Nehemiah 2 (BOGWICC)

1 Pa mwezi wa Nisani, mʼchaka cha makumi awiri cha ufumu wa Aritasasita, atabwera ndi vinyo pamaso pa mfumu ine ndinatenga vinyoyo ndi kupereka kwa mfumu. Koma ndinali ndisanakhalepo ndi nkhope yachisoni pamaso pake. 2 Tsono mfumu inandifunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani nkhope yako ikuoneka yachisoni pamene iwe sukudwala? Ichi si chinthu china koma chisoni cha mu mtima.”Ine ndinachita mantha kwambiri. 3 Ndinawuza mfumu kuti, “Mfumu ikhale ndi moyo wamuyaya! Kodi nkhope yanga ilekerenji kuoneka yachisoni pamene mzinda umene kuli manda a makolo anga, wasanduka bwinja ndipo zipata zake zinawonongedwa ndi moto?” 4 Apo mfumu inandifunsa kuti, “Tsono ukufuna kundipempha chiyani?”Ndipo ine ndinapemphera kwa Mulungu Wakumwamba. 5 Ndipo ndinayankha kuti, “Ngati amfumu chingakukondweretseni, ngati mungakomere mtima mtumiki wanune, mundilole kuti ndipite ku Yuda, ku mzinda kumene kuli manda a makolo anga kuti ndikawumangenso.” 6 Tsono mfumu, mfumukazi itakhala pambali pake, anandifunsa kuti, “Kodi kumeneko ukakhalako masiku angati ndipo udzabwera liti?” Ndinayiwuza mfumu nthawi yake ndipo inandilola kuti ndipite. 7 Ndipo ndinatinso kwa mfumu, “Ngati zikondweretse mfumu, mundipatse makalata oti ndikapereke kwa abwanamkubwa a ku chigawo cha Patsidya pa Yufurate, kuti akandilole kudutsa mwamtendere mpaka nditakafika ku Yuda. 8 Mundipatsenso kalata yokapereka kwa Asafu woyangʼanira nkhalango ya mfumu, kuti akandipatse mitengo yokapangira mitanda ya zipata za nsanja yoteteza Nyumba ya Mulungu, mitanda ya khoma la mzinda ndi ya nyumba yokhalamo ine.” Mfumu indipatse zomwe ndinapempha popeza Yehova wokoma mtima anali nane. 9 Choncho ndinanyamuka ulendo wanga ndipo ndinafika kwa abwanamkubwa a chigawo cha Patsidya pa Yufurate ndipo ndinawapatsa makalata a mfumu. Mfumu nʼkuti itatumiza akulu ankhondo ndi okwera pa akavalo kuti atsagane nane. 10 Sanibalati wa ku Horoni ndi Tobiya wa ku Amoni atamva zimenezi, iwo anayipidwa kwambiri kuti wina wabwera kudzachitira zabwino Aisraeli. 11 Ndinafika ku Yerusalemu, ndipo ndinakhala kumeneko masiku atatu. 12 Sindinawuze munthu aliyense za zimene Yehova anayika mu mtima mwanga kuti ndichitire mzinda wa Yerusalemu. Choncho ndinanyamuka usiku pamodzi ndi anthu ena owerengeka. Ndinalibe bulu wina aliyense kupatula amene ndinakwerapo. 13 Ndinatuluka usiku podzera ku Chipata cha ku Chigwa ndi kuyenda kupita ku Chitsime cha Chirombo Chamʼmadzi mpaka ku Chipata cha Zinyalala. Ndinayangʼana makoma a Yerusalemu, amene anagwetsedwa, ndi zipata zake, zimene zinawonongedwa ndi moto. 14 Kenaka ndinapita ku Chipata cha Kasupe ndi ku Dziwe la Mfumu. Koma panalibe malo okwanira akuti bulu wanga adutse. 15 Kotero usikuwo ndinapita ku chigwa, ndikuyangʼana khomalo. Pomaliza ndinabwerera ndi kukalowanso mu mzinda kudzera ku Chipata cha ku Chigwa. 16 Akuluakulu sanadziwe kumene ndinapita kapena zimene ndimachita, chifukwa pa nthawiyi nʼkuti ndisananene kalikonse kwa Ayuda kapena ansembe, anthu olemekezeka kapena akuluakulu, kapena wina aliyense amene anali woyenera kugwira ntchitoyi. 17 Ndinawawuza kuti, “Inu mukuona mavuto amene tili nawo. Mukuona kuti mzinda wa Yerusalemu wasanduka bwinja ndipo zipata zake zatenthedwa ndi moto. Tsono tiyeni timangenso makoma a Yerusalemu ndipo sitidzachitanso manyazi.” 18 Ndinawawuza za mmene Yehova Mulungu wanga anandichitira zabwino ndiponso mawu amene mfumu inandiwuza.Tsono anati, “Tiyeni tiyambenso kumanga.” Kotero analimbitsana mtima kuti ayambenso ntchito yabwinoyi. 19 Koma Sanibalati wa ku Horoni, Tobiya wa ku Amoni ndi Gesemu Mwarabu atamva zimenezi, anatiseka ndi kutinyoza. Iwo anafunsa kuti, “Kodi muti ndi chiyani chimene mukuchitachi? Kodi mufuna kuwukira mfumu?” 20 Koma ndinawayankha kuti, “Mulungu Wakumwamba atithandiza kuti zinthu zitiyendere bwino. Ife antchito ake tiyambapo kumanga. Koma inu mulibe gawo lanu muno mu Yerusalemu. Mulibe chokuyenerezani kulandira malo ano. Mulibenso chilichonse muno chokumbutsa za inu.”

In Other Versions

Nehemiah 2 in the ANGEFD

Nehemiah 2 in the ANTPNG2D

Nehemiah 2 in the AS21

Nehemiah 2 in the BAGH

Nehemiah 2 in the BBPNG

Nehemiah 2 in the BBT1E

Nehemiah 2 in the BDS

Nehemiah 2 in the BEV

Nehemiah 2 in the BHAD

Nehemiah 2 in the BIB

Nehemiah 2 in the BLPT

Nehemiah 2 in the BNT

Nehemiah 2 in the BNTABOOT

Nehemiah 2 in the BNTLV

Nehemiah 2 in the BOATCB

Nehemiah 2 in the BOATCB2

Nehemiah 2 in the BOBCV

Nehemiah 2 in the BOCNT

Nehemiah 2 in the BOECS

Nehemiah 2 in the BOHCB

Nehemiah 2 in the BOHCV

Nehemiah 2 in the BOHLNT

Nehemiah 2 in the BOHNTLTAL

Nehemiah 2 in the BOICB

Nehemiah 2 in the BOILNTAP

Nehemiah 2 in the BOITCV

Nehemiah 2 in the BOKCV

Nehemiah 2 in the BOKCV2

Nehemiah 2 in the BOKHWOG

Nehemiah 2 in the BOKSSV

Nehemiah 2 in the BOLCB

Nehemiah 2 in the BOLCB2

Nehemiah 2 in the BOMCV

Nehemiah 2 in the BONAV

Nehemiah 2 in the BONCB

Nehemiah 2 in the BONLT

Nehemiah 2 in the BONUT2

Nehemiah 2 in the BOPLNT

Nehemiah 2 in the BOSCB

Nehemiah 2 in the BOSNC

Nehemiah 2 in the BOTLNT

Nehemiah 2 in the BOVCB

Nehemiah 2 in the BOYCB

Nehemiah 2 in the BPBB

Nehemiah 2 in the BPH

Nehemiah 2 in the BSB

Nehemiah 2 in the CCB

Nehemiah 2 in the CUV

Nehemiah 2 in the CUVS

Nehemiah 2 in the DBT

Nehemiah 2 in the DGDNT

Nehemiah 2 in the DHNT

Nehemiah 2 in the DNT

Nehemiah 2 in the ELBE

Nehemiah 2 in the EMTV

Nehemiah 2 in the ESV

Nehemiah 2 in the FBV

Nehemiah 2 in the FEB

Nehemiah 2 in the GGMNT

Nehemiah 2 in the GNT

Nehemiah 2 in the HARY

Nehemiah 2 in the HNT

Nehemiah 2 in the IRVA

Nehemiah 2 in the IRVB

Nehemiah 2 in the IRVG

Nehemiah 2 in the IRVH

Nehemiah 2 in the IRVK

Nehemiah 2 in the IRVM

Nehemiah 2 in the IRVM2

Nehemiah 2 in the IRVO

Nehemiah 2 in the IRVP

Nehemiah 2 in the IRVT

Nehemiah 2 in the IRVT2

Nehemiah 2 in the IRVU

Nehemiah 2 in the ISVN

Nehemiah 2 in the JSNT

Nehemiah 2 in the KAPI

Nehemiah 2 in the KBT1ETNIK

Nehemiah 2 in the KBV

Nehemiah 2 in the KJV

Nehemiah 2 in the KNFD

Nehemiah 2 in the LBA

Nehemiah 2 in the LBLA

Nehemiah 2 in the LNT

Nehemiah 2 in the LSV

Nehemiah 2 in the MAAL

Nehemiah 2 in the MBV

Nehemiah 2 in the MBV2

Nehemiah 2 in the MHNT

Nehemiah 2 in the MKNFD

Nehemiah 2 in the MNG

Nehemiah 2 in the MNT

Nehemiah 2 in the MNT2

Nehemiah 2 in the MRS1T

Nehemiah 2 in the NAA

Nehemiah 2 in the NASB

Nehemiah 2 in the NBLA

Nehemiah 2 in the NBS

Nehemiah 2 in the NBVTP

Nehemiah 2 in the NET2

Nehemiah 2 in the NIV11

Nehemiah 2 in the NNT

Nehemiah 2 in the NNT2

Nehemiah 2 in the NNT3

Nehemiah 2 in the PDDPT

Nehemiah 2 in the PFNT

Nehemiah 2 in the RMNT

Nehemiah 2 in the SBIAS

Nehemiah 2 in the SBIBS

Nehemiah 2 in the SBIBS2

Nehemiah 2 in the SBICS

Nehemiah 2 in the SBIDS

Nehemiah 2 in the SBIGS

Nehemiah 2 in the SBIHS

Nehemiah 2 in the SBIIS

Nehemiah 2 in the SBIIS2

Nehemiah 2 in the SBIIS3

Nehemiah 2 in the SBIKS

Nehemiah 2 in the SBIKS2

Nehemiah 2 in the SBIMS

Nehemiah 2 in the SBIOS

Nehemiah 2 in the SBIPS

Nehemiah 2 in the SBISS

Nehemiah 2 in the SBITS

Nehemiah 2 in the SBITS2

Nehemiah 2 in the SBITS3

Nehemiah 2 in the SBITS4

Nehemiah 2 in the SBIUS

Nehemiah 2 in the SBIVS

Nehemiah 2 in the SBT

Nehemiah 2 in the SBT1E

Nehemiah 2 in the SCHL

Nehemiah 2 in the SNT

Nehemiah 2 in the SUSU

Nehemiah 2 in the SUSU2

Nehemiah 2 in the SYNO

Nehemiah 2 in the TBIAOTANT

Nehemiah 2 in the TBT1E

Nehemiah 2 in the TBT1E2

Nehemiah 2 in the TFTIP

Nehemiah 2 in the TFTU

Nehemiah 2 in the TGNTATF3T

Nehemiah 2 in the THAI

Nehemiah 2 in the TNFD

Nehemiah 2 in the TNT

Nehemiah 2 in the TNTIK

Nehemiah 2 in the TNTIL

Nehemiah 2 in the TNTIN

Nehemiah 2 in the TNTIP

Nehemiah 2 in the TNTIZ

Nehemiah 2 in the TOMA

Nehemiah 2 in the TTENT

Nehemiah 2 in the UBG

Nehemiah 2 in the UGV

Nehemiah 2 in the UGV2

Nehemiah 2 in the UGV3

Nehemiah 2 in the VBL

Nehemiah 2 in the VDCC

Nehemiah 2 in the YALU

Nehemiah 2 in the YAPE

Nehemiah 2 in the YBVTP

Nehemiah 2 in the ZBP