Leviticus 21 (BOGWICC)
1 Yehova anawuza Mose kuti, “Yankhula ndi ansembe, ana a Aaroni, ndipo uwawuze kuti, ‘Wansembe asadzidetse pokhudza munthu wakufa pakati pa abale ake. 2 Koma akhoza kukhudza thupi lakufa la amayi ake, abambo ake, mwana wake wamwamuna, mwana wake wamkazi, mchimwene wake, 3 kapena mlongo wake wosakwatiwa amene amadalira iye chifukwa sanakwatiwe. Iye akhoza kudzidetsa pokhudza thupi lakufa la mchemwali wake wosakwatiwa yekha. 4 Koma wansembe asadzidetse chifukwa cha anthu amene ali nawo pa ubale obwera chifukwa cha ukwati. 5 “ ‘Ansembe asamete tsitsi kumutu kwawo kapena mʼmphepete mwa ndevu zawo, kapenanso kudzichekacheka pa thupi lawo. 6 Ayenera kukhala oyera pamaso pa Mulungu wawo ndipo asachititse manyazi dzina la Mulungu wawo. Popeza amapereka nsembe zotentha pa moto kwa Yehova, chakudya cha Mulungu wawo, iwo azikhala woyera. 7 “ ‘Asakwatire akazi amene adzidetsa ndi chiwerewere kapena akazi amene amuna awo awasudzula, chifukwa ansembe ndi oyera pamaso pa Mulungu wawo. 8 Iwo akhale oyera chifukwa amapereka nsembe kwa Mulungu wanu. Muziwaona kuti ndi oyera, popeza Ine Yehova amene ndimawayeretsa ndine woyera, nawonso akhale oyera. 9 “ ‘Ngati mwana wamkazi wa wansembe adziyipitsa pochita zachiwerewere, ndiye kuti iye akuchititsa manyazi abambo ake; mwanayo atenthedwe pa moto. 10 “ ‘Munthu amene ali mkulu wa ansembe pakati pa abale ake, amene anamudzoza pomutsanulira mafuta pamutu pake, ndiponso amene anapatulidwa pomuveka zovala zaunsembe, asalekerere tsitsi lake kapena kungʼamba zovala zake kusonyeza kuti ali pa chisoni. 11 Asalowe mʼnyumba mmene muli munthu wakufa ngakhale womwalirayo ndi amayi ake kapena abambo ake. 12 Asadzidetse potulukira kunja kwa malo opatulika popeza mafuta womupatula kukhala wansembe ali pamutu pake. Ine ndine Yehova. 13 “ ‘Iye akwatire namwali wosadziwa mwamuna. 14 Asakwatire mkazi wamasiye, mkazi wosudzulidwa, kapena mkazi wachiwerewere, koma akwatire namwali wosadziwa mwamuna pakati pa anthu a mtundu wake, 15 kuti mtundu wake usakhale wodetsedwa pakati pa abale popeza ndine Yehova, amene ndimamuyeretsa.’ ” 16 Yehova anawuza Mose kuti, 17 “Muwuze Aaroni kuti, ‘Munthu aliyense mwa zidzukulu zake ku mibado yawo yonse ikubwera akakhala ndi chilema asabwere kudzapereka nsembe kwa Mulungu wake. 18 Munthu aliyense wachilema motere: munthu wakhungu kapena wolumala miyendo, munthu wolumala nkhope kapena waziwalo zambiri, 19 munthu wa phazi lolumala kapena dzanja lolumala, 20 kapena munthu wokhota msana kapena wamfupi kwambiri, kapena wolumala maso, munthu wa nthenda yonyerenyetsa, kapena wamphere, kapenanso wophwanyika mavalo, sayenera kusendera pafupi. 21 Mdzukulu aliyense wa Aaroni wansembe, amene ali ndi chilema asadzayandikire kukapereka nsembe zopsereza kwa Yehova. Popeza kuti ali ndi chilema, asayandikire kudzapereka nsembe ya chakudya kwa Mulungu wake. 22 Koma iye angathe kudya chakudya chopatulika kwambiri chija, ngakhalenso chakudya chotsala pa nsembe zopatulika. 23 Koma chifukwa cha kulumala kwake, sayenera kuyandikira katani kapena kufika pa guwa kuti angadetse malo anga wopatulika. Ine ndine Yehova, amene ndimawayeretsa.’ ” 24 Choncho Mose anawuza Aaroni ndi ana ake pamodzi ndi Aisraeli onse zimenezi.
In Other Versions
Leviticus 21 in the ANGEFD
Leviticus 21 in the ANTPNG2D
Leviticus 21 in the AS21
Leviticus 21 in the BAGH
Leviticus 21 in the BBPNG
Leviticus 21 in the BBT1E
Leviticus 21 in the BDS
Leviticus 21 in the BEV
Leviticus 21 in the BHAD
Leviticus 21 in the BIB
Leviticus 21 in the BLPT
Leviticus 21 in the BNT
Leviticus 21 in the BNTABOOT
Leviticus 21 in the BNTLV
Leviticus 21 in the BOATCB
Leviticus 21 in the BOATCB2
Leviticus 21 in the BOBCV
Leviticus 21 in the BOCNT
Leviticus 21 in the BOECS
Leviticus 21 in the BOHCB
Leviticus 21 in the BOHCV
Leviticus 21 in the BOHLNT
Leviticus 21 in the BOHNTLTAL
Leviticus 21 in the BOICB
Leviticus 21 in the BOILNTAP
Leviticus 21 in the BOITCV
Leviticus 21 in the BOKCV
Leviticus 21 in the BOKCV2
Leviticus 21 in the BOKHWOG
Leviticus 21 in the BOKSSV
Leviticus 21 in the BOLCB
Leviticus 21 in the BOLCB2
Leviticus 21 in the BOMCV
Leviticus 21 in the BONAV
Leviticus 21 in the BONCB
Leviticus 21 in the BONLT
Leviticus 21 in the BONUT2
Leviticus 21 in the BOPLNT
Leviticus 21 in the BOSCB
Leviticus 21 in the BOSNC
Leviticus 21 in the BOTLNT
Leviticus 21 in the BOVCB
Leviticus 21 in the BOYCB
Leviticus 21 in the BPBB
Leviticus 21 in the BPH
Leviticus 21 in the BSB
Leviticus 21 in the CCB
Leviticus 21 in the CUV
Leviticus 21 in the CUVS
Leviticus 21 in the DBT
Leviticus 21 in the DGDNT
Leviticus 21 in the DHNT
Leviticus 21 in the DNT
Leviticus 21 in the ELBE
Leviticus 21 in the EMTV
Leviticus 21 in the ESV
Leviticus 21 in the FBV
Leviticus 21 in the FEB
Leviticus 21 in the GGMNT
Leviticus 21 in the GNT
Leviticus 21 in the HARY
Leviticus 21 in the HNT
Leviticus 21 in the IRVA
Leviticus 21 in the IRVB
Leviticus 21 in the IRVG
Leviticus 21 in the IRVH
Leviticus 21 in the IRVK
Leviticus 21 in the IRVM
Leviticus 21 in the IRVM2
Leviticus 21 in the IRVO
Leviticus 21 in the IRVP
Leviticus 21 in the IRVT
Leviticus 21 in the IRVT2
Leviticus 21 in the IRVU
Leviticus 21 in the ISVN
Leviticus 21 in the JSNT
Leviticus 21 in the KAPI
Leviticus 21 in the KBT1ETNIK
Leviticus 21 in the KBV
Leviticus 21 in the KJV
Leviticus 21 in the KNFD
Leviticus 21 in the LBA
Leviticus 21 in the LBLA
Leviticus 21 in the LNT
Leviticus 21 in the LSV
Leviticus 21 in the MAAL
Leviticus 21 in the MBV
Leviticus 21 in the MBV2
Leviticus 21 in the MHNT
Leviticus 21 in the MKNFD
Leviticus 21 in the MNG
Leviticus 21 in the MNT
Leviticus 21 in the MNT2
Leviticus 21 in the MRS1T
Leviticus 21 in the NAA
Leviticus 21 in the NASB
Leviticus 21 in the NBLA
Leviticus 21 in the NBS
Leviticus 21 in the NBVTP
Leviticus 21 in the NET2
Leviticus 21 in the NIV11
Leviticus 21 in the NNT
Leviticus 21 in the NNT2
Leviticus 21 in the NNT3
Leviticus 21 in the PDDPT
Leviticus 21 in the PFNT
Leviticus 21 in the RMNT
Leviticus 21 in the SBIAS
Leviticus 21 in the SBIBS
Leviticus 21 in the SBIBS2
Leviticus 21 in the SBICS
Leviticus 21 in the SBIDS
Leviticus 21 in the SBIGS
Leviticus 21 in the SBIHS
Leviticus 21 in the SBIIS
Leviticus 21 in the SBIIS2
Leviticus 21 in the SBIIS3
Leviticus 21 in the SBIKS
Leviticus 21 in the SBIKS2
Leviticus 21 in the SBIMS
Leviticus 21 in the SBIOS
Leviticus 21 in the SBIPS
Leviticus 21 in the SBISS
Leviticus 21 in the SBITS
Leviticus 21 in the SBITS2
Leviticus 21 in the SBITS3
Leviticus 21 in the SBITS4
Leviticus 21 in the SBIUS
Leviticus 21 in the SBIVS
Leviticus 21 in the SBT
Leviticus 21 in the SBT1E
Leviticus 21 in the SCHL
Leviticus 21 in the SNT
Leviticus 21 in the SUSU
Leviticus 21 in the SUSU2
Leviticus 21 in the SYNO
Leviticus 21 in the TBIAOTANT
Leviticus 21 in the TBT1E
Leviticus 21 in the TBT1E2
Leviticus 21 in the TFTIP
Leviticus 21 in the TFTU
Leviticus 21 in the TGNTATF3T
Leviticus 21 in the THAI
Leviticus 21 in the TNFD
Leviticus 21 in the TNT
Leviticus 21 in the TNTIK
Leviticus 21 in the TNTIL
Leviticus 21 in the TNTIN
Leviticus 21 in the TNTIP
Leviticus 21 in the TNTIZ
Leviticus 21 in the TOMA
Leviticus 21 in the TTENT
Leviticus 21 in the UBG
Leviticus 21 in the UGV
Leviticus 21 in the UGV2
Leviticus 21 in the UGV3
Leviticus 21 in the VBL
Leviticus 21 in the VDCC
Leviticus 21 in the YALU
Leviticus 21 in the YAPE
Leviticus 21 in the YBVTP
Leviticus 21 in the ZBP