Joshua 3 (BOGWICC)

1 Yoswa ndi Aisraeli onse anadzuka mmamawa nanyamuka ku Sitimu kupita ku Yorodani. Iwo anagona kumeneko asanawoloke mtsinje wa Yorodaniwo. 2 Patatha masiku atatu, atsogoleri anayendera misasa yonse, 3 kulangiza anthu kuti, “Mukaona ansembe a Chilevi atanyamula Bokosi la Chipangano la Yehova Mulungu wanu, inu munyamuke pa malo ano ndi kumalitsatira. 4 Potero mudzadziwa njira yoti mudzere, popeza simunayendepo njira ino nʼkale lomwe. Koma musaliyandikire. Pakati pa inu ndi bokosilo pakhale mtunda pafupifupi kilomita imodzi.” 5 Yoswa anawuza anthu kuti, “Dzipatuleni tsono pakuti mawa Yehova adzachita zodabwitsa pakati panu.” 6 Mmawa mwake Yoswa ananena kwa ansembe kuti, “Nyamulani Bokosi la Chipangano muwoloke ndipo mukhale patsogolo pa anthu.” Motero iwo analinyamula ndi kupita patsogolo pawo. 7 Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, “Lero Ine ndidzayamba kukukweza pamaso pa Aisraeli onse kuti adziwe kuti ndili nawe monga ndinalili ndi Mose. 8 Ansembe amene akunyamula Bokosi la Chipangano uwalamule kuti, ‘Mukafika ku mtsinje wa Yorodani mulowe mu mtsinjemo ndi kuyima mʼmphepete.’ ” 9 Yoswa anati kwa Aisraeli, “Bwerani pano mudzamve mawu a Yehova Mulungu wanu. 10 Umu ndi mmene mudzadziwira kuti Mulungu wamoyo ali pakati panu. Inu mukamadzapita patsogolo Iye adzathamangitsa Akanaani, Ahiti, Ahivi, Aperezi, Agirigasi, Aamori ndi Ayebusi. 11 Pamenepo, Bokosi la Chipangano la Mbuye wa dziko lonse lapansi lidzawoloka mu Yorodani patsogolo panu. 12 Musankhe amuna khumi ndi awiri kuchokera ku fuko lililonse la Israeli. 13 Mapazi a ansembe onyamula Bokosi la Yehova, Mbuye wa dziko lapansi, akadzangoponda mu Yorodani, madzi ake onse ochokera ku mtunda adzaleka kuyenda ndipo adzayima ngati chipupa.” 14 Tsono Aisraeli anachoka ku misasa yawo kukawoloka mtsinje wa Yorodani. Ansembe onyamula Bokosi la Chipangano ndiwo anatsogolera anthuwo. 15 Nyengo imeneyi inali yokolola ndipo mtsinje wa Yorodani umakhala wodzaza. Komabe, ansembe onyamula Bokosi la Chipangano anafika ku Yorodani, ndipo atangoponda mʼmadzimo, 16 madzi ochokera ku mtunda anasiya kuyenda. Madzi a Yorodani ochokera ku mtunda anawunjikana pamodzi ngati khoma lalitali pa mtunda wautali ndithu ndi mzinda wa Adama chapafupi ndi mzinda wa Zaretani. Madzi othamangira ku nyanja ya Araba, ngakhalenso amene amachokera kuti Nyanja ya Mchere amathera pamenepo. Choncho anthu anawoloka tsidya lina moyangʼanana ndi Yeriko. 17 Ansembe onyamula Bokosi la Chipangano la Yehova anali chiyimire powuma, pakati pa Yorodani pamene Aisraeli amawoloka mpaka gulu lonse linamaliza kuwoloka powuma.

In Other Versions

Joshua 3 in the ANGEFD

Joshua 3 in the ANTPNG2D

Joshua 3 in the AS21

Joshua 3 in the BAGH

Joshua 3 in the BBPNG

Joshua 3 in the BBT1E

Joshua 3 in the BDS

Joshua 3 in the BEV

Joshua 3 in the BHAD

Joshua 3 in the BIB

Joshua 3 in the BLPT

Joshua 3 in the BNT

Joshua 3 in the BNTABOOT

Joshua 3 in the BNTLV

Joshua 3 in the BOATCB

Joshua 3 in the BOATCB2

Joshua 3 in the BOBCV

Joshua 3 in the BOCNT

Joshua 3 in the BOECS

Joshua 3 in the BOHCB

Joshua 3 in the BOHCV

Joshua 3 in the BOHLNT

Joshua 3 in the BOHNTLTAL

Joshua 3 in the BOICB

Joshua 3 in the BOILNTAP

Joshua 3 in the BOITCV

Joshua 3 in the BOKCV

Joshua 3 in the BOKCV2

Joshua 3 in the BOKHWOG

Joshua 3 in the BOKSSV

Joshua 3 in the BOLCB

Joshua 3 in the BOLCB2

Joshua 3 in the BOMCV

Joshua 3 in the BONAV

Joshua 3 in the BONCB

Joshua 3 in the BONLT

Joshua 3 in the BONUT2

Joshua 3 in the BOPLNT

Joshua 3 in the BOSCB

Joshua 3 in the BOSNC

Joshua 3 in the BOTLNT

Joshua 3 in the BOVCB

Joshua 3 in the BOYCB

Joshua 3 in the BPBB

Joshua 3 in the BPH

Joshua 3 in the BSB

Joshua 3 in the CCB

Joshua 3 in the CUV

Joshua 3 in the CUVS

Joshua 3 in the DBT

Joshua 3 in the DGDNT

Joshua 3 in the DHNT

Joshua 3 in the DNT

Joshua 3 in the ELBE

Joshua 3 in the EMTV

Joshua 3 in the ESV

Joshua 3 in the FBV

Joshua 3 in the FEB

Joshua 3 in the GGMNT

Joshua 3 in the GNT

Joshua 3 in the HARY

Joshua 3 in the HNT

Joshua 3 in the IRVA

Joshua 3 in the IRVB

Joshua 3 in the IRVG

Joshua 3 in the IRVH

Joshua 3 in the IRVK

Joshua 3 in the IRVM

Joshua 3 in the IRVM2

Joshua 3 in the IRVO

Joshua 3 in the IRVP

Joshua 3 in the IRVT

Joshua 3 in the IRVT2

Joshua 3 in the IRVU

Joshua 3 in the ISVN

Joshua 3 in the JSNT

Joshua 3 in the KAPI

Joshua 3 in the KBT1ETNIK

Joshua 3 in the KBV

Joshua 3 in the KJV

Joshua 3 in the KNFD

Joshua 3 in the LBA

Joshua 3 in the LBLA

Joshua 3 in the LNT

Joshua 3 in the LSV

Joshua 3 in the MAAL

Joshua 3 in the MBV

Joshua 3 in the MBV2

Joshua 3 in the MHNT

Joshua 3 in the MKNFD

Joshua 3 in the MNG

Joshua 3 in the MNT

Joshua 3 in the MNT2

Joshua 3 in the MRS1T

Joshua 3 in the NAA

Joshua 3 in the NASB

Joshua 3 in the NBLA

Joshua 3 in the NBS

Joshua 3 in the NBVTP

Joshua 3 in the NET2

Joshua 3 in the NIV11

Joshua 3 in the NNT

Joshua 3 in the NNT2

Joshua 3 in the NNT3

Joshua 3 in the PDDPT

Joshua 3 in the PFNT

Joshua 3 in the RMNT

Joshua 3 in the SBIAS

Joshua 3 in the SBIBS

Joshua 3 in the SBIBS2

Joshua 3 in the SBICS

Joshua 3 in the SBIDS

Joshua 3 in the SBIGS

Joshua 3 in the SBIHS

Joshua 3 in the SBIIS

Joshua 3 in the SBIIS2

Joshua 3 in the SBIIS3

Joshua 3 in the SBIKS

Joshua 3 in the SBIKS2

Joshua 3 in the SBIMS

Joshua 3 in the SBIOS

Joshua 3 in the SBIPS

Joshua 3 in the SBISS

Joshua 3 in the SBITS

Joshua 3 in the SBITS2

Joshua 3 in the SBITS3

Joshua 3 in the SBITS4

Joshua 3 in the SBIUS

Joshua 3 in the SBIVS

Joshua 3 in the SBT

Joshua 3 in the SBT1E

Joshua 3 in the SCHL

Joshua 3 in the SNT

Joshua 3 in the SUSU

Joshua 3 in the SUSU2

Joshua 3 in the SYNO

Joshua 3 in the TBIAOTANT

Joshua 3 in the TBT1E

Joshua 3 in the TBT1E2

Joshua 3 in the TFTIP

Joshua 3 in the TFTU

Joshua 3 in the TGNTATF3T

Joshua 3 in the THAI

Joshua 3 in the TNFD

Joshua 3 in the TNT

Joshua 3 in the TNTIK

Joshua 3 in the TNTIL

Joshua 3 in the TNTIN

Joshua 3 in the TNTIP

Joshua 3 in the TNTIZ

Joshua 3 in the TOMA

Joshua 3 in the TTENT

Joshua 3 in the UBG

Joshua 3 in the UGV

Joshua 3 in the UGV2

Joshua 3 in the UGV3

Joshua 3 in the VBL

Joshua 3 in the VDCC

Joshua 3 in the YALU

Joshua 3 in the YAPE

Joshua 3 in the YBVTP

Joshua 3 in the ZBP