Malachi 2 (BOGWICC)
1 “Tsono chenjezo ili ndi la inu, inu ansembe.” 2 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ngati simumvera, ndipo ngati simulemekeza dzina langa mʼmitima mwanu, ndidzakutembererani ndipo madalitso onse munawalandira ndidzawatemberera. Ndithu, ndawatemberera kale, chifukwa simunalemekeze Ine mʼmitima mwanu.” 3 “Ine ndidzalanga zidzukulu zanu chifukwa cha inu; ndidzakupakani kumaso ndowe za nsembe zanu zachikondwerero, ndipo ndidzakutayani pamodzi ndi ndowezo.” 4 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Apo mudzadziwa kuti Ine ndatumiza chenjezoli kuti pangano langa ndi Levi lipitirire. 5 Ine ndinali naye pa pangano, pangano lopatsa moyo ndi mtendere, ndipo ndinamupatsa zimenezi kuti azindiopa, ndipo anandiopadi ndi kulemekeza dzina langa. 6 Pakamwa pake pankatuluka malangizo woona, ndipo pa milomo yake sipanapezeke chinyengo. Iye anayenda nane mwamtendere ndi molungama mtima, ndipo anabweza anthu ambiri mʼnjira zawo zauchimo. 7 “Pakuti wansembe ayenera kukhala ndi chidziwitso, ndipo anthu ayenera kufunafuna malangizo kuchokera kwa iye, popeza iye ndi mthenga wa Yehova Wamphamvuzonse. 8 Koma inu mwasiya njira yanga ndipo mwapunthwitsa anthu ambiri ndi ziphunzitso zanu; mwayipitsa pangano langa ndi Levi,” akutero Yehova Wamphamvuzonse. 9 “Choncho Ine ndachititsa kuti munyozedwe ndi kuchititsidwa manyazi pamaso pa anthu onse, chifukwa simunatsate njira zanga koma mwakhala mukuonetsa kukondera pa nkhani za malamulo.” 10 Kodi sitili naye Atate mmodzi tonsefe? Kodi anatilenga si Mulungu mmodzi? Chifukwa chiyani tikudetsa pangano la makolo athu posamakhulupirirana wina ndi mnzake? 11 Yuda waleka kukhulupirika. Chinthu chonyansa chachitika mu Israeli ndi mu Yerusalemu: Yuda wayipitsa malo opatulika amene Yehova amawakonda, pokwatira mkazi wopembedza mulungu wachilendo. 12 Ndipo wina aliyense wochita zimenezi, kaya munthuyo ndi wotani, Yehova amuchotse ku banja la Yakobo, ngakhale atabweretsa zopereka kwa Yehova Wamphamvuzonse. 13 China chimene mumachita ndi ichi: Mumakhathamiritsa guwa lansembe la Yehova ndi misozi. Mumalira ndi kufuwula kwambiri chifukwa Iye amakana kuyangʼana nsembe zanu, kapena kulandira mokondwera nsembe za mʼmanja mwanu. 14 Inu mukufunsa kuti, “Chifukwa chake nʼchiyani?” Chifukwa chake nʼchakuti Yehova ndi mboni ya pangano limene unachita ndi mkazi wa unyamata wako, chifukwa sunakhulupirike kwa iye, ngakhale kuti iyeyo ndiye mnzako, ndi mkazi wako mwapangano. 15 Kodi Yehova sanawalenge iwo ngati munthu mmodzi? Ndi ake mʼthupi ndi mu mzimu. Nʼchifukwa chiyani ali mmodzi? Chifukwa Iye amafuna ana opembedza Mulungu. Motero samala moyo wako wauzimu, ndipo usakhale wosakhulupirika kwa mkazi wa unyamata wako. 16 Yehova Mulungu wa Israeli akuti, “Ndimadana ndi kulekana ukwati. Ndimadana ndi munthu wochita zankhanza zotere kwa mkazi wake,” akutero Yehova Wamphamvuzonse.Choncho tetezani mzimu wanu, ndipo musakhale osakhulupirika. 17 Mwamutopetsa Yehova ndi zoyankhula zanu.Inu mukufunsa kuti, “Kodi tamutopetsa bwanji?”Mwamutopetsa ponena kuti, “Aliyense amene amachita zoyipa ndi wabwino pamaso pa Yehova ndipo iye amakondwera naye” kapena pofunsa kuti, “Ali kuti Mulungu woweruza mwachilungamo?”
In Other Versions
Malachi 2 in the ANGEFD
Malachi 2 in the ANTPNG2D
Malachi 2 in the AS21
Malachi 2 in the BAGH
Malachi 2 in the BBPNG
Malachi 2 in the BBT1E
Malachi 2 in the BDS
Malachi 2 in the BEV
Malachi 2 in the BHAD
Malachi 2 in the BIB
Malachi 2 in the BLPT
Malachi 2 in the BNT
Malachi 2 in the BNTABOOT
Malachi 2 in the BNTLV
Malachi 2 in the BOATCB
Malachi 2 in the BOATCB2
Malachi 2 in the BOBCV
Malachi 2 in the BOCNT
Malachi 2 in the BOECS
Malachi 2 in the BOHCB
Malachi 2 in the BOHCV
Malachi 2 in the BOHLNT
Malachi 2 in the BOHNTLTAL
Malachi 2 in the BOICB
Malachi 2 in the BOILNTAP
Malachi 2 in the BOITCV
Malachi 2 in the BOKCV
Malachi 2 in the BOKCV2
Malachi 2 in the BOKHWOG
Malachi 2 in the BOKSSV
Malachi 2 in the BOLCB
Malachi 2 in the BOLCB2
Malachi 2 in the BOMCV
Malachi 2 in the BONAV
Malachi 2 in the BONCB
Malachi 2 in the BONLT
Malachi 2 in the BONUT2
Malachi 2 in the BOPLNT
Malachi 2 in the BOSCB
Malachi 2 in the BOSNC
Malachi 2 in the BOTLNT
Malachi 2 in the BOVCB
Malachi 2 in the BOYCB
Malachi 2 in the BPBB
Malachi 2 in the BPH
Malachi 2 in the BSB
Malachi 2 in the CCB
Malachi 2 in the CUV
Malachi 2 in the CUVS
Malachi 2 in the DBT
Malachi 2 in the DGDNT
Malachi 2 in the DHNT
Malachi 2 in the DNT
Malachi 2 in the ELBE
Malachi 2 in the EMTV
Malachi 2 in the ESV
Malachi 2 in the FBV
Malachi 2 in the FEB
Malachi 2 in the GGMNT
Malachi 2 in the GNT
Malachi 2 in the HARY
Malachi 2 in the HNT
Malachi 2 in the IRVA
Malachi 2 in the IRVB
Malachi 2 in the IRVG
Malachi 2 in the IRVH
Malachi 2 in the IRVK
Malachi 2 in the IRVM
Malachi 2 in the IRVM2
Malachi 2 in the IRVO
Malachi 2 in the IRVP
Malachi 2 in the IRVT
Malachi 2 in the IRVT2
Malachi 2 in the IRVU
Malachi 2 in the ISVN
Malachi 2 in the JSNT
Malachi 2 in the KAPI
Malachi 2 in the KBT1ETNIK
Malachi 2 in the KBV
Malachi 2 in the KJV
Malachi 2 in the KNFD
Malachi 2 in the LBA
Malachi 2 in the LBLA
Malachi 2 in the LNT
Malachi 2 in the LSV
Malachi 2 in the MAAL
Malachi 2 in the MBV
Malachi 2 in the MBV2
Malachi 2 in the MHNT
Malachi 2 in the MKNFD
Malachi 2 in the MNG
Malachi 2 in the MNT
Malachi 2 in the MNT2
Malachi 2 in the MRS1T
Malachi 2 in the NAA
Malachi 2 in the NASB
Malachi 2 in the NBLA
Malachi 2 in the NBS
Malachi 2 in the NBVTP
Malachi 2 in the NET2
Malachi 2 in the NIV11
Malachi 2 in the NNT
Malachi 2 in the NNT2
Malachi 2 in the NNT3
Malachi 2 in the PDDPT
Malachi 2 in the PFNT
Malachi 2 in the RMNT
Malachi 2 in the SBIAS
Malachi 2 in the SBIBS
Malachi 2 in the SBIBS2
Malachi 2 in the SBICS
Malachi 2 in the SBIDS
Malachi 2 in the SBIGS
Malachi 2 in the SBIHS
Malachi 2 in the SBIIS
Malachi 2 in the SBIIS2
Malachi 2 in the SBIIS3
Malachi 2 in the SBIKS
Malachi 2 in the SBIKS2
Malachi 2 in the SBIMS
Malachi 2 in the SBIOS
Malachi 2 in the SBIPS
Malachi 2 in the SBISS
Malachi 2 in the SBITS
Malachi 2 in the SBITS2
Malachi 2 in the SBITS3
Malachi 2 in the SBITS4
Malachi 2 in the SBIUS
Malachi 2 in the SBIVS
Malachi 2 in the SBT
Malachi 2 in the SBT1E
Malachi 2 in the SCHL
Malachi 2 in the SNT
Malachi 2 in the SUSU
Malachi 2 in the SUSU2
Malachi 2 in the SYNO
Malachi 2 in the TBIAOTANT
Malachi 2 in the TBT1E
Malachi 2 in the TBT1E2
Malachi 2 in the TFTIP
Malachi 2 in the TFTU
Malachi 2 in the TGNTATF3T
Malachi 2 in the THAI
Malachi 2 in the TNFD
Malachi 2 in the TNT
Malachi 2 in the TNTIK
Malachi 2 in the TNTIL
Malachi 2 in the TNTIN
Malachi 2 in the TNTIP
Malachi 2 in the TNTIZ
Malachi 2 in the TOMA
Malachi 2 in the TTENT
Malachi 2 in the UBG
Malachi 2 in the UGV
Malachi 2 in the UGV2
Malachi 2 in the UGV3
Malachi 2 in the VBL
Malachi 2 in the VDCC
Malachi 2 in the YALU
Malachi 2 in the YAPE
Malachi 2 in the YBVTP
Malachi 2 in the ZBP