Joshua 11 (BOGWICC)

1 Yabini, mfumu ya Hazori, inamva zimene zinachitikazi. Tsono inatumiza uthenga kwa Yobabu mfumu ya Madoni, ndiponso kwa mafumu a ku Simironi ndi Akisafu. 2 Inatumizanso uthenga kwa mafumu a kumpoto, kumapiri, ndi mʼchigwa cha Yorodani kummwera kwa nyanja ya Kinereti, ndiponso kumadzulo mʼmbali mwa nyanja pafupi ndi Dori. 3 Inatumizanso uthenga kwa Akanaani amene ankakhala kummawa ndi kumadzulo kwa Yorodani. Uthenga unapitanso kwa Aamori, Ahiti, Aperezi ndi Ayebusi amene amakhala mʼdziko la ku mapiri ndiponso kwa Ahivi amene ankakhala mʼmunsi mwa phiri la Herimoni ku chigwa cha Mizipa. 4 Mafumuwo anabwera pamodzi ndi ankhondo awo onse. Gulu la ankhondo linali lalikulu ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja. Analinso ndi akavalo ndi magaleta ambiri. 5 Mafumu onsewa anasonkhana pamodzi ndipo anamanga misasa yawo ku mtsinje wa Meromu, kuti amenyane ndi Israeli. 6 Yehova anati kwa Yoswa, “Usawaope chifukwa mawa nthawi ngati yomwe ino ndidzawapereka kuti muwaphe. Akavalo awo muwadule matsinde ndipo magaleta awo muwatenthe ndi moto.” 7 Kotero Yoswa pamodzi ndi gulu lonse la nkhondo anafika kwa adani awo aja ku mtsinje wa Meromu modzidzimutsa ndi kuwathira nkhondo. 8 Yehova anawapereka mʼmanja mwa Israeli mwakuti anawagonjetseratu ndi kuwapirikitsa njira yonse mpaka ku Sidoni Wamkulu ndi ku Misirefoti Maimu, ndiponso kummawa ku chigwa cha Mizipa. Onse anaphedwa popanda wopulumuka. 9 Yoswa anawachita zimene Yehova analamula. Iye anadula matsinde a akavalo awo ndi kutentha magaleta awo. 10 Pambuyo pake Yoswa anabwera nalanda mzinda wa Hazori ndi kupha mfumu yake. (Nthawi imeneyo mzinda wa Hazori unali wopambana mizinda ina yonse). 11 Anapha aliyense wa mu mzindamo popanda wotsala wamoyo, ndipo mzinda wa Hazori anawutentha ndi moto. 12 Yoswa analanda mizinda yonse ndi mafumu ake. Anthu onse anaphedwa ndi lupanga monga momwe analamulira Mose, mtumiki wa Yehova. 13 Israeli sanatenthe mizinda yomangidwa pa zitunda, kupatula mzinda wa Hazori, umene Yoswa anawutentha. 14 Aisraeli anatenga zinthu zonse za mʼmizindayi pamodzi ndi ziweto kuti zikhale zawo, koma anapha anthu onse ndi lupanga osasiyako ndi mmodzi yemwe wamoyo. 15 Monga momwe Yehova analamulira mtumiki wake Mose, nayenso Mose analamulira Yoswa ndipo Yoswa anachita chilichonse chimene Yehova analamulira Mose. 16 Kotero Yoswa analanda dziko lonse: dziko la ku mapiri, dera lonse la Negevi, chigawo chonse cha Goseni, ndi chigwa chake chonse, chigwa cha Yorodani, dziko lonse la lamapiri la Israeli pamodzi ndi chigwa chake chomwe. 17 Dziko lolandidwalo linayambira ku phiri la Halaki limene linali ku Seiri mpaka ku Baala-Gadi mʼchigwa cha Lebanoni, kumunsi kwa phiri la Herimoni. Yoswa anagwira ndi kupha mafumu a dziko lonselo 18 atachita nawo nkhondo kwa nthawi yayitali. 19 Palibe ngakhale ndi mfumu imodzi yomwe imene inachita mgwirizano wa mtendere ndi Aisraeli kupatula Ahivi okhala ku Gibiyoni. Koma mizinda ina yonse anachita kuyigonjetsa pa nkhondo. 20 Yehova anali atawumitsa mitima yawo kuti alimbane ndi Aisraeli kuti aphedwe popanda kuchitiridwa chifundo. Izi ndi zimene Yehova analamula Mose kuti zichitidwe. 21 Pa nthawi imeneyi Yoswa anapita kukawononga Aanaki okhala mʼdziko lija la ku mapiri ku Hebroni, Debri, Anabu komanso madera onse a ku mapiri a Yuda ndi Israeli. Yoswa anawawononga onse pamodzi ndi mizinda yawo. 22 Palibe ndi mmodzi yemwe amene anatsalako mʼdziko lonse la Israeli; komabe ku Gaza, ku Gati ndi Asidodi kokha ndi kumene anatsalako pangʼono. 23 Choncho Yoswa anagonjetsa dziko lonse monga momwe Yehova analamulira Mose. Tsono Yoswa analipereka kwa Aisraeli kuti likhale lawo, fuko lililonse gawo lake.Anthu onse anapumula, osamenyanso nkhondo.

In Other Versions

Joshua 11 in the ANGEFD

Joshua 11 in the ANTPNG2D

Joshua 11 in the AS21

Joshua 11 in the BAGH

Joshua 11 in the BBPNG

Joshua 11 in the BBT1E

Joshua 11 in the BDS

Joshua 11 in the BEV

Joshua 11 in the BHAD

Joshua 11 in the BIB

Joshua 11 in the BLPT

Joshua 11 in the BNT

Joshua 11 in the BNTABOOT

Joshua 11 in the BNTLV

Joshua 11 in the BOATCB

Joshua 11 in the BOATCB2

Joshua 11 in the BOBCV

Joshua 11 in the BOCNT

Joshua 11 in the BOECS

Joshua 11 in the BOHCB

Joshua 11 in the BOHCV

Joshua 11 in the BOHLNT

Joshua 11 in the BOHNTLTAL

Joshua 11 in the BOICB

Joshua 11 in the BOILNTAP

Joshua 11 in the BOITCV

Joshua 11 in the BOKCV

Joshua 11 in the BOKCV2

Joshua 11 in the BOKHWOG

Joshua 11 in the BOKSSV

Joshua 11 in the BOLCB

Joshua 11 in the BOLCB2

Joshua 11 in the BOMCV

Joshua 11 in the BONAV

Joshua 11 in the BONCB

Joshua 11 in the BONLT

Joshua 11 in the BONUT2

Joshua 11 in the BOPLNT

Joshua 11 in the BOSCB

Joshua 11 in the BOSNC

Joshua 11 in the BOTLNT

Joshua 11 in the BOVCB

Joshua 11 in the BOYCB

Joshua 11 in the BPBB

Joshua 11 in the BPH

Joshua 11 in the BSB

Joshua 11 in the CCB

Joshua 11 in the CUV

Joshua 11 in the CUVS

Joshua 11 in the DBT

Joshua 11 in the DGDNT

Joshua 11 in the DHNT

Joshua 11 in the DNT

Joshua 11 in the ELBE

Joshua 11 in the EMTV

Joshua 11 in the ESV

Joshua 11 in the FBV

Joshua 11 in the FEB

Joshua 11 in the GGMNT

Joshua 11 in the GNT

Joshua 11 in the HARY

Joshua 11 in the HNT

Joshua 11 in the IRVA

Joshua 11 in the IRVB

Joshua 11 in the IRVG

Joshua 11 in the IRVH

Joshua 11 in the IRVK

Joshua 11 in the IRVM

Joshua 11 in the IRVM2

Joshua 11 in the IRVO

Joshua 11 in the IRVP

Joshua 11 in the IRVT

Joshua 11 in the IRVT2

Joshua 11 in the IRVU

Joshua 11 in the ISVN

Joshua 11 in the JSNT

Joshua 11 in the KAPI

Joshua 11 in the KBT1ETNIK

Joshua 11 in the KBV

Joshua 11 in the KJV

Joshua 11 in the KNFD

Joshua 11 in the LBA

Joshua 11 in the LBLA

Joshua 11 in the LNT

Joshua 11 in the LSV

Joshua 11 in the MAAL

Joshua 11 in the MBV

Joshua 11 in the MBV2

Joshua 11 in the MHNT

Joshua 11 in the MKNFD

Joshua 11 in the MNG

Joshua 11 in the MNT

Joshua 11 in the MNT2

Joshua 11 in the MRS1T

Joshua 11 in the NAA

Joshua 11 in the NASB

Joshua 11 in the NBLA

Joshua 11 in the NBS

Joshua 11 in the NBVTP

Joshua 11 in the NET2

Joshua 11 in the NIV11

Joshua 11 in the NNT

Joshua 11 in the NNT2

Joshua 11 in the NNT3

Joshua 11 in the PDDPT

Joshua 11 in the PFNT

Joshua 11 in the RMNT

Joshua 11 in the SBIAS

Joshua 11 in the SBIBS

Joshua 11 in the SBIBS2

Joshua 11 in the SBICS

Joshua 11 in the SBIDS

Joshua 11 in the SBIGS

Joshua 11 in the SBIHS

Joshua 11 in the SBIIS

Joshua 11 in the SBIIS2

Joshua 11 in the SBIIS3

Joshua 11 in the SBIKS

Joshua 11 in the SBIKS2

Joshua 11 in the SBIMS

Joshua 11 in the SBIOS

Joshua 11 in the SBIPS

Joshua 11 in the SBISS

Joshua 11 in the SBITS

Joshua 11 in the SBITS2

Joshua 11 in the SBITS3

Joshua 11 in the SBITS4

Joshua 11 in the SBIUS

Joshua 11 in the SBIVS

Joshua 11 in the SBT

Joshua 11 in the SBT1E

Joshua 11 in the SCHL

Joshua 11 in the SNT

Joshua 11 in the SUSU

Joshua 11 in the SUSU2

Joshua 11 in the SYNO

Joshua 11 in the TBIAOTANT

Joshua 11 in the TBT1E

Joshua 11 in the TBT1E2

Joshua 11 in the TFTIP

Joshua 11 in the TFTU

Joshua 11 in the TGNTATF3T

Joshua 11 in the THAI

Joshua 11 in the TNFD

Joshua 11 in the TNT

Joshua 11 in the TNTIK

Joshua 11 in the TNTIL

Joshua 11 in the TNTIN

Joshua 11 in the TNTIP

Joshua 11 in the TNTIZ

Joshua 11 in the TOMA

Joshua 11 in the TTENT

Joshua 11 in the UBG

Joshua 11 in the UGV

Joshua 11 in the UGV2

Joshua 11 in the UGV3

Joshua 11 in the VBL

Joshua 11 in the VDCC

Joshua 11 in the YALU

Joshua 11 in the YAPE

Joshua 11 in the YBVTP

Joshua 11 in the ZBP