Luke 15 (BOGWICC)

1 Tsopano amisonkho ndi “ochimwa” ankasonkhana kudzamvera mawu ake. 2 Koma Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo amangʼungʼudza nati, “Munthu uyu amalandira ochimwa ndi kudya nawo.” 3 Ndipo Yesu anawawuza fanizo ili: 4 “Tiyerekeze kuti mmodzi mwa inu ali ndi nkhosa 100 ndipo imodzi yatayika, kodi iye sangasiye 99 zija kutchire ndi kupita kukafuna yotayikayo mpaka atayipeza? 5 Ndipo iye akayipeza, amayinyamula pa phewa lake mwachimwemwe 6 ndi kupita kwawo. Kenaka amayitana anzake ndi anansi pamodzi, ndi kuti, ‘Kondwerani nane; ine ndayipeza nkhosa yanga yotayika ija.’ 7 Ine ndikukuwuzani kuti momwemonso kudzakhala chikondwerero chachikulu kumwamba chifukwa cha wochimwa mmodzi amene watembenuka mtima kusiyana ndi anthu olungama 99 amene ali otembenuka mtima kale.” 8 “Kapena tiyeni tifanizire mayi amene anali ndi ndalama zasiliva khumi ndipo imodzi nʼkutayika, kodi sayatsa nyale ndi kusesa mʼnyumba ndi kufuna mosamalitsa mpaka atayipeza? 9 Ndipo pamene wayipeza, amayitana anzake, ndi anansi pamodzi nati, ‘Kondwerani nane; ine ndayipeza ndalama yanga yotayika ija.’ 10 Momwemonso, Ine ndikukuwuzani kuti angelo a Mulungu amakondwera kwambiri chifukwa cha wochimwa mmodzi amene watembenuka mtima.” 11 Yesu anapitiriza kunena kuti, “Panali munthu amene anali ndi ana aamuna awiri. 12 Wamngʼonoyo anati kwa abambo ake, ‘Abambo, patseni gawo langa la chuma chanu.’ Ndipo iye anawagawira awiriwo chuma chawo. 13 “Pasanapite nthawi, wamngʼonoyo anasonkhanitsa chuma chake chonse, napita ku dziko lakutali ndipo kumeneko anayamba kumwaza chuma chake mʼnjira zachitayiko. 14 Iye atawononga zonse, kunagwa njala yoopsa mʼdziko lonselo ndipo anayamba kusauka. 15 Iye anapita kwa nzika ina ya dzikolo nakakhala naye ndi kumagwira ntchito, amene anamutumiza ku munda kukadyetsa nkhumba. 16 Iye analakalaka atakhutitsa mimba yake ndi makoko amene nkhumbazo zinkadya, koma panalibe wina amene anamupatsa kanthu. 17 “Maganizo ake atabweramo, iye anati, ‘Ndi antchito angati a abambo anga amene ali ndi chakudya chimene amadya nʼkutsalako ndipo ine ndili pano kufa ndi njala! 18 Ine ndinyamuka ndi kubwerera kwa abambo anga ndipo ndikati kwa iwo: abambo, ine ndachimwira kumwamba ndi kwa inu. 19 Ndine wosayeneranso kutchedwa mwana wanu; munditenge ngati mmodzi wa antchito anu.’ 20 Ndipo iye ananyamuka ndi kupita kwa abambo ake. “Koma iye akanali patali, abambo ake anamuona ndipo anamvera chisoni; anathamangira mwanayo, namukumbatira ndi kupsompsona. 21 “Mwanayo anati, ‘Abambo, ine ndachimwira kumwamba ndi inunso. Ine sindiyenera konse kutchedwa mwana wanu.’ 22 “Koma abambowo anati kwa antchito ake, ‘Fulumirani! Bweretsani mkanjo wabwino kwambiri ndipo mumuveke. Muvekeni mphete ndi nsapato. 23 Bweretsani mwana wangʼombe wonenepa ndipo iphani. Tiyeni tikhale ndi phwando ndi kukondwerera. 24 Pakuti mwana wangayu anali wakufa, ndipo ali ndi moyonso; iye anatayika ndipo wapezeka.’ Chomwecho anayamba kukondwerera. 25 “Nthawi imeneyi, mwana wake wamkulu uja anali ku munda. Iye atafika pafupi ndi nyumba, anamva anthu akuyimba ndi kuvina. 26 Ndipo iye anayitana mmodzi wa antchito, namufunsa chimene chimachitika. 27 Iye anayankha kuti, ‘Mʼbale wako wabwera ndipo abambo ako apha mwana wangʼombe wonenepa chifukwa wabwera wamoyo ndipo ali bwino.’ 28 “Mwana wamkulu anakwiya ndipo anakana kulowa. Chomwecho abambo ake anatuluka ndi kumudandaulira. 29 Koma iye anayankha abambo ake kuti, ‘Taonani! Zaka zonsezi ndakhala ndikukutumikirani kugwira ntchito yowawa ndipo palibe pamene sindinamvere malamulo anu. Koma inu simunandipatse ngakhale mwana wambuzi kuti ine ndichite phwando ndi anzanga. 30 Koma pamene mwana wanu uyu amene wawononga chuma chanu ndi achiwerewere wabwera ku nyumba, inu mwamuphera mwana wangʼombe wonenepa.’ ” 31 Abambowo anati, “Mwana wanga, iwe umakhala ndi ine nthawi zonse ndipo zonse ndili nazo ndi zako. 32 Koma tinayenera kukondwera ndi kusangalala, chifukwa mʼbale wako uyu anali wakufa ndipo ali ndi moyonso; iye anali wotayika ndipo wapezeka.”

In Other Versions

Luke 15 in the ANGEFD

Luke 15 in the ANTPNG2D

Luke 15 in the AS21

Luke 15 in the BAGH

Luke 15 in the BBPNG

Luke 15 in the BBT1E

Luke 15 in the BDS

Luke 15 in the BEV

Luke 15 in the BHAD

Luke 15 in the BIB

Luke 15 in the BLPT

Luke 15 in the BNT

Luke 15 in the BNTABOOT

Luke 15 in the BNTLV

Luke 15 in the BOATCB

Luke 15 in the BOATCB2

Luke 15 in the BOBCV

Luke 15 in the BOCNT

Luke 15 in the BOECS

Luke 15 in the BOHCB

Luke 15 in the BOHCV

Luke 15 in the BOHLNT

Luke 15 in the BOHNTLTAL

Luke 15 in the BOICB

Luke 15 in the BOILNTAP

Luke 15 in the BOITCV

Luke 15 in the BOKCV

Luke 15 in the BOKCV2

Luke 15 in the BOKHWOG

Luke 15 in the BOKSSV

Luke 15 in the BOLCB

Luke 15 in the BOLCB2

Luke 15 in the BOMCV

Luke 15 in the BONAV

Luke 15 in the BONCB

Luke 15 in the BONLT

Luke 15 in the BONUT2

Luke 15 in the BOPLNT

Luke 15 in the BOSCB

Luke 15 in the BOSNC

Luke 15 in the BOTLNT

Luke 15 in the BOVCB

Luke 15 in the BOYCB

Luke 15 in the BPBB

Luke 15 in the BPH

Luke 15 in the BSB

Luke 15 in the CCB

Luke 15 in the CUV

Luke 15 in the CUVS

Luke 15 in the DBT

Luke 15 in the DGDNT

Luke 15 in the DHNT

Luke 15 in the DNT

Luke 15 in the ELBE

Luke 15 in the EMTV

Luke 15 in the ESV

Luke 15 in the FBV

Luke 15 in the FEB

Luke 15 in the GGMNT

Luke 15 in the GNT

Luke 15 in the HARY

Luke 15 in the HNT

Luke 15 in the IRVA

Luke 15 in the IRVB

Luke 15 in the IRVG

Luke 15 in the IRVH

Luke 15 in the IRVK

Luke 15 in the IRVM

Luke 15 in the IRVM2

Luke 15 in the IRVO

Luke 15 in the IRVP

Luke 15 in the IRVT

Luke 15 in the IRVT2

Luke 15 in the IRVU

Luke 15 in the ISVN

Luke 15 in the JSNT

Luke 15 in the KAPI

Luke 15 in the KBT1ETNIK

Luke 15 in the KBV

Luke 15 in the KJV

Luke 15 in the KNFD

Luke 15 in the LBA

Luke 15 in the LBLA

Luke 15 in the LNT

Luke 15 in the LSV

Luke 15 in the MAAL

Luke 15 in the MBV

Luke 15 in the MBV2

Luke 15 in the MHNT

Luke 15 in the MKNFD

Luke 15 in the MNG

Luke 15 in the MNT

Luke 15 in the MNT2

Luke 15 in the MRS1T

Luke 15 in the NAA

Luke 15 in the NASB

Luke 15 in the NBLA

Luke 15 in the NBS

Luke 15 in the NBVTP

Luke 15 in the NET2

Luke 15 in the NIV11

Luke 15 in the NNT

Luke 15 in the NNT2

Luke 15 in the NNT3

Luke 15 in the PDDPT

Luke 15 in the PFNT

Luke 15 in the RMNT

Luke 15 in the SBIAS

Luke 15 in the SBIBS

Luke 15 in the SBIBS2

Luke 15 in the SBICS

Luke 15 in the SBIDS

Luke 15 in the SBIGS

Luke 15 in the SBIHS

Luke 15 in the SBIIS

Luke 15 in the SBIIS2

Luke 15 in the SBIIS3

Luke 15 in the SBIKS

Luke 15 in the SBIKS2

Luke 15 in the SBIMS

Luke 15 in the SBIOS

Luke 15 in the SBIPS

Luke 15 in the SBISS

Luke 15 in the SBITS

Luke 15 in the SBITS2

Luke 15 in the SBITS3

Luke 15 in the SBITS4

Luke 15 in the SBIUS

Luke 15 in the SBIVS

Luke 15 in the SBT

Luke 15 in the SBT1E

Luke 15 in the SCHL

Luke 15 in the SNT

Luke 15 in the SUSU

Luke 15 in the SUSU2

Luke 15 in the SYNO

Luke 15 in the TBIAOTANT

Luke 15 in the TBT1E

Luke 15 in the TBT1E2

Luke 15 in the TFTIP

Luke 15 in the TFTU

Luke 15 in the TGNTATF3T

Luke 15 in the THAI

Luke 15 in the TNFD

Luke 15 in the TNT

Luke 15 in the TNTIK

Luke 15 in the TNTIL

Luke 15 in the TNTIN

Luke 15 in the TNTIP

Luke 15 in the TNTIZ

Luke 15 in the TOMA

Luke 15 in the TTENT

Luke 15 in the UBG

Luke 15 in the UGV

Luke 15 in the UGV2

Luke 15 in the UGV3

Luke 15 in the VBL

Luke 15 in the VDCC

Luke 15 in the YALU

Luke 15 in the YAPE

Luke 15 in the YBVTP

Luke 15 in the ZBP