Nehemiah 10 (BOGWICC)

1 Amene anasindikiza chidindo anali awa: Nehemiya, bwanamkubwa uja, mwana wa Hakaliya. Zedekiya, 2 Seraya, Azariya, Yeremiya 3 Pasuri, Amariya, Malikiya, 4 Hatusi, Sebaniya, Maluki, 5 Harimu, Meremoti, Obadiya, 6 Danieli, Ginetoni, Baruki, 7 Mesulamu, Abiya, Miyamini 8 Maziya, Biligai ndi SemayaAwa anali ansembe. 9 Alevi anali awa:Yesuwa mwana wa Azaniya, Binuyi wa fuko la Henadadi, Kadimieli, 10 ndi abale awo awa: Sebaniya,Hodiya, Kelita, Pelaya, Hanani, 11 Mika, Rehobu, Hasabiya, 12 Zakuri, Serebiya, Sebaniya, 13 Hodiya, Bani ndi Beninu. 14 Atsogoleri a anthu anali awa:Parosi, Pahati-Mowabu, Elamu, Zatu, Bani, 15 Buni, Azigadi, Bebai, 16 Adoniya, Bigivai, Adini, 17 Ateri, Hezekiya, Azuri, 18 Hodiya, Hasumu, Bezayi 19 Harifu, Anatoti, Nebayi, 20 Magipiyasi, Mesulamu, Heziri 21 Mesezabeli, Zadoki, Yaduwa 22 Pelatiya, Hanani, Ananiya, 23 Hoseya, Hananiya, Hasubu 24 Halohesi, Piliha, Sobeki, 25 Rehumu, Hasabiya, Maaseya, 26 Ahiya, Hanani, Anani, 27 Maluki, Harimu ndi Baana. 28 Ife otsalafe, ndiye kuti ansembe, Alevi, alonda a ku Nyumba ya Mulungu, oyimba nyimbo, ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu, onse amene anadzipatula pakati pa anthu a mitundu ina kuti atsate malamulo a Yehova, pamodzi ndi akazi athu, ana athu ndi onse amene ali ndi nzeru, 29 tikuphatikana ndi abale athu wolemekezeka, ndipo tikulonjeza molumbira kuti tidzayenda motsata malamulo a Mulungu amene anapereka kudzera mwa Mose mtumiki wa Mulungu. Tilonjeza kumvera ndi kutsata bwino mawu onse, miyambo yonse ndi malangizo onse a Yehova. Yehova atilange ngati sitidzachita zimenezi. 30 “Ife tikulonjeza kuti sitidzapereka ana athu aakazi kuti akwatiwe ndi amuna a mayiko ena kapena kutenga ana awo aakazi kuti akwatiwe ndi ana athu aamuna. 31 “Ngati anthu a mitundu ina abwera ndi zinthu za malonda, monga tirigu, kudzagulitsa pa tsiku la Sabata, sitidzawagula pa tsiku la Sabata kapena pa tsiku lina lililonse loyera. Pa chaka chilichonse cha chisanu ndi chiwiri tidzagoneka munda wosawulima ndipo tidzafafaniza ngongole zonse. 32 “Tikulonjezanso molumbira kuti chaka ndi chaka tizipereka magalamu anayi a siliva kuti zithandize ntchito ya ku Nyumba ya Mulungu wathu. 33 Ndalamayi izithandiza kulipirira buledi wa pa tebulo, chopereka cha chakudya cha nthawi zonse, zopereka zopsereza za nthawi zonse, zopereka za pa tsiku la Sabata, za pachikondwerero cha Mwezi Watsopano, za pa masiku a chikondwerero osankhika, zopereka za zinthu zopatulika, zopereka za nsembe yopepesera machimo a Aisraeli ndi ntchito ina iliyonse ya ku Nyumba ya Mulungu. 34 “Ife ansembe, Alevi ndi anthu onse, tachita maere kuti tidziwe pamene banja lathu lililonse lidzabweretsa ku nyumba ya Mulungu wathu pa nthawi yoyikika ya chaka zopereka za nkhuni zoyaka pa guwa lansembe la Yehova Mulungu wathu, monga momwe zinalembedwera mʼMalamulo.” 35 “Tilonjezanso kuti tidzabwera ndi zipatso zoyamba kucha za mʼminda yathu ndi zipatso zoyamba kucha za mtengo uliwonse wa zipatso chaka ndi chaka kuti tidzapereke ku Nyumba ya Mulungu wathu.” 36 “Tidzabweranso nawo ku Nyumba ya Mulungu, kwa ansembe amene amatumikira ku Nyumba ya Mulungu ana athu aamuna oyamba kubadwa ndi ana angʼombe oyamba kubadwa monga zalembedwera mu Malamulo. Tidzaperekanso ana oyamba kubadwa a ziweto zathu ndi ana ankhosa oyamba kubadwa.” 37 “Ndiponso ku zipinda za Nyumba ya Mulungu wathu, kwa ansembe tidzaperekanso mtanda wathu wa buledi wa ufa ndi mphatso zina monga zipatso za mtengo uliwonse, vinyo ndi mafuta. Tidzaperekanso kwa alevi chakhumi cha mbewu zathu pakuti alevi ndiwo amasonkhanitsa chakhumi mʼmidzi yathu yonse. 38 Wansembe, mdzukulu wa Aaroni azikhala pamodzi ndi Alevi pamene akulandira chakhumi. Ndipo Alevi azibwera ndi chakhumicho ku nyumba ya Mulungu wathu, kuzipinda zosungiramo chuma.” 39 Choncho Israeli, kuphatikiza zidzukulu za Alevi, azipititsa zopereka za tirigu, vinyo ndi mafuta ku zipinda zosungiramo katundu wopatulika, komanso kokhala ansembe amene akutumikira pamodzi ndi alonda a ku Nyumba ya Mulungu ndi anthu oyimba nyimbo.“Kwambiri ife sitidzaleka kusamala Nyumba ya Mulungu.”

In Other Versions

Nehemiah 10 in the ANGEFD

Nehemiah 10 in the ANTPNG2D

Nehemiah 10 in the AS21

Nehemiah 10 in the BAGH

Nehemiah 10 in the BBPNG

Nehemiah 10 in the BBT1E

Nehemiah 10 in the BDS

Nehemiah 10 in the BEV

Nehemiah 10 in the BHAD

Nehemiah 10 in the BIB

Nehemiah 10 in the BLPT

Nehemiah 10 in the BNT

Nehemiah 10 in the BNTABOOT

Nehemiah 10 in the BNTLV

Nehemiah 10 in the BOATCB

Nehemiah 10 in the BOATCB2

Nehemiah 10 in the BOBCV

Nehemiah 10 in the BOCNT

Nehemiah 10 in the BOECS

Nehemiah 10 in the BOHCB

Nehemiah 10 in the BOHCV

Nehemiah 10 in the BOHLNT

Nehemiah 10 in the BOHNTLTAL

Nehemiah 10 in the BOICB

Nehemiah 10 in the BOILNTAP

Nehemiah 10 in the BOITCV

Nehemiah 10 in the BOKCV

Nehemiah 10 in the BOKCV2

Nehemiah 10 in the BOKHWOG

Nehemiah 10 in the BOKSSV

Nehemiah 10 in the BOLCB

Nehemiah 10 in the BOLCB2

Nehemiah 10 in the BOMCV

Nehemiah 10 in the BONAV

Nehemiah 10 in the BONCB

Nehemiah 10 in the BONLT

Nehemiah 10 in the BONUT2

Nehemiah 10 in the BOPLNT

Nehemiah 10 in the BOSCB

Nehemiah 10 in the BOSNC

Nehemiah 10 in the BOTLNT

Nehemiah 10 in the BOVCB

Nehemiah 10 in the BOYCB

Nehemiah 10 in the BPBB

Nehemiah 10 in the BPH

Nehemiah 10 in the BSB

Nehemiah 10 in the CCB

Nehemiah 10 in the CUV

Nehemiah 10 in the CUVS

Nehemiah 10 in the DBT

Nehemiah 10 in the DGDNT

Nehemiah 10 in the DHNT

Nehemiah 10 in the DNT

Nehemiah 10 in the ELBE

Nehemiah 10 in the EMTV

Nehemiah 10 in the ESV

Nehemiah 10 in the FBV

Nehemiah 10 in the FEB

Nehemiah 10 in the GGMNT

Nehemiah 10 in the GNT

Nehemiah 10 in the HARY

Nehemiah 10 in the HNT

Nehemiah 10 in the IRVA

Nehemiah 10 in the IRVB

Nehemiah 10 in the IRVG

Nehemiah 10 in the IRVH

Nehemiah 10 in the IRVK

Nehemiah 10 in the IRVM

Nehemiah 10 in the IRVM2

Nehemiah 10 in the IRVO

Nehemiah 10 in the IRVP

Nehemiah 10 in the IRVT

Nehemiah 10 in the IRVT2

Nehemiah 10 in the IRVU

Nehemiah 10 in the ISVN

Nehemiah 10 in the JSNT

Nehemiah 10 in the KAPI

Nehemiah 10 in the KBT1ETNIK

Nehemiah 10 in the KBV

Nehemiah 10 in the KJV

Nehemiah 10 in the KNFD

Nehemiah 10 in the LBA

Nehemiah 10 in the LBLA

Nehemiah 10 in the LNT

Nehemiah 10 in the LSV

Nehemiah 10 in the MAAL

Nehemiah 10 in the MBV

Nehemiah 10 in the MBV2

Nehemiah 10 in the MHNT

Nehemiah 10 in the MKNFD

Nehemiah 10 in the MNG

Nehemiah 10 in the MNT

Nehemiah 10 in the MNT2

Nehemiah 10 in the MRS1T

Nehemiah 10 in the NAA

Nehemiah 10 in the NASB

Nehemiah 10 in the NBLA

Nehemiah 10 in the NBS

Nehemiah 10 in the NBVTP

Nehemiah 10 in the NET2

Nehemiah 10 in the NIV11

Nehemiah 10 in the NNT

Nehemiah 10 in the NNT2

Nehemiah 10 in the NNT3

Nehemiah 10 in the PDDPT

Nehemiah 10 in the PFNT

Nehemiah 10 in the RMNT

Nehemiah 10 in the SBIAS

Nehemiah 10 in the SBIBS

Nehemiah 10 in the SBIBS2

Nehemiah 10 in the SBICS

Nehemiah 10 in the SBIDS

Nehemiah 10 in the SBIGS

Nehemiah 10 in the SBIHS

Nehemiah 10 in the SBIIS

Nehemiah 10 in the SBIIS2

Nehemiah 10 in the SBIIS3

Nehemiah 10 in the SBIKS

Nehemiah 10 in the SBIKS2

Nehemiah 10 in the SBIMS

Nehemiah 10 in the SBIOS

Nehemiah 10 in the SBIPS

Nehemiah 10 in the SBISS

Nehemiah 10 in the SBITS

Nehemiah 10 in the SBITS2

Nehemiah 10 in the SBITS3

Nehemiah 10 in the SBITS4

Nehemiah 10 in the SBIUS

Nehemiah 10 in the SBIVS

Nehemiah 10 in the SBT

Nehemiah 10 in the SBT1E

Nehemiah 10 in the SCHL

Nehemiah 10 in the SNT

Nehemiah 10 in the SUSU

Nehemiah 10 in the SUSU2

Nehemiah 10 in the SYNO

Nehemiah 10 in the TBIAOTANT

Nehemiah 10 in the TBT1E

Nehemiah 10 in the TBT1E2

Nehemiah 10 in the TFTIP

Nehemiah 10 in the TFTU

Nehemiah 10 in the TGNTATF3T

Nehemiah 10 in the THAI

Nehemiah 10 in the TNFD

Nehemiah 10 in the TNT

Nehemiah 10 in the TNTIK

Nehemiah 10 in the TNTIL

Nehemiah 10 in the TNTIN

Nehemiah 10 in the TNTIP

Nehemiah 10 in the TNTIZ

Nehemiah 10 in the TOMA

Nehemiah 10 in the TTENT

Nehemiah 10 in the UBG

Nehemiah 10 in the UGV

Nehemiah 10 in the UGV2

Nehemiah 10 in the UGV3

Nehemiah 10 in the VBL

Nehemiah 10 in the VDCC

Nehemiah 10 in the YALU

Nehemiah 10 in the YAPE

Nehemiah 10 in the YBVTP

Nehemiah 10 in the ZBP