Matthew 16 (BOGWICC)
1 Afarisi ndi Asaduki anabwera kwa Yesu ndi kumuyesa pomufunsa kuti awaonetse chizindikiro chochokera kumwamba. 2 Iye anayankha kuti, “Kunja kukamada, inu mumati, kudzakhala nyengo yabwino popeza thambo ndi lofiira. 3 Ndipo mmawa mumati, ‘Lero kudzakhala mvula yamphepo popeza thambo ndi lofiira ndi mitambo ya mvula.’ Inu mumadziwa kutanthauzira maonekedwe a thambo koma simungathe kutanthauzira zizindikiro za nthawi. 4 Mʼbado woyipa ndi wachigololo umafuna chizindikiro chodabwitsa koma palibe ngakhale chimodzi chidzapatsidwa kupatula chizindikiro cha Yona.” Pamenepo Yesu anawasiya nachoka. 5 Koma atawoloka nyanja, ophunzira anayiwala kutenga buledi. 6 Yesu anawawuza kuti, “Chenjerani, khalani tcheru ndi yisiti wa Afarisi ndi Asaduki.” 7 Iwo anakambirana pakati pawo za izi ndipo anati, “Ichi nʼchifukwa chakuti sitinatenge buledi aliyense.” 8 Yesu atadziwa zokambirana zawo, anawafunsa kuti, “Chifukwa chiyani mukukambirana zakuti, ‘mulibe buledi?’ Inu achikhulupiriro chochepa. 9 Kodi inu simukumvetsetsabe? Kodi simukukumbukira za buledi musanu amene anadya anthu 5,000 ndi madengu amene munadzaza? 10 Kapena buledi musanu ndi muwiri amene anadya anthu 4,000, nanga ndi madengu angati amene munadzaza? 11 Zitheka bwanji kuti inu simukumvetsetsa kuti Ine sindinkayankhula nanu za buledi? Koma inu chenjerani ndi yisiti wa Afarisi ndi Asaduki.” 12 Kenaka iwo anazindikira kuti Iye samawawuza kuti achenjere ndi yisiti wa buledi koma ndi chiphunzitso cha Afarisi ndi Asaduki. 13 Yesu atafika ku chigawo cha Kaisareya Filipo, Iye anafunsa ophunzira ake kuti, “Kodi anthu amati Mwana wa Munthu ndi ndani?” 14 Iwo anayankha kuti, “Ena amati ndi Yohane Mʼbatizi; ena amati ndi Eliya; komanso ena amati Yeremiya kapena mmodzi wa aneneri.” 15 Iye anafunsa kuti, “Nanga inuyo mumati ndine yani?” 16 Simoni Petro anayankha kuti, “Inu ndinu Khristu, Mwana wa Mulungu wamoyo.” 17 Yesu anati kwa iye, “Ndiwe wodala Simoni mwana wa Yona, popeza si munthu amene anakuwululira izi koma Atate anga akumwamba. 18 Ndipo Ine ndikuwuza iwe kuti ndiwe Petro ndipo pa thanthwe ili Ine ndidzamangapo mpingo wanga ndipo makomo a ku gehena sadzawugonjetsa. 19 Ine ndidzakupatsa makiyi a Ufumu wakumwamba, ndipo chilichonse chimene iwe udzachimanga pansi pano chidzamangidwanso kumwamba.” 20 Pamenepo Iye anachenjeza ophunzira ake kuti asawuze wina aliyense kuti ndi Khristu. 21 Kuyambira nthawi imeneyo Yesu anayamba kuwafotokozera ophunzira ake kuti Iye ayenera kupita ku Yerusalemu ndi kukazunzidwa kwambiri mʼmanja mwa akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo kuti ayenera kuphedwa, ndi kuti tsiku lachitatu adzaukitsidwa. 22 Petro anamutengera Iye pambali nayamba kumudzudzula kuti, “Dzichitireni chifundo Ambuye, sizingachitike kwa Inu ayi.” 23 Yesu anatembenuka nati kwa Petro, “Choka pamaso panga Satana! Iwe ndi chokhumudwitsa kwa Ine; iwe suganizira zinthu za Mulungu koma zinthu za anthu.” 24 Pamenepo Yesu anati kwa ophunzira ake, “Ngati wina aliyense abwera pambuyo panga ayenera kudzikana ndi kutenga mtanda wake ndi kunditsata Ine. 25 Pakuti aliyense amene afuna kupulumutsa moyo wake adzawutaya koma aliyense amene ataya moyo wake chifukwa cha Ine adzawupeza. 26 Kodi munthu adzapindula chiyani ngati atapeza zonse za dziko lapansi nataya moyo wake? Kapena munthu angapereke chiyani chosinthana ndi moyo wake? 27 Pakuti Mwana wa Munthu adzabwera mu ulemerero wa Atate ake ndi angelo ake ndipo pamenepo Iye adzapereka mphotho kwa munthu mofanana ndi zimene anachita. 28 “Ine ndikuwuzani inu choonadi, ena amene akuyimirira pano sadzalawa imfa asanaone Mwana wa Munthu akudza mu ufumu.”
In Other Versions
Matthew 16 in the ANGEFD
Matthew 16 in the ANTPNG2D
Matthew 16 in the AS21
Matthew 16 in the BAGH
Matthew 16 in the BBPNG
Matthew 16 in the BBT1E
Matthew 16 in the BDS
Matthew 16 in the BEV
Matthew 16 in the BHAD
Matthew 16 in the BIB
Matthew 16 in the BLPT
Matthew 16 in the BNT
Matthew 16 in the BNTABOOT
Matthew 16 in the BNTLV
Matthew 16 in the BOATCB
Matthew 16 in the BOATCB2
Matthew 16 in the BOBCV
Matthew 16 in the BOCNT
Matthew 16 in the BOECS
Matthew 16 in the BOHCB
Matthew 16 in the BOHCV
Matthew 16 in the BOHLNT
Matthew 16 in the BOHNTLTAL
Matthew 16 in the BOICB
Matthew 16 in the BOILNTAP
Matthew 16 in the BOITCV
Matthew 16 in the BOKCV
Matthew 16 in the BOKCV2
Matthew 16 in the BOKHWOG
Matthew 16 in the BOKSSV
Matthew 16 in the BOLCB
Matthew 16 in the BOLCB2
Matthew 16 in the BOMCV
Matthew 16 in the BONAV
Matthew 16 in the BONCB
Matthew 16 in the BONLT
Matthew 16 in the BONUT2
Matthew 16 in the BOPLNT
Matthew 16 in the BOSCB
Matthew 16 in the BOSNC
Matthew 16 in the BOTLNT
Matthew 16 in the BOVCB
Matthew 16 in the BOYCB
Matthew 16 in the BPBB
Matthew 16 in the BPH
Matthew 16 in the BSB
Matthew 16 in the CCB
Matthew 16 in the CUV
Matthew 16 in the CUVS
Matthew 16 in the DBT
Matthew 16 in the DGDNT
Matthew 16 in the DHNT
Matthew 16 in the DNT
Matthew 16 in the ELBE
Matthew 16 in the EMTV
Matthew 16 in the ESV
Matthew 16 in the FBV
Matthew 16 in the FEB
Matthew 16 in the GGMNT
Matthew 16 in the GNT
Matthew 16 in the HARY
Matthew 16 in the HNT
Matthew 16 in the IRVA
Matthew 16 in the IRVB
Matthew 16 in the IRVG
Matthew 16 in the IRVH
Matthew 16 in the IRVK
Matthew 16 in the IRVM
Matthew 16 in the IRVM2
Matthew 16 in the IRVO
Matthew 16 in the IRVP
Matthew 16 in the IRVT
Matthew 16 in the IRVT2
Matthew 16 in the IRVU
Matthew 16 in the ISVN
Matthew 16 in the JSNT
Matthew 16 in the KAPI
Matthew 16 in the KBT1ETNIK
Matthew 16 in the KBV
Matthew 16 in the KJV
Matthew 16 in the KNFD
Matthew 16 in the LBA
Matthew 16 in the LBLA
Matthew 16 in the LNT
Matthew 16 in the LSV
Matthew 16 in the MAAL
Matthew 16 in the MBV
Matthew 16 in the MBV2
Matthew 16 in the MHNT
Matthew 16 in the MKNFD
Matthew 16 in the MNG
Matthew 16 in the MNT
Matthew 16 in the MNT2
Matthew 16 in the MRS1T
Matthew 16 in the NAA
Matthew 16 in the NASB
Matthew 16 in the NBLA
Matthew 16 in the NBS
Matthew 16 in the NBVTP
Matthew 16 in the NET2
Matthew 16 in the NIV11
Matthew 16 in the NNT
Matthew 16 in the NNT2
Matthew 16 in the NNT3
Matthew 16 in the PDDPT
Matthew 16 in the PFNT
Matthew 16 in the RMNT
Matthew 16 in the SBIAS
Matthew 16 in the SBIBS
Matthew 16 in the SBIBS2
Matthew 16 in the SBICS
Matthew 16 in the SBIDS
Matthew 16 in the SBIGS
Matthew 16 in the SBIHS
Matthew 16 in the SBIIS
Matthew 16 in the SBIIS2
Matthew 16 in the SBIIS3
Matthew 16 in the SBIKS
Matthew 16 in the SBIKS2
Matthew 16 in the SBIMS
Matthew 16 in the SBIOS
Matthew 16 in the SBIPS
Matthew 16 in the SBISS
Matthew 16 in the SBITS
Matthew 16 in the SBITS2
Matthew 16 in the SBITS3
Matthew 16 in the SBITS4
Matthew 16 in the SBIUS
Matthew 16 in the SBIVS
Matthew 16 in the SBT
Matthew 16 in the SBT1E
Matthew 16 in the SCHL
Matthew 16 in the SNT
Matthew 16 in the SUSU
Matthew 16 in the SUSU2
Matthew 16 in the SYNO
Matthew 16 in the TBIAOTANT
Matthew 16 in the TBT1E
Matthew 16 in the TBT1E2
Matthew 16 in the TFTIP
Matthew 16 in the TFTU
Matthew 16 in the TGNTATF3T
Matthew 16 in the THAI
Matthew 16 in the TNFD
Matthew 16 in the TNT
Matthew 16 in the TNTIK
Matthew 16 in the TNTIL
Matthew 16 in the TNTIN
Matthew 16 in the TNTIP
Matthew 16 in the TNTIZ
Matthew 16 in the TOMA
Matthew 16 in the TTENT
Matthew 16 in the UBG
Matthew 16 in the UGV
Matthew 16 in the UGV2
Matthew 16 in the UGV3
Matthew 16 in the VBL
Matthew 16 in the VDCC
Matthew 16 in the YALU
Matthew 16 in the YAPE
Matthew 16 in the YBVTP
Matthew 16 in the ZBP