Luke 14 (BOGWICC)

1 Pa tsiku lina la Sabata, Yesu atapita kukadya ku nyumba ya Mfarisi wodziwika, Afarisi anamulonda mosamalitsa. 2 Poteropo, patsogolo pake panali munthu amene anadwala matenda otupa mimba ndi miyendo. 3 Yesu anafunsa Afarisi ndi akatswiri amalamulo kuti, “Kodi ndi zololedwa kuchiritsa pa tsiku la Sabata kapena ayi?” 4 Koma iwo sanayankhe. Tsono atamutenga munthuyo, Iye anamuchiritsa ndipo anamuwuza kuti azipita. 5 Kenaka Iye anawafunsa kuti, “Kodi ngati mmodzi mwa inu ali ndi mwana wamwamuna kapena ngʼombe imene yagwera mʼchitsime tsiku la Sabata, kodi simungamuvuwulemo tsiku lomwelo?” 6 Ndipo iwo analibe choyankha. 7 Iye ataona momwe alendo amasankhira malo aulemu pa tebulo, Iye anawawuza fanizo ili: 8 “Pamene wina wakuyitanani ku phwando la ukwati, musakhale pa malo aulemu ayi, chifukwa mwina anayitananso munthu wina wolemekezeka kuposa inu. 9 Ngati zitatero, ndiye kuti munthu uja amene anakuyitani inu nonse awiri adzakuwuzani kuti, ‘Mupatseni munthu uyu malo anu.’ Pamenepo inu mudzachita manyazi, pokakhala malo wotsika. 10 Koma akakuyitanani, khalani pa malo otsika, kuti amene anakuyitanani uja adzakuwuzeni kuti, ‘Bwenzi, bwera udzakhale pa malo aulemu pano.’ Pamenepo inu mudzalandira ulemu pamaso pa alendo anzanu onse. 11 Pakuti aliyense wodzikuza adzamuchepetsa, ndipo aliyense wodzichepetsa adzamukweza.” 12 Kenaka Yesu anati kwa mwini malo uja, “Ukakonza chakudya chamasana kapena chamadzulo, usamayitane abwenzi ako, abale ako, anthu afuko lako kapena anzako achuma; ngati iwe utero, iwo adzakuyitananso, choncho udzalandiriratu mphotho yako. 13 Koma ukakonza phwando, itana anthu osauka, ofa ziwalo, olumala ndi osaona. 14 Pamenepo udzakhala wodala, chifukwa iwo sangakubwezere kanthu, koma Mulungu ndiye adzakubwezera pa chiukitso cha olungama.” 15 Mmodzi mwa amene amadya naye atamva izi, anati kwa Yesu, “Ndi wodala munthu amene adzadye nawo mu ufumu wa Mulungu.” 16 Yesu anayankha kuti, “Munthu wina ankakonza phwando lalikulu ndipo anayitana alendo ambiri. 17 Nthawi yaphwando itakwana anatuma wantchito wake kuti akawuze onse amene anayitanidwa kuti, ‘Bwerani, pakuti zonse zakonzeka.’ 18 “Koma onse anayamba kupereka zifukwa mofanana. Woyamba anati, ‘Ine ndangogula kumene munda, ndipo ndikuyenera kupita kuti ndikawuone. Pepani mundikhululukire.’ 19 “Wina anati, ‘Ndangogula kumene ngʼombe khumi zokoka ngolo ndipo kupita kukaziyesa. Pepani mundikhululukire.’ 20 “Wina anatinso, ‘Ine ndangokwatira kumene, choncho sinditha kubwera.’ 21 “Wantchitoyo anabwera ndikudzamuwuza bwana wakeyo zimenezi. Pamenepo mphwandoyo anapsa mtima ndipo analamula wantchito wakeyo kuti, ‘Pita msangamsanga kunja mʼmisewu ndi mʼmakwalala a mu mzinda ndipo ukabweretse osauka, ofa ziwalo, osaona ndi olumala.’ 22 “Wantchitoyo anati, ‘Bwana, zimene munanena zachitika koma malo akanalipobe.’ 23 “Ndipo mbuye uja anawuza wantchito wake kuti, ‘Pita kunja ku misewu ikuluikulu ndi kunja kwa mpanda ndipo ukawawuze kuti alowe, kuti nyumba yanga idzaze. 24 Ine ndikukuwuzani inu kuti palibe ndi mmodzi yemwe mwa anthu amene anayitanidwa adzalawa phwandolo.’ ” 25 Gulu lalikulu la anthu linkayenda naye Yesu ndipo atatembenukira kwa iwo anati, 26 “Ngati wina aliyense abwera kwa Ine ndipo sadana ndi abambo ndi amayi ake, mkazi wake ndi ana, abale ake ndi alongo ake, inde ngakhale moyo wake omwe, iye sangakhale ophunzira wanga. 27 Ndipo aliyense amene sasenza mtanda wake ndi kunditsata Ine sangakhale ophunzira wanga. 28 “Taganizani, ngati wina mwa inu akufuna kumanga nsanja, kodi iye sayamba wakhala pansi ndi kuganizira za mtengo wake kuti aone ngati ali ndi ndalama zokwanira kuti atsirizire? 29 Pakuti ngati ayika maziko ndi kulephera kutsiriza, aliyense amene adzayiona adzamuseka, 30 nanena kuti, ‘Munthu uyu anayamba kumanga koma sanathe kutsiriza.’ 31 “Kapena mfumu imene ikupita ku nkhondo kukamenyana ndi mfumu ina, kodi siyamba yakhala pansi ndi kulingalira ngati ingathe ndi anthu 10,000 kulimbana ndi amene akubwera ndi 20,000? 32 Ngati singathe, idzatuma nthumwi pomwe winayo ali kutali ndi kukapempha mgwirizano wamtendere. 33 Mʼnjira yomweyo, wina aliyense wa inu amene sasiya zonse ali nazo sangakhale ophunzira wanga. 34 “Mchere ndi wabwino, koma ngati usukuluka adzawukoleretsanso ndi chiyani? 35 Suyeneranso ngakhale mʼnthaka kapena kudzala la manyowa; umatayidwa kunja. “Amene ali ndi makutu akumva, amve.”

In Other Versions

Luke 14 in the ANGEFD

Luke 14 in the ANTPNG2D

Luke 14 in the AS21

Luke 14 in the BAGH

Luke 14 in the BBPNG

Luke 14 in the BBT1E

Luke 14 in the BDS

Luke 14 in the BEV

Luke 14 in the BHAD

Luke 14 in the BIB

Luke 14 in the BLPT

Luke 14 in the BNT

Luke 14 in the BNTABOOT

Luke 14 in the BNTLV

Luke 14 in the BOATCB

Luke 14 in the BOATCB2

Luke 14 in the BOBCV

Luke 14 in the BOCNT

Luke 14 in the BOECS

Luke 14 in the BOHCB

Luke 14 in the BOHCV

Luke 14 in the BOHLNT

Luke 14 in the BOHNTLTAL

Luke 14 in the BOICB

Luke 14 in the BOILNTAP

Luke 14 in the BOITCV

Luke 14 in the BOKCV

Luke 14 in the BOKCV2

Luke 14 in the BOKHWOG

Luke 14 in the BOKSSV

Luke 14 in the BOLCB

Luke 14 in the BOLCB2

Luke 14 in the BOMCV

Luke 14 in the BONAV

Luke 14 in the BONCB

Luke 14 in the BONLT

Luke 14 in the BONUT2

Luke 14 in the BOPLNT

Luke 14 in the BOSCB

Luke 14 in the BOSNC

Luke 14 in the BOTLNT

Luke 14 in the BOVCB

Luke 14 in the BOYCB

Luke 14 in the BPBB

Luke 14 in the BPH

Luke 14 in the BSB

Luke 14 in the CCB

Luke 14 in the CUV

Luke 14 in the CUVS

Luke 14 in the DBT

Luke 14 in the DGDNT

Luke 14 in the DHNT

Luke 14 in the DNT

Luke 14 in the ELBE

Luke 14 in the EMTV

Luke 14 in the ESV

Luke 14 in the FBV

Luke 14 in the FEB

Luke 14 in the GGMNT

Luke 14 in the GNT

Luke 14 in the HARY

Luke 14 in the HNT

Luke 14 in the IRVA

Luke 14 in the IRVB

Luke 14 in the IRVG

Luke 14 in the IRVH

Luke 14 in the IRVK

Luke 14 in the IRVM

Luke 14 in the IRVM2

Luke 14 in the IRVO

Luke 14 in the IRVP

Luke 14 in the IRVT

Luke 14 in the IRVT2

Luke 14 in the IRVU

Luke 14 in the ISVN

Luke 14 in the JSNT

Luke 14 in the KAPI

Luke 14 in the KBT1ETNIK

Luke 14 in the KBV

Luke 14 in the KJV

Luke 14 in the KNFD

Luke 14 in the LBA

Luke 14 in the LBLA

Luke 14 in the LNT

Luke 14 in the LSV

Luke 14 in the MAAL

Luke 14 in the MBV

Luke 14 in the MBV2

Luke 14 in the MHNT

Luke 14 in the MKNFD

Luke 14 in the MNG

Luke 14 in the MNT

Luke 14 in the MNT2

Luke 14 in the MRS1T

Luke 14 in the NAA

Luke 14 in the NASB

Luke 14 in the NBLA

Luke 14 in the NBS

Luke 14 in the NBVTP

Luke 14 in the NET2

Luke 14 in the NIV11

Luke 14 in the NNT

Luke 14 in the NNT2

Luke 14 in the NNT3

Luke 14 in the PDDPT

Luke 14 in the PFNT

Luke 14 in the RMNT

Luke 14 in the SBIAS

Luke 14 in the SBIBS

Luke 14 in the SBIBS2

Luke 14 in the SBICS

Luke 14 in the SBIDS

Luke 14 in the SBIGS

Luke 14 in the SBIHS

Luke 14 in the SBIIS

Luke 14 in the SBIIS2

Luke 14 in the SBIIS3

Luke 14 in the SBIKS

Luke 14 in the SBIKS2

Luke 14 in the SBIMS

Luke 14 in the SBIOS

Luke 14 in the SBIPS

Luke 14 in the SBISS

Luke 14 in the SBITS

Luke 14 in the SBITS2

Luke 14 in the SBITS3

Luke 14 in the SBITS4

Luke 14 in the SBIUS

Luke 14 in the SBIVS

Luke 14 in the SBT

Luke 14 in the SBT1E

Luke 14 in the SCHL

Luke 14 in the SNT

Luke 14 in the SUSU

Luke 14 in the SUSU2

Luke 14 in the SYNO

Luke 14 in the TBIAOTANT

Luke 14 in the TBT1E

Luke 14 in the TBT1E2

Luke 14 in the TFTIP

Luke 14 in the TFTU

Luke 14 in the TGNTATF3T

Luke 14 in the THAI

Luke 14 in the TNFD

Luke 14 in the TNT

Luke 14 in the TNTIK

Luke 14 in the TNTIL

Luke 14 in the TNTIN

Luke 14 in the TNTIP

Luke 14 in the TNTIZ

Luke 14 in the TOMA

Luke 14 in the TTENT

Luke 14 in the UBG

Luke 14 in the UGV

Luke 14 in the UGV2

Luke 14 in the UGV3

Luke 14 in the VBL

Luke 14 in the VDCC

Luke 14 in the YALU

Luke 14 in the YAPE

Luke 14 in the YBVTP

Luke 14 in the ZBP