Judges 15 (BOGWICC)
1 Patapita nthawi, mu nyengo yodula tirigu, Samsoni anatenga kamwana kambuzi ndipo anapita kukacheza kwa mkazi wake. Iye anati, “Ndikufuna kukalowa ku chipinda cha mkazi wanga.” Koma abambo a mkaziyo anamuletsa kutero. 2 Abambo a mkaziyo anati, “Ine ndimaganiza kuti umamuda kwambiri nʼchifukwa chake ndinamupereka kwa mnzako. Kodi mngʼono wake uja sindiye wokongola kupambana iye? Ingotengani ameneyo mʼmalo mwake.” 3 Samsoni anawawuza kuti, “Pano sindikhala wochimwa ndikawachita choyipa chachikulu Afilistiwa.” 4 Choncho Samsoni anapita nakagwira nkhandwe 300 nazimangirira michira ziwiriziwiri ndipo pa fundo iliyonse ya michirayo anamangirira nsakali. 5 Anayatsa nsakalizo kenaka ndi kuzitayira nkhandwe zija mʼminda ya tirigu ya Afilisti, ndipo zinatentha milu ya tirigu, ndi wosadula yemwe pamodzi ndi mitengo ya mpesa ndi ya olivi. 6 Tsono Afilisti anayamba kufunsana kuti, “Ndani wachita izi?” Ena anati, “Ndi Samsoni mkamwini wa munthu wa ku Timna uja chifukwa Mtimunayo anatenga mkazi wake ndi kumupereka kwa mnzake.”Choncho Afilisti anapita kukatentha mtsikanayo pamodzi ndi abambo ake. 7 Samsoni anawawuza kuti, “Ngati mumachita zangati zimenezi, ndiye ine sindileka mpaka nditakulipsirani.” 8 Choncho Samsoni anamenyana nawo koopsa ndipo anapha ambiri a iwo. Kenaka anakalowa mʼphanga la Etamu, nakhala momwemo. 9 Pambuyo pake Afilisti anakamanga misasa ya nkhondo mʼdziko la Yuda, ndi kuthira nkhondo mʼdera la Lehi. 10 Anthu a fuko la Yuda anafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani mwabwera kudzamenyana nafe?”Iwo anayankha kuti, “Tabwera kudzamanga Samsoni ndi kuti timuchite zofanana ndi zimene anatichita.” 11 Ndipo anthu 3,000 a ku Yuda anapita ku phanga la Etamu, ndi kukamufunsa Samsoni kuti, “Kodi iwe sudziwa kuti ife amatilamulira ndi Afilisti? Tsono ndi chiyani chimene watichitachi?”Iye anayankha kuti, “Ine ndinachita zomwe iwo anandichita.” 12 Iwo anati kwa iye, “Ife tabwera kuti tikumange ndi kukupereka kwa Afilisti.”Ndipo Samsoni anati, “Lonjezani mwa lumbiro kuti simundipha ndinu.” 13 Iwo anamuyankha kuti, “Ayi, ife sitikupha. Koma tingokumanga ndi kukupereka mʼmanja mwa Afilisti.” Choncho anamumanga ndi zingwe ziwiri zatsopano namutulutsa mʼphanga muja. 14 Samsoni anafika ku Lehi, ndipo Afilisti anamuchingamira akufuwula. Nthawi yomweyo Mzimu wa Yehova unatsika pa iye mwamphamvu ndipo zingwe zimene anamumanga nazo zinasanduka ngati thonje lopsa mʼmoto, zinachita ngati zasungunuka nʼkuchoka mʼmanja mwake. 15 Anapeza chibwano cha bulu amene anali atangofa kumene. Anachitola ndi kuphera nacho anthu 1,000. 16 Ndipo Samsoni anati,“Ndi chibwano cha bulu,milu ndi milu ya anthu.Ndi chibwano cha bulu,ndapha anthu 1,000.” 17 Atatsiriza kuyankhula, anataya chibwanocho, ndipo malowo anawatcha Ramati-Lehi. 18 Pambuyo pake anamva ludzu kwambiri ndipo anayitana Yehova mopempha kuti, “Inu mwapatsa mtumiki wanu chipulumutso chachikulu chotere. Kodi tsopano ndife ndi ludzu ndi kugwidwa ndi anthu osachita mdulidwewa?” 19 Pamenepo Mulungu anangʼamba nthaka ku Lehi, ndipo madzi anatuluka mʼdzenjemo. Samsoni anamwa madziwo, ndipo mphamvu zake zinabwerera nakhalanso monga analili. Choncho chitsimecho chinatchedwa Eni-Hakore, ndipo chilipobe ku Lehiko mpaka lero. 20 Samsoni anatsogolera Israeli pa nthawi ya Afilisti kwa zaka makumi awiri.
In Other Versions
Judges 15 in the ANGEFD
Judges 15 in the ANTPNG2D
Judges 15 in the AS21
Judges 15 in the BAGH
Judges 15 in the BBPNG
Judges 15 in the BBT1E
Judges 15 in the BDS
Judges 15 in the BEV
Judges 15 in the BHAD
Judges 15 in the BIB
Judges 15 in the BLPT
Judges 15 in the BNT
Judges 15 in the BNTABOOT
Judges 15 in the BNTLV
Judges 15 in the BOATCB
Judges 15 in the BOATCB2
Judges 15 in the BOBCV
Judges 15 in the BOCNT
Judges 15 in the BOECS
Judges 15 in the BOHCB
Judges 15 in the BOHCV
Judges 15 in the BOHLNT
Judges 15 in the BOHNTLTAL
Judges 15 in the BOICB
Judges 15 in the BOILNTAP
Judges 15 in the BOITCV
Judges 15 in the BOKCV
Judges 15 in the BOKCV2
Judges 15 in the BOKHWOG
Judges 15 in the BOKSSV
Judges 15 in the BOLCB
Judges 15 in the BOLCB2
Judges 15 in the BOMCV
Judges 15 in the BONAV
Judges 15 in the BONCB
Judges 15 in the BONLT
Judges 15 in the BONUT2
Judges 15 in the BOPLNT
Judges 15 in the BOSCB
Judges 15 in the BOSNC
Judges 15 in the BOTLNT
Judges 15 in the BOVCB
Judges 15 in the BOYCB
Judges 15 in the BPBB
Judges 15 in the BPH
Judges 15 in the BSB
Judges 15 in the CCB
Judges 15 in the CUV
Judges 15 in the CUVS
Judges 15 in the DBT
Judges 15 in the DGDNT
Judges 15 in the DHNT
Judges 15 in the DNT
Judges 15 in the ELBE
Judges 15 in the EMTV
Judges 15 in the ESV
Judges 15 in the FBV
Judges 15 in the FEB
Judges 15 in the GGMNT
Judges 15 in the GNT
Judges 15 in the HARY
Judges 15 in the HNT
Judges 15 in the IRVA
Judges 15 in the IRVB
Judges 15 in the IRVG
Judges 15 in the IRVH
Judges 15 in the IRVK
Judges 15 in the IRVM
Judges 15 in the IRVM2
Judges 15 in the IRVO
Judges 15 in the IRVP
Judges 15 in the IRVT
Judges 15 in the IRVT2
Judges 15 in the IRVU
Judges 15 in the ISVN
Judges 15 in the JSNT
Judges 15 in the KAPI
Judges 15 in the KBT1ETNIK
Judges 15 in the KBV
Judges 15 in the KJV
Judges 15 in the KNFD
Judges 15 in the LBA
Judges 15 in the LBLA
Judges 15 in the LNT
Judges 15 in the LSV
Judges 15 in the MAAL
Judges 15 in the MBV
Judges 15 in the MBV2
Judges 15 in the MHNT
Judges 15 in the MKNFD
Judges 15 in the MNG
Judges 15 in the MNT
Judges 15 in the MNT2
Judges 15 in the MRS1T
Judges 15 in the NAA
Judges 15 in the NASB
Judges 15 in the NBLA
Judges 15 in the NBS
Judges 15 in the NBVTP
Judges 15 in the NET2
Judges 15 in the NIV11
Judges 15 in the NNT
Judges 15 in the NNT2
Judges 15 in the NNT3
Judges 15 in the PDDPT
Judges 15 in the PFNT
Judges 15 in the RMNT
Judges 15 in the SBIAS
Judges 15 in the SBIBS
Judges 15 in the SBIBS2
Judges 15 in the SBICS
Judges 15 in the SBIDS
Judges 15 in the SBIGS
Judges 15 in the SBIHS
Judges 15 in the SBIIS
Judges 15 in the SBIIS2
Judges 15 in the SBIIS3
Judges 15 in the SBIKS
Judges 15 in the SBIKS2
Judges 15 in the SBIMS
Judges 15 in the SBIOS
Judges 15 in the SBIPS
Judges 15 in the SBISS
Judges 15 in the SBITS
Judges 15 in the SBITS2
Judges 15 in the SBITS3
Judges 15 in the SBITS4
Judges 15 in the SBIUS
Judges 15 in the SBIVS
Judges 15 in the SBT
Judges 15 in the SBT1E
Judges 15 in the SCHL
Judges 15 in the SNT
Judges 15 in the SUSU
Judges 15 in the SUSU2
Judges 15 in the SYNO
Judges 15 in the TBIAOTANT
Judges 15 in the TBT1E
Judges 15 in the TBT1E2
Judges 15 in the TFTIP
Judges 15 in the TFTU
Judges 15 in the TGNTATF3T
Judges 15 in the THAI
Judges 15 in the TNFD
Judges 15 in the TNT
Judges 15 in the TNTIK
Judges 15 in the TNTIL
Judges 15 in the TNTIN
Judges 15 in the TNTIP
Judges 15 in the TNTIZ
Judges 15 in the TOMA
Judges 15 in the TTENT
Judges 15 in the UBG
Judges 15 in the UGV
Judges 15 in the UGV2
Judges 15 in the UGV3
Judges 15 in the VBL
Judges 15 in the VDCC
Judges 15 in the YALU
Judges 15 in the YAPE
Judges 15 in the YBVTP
Judges 15 in the ZBP