS

Haggai 2 in the BOHCB

Haggai 2 in the BOHCV

Haggai 2 in the BOHLNT

Haggai 2 in the BOHNTLTAL

Haggai 2 in the BOICB

Haggai 2 in the BOILNTAP

Haggai 2 in the BOITCV

Haggai 2 in the BOKCV

Haggai 2 in the BOKCV2

Haggai 2 in the BOKHWOG

Haggai 2 in the BOKSSV

Haggai 2 in the BOLCB

Haggai 2 in the BOLCB2

Haggai 2 in the BOMCV

Haggai 2 in the BONAV

Haggai 2 in the BONCB

Haggai 2 in the BONLT

Haggai 2 in the BONUT2

Haggai 2 in the BOPLNT

Haggai 2 in the BOSCB

Haggai 2 in the BOSNC

Haggai 2 in the BOTLNT

Haggai 2 in the BOVCB

Haggai 2 in the BOYCB

Haggai 2 in the BPBB

Haggai 2 in the BPH

Haggai 2 in the BSB

Haggai 2 in the CCB

Haggai 2 in the CUV

Haggai 2 in the CUVS

Haggai 2 in the DBT

Haggai 2 in the DGDNT

Haggai 2 in the DHNT

Haggai 2 in the DNT

Haggai 2 in the ELBE

Haggai 2 in the EMTV

Haggai 2 in the ESV

Haggai 2 in the FBV

Haggai 2 in the FEB

Haggai 2 in the GGMNT

Haggai 2 in the GNT

Haggai 2 in the HARY

Haggai 2 in the HNT

Haggai 2 in the IRVA

Haggai 2 in the IRVB

Haggai 2 in the IRVG

Haggai 2 in the IRVH

Haggai 2 in the IRVK

Haggai 2 in the IRVM

Haggai 2 in the IRVM2

Haggai 2 in the IRVO

Haggai 2 in the IRVP

Haggai 2 in the IRVT

Haggai 2 in the IRVT2

Haggai 2 in the IRVU

Haggai 2 in the ISVN

Haggai 2 in the JSNT

Haggai 2 in the KAPI

Haggai 2 in the KBT1ETNIK

Haggai 2 in the KBV

Haggai 2 in the KJV

Haggai 2 in the KNFD

Haggai 2 in the LBA

Haggai 2 in the LBLA

Haggai 2 in the LNT

Haggai 2 in the LSV

Haggai 2 in the MAAL

Haggai 2 in the MBV

Haggai 2 in the MBV2

Haggai 2 in the MHNT

Haggai 2 in the MKNFD

Haggai 2 in the MNG

Haggai 2 in the MNT

Haggai 2 in the MNT2

Haggai 2 in the MRS1T

Haggai 2 in the NAA

Haggai 2 in the NASB

Haggai 2 in the NBLA

Haggai 2 in the NBS

Haggai 2 in the NBVTP

Haggai 2 in the NET2

Haggai 2 in the NIV11

Haggai 2 in the NNT

Haggai 2 in the NNT2

Haggai 2 in the NNT3

Haggai 2 in the PDDPT

Haggai 2 in the PFNT

Haggai 2 in the RMNT

Haggai 2 in the SBIAS

Haggai 2 in the SBIBS

Haggai 2 in the SBIBS2

Haggai 2 in the SBICS

Haggai 2 in the SBIDS

Haggai 2 in the SBIGS

Haggai 2 in the SBIHS

Haggai 2 in the SBIIS

Haggai 2 in the SBIIS2

Haggai 2 in the SBIIS3

Haggai 2 in the SBIKS

Haggai 2 in the SBIKS2

Haggai 2 in the SBIMS

Haggai 2 in the SBIOS

Haggai 2 in the SBIPS

Haggai 2 in the SBISS

Haggai 2 in the SBITS

Haggai 2 in the SBITS2

Haggai 2 in the SBITS3

Haggai 2 in the SBITS4

Haggai 2 in the SBIUS

Haggai 2 in the SBIVS

Haggai 2 in the SBT

Haggai 2 in the SBT1E

Haggai 2 in the SCHL

Haggai 2 in the SNT

Haggai 2 in the SUSU

Haggai 2 in the SUSU2

Haggai 2 in the SYNO

Haggai 2 in the TBIAOTANT

Haggai 2 in the TBT1E

Haggai 2 in the TBT1E2

Haggai 2 in the TFTIP

Haggai 2 in the TFTU

Haggai 2 in the TGNTATF3T

Haggai 2 in the THAI

Haggai 2 in the TNFD

Haggai 2 in the TNT

Haggai 2 in the TNTIK

Haggai 2 in the TNTIL

Haggai 2 in the TNTIN

Haggai 2 in the TNTIP

Haggai 2 in the TNTIZ

Haggai 2 in the TOMA

Haggai 2 in the TTENT

Haggai 2 in the UBG

Haggai 2 in the UGV

Haggai 2 in the UGV2

Haggai 2 in the UGV3

Haggai 2 in the VBL

Haggai 2 in the VDCC

Haggai 2 in the YALU

Haggai 2 in the YAPE

Haggai 2 in the YBVTP

Haggai 2 in the ZBP