Leviticus 9 (BOGWICC)

1 Pa tsiku lachisanu ndi chitatu Mose anayitana Aaroni, ana ake ndi akuluakulu a Aisraeli. 2 Ndipo anawuza Aaroni kuti, “Tenga mwana wangʼombe wamwamuna kuti akhale nsembe yako yopepesera machimo ndi nkhosa yayimuna kuti ikhale nsembe yopsereza. Zonsezi zikhale zopanda chilema ndipo uzipereke pamaso pa Yehova. 3 Kenaka uwawuze Aisraeli kuti, ‘Tengani mbuzi yayimuna kuti ikhale nsembe yopepesera machimo. Mutengenso mwana wangʼombe ndi mwana wankhosa. Zonsezi zikhale za chaka chimodzi ndi zopanda chilema kuti zikhale nsembe yopsereza. 4 Mutengenso ngʼombe yayimuna ndi nkhosa yayimuna kuti zikhale nsembe yachiyanjano zoti ziperekedwe pamaso pa Yehova. Pamodzi ndi izi mubwerenso ndi nsembe yachakudya yosakaniza ndi mafuta pakuti lero Yehova akuonekerani.’ ” 5 Anthu anatenga zonse zimene Mose analamula nabwera nazo pa khomo la tenti ya msonkhano. Gululo linasendera pafupi ndi kuyima pamaso pa Yehova. 6 Tsono Mose anati, “Izi ndi zimene Yehova walamula kuti muchite kuti ulemerero wa Yehova ukuonekereni.” 7 Pambuyo pake Mose anawuza Aaroni kuti, “Sendera pafupi ndi guwa ndipo upereka nsembe yako yopepesera machimo ndi nsembe yako yopsereza ndikuchita mwambo wopepesera machimo ako ndi machimo a anthu. Anthuwa apereke nsembe zawo zopepesera machimo monga momwe Yehova walamulira.” 8 Choncho Aaroni anasendera pafupi ndi guwa, napha mwana wangʼombe uja kukhala nsembe yake yopepesera machimo. 9 Ana a Aaroni anabwera ndi magazi kwa Aaroni ndipo iye anaviyika chala chake mʼmagaziwo, nawapaka pa nyanga za guwa. Magazi wotsalawo anawathira pa tsinde la guwalo. 10 Kenaka anatentha paguwapo, mafuta, impsyo pamodzi ndi mafuta amene amakuta chiwindi ngati nsembe yopepesera machimoyo, monga momwe Yehova analamulira Mose. 11 Koma nyama ndi chikopa anazitenthera kunja kwa msasa. 12 Kenaka anapha nsembe yopsereza. Ana a Aaroni atabwera ndi magazi kwa iye, Aaroniyo anawawaza mbali zonse za guwa. 13 Ana akewo anamupatsa nyama yoduladula ya nsembe yopsereza ija pamodzi ndi mutu ndipo anazitentha pa guwa. 14 Aaroni anatsuka matumbo ndi miyendo nazitentha pa guwa pamodzi ndi nsembe yopsereza ija. 15 Kenaka Aaroni anapereka zopereka za anthuwo. Anatenga mbuzi yopepesera machimo a anthuwo, yopereka chifukwa cha tchimo, nayipha ndi kuyipereka kuti ikhale yopepesera machimo monga anachitira ndi nsembe yoyamba ija. 16 Anabwera ndi nsembe yopsereza, nayipereka potsata mwambo wake. 17 Anabweranso ndi chopereka cha chakudya. Anatapa ufa dzanja limodzi ndi kutentha pa guwa, kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya mmawa ija. 18 Tsono Aaroni anapha ngʼombe ndi nkhosa yayimuna monga nsembe yachiyanjano ya anthu. Ana ake anamupatsira magazi ndipo anawawaza mbali zonse za guwa. 19 Anamupatsiranso mafuta a ngʼombeyo ndi nkhosa yayimunayo: mchira wamafuta, mafuta wokuta matumbo, impsyo ndi mafuta wokuta chiwindi. 20 Ana a Aaroni anayika mafutawo pa zidale. Pambuyo pake Aaroni anatentha mafutawo pa guwa lansembe. 21 Koma zidale ndi ntchafu ya kumanja Aaroni anaziweyula ngati chopereka choweyula pamaso pa Yehova. 22 Kenaka Aaroni anakweza manja ake pa anthuwo nawadalitsa. Ndipo atatha kupereka nsembe yopepesera machimo, nsembe yopsereza ndi nsembe yachiyanjano, anatsika pa guwapo. 23 Ndipo Mose pamodzi ndi Aaroni analowa mu tenti ya msonkhano. Atatulukamo anadalitsa anthuwo ndipo ulemerero wa Yehova unaonekera kwa anthu onse. 24 Pomwepo moto unatuluka pamaso pa Yehova niwutentha nsembe zopsereza ndi mafuta zimene zinali pa guwa. Anthu onse ataona zimenezi anafuwula mwachimwemwe ndipo anaweramitsa nkhope zawo pansi.

In Other Versions

Leviticus 9 in the ANGEFD

Leviticus 9 in the ANTPNG2D

Leviticus 9 in the AS21

Leviticus 9 in the BAGH

Leviticus 9 in the BBPNG

Leviticus 9 in the BBT1E

Leviticus 9 in the BDS

Leviticus 9 in the BEV

Leviticus 9 in the BHAD

Leviticus 9 in the BIB

Leviticus 9 in the BLPT

Leviticus 9 in the BNT

Leviticus 9 in the BNTABOOT

Leviticus 9 in the BNTLV

Leviticus 9 in the BOATCB

Leviticus 9 in the BOATCB2

Leviticus 9 in the BOBCV

Leviticus 9 in the BOCNT

Leviticus 9 in the BOECS

Leviticus 9 in the BOHCB

Leviticus 9 in the BOHCV

Leviticus 9 in the BOHLNT

Leviticus 9 in the BOHNTLTAL

Leviticus 9 in the BOICB

Leviticus 9 in the BOILNTAP

Leviticus 9 in the BOITCV

Leviticus 9 in the BOKCV

Leviticus 9 in the BOKCV2

Leviticus 9 in the BOKHWOG

Leviticus 9 in the BOKSSV

Leviticus 9 in the BOLCB

Leviticus 9 in the BOLCB2

Leviticus 9 in the BOMCV

Leviticus 9 in the BONAV

Leviticus 9 in the BONCB

Leviticus 9 in the BONLT

Leviticus 9 in the BONUT2

Leviticus 9 in the BOPLNT

Leviticus 9 in the BOSCB

Leviticus 9 in the BOSNC

Leviticus 9 in the BOTLNT

Leviticus 9 in the BOVCB

Leviticus 9 in the BOYCB

Leviticus 9 in the BPBB

Leviticus 9 in the BPH

Leviticus 9 in the BSB

Leviticus 9 in the CCB

Leviticus 9 in the CUV

Leviticus 9 in the CUVS

Leviticus 9 in the DBT

Leviticus 9 in the DGDNT

Leviticus 9 in the DHNT

Leviticus 9 in the DNT

Leviticus 9 in the ELBE

Leviticus 9 in the EMTV

Leviticus 9 in the ESV

Leviticus 9 in the FBV

Leviticus 9 in the FEB

Leviticus 9 in the GGMNT

Leviticus 9 in the GNT

Leviticus 9 in the HARY

Leviticus 9 in the HNT

Leviticus 9 in the IRVA

Leviticus 9 in the IRVB

Leviticus 9 in the IRVG

Leviticus 9 in the IRVH

Leviticus 9 in the IRVK

Leviticus 9 in the IRVM

Leviticus 9 in the IRVM2

Leviticus 9 in the IRVO

Leviticus 9 in the IRVP

Leviticus 9 in the IRVT

Leviticus 9 in the IRVT2

Leviticus 9 in the IRVU

Leviticus 9 in the ISVN

Leviticus 9 in the JSNT

Leviticus 9 in the KAPI

Leviticus 9 in the KBT1ETNIK

Leviticus 9 in the KBV

Leviticus 9 in the KJV

Leviticus 9 in the KNFD

Leviticus 9 in the LBA

Leviticus 9 in the LBLA

Leviticus 9 in the LNT

Leviticus 9 in the LSV

Leviticus 9 in the MAAL

Leviticus 9 in the MBV

Leviticus 9 in the MBV2

Leviticus 9 in the MHNT

Leviticus 9 in the MKNFD

Leviticus 9 in the MNG

Leviticus 9 in the MNT

Leviticus 9 in the MNT2

Leviticus 9 in the MRS1T

Leviticus 9 in the NAA

Leviticus 9 in the NASB

Leviticus 9 in the NBLA

Leviticus 9 in the NBS

Leviticus 9 in the NBVTP

Leviticus 9 in the NET2

Leviticus 9 in the NIV11

Leviticus 9 in the NNT

Leviticus 9 in the NNT2

Leviticus 9 in the NNT3

Leviticus 9 in the PDDPT

Leviticus 9 in the PFNT

Leviticus 9 in the RMNT

Leviticus 9 in the SBIAS

Leviticus 9 in the SBIBS

Leviticus 9 in the SBIBS2

Leviticus 9 in the SBICS

Leviticus 9 in the SBIDS

Leviticus 9 in the SBIGS

Leviticus 9 in the SBIHS

Leviticus 9 in the SBIIS

Leviticus 9 in the SBIIS2

Leviticus 9 in the SBIIS3

Leviticus 9 in the SBIKS

Leviticus 9 in the SBIKS2

Leviticus 9 in the SBIMS

Leviticus 9 in the SBIOS

Leviticus 9 in the SBIPS

Leviticus 9 in the SBISS

Leviticus 9 in the SBITS

Leviticus 9 in the SBITS2

Leviticus 9 in the SBITS3

Leviticus 9 in the SBITS4

Leviticus 9 in the SBIUS

Leviticus 9 in the SBIVS

Leviticus 9 in the SBT

Leviticus 9 in the SBT1E

Leviticus 9 in the SCHL

Leviticus 9 in the SNT

Leviticus 9 in the SUSU

Leviticus 9 in the SUSU2

Leviticus 9 in the SYNO

Leviticus 9 in the TBIAOTANT

Leviticus 9 in the TBT1E

Leviticus 9 in the TBT1E2

Leviticus 9 in the TFTIP

Leviticus 9 in the TFTU

Leviticus 9 in the TGNTATF3T

Leviticus 9 in the THAI

Leviticus 9 in the TNFD

Leviticus 9 in the TNT

Leviticus 9 in the TNTIK

Leviticus 9 in the TNTIL

Leviticus 9 in the TNTIN

Leviticus 9 in the TNTIP

Leviticus 9 in the TNTIZ

Leviticus 9 in the TOMA

Leviticus 9 in the TTENT

Leviticus 9 in the UBG

Leviticus 9 in the UGV

Leviticus 9 in the UGV2

Leviticus 9 in the UGV3

Leviticus 9 in the VBL

Leviticus 9 in the VDCC

Leviticus 9 in the YALU

Leviticus 9 in the YAPE

Leviticus 9 in the YBVTP

Leviticus 9 in the ZBP