Matthew 21 (BOGWICC)

1 Akuyandikira ku Yerusalemu anafika ku Betifage pa phiri la Olivi, Yesu anatumiza ophunzira awiri, 2 nawawuza kuti, “Pitani ku mudzi uli patsogolo panu, ndipo mukakangolowa mʼmenemo mukapeza bulu womangidwa ali ndi mwana pa mbali pake. Mukawamasule ndipo mubwere nawo kwa Ine. 3 Wina akakayankhula, mukamuwuze kuti Ambuye akuwafuna, ndipo adzawatumiza nthawi yomweyo.” 4 Izi zinachitika kukwaniritsa zimene zinayankhulidwa ndi mneneri: 5 “Uza mwana wamkazi wa Ziyoni,taona, mfumu yako ikubwera kwa iwe,yofatsa ndi yokwera pa bulu,pa kamwana ka bulu, mwana wa nyama yonyamula katundu.” 6 Ophunzirawo anapita nachita monga Yesu anawalamulira. 7 Anabweretsa bulu ndi mwana wake, nayala zovala zawo pa abuluwo, ndipo Yesu anakwerapo. 8 Gulu lalikulu la anthu linayala zovala zawo mu msewu pamene ena anadula nthambi zamitengo ndi kuziyala mu msewumo. 9 Magulu amene anali patsogolo pake ndi amene amamutsatira anafuwula kuti,“Hosana Mwana wa Davide!” “Wodala Iye amene abwera mʼdzina la Ambuye!” “Hosana mmwambamwamba!” 10 Yesu atalowa mu Yerusalemu, mzinda wonse unatekeseka ndipo anthu anafunsa kuti, “Ndani ameneyu?” 11 Magulu a anthu anayankha kuti, “Uyu ndi Yesu, mneneri wochokera ku Nazareti.” 12 Yesu analowa mʼdera lina la Nyumba ya Mulungu ndipo anatulutsa kunja anthu onse amene ankachita malonda. Anagubuduza matebulo a osinthira ndalama ndi mipando ya ogulitsa nkhunda. 13 Iye anawawuza kuti, “Zinalembedwa kuti Nyumba yanga idzatchedwa Nyumba ya mapemphero koma inu mwayisandutsa phanga la anthu achifwamba.” 14 Anthu osaona ndi olumala anabwera kwa Iye mʼNyumba ya Mulungu ndipo anawachiritsa. 15 Koma akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo ataona zodabwitsa zimene anachita, komanso ana akufuwula mʼNyumbayo kuti, “Hosana kwa Mwana wa Davide,” anapsa mtima. 16 Anamufunsa kuti, “Kodi mukumva zimene anawa akunena?”Yesu anayankha nati, “Inde. Kodi simunawerenge kuti, “Kuchokera mʼkamwa mwa ana ndi makanda mwatuluka mayamiko?” 17 Ndipo anawasiya natuluka mu mzindawo ndi kupita ku Betaniya, kumene anakagona. 18 Mmamawa, pamene amabwera ku mzinda, anamva njala. 19 Ataona mtengo wamkuyu mʼmbali mwa msewu, anapitapo koma sanapeze kanthu koma masamba okhaokha. Pamenepo anati kwa mtengowo, “Usadzabalenso chipatso!” Nthawi yomweyo mtengowo unafota. 20 Ophunzira ataona zimenezi, anadabwa nafunsa kuti, “Kodi mtengo wamkuyuwu wauma msanga bwanji?” 21 Yesu anayankha kuti, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti ngati muli ndi chikhulupiriro ndipo simukayika, simudzangochita zokha zachitika kwa mkuyuzi, koma mudzatha kuwuza phiri ili kuti, ‘Pita, kadziponye wekha mʼnyanja,’ ndipo zidzachitikadi. 22 Ngati mukhulupirira, mudzalandira chilichonse chimene muchipempha mʼpemphero.” 23 Yesu analowa mʼNyumba ya Mulungu, ndipo pamene ankaphunzitsa, akulu a ansembe ndi akuluakulu anabwera kwa Iye namufunsa kuti, “Muchita izi ndi ulamuliro wanji ndipo anakupatsani ndani ulamuliro umenewu?” 24 Yesu anayankha kuti, “Inenso ndikufunsani funso limodzi, mukandiyankha, Inenso ndikukuwuzani ndi ulamuliro wa yani umene ndikuchitira izi. 25 Ubatizo wa Yohane unachokera kuti? Kumwamba kapena kwa anthu?”Anakambirana pakati pawo ndipo anati, “Tikati, ‘Kuchokera kumwamba,’ Iye adzafunsa kuti, ‘Bwanji simunakhulupirire?’ 26 Koma tikati, ‘Kuchokera kwa anthu,’ ife tikuopa anthuwa, pakuti onse amakhulupirira kuti Yohane anali mneneri.” 27 Choncho anamuwuza Yesu kuti, “Sitikudziwa.”Pamenepo Iye anati, “Inenso sindikuwuzani kuti ndi ulamuliro wa yani umene ndichitira izi.” 28 “Kodi muganiza bwanji? Panali munthu wina anali ndi ana aamuna awiri. Anapita kwa woyamba nati, ‘Mwanawe pita kagwire ntchito lero mʼmunda wamphesa.’ 29 “Iye anayankha kuti, ‘Sindipita,’ koma pambuyo pake anasintha maganizo napita. 30 “Kenaka abambowo anapita kwa mwana winayo nanena chimodzimodzi. Iye anayankha kuti, ‘Ndipita abambo,’ koma sanapite. 31 “Ndani wa awiriwa anachita chimene abambo ake amafuna?”Anamuyankha nati, “Woyambayo.”Yesu anawawuza kuti, “Ndikuwuzani zoonadi, kuti amisonkho ndi adama akulowa mu ufumu wa Mulungu inu musanalowemo.” 32 Pakuti Yohane anabwera kwa inu kuti akuonetseni njira yachilungamo, koma inu simunakhulupirire iye, koma amisonkho ndi adama anamukhulupirira. Koma ngakhale munaona izi, simunatembenuke mtima ndi kumukhulupirira iye. 33 “Tamverani fanizo lina: Panali mwini munda amene anadzala mphesa. Anamanga mpanda kuzungulira mundawo, nakumba moponderamo mphesa ndipo anamanga nsanja. Kenaka anabwereketsa munda wamphesawo kwa alimi ena napita pa ulendo. 34 Pamene nthawi yokolola inakwana, anatumiza antchito ake kwa matenanti aja kuti akatenge zipatso zake. 35 “Alimi aja anagwira antchito ake; namenya mmodzi, napha wina, ndi kumuponya miyala wachitatuyo. 36 Kenaka anatumiza antchito ena oposa oyambawo ndipo matenantiwo anawachitira chimodzimodzi. 37 Pomalizira anatumiza mwana wake. Anati adzamuchitira ulemu mwana wanga. 38 “Koma alimiwo ataona mwanayo anati kwa wina ndi mnzake, ‘Uyu ndiye olowa mʼmalo mwa abambo ake. Tiyeni timuphe ndipo titenge cholowa chake.’ 39 Pamenepo anamutenga namuponyera kunja kwa munda wamphesa namupha. 40 “Tsono akabwera mwini munda wamphesa adzachita nawo chiyani matenantiwo?” 41 Iwo anayankha kuti, “Adzawapha moyipa alimi oyipawo ndipo adzabwereketsa mundawo kwa alimi ena amene adzamupatsa gawo lake la mbewu pa nthawi yokolola.” 42 Yesu anawawuza kuti, “Kodi simunawerenge mʼmalemba kuti: “ ‘Mwala umene omanga nyumba anawukana, womwewo wasanduka mwala wofunika kwambiri wa pa ngodya. Ambuye wachita izi, ndipo ndi zodabwitsa mʼmaso mwathu.’ 43 “Nʼchifukwa chake ndi kukuwuzani kuti ufumu wa Mulungu udzalandidwa kwa inu ndipo udzapatsidwa kwa anthu amene adzabereka chipatso chake. 44 Amene agwa pa mwalawu adzadukaduka, ndipo amene udzamugwere udzamuthudzula.” 45 Akulu a ansembe ndi Afarisi atamva mafanizo a Yesu, anadziwa kuti ankanena iwo. 46 Pamenepo anafuna njira yoti amugwirire, koma anaopa gulu la anthu chifukwa anthu onse ankakhulupirira kuti Iye anali mneneri.

In Other Versions

Matthew 21 in the ANGEFD

Matthew 21 in the ANTPNG2D

Matthew 21 in the AS21

Matthew 21 in the BAGH

Matthew 21 in the BBPNG

Matthew 21 in the BBT1E

Matthew 21 in the BDS

Matthew 21 in the BEV

Matthew 21 in the BHAD

Matthew 21 in the BIB

Matthew 21 in the BLPT

Matthew 21 in the BNT

Matthew 21 in the BNTABOOT

Matthew 21 in the BNTLV

Matthew 21 in the BOATCB

Matthew 21 in the BOATCB2

Matthew 21 in the BOBCV

Matthew 21 in the BOCNT

Matthew 21 in the BOECS

Matthew 21 in the BOHCB

Matthew 21 in the BOHCV

Matthew 21 in the BOHLNT

Matthew 21 in the BOHNTLTAL

Matthew 21 in the BOICB

Matthew 21 in the BOILNTAP

Matthew 21 in the BOITCV

Matthew 21 in the BOKCV

Matthew 21 in the BOKCV2

Matthew 21 in the BOKHWOG

Matthew 21 in the BOKSSV

Matthew 21 in the BOLCB

Matthew 21 in the BOLCB2

Matthew 21 in the BOMCV

Matthew 21 in the BONAV

Matthew 21 in the BONCB

Matthew 21 in the BONLT

Matthew 21 in the BONUT2

Matthew 21 in the BOPLNT

Matthew 21 in the BOSCB

Matthew 21 in the BOSNC

Matthew 21 in the BOTLNT

Matthew 21 in the BOVCB

Matthew 21 in the BOYCB

Matthew 21 in the BPBB

Matthew 21 in the BPH

Matthew 21 in the BSB

Matthew 21 in the CCB

Matthew 21 in the CUV

Matthew 21 in the CUVS

Matthew 21 in the DBT

Matthew 21 in the DGDNT

Matthew 21 in the DHNT

Matthew 21 in the DNT

Matthew 21 in the ELBE

Matthew 21 in the EMTV

Matthew 21 in the ESV

Matthew 21 in the FBV

Matthew 21 in the FEB

Matthew 21 in the GGMNT

Matthew 21 in the GNT

Matthew 21 in the HARY

Matthew 21 in the HNT

Matthew 21 in the IRVA

Matthew 21 in the IRVB

Matthew 21 in the IRVG

Matthew 21 in the IRVH

Matthew 21 in the IRVK

Matthew 21 in the IRVM

Matthew 21 in the IRVM2

Matthew 21 in the IRVO

Matthew 21 in the IRVP

Matthew 21 in the IRVT

Matthew 21 in the IRVT2

Matthew 21 in the IRVU

Matthew 21 in the ISVN

Matthew 21 in the JSNT

Matthew 21 in the KAPI

Matthew 21 in the KBT1ETNIK

Matthew 21 in the KBV

Matthew 21 in the KJV

Matthew 21 in the KNFD

Matthew 21 in the LBA

Matthew 21 in the LBLA

Matthew 21 in the LNT

Matthew 21 in the LSV

Matthew 21 in the MAAL

Matthew 21 in the MBV

Matthew 21 in the MBV2

Matthew 21 in the MHNT

Matthew 21 in the MKNFD

Matthew 21 in the MNG

Matthew 21 in the MNT

Matthew 21 in the MNT2

Matthew 21 in the MRS1T

Matthew 21 in the NAA

Matthew 21 in the NASB

Matthew 21 in the NBLA

Matthew 21 in the NBS

Matthew 21 in the NBVTP

Matthew 21 in the NET2

Matthew 21 in the NIV11

Matthew 21 in the NNT

Matthew 21 in the NNT2

Matthew 21 in the NNT3

Matthew 21 in the PDDPT

Matthew 21 in the PFNT

Matthew 21 in the RMNT

Matthew 21 in the SBIAS

Matthew 21 in the SBIBS

Matthew 21 in the SBIBS2

Matthew 21 in the SBICS

Matthew 21 in the SBIDS

Matthew 21 in the SBIGS

Matthew 21 in the SBIHS

Matthew 21 in the SBIIS

Matthew 21 in the SBIIS2

Matthew 21 in the SBIIS3

Matthew 21 in the SBIKS

Matthew 21 in the SBIKS2

Matthew 21 in the SBIMS

Matthew 21 in the SBIOS

Matthew 21 in the SBIPS

Matthew 21 in the SBISS

Matthew 21 in the SBITS

Matthew 21 in the SBITS2

Matthew 21 in the SBITS3

Matthew 21 in the SBITS4

Matthew 21 in the SBIUS

Matthew 21 in the SBIVS

Matthew 21 in the SBT

Matthew 21 in the SBT1E

Matthew 21 in the SCHL

Matthew 21 in the SNT

Matthew 21 in the SUSU

Matthew 21 in the SUSU2

Matthew 21 in the SYNO

Matthew 21 in the TBIAOTANT

Matthew 21 in the TBT1E

Matthew 21 in the TBT1E2

Matthew 21 in the TFTIP

Matthew 21 in the TFTU

Matthew 21 in the TGNTATF3T

Matthew 21 in the THAI

Matthew 21 in the TNFD

Matthew 21 in the TNT

Matthew 21 in the TNTIK

Matthew 21 in the TNTIL

Matthew 21 in the TNTIN

Matthew 21 in the TNTIP

Matthew 21 in the TNTIZ

Matthew 21 in the TOMA

Matthew 21 in the TTENT

Matthew 21 in the UBG

Matthew 21 in the UGV

Matthew 21 in the UGV2

Matthew 21 in the UGV3

Matthew 21 in the VBL

Matthew 21 in the VDCC

Matthew 21 in the YALU

Matthew 21 in the YAPE

Matthew 21 in the YBVTP

Matthew 21 in the ZBP