Jeremiah 18 (BOGWICC)
1 Yehova anawuza Yeremiya kuti, 2 “Pita ku nyumba ya munthu wowumba mbiya, ndipo kumeneko ndikakuwuza mawu anga.” 3 Choncho ndinatsikira ku nyumba ya wowumba mbiya, ndipo ndinamuona akuwumba mbiya pa mkombero. 4 Tsono amati ngati mbiya imene waumba ikhala yosawumbika bwino ankayiphwanya nʼkuwumbanso ina monga mmene afunira ndi dothi lake lomwe lija. 5 Kenaka Yehova anandiwuza kuti, 6 “Inu Aisraeli, kodi Ine sindingathe kuchita nanu monga amachitira wowumba mbiya?” akutero Yehova. “Inu muli mʼmanja mwanga ngati mtapo mʼmanja mwa wowumba mbiya. 7 Ngati nditalengeza kuti mtundu wina wa anthu kapena ufumu wina ndiwuzula, kuwugwetsa ndi kuwuwononga, 8 ndipo ngati mtundu wa anthu umene ndawuchenjezawo ulapa zoyipa zawo, ndiye kuti Ine ndidzaleka ndipo sindidzabweretsa pa anthuwo mavuto amene ndinakonzekera kuwachitira. 9 Ndipo ngati ndilengeza kuti ndikufuna kumanga ndi kukhazikitsa mtundu wa anthu kapena ufumu. 10 Koma mtunduwo ukachita choyipa pamaso panga nʼkusandimvera, ndiye kuti sindidzawuchitiranso zabwino zimene ndimafuna ndiwuchitire. 11 “Ndipo tsopano kawawuze anthu a ku Yuda ndi amene akukhala mu Yerusalemu kuti, ‘Yehova akuti, Taonani! Ndikukukonzerani mavuto, ndi kuganizira zoti ndikulangeni. Kotero siyani makhalidwe anu oyipa aliyense wa inu, ndipo mukonzenso makhalidwe anu ndi zochita zanu.’ 12 Koma iwo adzayankha kuti, ‘Zimenezo nʼzosathandiza. Ife tidzapitiriza kuchita zomwe takonzekera; aliyense wa ife adzatsatira zoyipa za mtima wake wokanika.’ ” 13 Yehova akuti,“Uwafunse anthu a mitundu ina kuti:Kodi ndani anamvapo zinthu zofanana ndi zimenezi?Israeli amene anali ngati namwali wanga wachitachinthu choopsa kwambiri. 14 Kodi chisanu chimatha pa matanthweotsetsereka a phiri la Lebanoni?Kodi madzi ozizira amitsinje ochokeraku phiri la Lebanoni adzamphwa? 15 Komatu anthu anga andiyiwala;akufukiza lubani kwa mafano achabechabe.Amapunthwa mʼnjirazawo zakale.Amayenda mʼnjira zachidulendi kusiya njira zabwino. 16 Dziko lawo amalisandutsa chipululu,chinthu chochititsa manyazi nthawi zonse;onse odutsapo adzadabwa kwambirindipo adzapukusa mitu yawo. 17 Ngati mphepo yochokera kummawa,ndidzawabalalitsa pamaso pa adani awo;ndidzawafulatira osawathandizapa tsiku la mavuto awo.” 18 Anthuwo anati, “Tiyeni, tipangane zoti timuchitire Yeremiya; pakuti ansembe otiphunzitsa malamulo tidzakhala nawobe. Anthu anzeru otilangiza tidzakhala nawo, ndiponso aneneri otilalikira mawu. Choncho tiyeni timupezere chifukwa ndipo tisamvere chilichonse chimene akunena.” 19 Ndipo ndinapemphera kwa Yehova kuti, “Inu Yehova, ndimvereni;imvani zimene adani anga akunena za ine! 20 Kodi chinthu choyipa nʼkukhala dipo la chinthu chabwino?Komabe iwo andikumbira dzenje.Kumbukirani kuti ndinadzayima pamaso panukudzawapemphererakuti muwachotsere mkwiyo wanu. 21 Choncho langani ana awo ndi njala;aperekeni kuti aphedwe ndi lupanga.Akazi awo asanduke opanda ana ndi amasiye;amuna awo aphedwe ndi mliri,anyamata awo aphedwe ndi lupanga ku nkhondo. 22 Kulira kumveke kuchokera mʼnyumba zawomutawatumizira gulu lankhondo mwadzidzidzi kuti liwakanthe.Iwo andikumbira dzenje kuti ndigweremondipo atchera msampha mapazi anga. 23 Koma Inu Yehova, mukudziwaziwembu zawo zonse zofuna kundipha.Musawakhululukire zolakwa zawokapena kufafaniza machimo awo pamaso panu.Agonjetsedwe pamaso panu;muwalange muli wokwiya.”
In Other Versions
Jeremiah 18 in the ANGEFD
Jeremiah 18 in the ANTPNG2D
Jeremiah 18 in the AS21
Jeremiah 18 in the BAGH
Jeremiah 18 in the BBPNG
Jeremiah 18 in the BBT1E
Jeremiah 18 in the BDS
Jeremiah 18 in the BEV
Jeremiah 18 in the BHAD
Jeremiah 18 in the BIB
Jeremiah 18 in the BLPT
Jeremiah 18 in the BNT
Jeremiah 18 in the BNTABOOT
Jeremiah 18 in the BNTLV
Jeremiah 18 in the BOATCB
Jeremiah 18 in the BOATCB2
Jeremiah 18 in the BOBCV
Jeremiah 18 in the BOCNT
Jeremiah 18 in the BOECS
Jeremiah 18 in the BOHCB
Jeremiah 18 in the BOHCV
Jeremiah 18 in the BOHLNT
Jeremiah 18 in the BOHNTLTAL
Jeremiah 18 in the BOICB
Jeremiah 18 in the BOILNTAP
Jeremiah 18 in the BOITCV
Jeremiah 18 in the BOKCV
Jeremiah 18 in the BOKCV2
Jeremiah 18 in the BOKHWOG
Jeremiah 18 in the BOKSSV
Jeremiah 18 in the BOLCB
Jeremiah 18 in the BOLCB2
Jeremiah 18 in the BOMCV
Jeremiah 18 in the BONAV
Jeremiah 18 in the BONCB
Jeremiah 18 in the BONLT
Jeremiah 18 in the BONUT2
Jeremiah 18 in the BOPLNT
Jeremiah 18 in the BOSCB
Jeremiah 18 in the BOSNC
Jeremiah 18 in the BOTLNT
Jeremiah 18 in the BOVCB
Jeremiah 18 in the BOYCB
Jeremiah 18 in the BPBB
Jeremiah 18 in the BPH
Jeremiah 18 in the BSB
Jeremiah 18 in the CCB
Jeremiah 18 in the CUV
Jeremiah 18 in the CUVS
Jeremiah 18 in the DBT
Jeremiah 18 in the DGDNT
Jeremiah 18 in the DHNT
Jeremiah 18 in the DNT
Jeremiah 18 in the ELBE
Jeremiah 18 in the EMTV
Jeremiah 18 in the ESV
Jeremiah 18 in the FBV
Jeremiah 18 in the FEB
Jeremiah 18 in the GGMNT
Jeremiah 18 in the GNT
Jeremiah 18 in the HARY
Jeremiah 18 in the HNT
Jeremiah 18 in the IRVA
Jeremiah 18 in the IRVB
Jeremiah 18 in the IRVG
Jeremiah 18 in the IRVH
Jeremiah 18 in the IRVK
Jeremiah 18 in the IRVM
Jeremiah 18 in the IRVM2
Jeremiah 18 in the IRVO
Jeremiah 18 in the IRVP
Jeremiah 18 in the IRVT
Jeremiah 18 in the IRVT2
Jeremiah 18 in the IRVU
Jeremiah 18 in the ISVN
Jeremiah 18 in the JSNT
Jeremiah 18 in the KAPI
Jeremiah 18 in the KBT1ETNIK
Jeremiah 18 in the KBV
Jeremiah 18 in the KJV
Jeremiah 18 in the KNFD
Jeremiah 18 in the LBA
Jeremiah 18 in the LBLA
Jeremiah 18 in the LNT
Jeremiah 18 in the LSV
Jeremiah 18 in the MAAL
Jeremiah 18 in the MBV
Jeremiah 18 in the MBV2
Jeremiah 18 in the MHNT
Jeremiah 18 in the MKNFD
Jeremiah 18 in the MNG
Jeremiah 18 in the MNT
Jeremiah 18 in the MNT2
Jeremiah 18 in the MRS1T
Jeremiah 18 in the NAA
Jeremiah 18 in the NASB
Jeremiah 18 in the NBLA
Jeremiah 18 in the NBS
Jeremiah 18 in the NBVTP
Jeremiah 18 in the NET2
Jeremiah 18 in the NIV11
Jeremiah 18 in the NNT
Jeremiah 18 in the NNT2
Jeremiah 18 in the NNT3
Jeremiah 18 in the PDDPT
Jeremiah 18 in the PFNT
Jeremiah 18 in the RMNT
Jeremiah 18 in the SBIAS
Jeremiah 18 in the SBIBS
Jeremiah 18 in the SBIBS2
Jeremiah 18 in the SBICS
Jeremiah 18 in the SBIDS
Jeremiah 18 in the SBIGS
Jeremiah 18 in the SBIHS
Jeremiah 18 in the SBIIS
Jeremiah 18 in the SBIIS2
Jeremiah 18 in the SBIIS3
Jeremiah 18 in the SBIKS
Jeremiah 18 in the SBIKS2
Jeremiah 18 in the SBIMS
Jeremiah 18 in the SBIOS
Jeremiah 18 in the SBIPS
Jeremiah 18 in the SBISS
Jeremiah 18 in the SBITS
Jeremiah 18 in the SBITS2
Jeremiah 18 in the SBITS3
Jeremiah 18 in the SBITS4
Jeremiah 18 in the SBIUS
Jeremiah 18 in the SBIVS
Jeremiah 18 in the SBT
Jeremiah 18 in the SBT1E
Jeremiah 18 in the SCHL
Jeremiah 18 in the SNT
Jeremiah 18 in the SUSU
Jeremiah 18 in the SUSU2
Jeremiah 18 in the SYNO
Jeremiah 18 in the TBIAOTANT
Jeremiah 18 in the TBT1E
Jeremiah 18 in the TBT1E2
Jeremiah 18 in the TFTIP
Jeremiah 18 in the TFTU
Jeremiah 18 in the TGNTATF3T
Jeremiah 18 in the THAI
Jeremiah 18 in the TNFD
Jeremiah 18 in the TNT
Jeremiah 18 in the TNTIK
Jeremiah 18 in the TNTIL
Jeremiah 18 in the TNTIN
Jeremiah 18 in the TNTIP
Jeremiah 18 in the TNTIZ
Jeremiah 18 in the TOMA
Jeremiah 18 in the TTENT
Jeremiah 18 in the UBG
Jeremiah 18 in the UGV
Jeremiah 18 in the UGV2
Jeremiah 18 in the UGV3
Jeremiah 18 in the VBL
Jeremiah 18 in the VDCC
Jeremiah 18 in the YALU
Jeremiah 18 in the YAPE
Jeremiah 18 in the YBVTP
Jeremiah 18 in the ZBP