John 15 (BOGWICC)

1 “Ine ndine mpesa weniweni, ndipo Atate anga ndiye mwini munda. 2 Iye amadula nthambi iliyonse ya mwa Ine imene sibala chipatso, koma nthambi iliyonse imene imabala chipatso amayisadzira bwino kuti ibale zipatso zambiri. 3 Inu ndinu oyera kale chifukwa cha mawu amene ndayankhula inu. 4 Khalani mwa Ine, monga Ine ndili mwa inu. Palibe nthambi imene ingabereke chipatso pa yokha ngati sinalumikizike ku mpesa. Chomwechonso inu simungathe kubereka chipatso pokhapokha mutakhala mwa Ine. 5 “Ine ndine mpesa; inu ndinu nthambi zake. Ngati munthu akhala mwa Ine ndi Ine mwa iye, adzabereka zipatso zambiri; popanda Ine simungathe kuchita kanthu. 6 Ngati wina aliyense sakhala mwa Ine, iyeyo ali ngati nthambi imene yatayidwa ndi kufota. Nthambi zotero zimatoledwa, kuponyedwa pa moto ndi kupsa. 7 Ngati inu mukhala mwa Ine ndipo mawu anga akhala mwa inu, pemphani chilichonse chimene mukufuna ndipo mudzapatsidwa. 8 Atate anga amalemekezedwa mukamabereka zipatso zochuluka, ndipo potero mudzionetsa kuti ndinu ophunzira anga. 9 “Monga momwe Atate amandikondera Ine, Inenso ndakukondani. Tsopano khalani mʼchikondi changa. 10 Ngati mumvera malamulo anga, mudzakhala mʼchikondi changa, monga Ine ndimamvera malamulo a Atate anga, ndipo ndimakhala mʼchikondi chawo. 11 Ine ndakuwuzani izi kuti chimwemwe changa chikhale mwa Inu, kuti chimwemwe chanu chikhale chokwanira. 12 Lamulo langa ndi ili: ‘Kondanani wina ndi mnzake monga Ine ndakonda inu.’ 13 Palibe munthu ali ndi chikondi choposa ichi, choti munthu nʼkutaya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake. 14 Inu ndinu abwenzi anga ngati muchita zimene Ine ndikulamulani. 15 Ine sindikutchulaninso antchito, chifukwa wantchito sadziwa zimene bwana wake akuchita. Mʼmalo mwake Ine ndakutchani abwenzi pakuti zilizonse zimene ndinaphunzira kwa Atate, Ine ndakudziwitsani. 16 Inu simunandisankhe Ine, koma Ine ndinakusankhani kuti mupite ndi kukabereka zipatso, zipatso zake za nthawi yayitali. Choncho Atate adzakupatsani chilichonse chimene mudzapempha mʼdzina langa. 17 Lamulo langa ndi ili: ‘Muzikondana.’ 18 “Ngati dziko lapansi lidana nanu, dziwani kuti linayamba kudana ndi Ine. 19 Inu mukanakhala anthu a dziko lapansi, dziko lapansi likanakukondani ngati anthu ake omwe. Koma mmene zilili, inu si anthu a dziko lapansi. Ine ndakusankhani kuchokera mʼdziko lapansi, nʼchifukwa chake dziko lapansi limakudani. 20 Kumbukirani mawu amene ndinayankhula nanu akuti, ‘Palibe wantchito amene amaposa bwana wake.’ Ngati anandizunza Ine, iwo adzakuzunzaninso inu. Ngati anamvera chiphunzitso changa, iwo adzamvera chanunso. 21 Iwo adzakuchitani zimenezi chifukwa cha dzina langa, popeza sakudziwa amene anandituma Ine. 22 Ine ndikanapanda kubwera ndi kuyankhula nawo, sakanakhala ndi mlandu. Koma tsopano alibe choti nʼkukanira mlandu wawo. 23 Iye amene amadana ndi Ine amadananso Atate anga. 24 Ine ndikanapanda kuchita pakati pawo zinthu zimene wina aliyense sanachitepo, iwo sakanakhala ochimwa. Koma tsopano aona zodabwitsa izi, komabe akundida Ine pamodzi ndi Atate anga. 25 Koma zatere kuti zikwaniritse zimene zinalembedwa mʼmalamulo awo: ‘Iwo anandida Ine popanda chifukwa.’ 26 “Nkhoswe ikadzabwera imene Ine ndidzakutumizireni kuchokera kwa Atate, ndiye Mzimu Woyera wachoonadi amene achokera kwa Atate, Iyeyo adzandichitira umboni Ine. 27 Inunso mudzandichitira umboni Ine, popeza mwakhala nane kuchokera pachiyambi.”

In Other Versions

John 15 in the ANGEFD

John 15 in the ANTPNG2D

John 15 in the AS21

John 15 in the BAGH

John 15 in the BBPNG

John 15 in the BBT1E

John 15 in the BDS

John 15 in the BEV

John 15 in the BHAD

John 15 in the BIB

John 15 in the BLPT

John 15 in the BNT

John 15 in the BNTABOOT

John 15 in the BNTLV

John 15 in the BOATCB

John 15 in the BOATCB2

John 15 in the BOBCV

John 15 in the BOCNT

John 15 in the BOECS

John 15 in the BOHCB

John 15 in the BOHCV

John 15 in the BOHLNT

John 15 in the BOHNTLTAL

John 15 in the BOICB

John 15 in the BOILNTAP

John 15 in the BOITCV

John 15 in the BOKCV

John 15 in the BOKCV2

John 15 in the BOKHWOG

John 15 in the BOKSSV

John 15 in the BOLCB

John 15 in the BOLCB2

John 15 in the BOMCV

John 15 in the BONAV

John 15 in the BONCB

John 15 in the BONLT

John 15 in the BONUT2

John 15 in the BOPLNT

John 15 in the BOSCB

John 15 in the BOSNC

John 15 in the BOTLNT

John 15 in the BOVCB

John 15 in the BOYCB

John 15 in the BPBB

John 15 in the BPH

John 15 in the BSB

John 15 in the CCB

John 15 in the CUV

John 15 in the CUVS

John 15 in the DBT

John 15 in the DGDNT

John 15 in the DHNT

John 15 in the DNT

John 15 in the ELBE

John 15 in the EMTV

John 15 in the ESV

John 15 in the FBV

John 15 in the FEB

John 15 in the GGMNT

John 15 in the GNT

John 15 in the HARY

John 15 in the HNT

John 15 in the IRVA

John 15 in the IRVB

John 15 in the IRVG

John 15 in the IRVH

John 15 in the IRVK

John 15 in the IRVM

John 15 in the IRVM2

John 15 in the IRVO

John 15 in the IRVP

John 15 in the IRVT

John 15 in the IRVT2

John 15 in the IRVU

John 15 in the ISVN

John 15 in the JSNT

John 15 in the KAPI

John 15 in the KBT1ETNIK

John 15 in the KBV

John 15 in the KJV

John 15 in the KNFD

John 15 in the LBA

John 15 in the LBLA

John 15 in the LNT

John 15 in the LSV

John 15 in the MAAL

John 15 in the MBV

John 15 in the MBV2

John 15 in the MHNT

John 15 in the MKNFD

John 15 in the MNG

John 15 in the MNT

John 15 in the MNT2

John 15 in the MRS1T

John 15 in the NAA

John 15 in the NASB

John 15 in the NBLA

John 15 in the NBS

John 15 in the NBVTP

John 15 in the NET2

John 15 in the NIV11

John 15 in the NNT

John 15 in the NNT2

John 15 in the NNT3

John 15 in the PDDPT

John 15 in the PFNT

John 15 in the RMNT

John 15 in the SBIAS

John 15 in the SBIBS

John 15 in the SBIBS2

John 15 in the SBICS

John 15 in the SBIDS

John 15 in the SBIGS

John 15 in the SBIHS

John 15 in the SBIIS

John 15 in the SBIIS2

John 15 in the SBIIS3

John 15 in the SBIKS

John 15 in the SBIKS2

John 15 in the SBIMS

John 15 in the SBIOS

John 15 in the SBIPS

John 15 in the SBISS

John 15 in the SBITS

John 15 in the SBITS2

John 15 in the SBITS3

John 15 in the SBITS4

John 15 in the SBIUS

John 15 in the SBIVS

John 15 in the SBT

John 15 in the SBT1E

John 15 in the SCHL

John 15 in the SNT

John 15 in the SUSU

John 15 in the SUSU2

John 15 in the SYNO

John 15 in the TBIAOTANT

John 15 in the TBT1E

John 15 in the TBT1E2

John 15 in the TFTIP

John 15 in the TFTU

John 15 in the TGNTATF3T

John 15 in the THAI

John 15 in the TNFD

John 15 in the TNT

John 15 in the TNTIK

John 15 in the TNTIL

John 15 in the TNTIN

John 15 in the TNTIP

John 15 in the TNTIZ

John 15 in the TOMA

John 15 in the TTENT

John 15 in the UBG

John 15 in the UGV

John 15 in the UGV2

John 15 in the UGV3

John 15 in the VBL

John 15 in the VDCC

John 15 in the YALU

John 15 in the YAPE

John 15 in the YBVTP

John 15 in the ZBP