Jeremiah 21 (BOGWICC)
1 Mfumu Zedekiya inatuma Pasuri mwana wa Malikiya ndi wansembe Zefaniya mwana wa Maseya kwa Yeremiya. 2 Iwo amati akanene kwa Yeremiya mawu akuti, “Tinenere kwa Yehova chifukwa Nebukadinezara mfumu ya Babuloni akutithira nkhondo. Mwina mwake Yehova nʼkutichitira zodabwitsa kuti Nebukadinezarayo achoke kwathu kuno.” 3 Koma Yehova anawuza Yeremiya kuti ayankhe Pasuri ndi Zefaniya kuti, “Kamuwuzeni Zedekiya kuti, 4 ‘Yehova, Mulungu wa Israeli akuti ndikulandeni zida zimene zili mʼmanja mwanu zimene mukugwiritsa ntchito polimbana ndi mfumu ya ku Babuloni ndi ankhondo ake amene akuzingani kunja kwa lingali. Ndipo ndidzasonkhanitsa zidazo mʼkati mwa mzindawu. 5 Ineyo mwini wakene ndi mkono wotambasula ndi dzanja lamphamvu, ndidzachita nanu nkhondo ndili wokwiya, wokalipa ndi waukali. 6 Ndidzakantha amene amakhala mu mzinda muno, anthu pamodzi ndi zirombo, ndipo zidzafa ndi mliri woopsa. 7 Pambuyo pake, ndidzapereka Zedekiya mfumu ya ku Yuda, nduna zake pamodzi ndi anthu a mu mzinda muno amene adzapulumuke pa nthawi ya mliri, lupanga ndi njala kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni ndi kwa adani awo amene ankafuna kuwapha. Iye adzawapha ndi lupanga. Sadzawachitira chifundo kapena kuwamvera chisoni kapenanso kuwakomera mtima.’ 8 “Yehova anati ndiwawuzenso anthu amenewa kuti asankhe pakati pa moyo ndi imfa. 9 Aliyense amene akhale mu mzinda muno adzaphedwa ndi lupanga, njala kapena mliri. Koma aliyense amene apite kukadzipereka kwa Ababuloni amene akuzinganiwa adzakhala ndi moyo, adzapulumuka. 10 Ine ndatsimikiza kuchitira mzinda uno choyipa osati chabwino, akutero Yehova. Udzaperekedwa mʼdzanja la mfumu ya ku Babuloni, ndipo iyeyo adzawutentha ndi moto. 11 “Komanso, uwuze banja laufumu la Yuda kuti, ‘Imva mawu a Yehova; 12 inu a mʼbanja la Davide, Yehova akuti,“ ‘Weruzani mwachilungamo mmawa uliwonse;pulumutsani mʼdzanja la wozunzaaliyense amene walandidwa katundu wake,kuopa kuti ukali wanga ungabukendi kuyaka ngati moto wosazimitsikachifukwa cha zoyipa zimene mwachita. 13 Ndidzalimbana nanu,inu amene mukukhala pamwamba pa chigwa,inu okhala ngati thanthwe lapachidikha,akutero Yehova.Inu amene mumanena kuti, ‘Ndani amene angabwere kudzalimbana nafe?Ndani amene angathe kulowa mʼmalinga mwathu?’ 14 Ndidzakulangani molingana ndi ntchito zanu,akutero Yehova.Ndidzatentha nkhalango zanu;moto udzapsereza zonse zimene zakuzungulirani.’ ”
In Other Versions
Jeremiah 21 in the ANGEFD
Jeremiah 21 in the ANTPNG2D
Jeremiah 21 in the AS21
Jeremiah 21 in the BAGH
Jeremiah 21 in the BBPNG
Jeremiah 21 in the BBT1E
Jeremiah 21 in the BDS
Jeremiah 21 in the BEV
Jeremiah 21 in the BHAD
Jeremiah 21 in the BIB
Jeremiah 21 in the BLPT
Jeremiah 21 in the BNT
Jeremiah 21 in the BNTABOOT
Jeremiah 21 in the BNTLV
Jeremiah 21 in the BOATCB
Jeremiah 21 in the BOATCB2
Jeremiah 21 in the BOBCV
Jeremiah 21 in the BOCNT
Jeremiah 21 in the BOECS
Jeremiah 21 in the BOHCB
Jeremiah 21 in the BOHCV
Jeremiah 21 in the BOHLNT
Jeremiah 21 in the BOHNTLTAL
Jeremiah 21 in the BOICB
Jeremiah 21 in the BOILNTAP
Jeremiah 21 in the BOITCV
Jeremiah 21 in the BOKCV
Jeremiah 21 in the BOKCV2
Jeremiah 21 in the BOKHWOG
Jeremiah 21 in the BOKSSV
Jeremiah 21 in the BOLCB
Jeremiah 21 in the BOLCB2
Jeremiah 21 in the BOMCV
Jeremiah 21 in the BONAV
Jeremiah 21 in the BONCB
Jeremiah 21 in the BONLT
Jeremiah 21 in the BONUT2
Jeremiah 21 in the BOPLNT
Jeremiah 21 in the BOSCB
Jeremiah 21 in the BOSNC
Jeremiah 21 in the BOTLNT
Jeremiah 21 in the BOVCB
Jeremiah 21 in the BOYCB
Jeremiah 21 in the BPBB
Jeremiah 21 in the BPH
Jeremiah 21 in the BSB
Jeremiah 21 in the CCB
Jeremiah 21 in the CUV
Jeremiah 21 in the CUVS
Jeremiah 21 in the DBT
Jeremiah 21 in the DGDNT
Jeremiah 21 in the DHNT
Jeremiah 21 in the DNT
Jeremiah 21 in the ELBE
Jeremiah 21 in the EMTV
Jeremiah 21 in the ESV
Jeremiah 21 in the FBV
Jeremiah 21 in the FEB
Jeremiah 21 in the GGMNT
Jeremiah 21 in the GNT
Jeremiah 21 in the HARY
Jeremiah 21 in the HNT
Jeremiah 21 in the IRVA
Jeremiah 21 in the IRVB
Jeremiah 21 in the IRVG
Jeremiah 21 in the IRVH
Jeremiah 21 in the IRVK
Jeremiah 21 in the IRVM
Jeremiah 21 in the IRVM2
Jeremiah 21 in the IRVO
Jeremiah 21 in the IRVP
Jeremiah 21 in the IRVT
Jeremiah 21 in the IRVT2
Jeremiah 21 in the IRVU
Jeremiah 21 in the ISVN
Jeremiah 21 in the JSNT
Jeremiah 21 in the KAPI
Jeremiah 21 in the KBT1ETNIK
Jeremiah 21 in the KBV
Jeremiah 21 in the KJV
Jeremiah 21 in the KNFD
Jeremiah 21 in the LBA
Jeremiah 21 in the LBLA
Jeremiah 21 in the LNT
Jeremiah 21 in the LSV
Jeremiah 21 in the MAAL
Jeremiah 21 in the MBV
Jeremiah 21 in the MBV2
Jeremiah 21 in the MHNT
Jeremiah 21 in the MKNFD
Jeremiah 21 in the MNG
Jeremiah 21 in the MNT
Jeremiah 21 in the MNT2
Jeremiah 21 in the MRS1T
Jeremiah 21 in the NAA
Jeremiah 21 in the NASB
Jeremiah 21 in the NBLA
Jeremiah 21 in the NBS
Jeremiah 21 in the NBVTP
Jeremiah 21 in the NET2
Jeremiah 21 in the NIV11
Jeremiah 21 in the NNT
Jeremiah 21 in the NNT2
Jeremiah 21 in the NNT3
Jeremiah 21 in the PDDPT
Jeremiah 21 in the PFNT
Jeremiah 21 in the RMNT
Jeremiah 21 in the SBIAS
Jeremiah 21 in the SBIBS
Jeremiah 21 in the SBIBS2
Jeremiah 21 in the SBICS
Jeremiah 21 in the SBIDS
Jeremiah 21 in the SBIGS
Jeremiah 21 in the SBIHS
Jeremiah 21 in the SBIIS
Jeremiah 21 in the SBIIS2
Jeremiah 21 in the SBIIS3
Jeremiah 21 in the SBIKS
Jeremiah 21 in the SBIKS2
Jeremiah 21 in the SBIMS
Jeremiah 21 in the SBIOS
Jeremiah 21 in the SBIPS
Jeremiah 21 in the SBISS
Jeremiah 21 in the SBITS
Jeremiah 21 in the SBITS2
Jeremiah 21 in the SBITS3
Jeremiah 21 in the SBITS4
Jeremiah 21 in the SBIUS
Jeremiah 21 in the SBIVS
Jeremiah 21 in the SBT
Jeremiah 21 in the SBT1E
Jeremiah 21 in the SCHL
Jeremiah 21 in the SNT
Jeremiah 21 in the SUSU
Jeremiah 21 in the SUSU2
Jeremiah 21 in the SYNO
Jeremiah 21 in the TBIAOTANT
Jeremiah 21 in the TBT1E
Jeremiah 21 in the TBT1E2
Jeremiah 21 in the TFTIP
Jeremiah 21 in the TFTU
Jeremiah 21 in the TGNTATF3T
Jeremiah 21 in the THAI
Jeremiah 21 in the TNFD
Jeremiah 21 in the TNT
Jeremiah 21 in the TNTIK
Jeremiah 21 in the TNTIL
Jeremiah 21 in the TNTIN
Jeremiah 21 in the TNTIP
Jeremiah 21 in the TNTIZ
Jeremiah 21 in the TOMA
Jeremiah 21 in the TTENT
Jeremiah 21 in the UBG
Jeremiah 21 in the UGV
Jeremiah 21 in the UGV2
Jeremiah 21 in the UGV3
Jeremiah 21 in the VBL
Jeremiah 21 in the VDCC
Jeremiah 21 in the YALU
Jeremiah 21 in the YAPE
Jeremiah 21 in the YBVTP
Jeremiah 21 in the ZBP