Jeremiah 27 (BOGWICC)
1 Zedekiya mwana wa Yosiya, mfumu ya ku Yuda, atangoyamba kulamulira, Yehova anawuza Yeremiya kuti, 2 “Tenga zingwe zomangira ndi mitengo ya goli ndipo uzimangirire mʼkhosi mwako. 3 Tsono utumize uthenga kwa mafumu a Edomu, Mowabu, Amoni, Turo ndi Sidoni kudzera mwa amithenga amene abwera ku Yerusalemu kwa Zedekiya, mfumu ya Yuda. 4 Uwapatse uthenga wokapereka kwa ambuye awo ndipo uwawuze kuti: Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti, ‘Mukawuze ambuye anu kuti: 5 Ndi mphamvu zanga ndi dzanja langa lamphamvu ndinalenga dziko lapansi ndi anthu ake onse pamodzi ndi nyama zili mʼmenemo, ndipo ndimalipereka kwa aliyense amene ndikufuna. 6 Tsopano ndidzapereka mayiko anu onse kwa mtumiki wanga Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni. Ndamupatsanso nyama zakuthengo zonse kuti zimutumikire. 7 Anthu a mitundu yonse adzamutumikira iyeyo, mwana wake ndi chidzukulu chake mpaka nthawi itakwana yoti dziko lake liwonongedwe. Pamenepo mitundu yambiri ndi mafumu amphamvu adzamugonjetsa. 8 “ ‘Koma ngati anthu a mtundu wina uliwonse kapena ufumu wina uliwonse adzakana kutumikira Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni kapena kusenza goli lake, Ine ndidzalanga mtundu umenewo ndi lupanga, ndi njala ndi mliri, akutero Yehova, mpaka nditawapereka mʼmanja mwake kotheratu. 9 Choncho musamvere aneneri anu, owombeza anu, otanthauza maloto anu, amawula anu kapena amatsenga anu akamakuwuzani kuti, ‘Simudzatumikira mfumu ya ku Babuloni.’ 10 Iwo akukuloserani zabodza kotero kuti adani adzakuchotsani mʼdziko lanu nʼkupita nanu ku dziko lakutali. Ndidzakupirikitsani ndi kukuwonongani kotheratu. 11 Koma ngati mtundu wina uliwonse udzagonjera mfumu ya ku Babuloni ndi kuyitumukira, ndidzawusiya kuti ukhale mʼdziko lake kuti uzilima ndi kukhalamo, akutero Yehova.’ ” 12 Uthenga womwewu ndinawuzanso Hezekiya mfumu ya Yuda. Ndinati, “Gonjerani mfumu ya ku Babuloni. Itumikireni iyoyo pamodzi ndi anthu ake ndipo mudzakhala ndi moyo. 13 Nanga inu ndi anthu anu, muferenji ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri, zimene Yehova waopsezera mtundu wina uliwonse umene sudzatumikira mfumu ya ku Babuloni? 14 Musamvere mawu a aneneri akamakuwuzani kuti, ‘Simudzatumikira mfumu ya ku Babuloni,’ chifukwa zimene akukuloseranizo nʼzabodza. 15 Sindinawatume ngakhale iwo akulosera mʼdzina langa. Nʼchifukwa chake, ndidzakupirikitsani ndipo mudzawonongeka kotheratu, inu pamodzi ndi aneneri amene akunenera zabodza kwa inu.” 16 Kenaka ndinawuza ansembe pamodzi ndi anthu ena onse kuti, “Yehova akuti: Musamvere aneneri amene akumanena kuti, ‘Posachedwapa ziwiya za mʼNyumba ya Yehova zibwera kuchokera ku Babuloni.’ Iwowo akunenera zabodza kwa inu. 17 Musawamvere. Tumikirani mfumu ya ku Babuloni, ndipo mudzakhala ndi moyo. Mzindawu usandukirenji bwinja? 18 Ngati iwo ndi aneneri ndipo ali ndi mawu a Yehova, apempheretu kwa Yehova Wamphamvuzonse kuti ziwiya zimene zatsala mʼNyumba ya Yehova ndi mʼnyumba ya mfumu ya Yuda ndiponso mu Yerusalemu zisatengedwe kupita ku Babuloni. 19 Pakuti Yehova akunena za zipilala, za mbiya ya madzi, maphaka ndi ziwiya zina zimene zatsala mu Yerusalemu. 20 Izi ndi zimene Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni sanatenge pamene anatenga ukapolo Yekoniya mwana wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda kupita ku Babuloni kuchokera ku Yerusalemu, pamodzi ndi anthu olemekezeka a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu. 21 Inde, Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, akunena za zinthu zimene zinatsala mʼNyumba ya Yehova ndi mʼnyumba ya mfumu ya Yuda ndi mu Yerusalemu kuti, 22 ‘Zidzatengedwa kupita ku Babuloni ndipo zidzakhala kumeneko mpaka tsiku limene ndidzawakumbukirenso,’ akutero Yehova. ‘Pamenepo ndidzazitenganso ndi kuzibwezanso ku malo ano.’ ”
In Other Versions
Jeremiah 27 in the ANGEFD
Jeremiah 27 in the ANTPNG2D
Jeremiah 27 in the AS21
Jeremiah 27 in the BAGH
Jeremiah 27 in the BBPNG
Jeremiah 27 in the BBT1E
Jeremiah 27 in the BDS
Jeremiah 27 in the BEV
Jeremiah 27 in the BHAD
Jeremiah 27 in the BIB
Jeremiah 27 in the BLPT
Jeremiah 27 in the BNT
Jeremiah 27 in the BNTABOOT
Jeremiah 27 in the BNTLV
Jeremiah 27 in the BOATCB
Jeremiah 27 in the BOATCB2
Jeremiah 27 in the BOBCV
Jeremiah 27 in the BOCNT
Jeremiah 27 in the BOECS
Jeremiah 27 in the BOHCB
Jeremiah 27 in the BOHCV
Jeremiah 27 in the BOHLNT
Jeremiah 27 in the BOHNTLTAL
Jeremiah 27 in the BOICB
Jeremiah 27 in the BOILNTAP
Jeremiah 27 in the BOITCV
Jeremiah 27 in the BOKCV
Jeremiah 27 in the BOKCV2
Jeremiah 27 in the BOKHWOG
Jeremiah 27 in the BOKSSV
Jeremiah 27 in the BOLCB
Jeremiah 27 in the BOLCB2
Jeremiah 27 in the BOMCV
Jeremiah 27 in the BONAV
Jeremiah 27 in the BONCB
Jeremiah 27 in the BONLT
Jeremiah 27 in the BONUT2
Jeremiah 27 in the BOPLNT
Jeremiah 27 in the BOSCB
Jeremiah 27 in the BOSNC
Jeremiah 27 in the BOTLNT
Jeremiah 27 in the BOVCB
Jeremiah 27 in the BOYCB
Jeremiah 27 in the BPBB
Jeremiah 27 in the BPH
Jeremiah 27 in the BSB
Jeremiah 27 in the CCB
Jeremiah 27 in the CUV
Jeremiah 27 in the CUVS
Jeremiah 27 in the DBT
Jeremiah 27 in the DGDNT
Jeremiah 27 in the DHNT
Jeremiah 27 in the DNT
Jeremiah 27 in the ELBE
Jeremiah 27 in the EMTV
Jeremiah 27 in the ESV
Jeremiah 27 in the FBV
Jeremiah 27 in the FEB
Jeremiah 27 in the GGMNT
Jeremiah 27 in the GNT
Jeremiah 27 in the HARY
Jeremiah 27 in the HNT
Jeremiah 27 in the IRVA
Jeremiah 27 in the IRVB
Jeremiah 27 in the IRVG
Jeremiah 27 in the IRVH
Jeremiah 27 in the IRVK
Jeremiah 27 in the IRVM
Jeremiah 27 in the IRVM2
Jeremiah 27 in the IRVO
Jeremiah 27 in the IRVP
Jeremiah 27 in the IRVT
Jeremiah 27 in the IRVT2
Jeremiah 27 in the IRVU
Jeremiah 27 in the ISVN
Jeremiah 27 in the JSNT
Jeremiah 27 in the KAPI
Jeremiah 27 in the KBT1ETNIK
Jeremiah 27 in the KBV
Jeremiah 27 in the KJV
Jeremiah 27 in the KNFD
Jeremiah 27 in the LBA
Jeremiah 27 in the LBLA
Jeremiah 27 in the LNT
Jeremiah 27 in the LSV
Jeremiah 27 in the MAAL
Jeremiah 27 in the MBV
Jeremiah 27 in the MBV2
Jeremiah 27 in the MHNT
Jeremiah 27 in the MKNFD
Jeremiah 27 in the MNG
Jeremiah 27 in the MNT
Jeremiah 27 in the MNT2
Jeremiah 27 in the MRS1T
Jeremiah 27 in the NAA
Jeremiah 27 in the NASB
Jeremiah 27 in the NBLA
Jeremiah 27 in the NBS
Jeremiah 27 in the NBVTP
Jeremiah 27 in the NET2
Jeremiah 27 in the NIV11
Jeremiah 27 in the NNT
Jeremiah 27 in the NNT2
Jeremiah 27 in the NNT3
Jeremiah 27 in the PDDPT
Jeremiah 27 in the PFNT
Jeremiah 27 in the RMNT
Jeremiah 27 in the SBIAS
Jeremiah 27 in the SBIBS
Jeremiah 27 in the SBIBS2
Jeremiah 27 in the SBICS
Jeremiah 27 in the SBIDS
Jeremiah 27 in the SBIGS
Jeremiah 27 in the SBIHS
Jeremiah 27 in the SBIIS
Jeremiah 27 in the SBIIS2
Jeremiah 27 in the SBIIS3
Jeremiah 27 in the SBIKS
Jeremiah 27 in the SBIKS2
Jeremiah 27 in the SBIMS
Jeremiah 27 in the SBIOS
Jeremiah 27 in the SBIPS
Jeremiah 27 in the SBISS
Jeremiah 27 in the SBITS
Jeremiah 27 in the SBITS2
Jeremiah 27 in the SBITS3
Jeremiah 27 in the SBITS4
Jeremiah 27 in the SBIUS
Jeremiah 27 in the SBIVS
Jeremiah 27 in the SBT
Jeremiah 27 in the SBT1E
Jeremiah 27 in the SCHL
Jeremiah 27 in the SNT
Jeremiah 27 in the SUSU
Jeremiah 27 in the SUSU2
Jeremiah 27 in the SYNO
Jeremiah 27 in the TBIAOTANT
Jeremiah 27 in the TBT1E
Jeremiah 27 in the TBT1E2
Jeremiah 27 in the TFTIP
Jeremiah 27 in the TFTU
Jeremiah 27 in the TGNTATF3T
Jeremiah 27 in the THAI
Jeremiah 27 in the TNFD
Jeremiah 27 in the TNT
Jeremiah 27 in the TNTIK
Jeremiah 27 in the TNTIL
Jeremiah 27 in the TNTIN
Jeremiah 27 in the TNTIP
Jeremiah 27 in the TNTIZ
Jeremiah 27 in the TOMA
Jeremiah 27 in the TTENT
Jeremiah 27 in the UBG
Jeremiah 27 in the UGV
Jeremiah 27 in the UGV2
Jeremiah 27 in the UGV3
Jeremiah 27 in the VBL
Jeremiah 27 in the VDCC
Jeremiah 27 in the YALU
Jeremiah 27 in the YAPE
Jeremiah 27 in the YBVTP
Jeremiah 27 in the ZBP