Joshua 19 (BOGWICC)

1 Maere achiwiri anagwera mabanja a fuko la Simeoni. Dziko lawo linali mʼkati mwenimweni mwa dziko la Yuda. 2 Dzikolo linaphatikiza zigawo izi:Beeriseba (ndi Seba), Molada, 3 Hazari-Suwali, Bala, Ezemu, 4 Elitoladi, Betuli, Horima, 5 Zikilagi, Beti-Marikaboti, Hazari-Susa, 6 Beti-Lebaoti ndi Saruheni. Yonse pamodzi inali mizinda 13 ndi midzi yawo. 7 Panalinso mizinda inayi iyi: Aini, Rimoni, Eteri ndi Asani pamodzi ndi midzi yawo. 8 Dzikolo linaphatikizanso midzi yonse yozungulira mizinda imeneyi mpaka ku Baalati-Beeri, ndiye kuti Rama wa kummwera.Ili ndi dziko limene mabanja a fuko la Simeoni analandira kukhala lawo. 9 Cholowa cha fuko la Simeoni chinatengedwa kuchokera ku gawo la Yuda chifukwa fuko la Yuda linali lalikulu kwambiri. Izi zinachititsa fuko la Simeoni kukhala mʼkati mwenimweni mwa dziko la Yuda. 10 Maere achitatu anagwera mabanja a fuko la Zebuloni:Malire a dziko lawo anafika mpaka ku Saridi. 11 Malirewo anakwera kupita cha kumadzulo ku Marala nakafika ku Dabeseti ndi ku mtsinje wa kummawa kwa Yokineamu. 12 Kuchokera ku mbali ina ya Saridi malire anakhota kupita kummawa ku malire a Kisiloti-Tabori mpaka ku Daberati nakwera mpaka ku Yafiya. 13 Kuchokera kumeneko anabzola kulowa cha kummawa mpaka ku Gati-Heferi ndi ku Eti Kazini ndi kumaloza ku Neya njira ya ku Rimoni. 14 Mbali ya kumpoto malirewo analoza ku Hanatoni ndipo anakathera ku chigwa cha Ifita Eli. 15 Anaphatikizapo Katati, Nahalala, Simironi, Idala ndi Betelehemu. Mizinda yonse inakwana khumi ndi iwiri pamodzi ndi midzi yake. 16 Mizinda imeneyi pamodzi ndi midzi yake ndi imene mabanja a fuko la Zebuloni analandira. 17 Maere achinayi anagwera mabanja a fuko la Isakara. 18 Dziko lawo linaphatikiza zigawo izi:Yezireeli, Kesuloti, Sunemu, 19 Hafaraimu, Sioni, Anaharati, 20 Rabiti, Kisoni, Ebezi, 21 Remeti, Eni Ganimu, Eni Hada ndi Beti-Pazezi. 22 Malirewa anakafikanso ku Tabori, Sahazuma ndi Beti-Semesi ndipo anakathera ku Yorodani. Mizinda yonse inalipo 16 ndi midzi yake. 23 Mizinda imeneyi pamodzi ndi midzi yake ndiyo inali cholowa cha mabanja a fuko la Isakara. 24 Maere achisanu anagwera mabanja a fuko la Aseri. 25 Gawo lawo linaphatikizaHelikati, Hali, Beteni, Akisafu, 26 Alameleki, Amadi ndi Misali. Kumadzulo malire anafika ku Karimeli ndi Sihori Libinati. 27 Kenaka anakhotera kummawa kulowera ku Beti-Dagoni nafika ku dziko la Zebuloni ndi ku chigwa cha Ifita Eli, ndipo anapita kumpoto ku Beti-Emeki ndi Neieli. Anapitirirabe kumpoto mpaka kukafika ku Kabuli, 28 Ebroni, Rehobu, Hamoni, ndi Kana, mpaka ku Sidoni Wamkulu. 29 Kenaka malirewo anakhotera ku Rama ndi kupita ku mzinda wotetezedwa wa ku Turo. Kuchokera pamenepo malirewo anakhota kupita ku Hosa nakatulukira ku Nyanja, mʼchigawo cha Akizibu, 30 Uma, Afeki ndi Rehobu. Mizinda yonse inalipo 22 pamodzi ndi midzi yake. 31 Mizinda yonseyi pamodzi ndi midzi yake ndiyo inali cholowa cha mabanja a fuko la Aseri. 32 Maere achisanu ndi chimodzi anagwera mabanja a fuko la Nafutali. 33 Malire awo anayambira ku Helefu mpaka ku mtengo wa thundu wa ku Zaananimu, ndipo anapitirira nʼkukafika ku Adami Nekebu, Yabineeli mpaka ku Lakumi ndi kukathera ku Yorodani. 34 Tsono malirewo anakhotera kumadzulo kupita ku Azinoti-Tabori. Kuchoka kumeneko anapita ku Hukoki, modutsa Zebuloni cha kummwera, Aseri cha kumadzulo ndi mtsinje wa Yorodani cha kummawa. 35 Mizinda yotetezedwa inali Zidimi, Zeri, Hamati, Rakati, Kinereti, 36 Adama, Rama, Hazori, 37 Kedesi, Ederi, Eni Hazori, 38 Yironi, Migidali Eli, Horemu, Beti-Anati ndi Beti-Semesi. Yonse pamodzi inalipo mizinda 19 ndi midzi yake. 39 Mizinda yonseyi pamodzi ndi midzi yawo ndiyo inali cholowa cha mabanja a fuko la Nafutali. 40 Maere achisanu ndi chiwiri anagwera mabanja a fuko la Dani. 41 Gawo lawo linaphatikiza mizinda iyi:Zora, Esitaoli, Iri Semesi, 42 Saalabini, Ayaloni, Itira, 43 Eloni, Timna, Ekroni, 44 Eliteke, Gibetoni, Baalati, 45 Yehudi, Beni Beraki, Gati-Rimoni, 46 Me-Yarikoni ndi Rakoni, pamodzi ndi dera loyangʼanana ndi Yopa. 47 Anthu a fuko la Dani atalandidwa dziko lawo, anapita kukathira nkhondo Lesemu. Iwo anapha anthu ake onse, nawulandiratu mzindawo, kuwusandutsa wawo ndi kumakhalamo. Tsono anatcha mzindawo dzina loti Dani popeza ndilo linali dzina la kholo lawo. 48 Mizinda yonseyi pamodzi ndi midzi yake ndiyo inali cholowa cha mabanja a fuko la Dani. 49 Atatha kugawana zigawo zosiyanasiyana za dzikolo, Aisraeli anamupatsa Yoswa mwana wa Nuni chigawo chake. 50 Potsata zimene Yehova anawalamula, anamupatsa mzinda wa Timnati-Sera umene anawupempha. Mzindawu unali mʼdziko lamapiri la Efereimu. Iye anawumanga mzindawu ndi kukhazikikako. 51 Wansembe Eliezara, Yoswa ndi atsogoleri a mabanja onse a Israeli anagawa dziko lija zigawozigawo pogwiritsa ntchito maere pamaso pa Yehova. Izi zinachitika ku Silo pa khomo la tenti ya msonkhano. Choncho anamaliza kugawa dzikolo.

In Other Versions

Joshua 19 in the ANGEFD

Joshua 19 in the ANTPNG2D

Joshua 19 in the AS21

Joshua 19 in the BAGH

Joshua 19 in the BBPNG

Joshua 19 in the BBT1E

Joshua 19 in the BDS

Joshua 19 in the BEV

Joshua 19 in the BHAD

Joshua 19 in the BIB

Joshua 19 in the BLPT

Joshua 19 in the BNT

Joshua 19 in the BNTABOOT

Joshua 19 in the BNTLV

Joshua 19 in the BOATCB

Joshua 19 in the BOATCB2

Joshua 19 in the BOBCV

Joshua 19 in the BOCNT

Joshua 19 in the BOECS

Joshua 19 in the BOHCB

Joshua 19 in the BOHCV

Joshua 19 in the BOHLNT

Joshua 19 in the BOHNTLTAL

Joshua 19 in the BOICB

Joshua 19 in the BOILNTAP

Joshua 19 in the BOITCV

Joshua 19 in the BOKCV

Joshua 19 in the BOKCV2

Joshua 19 in the BOKHWOG

Joshua 19 in the BOKSSV

Joshua 19 in the BOLCB

Joshua 19 in the BOLCB2

Joshua 19 in the BOMCV

Joshua 19 in the BONAV

Joshua 19 in the BONCB

Joshua 19 in the BONLT

Joshua 19 in the BONUT2

Joshua 19 in the BOPLNT

Joshua 19 in the BOSCB

Joshua 19 in the BOSNC

Joshua 19 in the BOTLNT

Joshua 19 in the BOVCB

Joshua 19 in the BOYCB

Joshua 19 in the BPBB

Joshua 19 in the BPH

Joshua 19 in the BSB

Joshua 19 in the CCB

Joshua 19 in the CUV

Joshua 19 in the CUVS

Joshua 19 in the DBT

Joshua 19 in the DGDNT

Joshua 19 in the DHNT

Joshua 19 in the DNT

Joshua 19 in the ELBE

Joshua 19 in the EMTV

Joshua 19 in the ESV

Joshua 19 in the FBV

Joshua 19 in the FEB

Joshua 19 in the GGMNT

Joshua 19 in the GNT

Joshua 19 in the HARY

Joshua 19 in the HNT

Joshua 19 in the IRVA

Joshua 19 in the IRVB

Joshua 19 in the IRVG

Joshua 19 in the IRVH

Joshua 19 in the IRVK

Joshua 19 in the IRVM

Joshua 19 in the IRVM2

Joshua 19 in the IRVO

Joshua 19 in the IRVP

Joshua 19 in the IRVT

Joshua 19 in the IRVT2

Joshua 19 in the IRVU

Joshua 19 in the ISVN

Joshua 19 in the JSNT

Joshua 19 in the KAPI

Joshua 19 in the KBT1ETNIK

Joshua 19 in the KBV

Joshua 19 in the KJV

Joshua 19 in the KNFD

Joshua 19 in the LBA

Joshua 19 in the LBLA

Joshua 19 in the LNT

Joshua 19 in the LSV

Joshua 19 in the MAAL

Joshua 19 in the MBV

Joshua 19 in the MBV2

Joshua 19 in the MHNT

Joshua 19 in the MKNFD

Joshua 19 in the MNG

Joshua 19 in the MNT

Joshua 19 in the MNT2

Joshua 19 in the MRS1T

Joshua 19 in the NAA

Joshua 19 in the NASB

Joshua 19 in the NBLA

Joshua 19 in the NBS

Joshua 19 in the NBVTP

Joshua 19 in the NET2

Joshua 19 in the NIV11

Joshua 19 in the NNT

Joshua 19 in the NNT2

Joshua 19 in the NNT3

Joshua 19 in the PDDPT

Joshua 19 in the PFNT

Joshua 19 in the RMNT

Joshua 19 in the SBIAS

Joshua 19 in the SBIBS

Joshua 19 in the SBIBS2

Joshua 19 in the SBICS

Joshua 19 in the SBIDS

Joshua 19 in the SBIGS

Joshua 19 in the SBIHS

Joshua 19 in the SBIIS

Joshua 19 in the SBIIS2

Joshua 19 in the SBIIS3

Joshua 19 in the SBIKS

Joshua 19 in the SBIKS2

Joshua 19 in the SBIMS

Joshua 19 in the SBIOS

Joshua 19 in the SBIPS

Joshua 19 in the SBISS

Joshua 19 in the SBITS

Joshua 19 in the SBITS2

Joshua 19 in the SBITS3

Joshua 19 in the SBITS4

Joshua 19 in the SBIUS

Joshua 19 in the SBIVS

Joshua 19 in the SBT

Joshua 19 in the SBT1E

Joshua 19 in the SCHL

Joshua 19 in the SNT

Joshua 19 in the SUSU

Joshua 19 in the SUSU2

Joshua 19 in the SYNO

Joshua 19 in the TBIAOTANT

Joshua 19 in the TBT1E

Joshua 19 in the TBT1E2

Joshua 19 in the TFTIP

Joshua 19 in the TFTU

Joshua 19 in the TGNTATF3T

Joshua 19 in the THAI

Joshua 19 in the TNFD

Joshua 19 in the TNT

Joshua 19 in the TNTIK

Joshua 19 in the TNTIL

Joshua 19 in the TNTIN

Joshua 19 in the TNTIP

Joshua 19 in the TNTIZ

Joshua 19 in the TOMA

Joshua 19 in the TTENT

Joshua 19 in the UBG

Joshua 19 in the UGV

Joshua 19 in the UGV2

Joshua 19 in the UGV3

Joshua 19 in the VBL

Joshua 19 in the VDCC

Joshua 19 in the YALU

Joshua 19 in the YAPE

Joshua 19 in the YBVTP

Joshua 19 in the ZBP