Joshua 2 (BOGWICC)

1 Tsono Yoswa mwana wa Nuni anatuma anthu awiri okazonda dziko mwachinsinsi kuchokera ku Sitimu. Iye anawawuza kuti, “Pitani mukaone dzikolo makamaka mzinda wa Yeriko.” Kotero iwo anapita ndipo anakafika ku nyumba ya mkazi wadama dzina lake Rahabe, ndipo anagona kumeneko. 2 Mfumu ya Yeriko inawuzidwa kuti, “Aisraeli ena afika mu mzinda muno usiku uno kudzazonda dziko.” 3 Choncho Mfumu ya Yeriko inatumiza uthenga kwa Rahabe kuti, “Atulutse anthu amene abwera ku nyumba kwakowo chifukwa iwo abwera kuti adzazonde dzikoli.” 4 Koma pa nthawiyi nʼkuti mkaziyo atatenga amuna awiriwo ndi kuwabisa. Tsono anayankha kuti, “Inde, anthuwo anafikadi ku nyumba kuno. Koma sindinadziwe kumene anachokera. 5 Iwo achoka kuno ndi chisisira, chipata cha mzinda chili pafupi kutsekedwa. Ndiye sindidziwa kumene alowera. Koma mukawalondola msanga muwapeza.” 6 Koma nʼkuti atawakweza pa denga azondiwo ndi kuwabisa pansi pa mapesi a thonje amene iye anawayika pa dengapo. 7 Nthumwi za mfumu zija zitatuluka ndipo chipata chinatsekedwa. Nthumwizo zinapita kukawafunafuna azondi aja mpaka ku dooko la Yorodani. 8 Azondiwo asanagone, Rahabe anakwera pa denga 9 ndipo anawawuza kuti, “Ine ndikudziwa kuti Yehova wakupatsani dziko lino ndipo tili ndi mantha. Anthu onse a mʼdziko lino ali ndi mantha chifukwa cha inu. 10 Ife tinamva mmene Yehova anawumitsira madzi a Nyanja Yofiira inu mukufika pamene munatuluka mʼdziko la Igupto. Tamvanso zimene munachita kwa Sihoni ndi Ogi, mafumu awiri a Aamori amene ali kummawa kwa Yorodani. Inu munawawononga kotheratu. 11 Titamva zimenezi, ife tinataya mtima ndipo aliyense wa ife ali ndi mantha chifukwa cha inu. Tikudziwa kuti Yehova Mulungu wanu ndi Mulungu wa kumwamba ndi dziko lapansi. 12 Choncho mulumbire pamaso pa Yehova ndi kundipatsa chizindikiro choti mudzachitadi zimene mwalonjeza, kuti monga inu ndakuchitirani chifundo, inunso mudzachitira chifundo a pa banja la abambo anga. 13 Inu mulonjeze kuti simudzapha abambo anga ndi amayi anga, abale anga ndi alongo anga ndi mabanja awo omwe.” 14 Anthuwo anamuyankha kuti, “Ife ndife okonzeka kufa chifukwa cha inu. Ngati iwe sudzawulula zimene tachitazi, ndiye kuti ife tidzakukomera mtima ndi kusunga pangano lathu ndi iwe, Yehova akadzatipatsa dziko lino.” 15 Popeza nyumba ya Rahabe inali pa linga la mzindawo, azondi aja anatulukira pa zenera. Rahabe anawatsitsa pansi ndi chingwe. 16 Iye anawawuza kuti, “Pitani ku mapiri kuti okuthamangiraniwo asakupezeni. Mukabisale kumeneko masiku atatu mpaka iwo atabwerera, ndipo kenaka muzikapita kwanu.” 17 Anthuwo anati kwa iye, “Lonjezo limene watichititsa ifeli tidzalisungadi 18 tikadzalowa mʼdzikoli, iwe udzamangirire kansalu kofiira pa zenera limene unatitulutsira, ndi kusonkhanitsa abambo ako, amayi ako, abale ako ndi banja lako lonse mʼnyumba muno. 19 Ngati wina aliyense adzatuluka mʼnyumbamo kuti azikayendayenda mu msewu, magazi ake adzakhala pamutu pake, ife sitidzapalamula kanthu. Koma wina aliyense wokhala mʼnyumba mwakomo akadzaphedwa, mlandu udzakhala wathu. 20 Komanso iwe ukangowulula zimene ife tikuchitazi ndiye kuti ife sitidzasunga zimene talonjezazi.” 21 Rahabe anayankha kuti, “Zikhale monga mwaneneramo.” Kenaka iye anawatulutsa ndipo iwowo anapita. Pambuyo pake Rahabe anamangirira kansalu kofiira pa zenera paja. 22 Azondi aja anachoka napita ku mapiri ndipo anakhalako masiku atatu. Apa nʼkuti otumidwa ndi mfumu aja atawafunafuna ponseponse nʼkubwerera osawapeza. 23 Pambuyo pake azondi awiri aja anayamba ulendo wobwerera kwawo. Anatsika ku mapiri kuja, nawoloka mtsinje mpaka anakafika kwa Yoswa mwana wa Nuni. Ndipo anamuwuza zonse zimene zinawachitikira. 24 Iwo anati kwa Yoswa, “Ndithu, Yehova wapereka dziko lonse mʼmanja mwathu. Anthu onse kumeneko akuchita nafe mantha.”

In Other Versions

Joshua 2 in the ANGEFD

Joshua 2 in the ANTPNG2D

Joshua 2 in the AS21

Joshua 2 in the BAGH

Joshua 2 in the BBPNG

Joshua 2 in the BBT1E

Joshua 2 in the BDS

Joshua 2 in the BEV

Joshua 2 in the BHAD

Joshua 2 in the BIB

Joshua 2 in the BLPT

Joshua 2 in the BNT

Joshua 2 in the BNTABOOT

Joshua 2 in the BNTLV

Joshua 2 in the BOATCB

Joshua 2 in the BOATCB2

Joshua 2 in the BOBCV

Joshua 2 in the BOCNT

Joshua 2 in the BOECS

Joshua 2 in the BOHCB

Joshua 2 in the BOHCV

Joshua 2 in the BOHLNT

Joshua 2 in the BOHNTLTAL

Joshua 2 in the BOICB

Joshua 2 in the BOILNTAP

Joshua 2 in the BOITCV

Joshua 2 in the BOKCV

Joshua 2 in the BOKCV2

Joshua 2 in the BOKHWOG

Joshua 2 in the BOKSSV

Joshua 2 in the BOLCB

Joshua 2 in the BOLCB2

Joshua 2 in the BOMCV

Joshua 2 in the BONAV

Joshua 2 in the BONCB

Joshua 2 in the BONLT

Joshua 2 in the BONUT2

Joshua 2 in the BOPLNT

Joshua 2 in the BOSCB

Joshua 2 in the BOSNC

Joshua 2 in the BOTLNT

Joshua 2 in the BOVCB

Joshua 2 in the BOYCB

Joshua 2 in the BPBB

Joshua 2 in the BPH

Joshua 2 in the BSB

Joshua 2 in the CCB

Joshua 2 in the CUV

Joshua 2 in the CUVS

Joshua 2 in the DBT

Joshua 2 in the DGDNT

Joshua 2 in the DHNT

Joshua 2 in the DNT

Joshua 2 in the ELBE

Joshua 2 in the EMTV

Joshua 2 in the ESV

Joshua 2 in the FBV

Joshua 2 in the FEB

Joshua 2 in the GGMNT

Joshua 2 in the GNT

Joshua 2 in the HARY

Joshua 2 in the HNT

Joshua 2 in the IRVA

Joshua 2 in the IRVB

Joshua 2 in the IRVG

Joshua 2 in the IRVH

Joshua 2 in the IRVK

Joshua 2 in the IRVM

Joshua 2 in the IRVM2

Joshua 2 in the IRVO

Joshua 2 in the IRVP

Joshua 2 in the IRVT

Joshua 2 in the IRVT2

Joshua 2 in the IRVU

Joshua 2 in the ISVN

Joshua 2 in the JSNT

Joshua 2 in the KAPI

Joshua 2 in the KBT1ETNIK

Joshua 2 in the KBV

Joshua 2 in the KJV

Joshua 2 in the KNFD

Joshua 2 in the LBA

Joshua 2 in the LBLA

Joshua 2 in the LNT

Joshua 2 in the LSV

Joshua 2 in the MAAL

Joshua 2 in the MBV

Joshua 2 in the MBV2

Joshua 2 in the MHNT

Joshua 2 in the MKNFD

Joshua 2 in the MNG

Joshua 2 in the MNT

Joshua 2 in the MNT2

Joshua 2 in the MRS1T

Joshua 2 in the NAA

Joshua 2 in the NASB

Joshua 2 in the NBLA

Joshua 2 in the NBS

Joshua 2 in the NBVTP

Joshua 2 in the NET2

Joshua 2 in the NIV11

Joshua 2 in the NNT

Joshua 2 in the NNT2

Joshua 2 in the NNT3

Joshua 2 in the PDDPT

Joshua 2 in the PFNT

Joshua 2 in the RMNT

Joshua 2 in the SBIAS

Joshua 2 in the SBIBS

Joshua 2 in the SBIBS2

Joshua 2 in the SBICS

Joshua 2 in the SBIDS

Joshua 2 in the SBIGS

Joshua 2 in the SBIHS

Joshua 2 in the SBIIS

Joshua 2 in the SBIIS2

Joshua 2 in the SBIIS3

Joshua 2 in the SBIKS

Joshua 2 in the SBIKS2

Joshua 2 in the SBIMS

Joshua 2 in the SBIOS

Joshua 2 in the SBIPS

Joshua 2 in the SBISS

Joshua 2 in the SBITS

Joshua 2 in the SBITS2

Joshua 2 in the SBITS3

Joshua 2 in the SBITS4

Joshua 2 in the SBIUS

Joshua 2 in the SBIVS

Joshua 2 in the SBT

Joshua 2 in the SBT1E

Joshua 2 in the SCHL

Joshua 2 in the SNT

Joshua 2 in the SUSU

Joshua 2 in the SUSU2

Joshua 2 in the SYNO

Joshua 2 in the TBIAOTANT

Joshua 2 in the TBT1E

Joshua 2 in the TBT1E2

Joshua 2 in the TFTIP

Joshua 2 in the TFTU

Joshua 2 in the TGNTATF3T

Joshua 2 in the THAI

Joshua 2 in the TNFD

Joshua 2 in the TNT

Joshua 2 in the TNTIK

Joshua 2 in the TNTIL

Joshua 2 in the TNTIN

Joshua 2 in the TNTIP

Joshua 2 in the TNTIZ

Joshua 2 in the TOMA

Joshua 2 in the TTENT

Joshua 2 in the UBG

Joshua 2 in the UGV

Joshua 2 in the UGV2

Joshua 2 in the UGV3

Joshua 2 in the VBL

Joshua 2 in the VDCC

Joshua 2 in the YALU

Joshua 2 in the YAPE

Joshua 2 in the YBVTP

Joshua 2 in the ZBP