Joshua 17 (BOGWICC)
1 Gawo lina la dzikolo linapatsidwa kwa mabanja ena a fuko la Manase, mwana woyamba kubadwa wa Yosefe. Makiri anali mwana woyamba kubadwa wa Manase ndiponso kholo la anthu okhala ku Giliyadi. Popeza kuti iye anali munthu wankhondo, analandira Giliyadi ndi Basani. 2 Mabanja ena otsala a fuko la Manase amene analandira dziko ndi awa: Abiezeri, Heleki, Asirieli, Sekemu, Heferi ndi Semida. Izi ndi zidzukulu zina zazimuna za Manase mwana wa Yosefe ndiponso eni mbumba. 3 Panali Zelofehadi mwana wa Heferi, mwana wa Giliyadi, mwana wa Makiri mwana wa Manase. Iyeyu analibe ana aamuna koma aakazi okhaokha ndipo mayina awo ndi awa: Mahila, Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza. 4 Iwo anapita kwa Eliezara wansembe, Yoswa mwana wa Nuni, ndi atsogoleri ndipo anati: “Yehova analamula Mose kuti ife ndi alongo athu atipatse cholowa chathu.” Choncho iwowo pamodzi ndi abale a abambo awo anawapatsa dera lina la dzikolo kuti likhale monga mwa lamulo la Yehova. 5 Choncho kuwonjezera pa mayiko a Giliyadi ndi Basani kummawa kwa Yorodani, anthu a fuko la Manase analandiranso magawo khumi 6 chifukwa ana aakazi a fuko la Manase analandira cholowa chawo pakati pa ana aamuna. Dziko la Giliyadi linali dziko la zidzukulu zonse za Manase. 7 Malire a dziko la Manase anayambira ku Aseri, ndipo anakafika ku Mikimetati kummawa kwa Sekemu. Tsono malire anapita kummwera kuloza kwa anthu a ku Eni-Tapuwa. 8 (Manase anatenga dziko la Tapuwa, koma mzinda wa Tapuwawo, umene unali mʼmalire mwa Manase unali wa fuko la Efereimu). 9 Ndipo malire ake anapitirira kummwera mpaka ku mtsinje wa ku Kana. Mizinda ya kummwera kwa mtsinjewo inali ya fuko la Efereimu ngakhale kuti inali mʼdziko la Manase. Malire a fuko la Manase anapita kumpoto kwa mtsinje wa Kana ndi kukathera ku Nyanja. 10 Dziko la kummwera linali la Efereimu ndipo la kumpoto linali la Manase. Dziko la Manase linafika ku nyanja ndipo linachita malire ndi Aseri, kumpoto ndiponso Isakara, kummawa. 11 Mʼdziko la Isakara ndi Aseri, Manase analinso ndi mizinda ya Beti-Seani ndi Ibuleamu pamodzi ndi midzi yawo yozungulira. Panalinso Akanaani amene ankakhala ku Dori, Endori, Taanaki ndi Megido pamodzi ndi mizinda yozungulira (wachitatu pa mʼndandandawu ndi Nafati Dori). 12 Komabe anthu a fuko la Manase sanathe kuwapirikitsa anthu okhala mʼmizinda imeneyi. Choncho Akanaani anakhalabe mʼmizindayi. 13 Ngakhale Aisraeli anali a mphamvu mʼdzikomo, sanapirikitse Akanaani onse koma anangowasandutsa kukhala akapolo. 14 Anthu a fuko la Yosefe anati kwa Yoswa, “Chifukwa chiyani mwatipatsa gawo limodzi lokha la dziko kuti likhale cholowa chathu? Ife tilipo anthu ambiri popeza Yehova watidalitsa kwambiri.” 15 Yoswa anayankha kuti, “Ngati muli ambiri ndipo dziko la ku mapiri la Efereimu lakucheperani kwambiri, lowani ku nkhalango mudule mitengo, mudzikonzere malo akuti mukhalemo, mʼdziko la Aperezi ndi Arefai.” 16 Tsono zidzukulu za Yosefe zinati, “Dziko la ku mapiri ndi losatikwaniradi, komanso Akanaani onse amene akukhala ku chigwa pamodzi ndi amene akukhala ku Beti-Seani ndi madera awo ndiponso amene ali ku chigwa cha Yezireeli ali ndi magaleta azitsulo.” 17 Koma Yoswa anawuza zidzukulu za Yosefe, za fuko la Efereimu ndi za fuko la Manase kuti, “Inu mulipodi ambiri ndiponso amphamvu. Simulandira gawo limodzi lokha, 18 dziko la ku mapiri lidzakhalanso lanu. Ngakhale kuti ndi nkhalango yokhayokha koma inu mudzadula mitengo yake ndipo lidzakhala lanu mpaka kumapeto. Ngakhale kuti Akanaani ali ndi magaleta azitsulo ndiponso kuti iwo ndi amphamvu, koma inu mudzawapirikitsa.”
In Other Versions
Joshua 17 in the ANGEFD
Joshua 17 in the ANTPNG2D
Joshua 17 in the AS21
Joshua 17 in the BAGH
Joshua 17 in the BBPNG
Joshua 17 in the BBT1E
Joshua 17 in the BDS
Joshua 17 in the BEV
Joshua 17 in the BHAD
Joshua 17 in the BIB
Joshua 17 in the BLPT
Joshua 17 in the BNT
Joshua 17 in the BNTABOOT
Joshua 17 in the BNTLV
Joshua 17 in the BOATCB
Joshua 17 in the BOATCB2
Joshua 17 in the BOBCV
Joshua 17 in the BOCNT
Joshua 17 in the BOECS
Joshua 17 in the BOHCB
Joshua 17 in the BOHCV
Joshua 17 in the BOHLNT
Joshua 17 in the BOHNTLTAL
Joshua 17 in the BOICB
Joshua 17 in the BOILNTAP
Joshua 17 in the BOITCV
Joshua 17 in the BOKCV
Joshua 17 in the BOKCV2
Joshua 17 in the BOKHWOG
Joshua 17 in the BOKSSV
Joshua 17 in the BOLCB
Joshua 17 in the BOLCB2
Joshua 17 in the BOMCV
Joshua 17 in the BONAV
Joshua 17 in the BONCB
Joshua 17 in the BONLT
Joshua 17 in the BONUT2
Joshua 17 in the BOPLNT
Joshua 17 in the BOSCB
Joshua 17 in the BOSNC
Joshua 17 in the BOTLNT
Joshua 17 in the BOVCB
Joshua 17 in the BOYCB
Joshua 17 in the BPBB
Joshua 17 in the BPH
Joshua 17 in the BSB
Joshua 17 in the CCB
Joshua 17 in the CUV
Joshua 17 in the CUVS
Joshua 17 in the DBT
Joshua 17 in the DGDNT
Joshua 17 in the DHNT
Joshua 17 in the DNT
Joshua 17 in the ELBE
Joshua 17 in the EMTV
Joshua 17 in the ESV
Joshua 17 in the FBV
Joshua 17 in the FEB
Joshua 17 in the GGMNT
Joshua 17 in the GNT
Joshua 17 in the HARY
Joshua 17 in the HNT
Joshua 17 in the IRVA
Joshua 17 in the IRVB
Joshua 17 in the IRVG
Joshua 17 in the IRVH
Joshua 17 in the IRVK
Joshua 17 in the IRVM
Joshua 17 in the IRVM2
Joshua 17 in the IRVO
Joshua 17 in the IRVP
Joshua 17 in the IRVT
Joshua 17 in the IRVT2
Joshua 17 in the IRVU
Joshua 17 in the ISVN
Joshua 17 in the JSNT
Joshua 17 in the KAPI
Joshua 17 in the KBT1ETNIK
Joshua 17 in the KBV
Joshua 17 in the KJV
Joshua 17 in the KNFD
Joshua 17 in the LBA
Joshua 17 in the LBLA
Joshua 17 in the LNT
Joshua 17 in the LSV
Joshua 17 in the MAAL
Joshua 17 in the MBV
Joshua 17 in the MBV2
Joshua 17 in the MHNT
Joshua 17 in the MKNFD
Joshua 17 in the MNG
Joshua 17 in the MNT
Joshua 17 in the MNT2
Joshua 17 in the MRS1T
Joshua 17 in the NAA
Joshua 17 in the NASB
Joshua 17 in the NBLA
Joshua 17 in the NBS
Joshua 17 in the NBVTP
Joshua 17 in the NET2
Joshua 17 in the NIV11
Joshua 17 in the NNT
Joshua 17 in the NNT2
Joshua 17 in the NNT3
Joshua 17 in the PDDPT
Joshua 17 in the PFNT
Joshua 17 in the RMNT
Joshua 17 in the SBIAS
Joshua 17 in the SBIBS
Joshua 17 in the SBIBS2
Joshua 17 in the SBICS
Joshua 17 in the SBIDS
Joshua 17 in the SBIGS
Joshua 17 in the SBIHS
Joshua 17 in the SBIIS
Joshua 17 in the SBIIS2
Joshua 17 in the SBIIS3
Joshua 17 in the SBIKS
Joshua 17 in the SBIKS2
Joshua 17 in the SBIMS
Joshua 17 in the SBIOS
Joshua 17 in the SBIPS
Joshua 17 in the SBISS
Joshua 17 in the SBITS
Joshua 17 in the SBITS2
Joshua 17 in the SBITS3
Joshua 17 in the SBITS4
Joshua 17 in the SBIUS
Joshua 17 in the SBIVS
Joshua 17 in the SBT
Joshua 17 in the SBT1E
Joshua 17 in the SCHL
Joshua 17 in the SNT
Joshua 17 in the SUSU
Joshua 17 in the SUSU2
Joshua 17 in the SYNO
Joshua 17 in the TBIAOTANT
Joshua 17 in the TBT1E
Joshua 17 in the TBT1E2
Joshua 17 in the TFTIP
Joshua 17 in the TFTU
Joshua 17 in the TGNTATF3T
Joshua 17 in the THAI
Joshua 17 in the TNFD
Joshua 17 in the TNT
Joshua 17 in the TNTIK
Joshua 17 in the TNTIL
Joshua 17 in the TNTIN
Joshua 17 in the TNTIP
Joshua 17 in the TNTIZ
Joshua 17 in the TOMA
Joshua 17 in the TTENT
Joshua 17 in the UBG
Joshua 17 in the UGV
Joshua 17 in the UGV2
Joshua 17 in the UGV3
Joshua 17 in the VBL
Joshua 17 in the VDCC
Joshua 17 in the YALU
Joshua 17 in the YAPE
Joshua 17 in the YBVTP
Joshua 17 in the ZBP