Nehemiah 3 (BOGWICC)

1 Pambuyo pake Eliyasibu mkulu wa ansembe ndi ansembe anzake anayamba kugwira ntchito ndipo anamanganso Chipata cha Nkhosa. Iwo anachipatulira Mulungu ndipo anayika zitseko zake. Khoma limene analipatula linafika mpaka pa Nsanja ya Zana ndi Nsanja ya Hananeli. 2 Anthu a ku Yeriko anamanga chigawo china pambali pake ndipo Zakuri mwana wa Imuri anamanga chigawo chinanso choyandikana nawo. 3 Chipata cha Nsomba chinamangidwanso ndi ana a fuko la Hasena. Iwo anayika mitanda yake ndi zitseko, zotsekera zake, ndi mipiringidzo yake. 4 Meremoti mwana wa Uriya, mwana wa Hakozi, anakonza chigawo choyandikana nacho. Motsatana naye, Mesulamu mwana wa Berekiya, mwana wa Mesezabeli anakonza chigawo china. Pambali pake, Zadoki mwana wa Baana anakonzanso chigawo china. 5 Pambali pa iwowa anthu a ku Tekowa anakonza chigawo china. Koma wolemekezeka awo anakana kugwira ntchito imene akuluakulu awo anawapatsa. 6 Chipata cha Yesana chinakonzedwa ndi Yoyada mwana wa Paseya ndi Mesulamu mwana wa Besodeya. Iwo anayika mitanda yake ndi kuyika zitseko, zotsekera zake ndi mipiringidzo yake. 7 Pambali pawo Melatiya Mgibeyoni ndi Yadoni Mmerenoti ndiponso anthu a ku Gibiyoni ndi a ku Mizipa anakonza chigawo chawo mpaka ku nyumba ya bwanamkubwa wa chigawo cha Patsidya pa Yufurate. 8 Pambali pawo Uzieli mwana wa Harihaya wa mʼgulu amisiri osula golide anakonzanso chigawo china. Pambali pake Hananiya mmodzi mwa anthu oyenga mafuta onunkhira, anakonzanso chigawo china. Iwo anakonzanso Yerusalemu mpaka ku Khoma Lotambasuka. 9 Refaya mwana wa Huri wolamulira theka la chigawo cha Yerusalemu anakonza chigawo china motsatana nawo. 10 Kulumikiza ichi, Yedaya mwana wa Harumafi anakonza chigawo choyangʼanana ndi nyumba yake, ndipo Hatusi mwana wa Hasabaneya anakonzanso motsatana naye. 11 Malikiya mwana wa Harimu ndi Hasubu mwana wa Pahati-Mowabu anakonzanso chigawo china ndiponso Nsanja ya Ngʼanjo. 12 Salumu mwana wa Halohesi wolamulira theka la chigawo cha Yerusalemu, anakonzanso chigawo chotsatana nawo mothandizidwa ndi ana ake akazi. 13 Chipata cha ku chigwa chinakonzedwa ndi Hanuni ndi anthu okhala ku Zanowa. Iwo anachimanganso ndi kuyika zitseko zake ndi zotsekera ndi mipiringidzo yake. Iwo anakonzanso khoma lotalika mamita 450 mpaka ku Chipata cha Zinyalala. 14 Chipata cha Zinyalala chinakonzedwa ndi Malikiya mwana wa Rekabu, wolamulira chigawo cha Beti-Hakeremu. Iye anachimanganso ndi kuyika zitseko zake, zotsekera zake ndi mipiringidzo. 15 Chipata cha Kasupe chinakonzedwa ndi Saluni mwana wa Koli-Hoze, wolamulira chigawo cha Mizipa. Iye anachimanganso ndi kuyikanso denga ndiponso zitseko, zotsekera ndi mipiringidzo yake. Iye anakonzanso khoma la Dziwe la Siloamu limene lili pafupi ndi munda wa mfumu mpaka ku makwerero otsikira potuluka mzinda wa Davide. 16 Pambali pa iyeyo, Nehemiya mwana wa Azibuki, wolamulira theka la chigawo cha Beti Zuri anakonza chigawo china mpaka kumalo oyangʼanana ndi manda a Davide, mpaka ku dziwe lokumba ndi ku nyumba ya anthu ankhondo. 17 Pambali pake Alevi anakonza chigawo china, ndipo mtsogoleri wawo anali Rehumi mwana wa Bani. Pambali pa iye Hasabiya wolamulira theka la chigawo cha Keyila anagwira ntchito ku chigawo chake. 18 Pambuyo pa iyeyu abale awo anapitiriza kukonza, ndipo mtsogoleri wawo anali Bawai mwana wa Henadadi, wolamulira theka lina la chigawo cha Keyila. 19 Motsatana naye Ezeri mwana wa Yesuwa, wolamulira Mizipa anakonza chigawo chinanso choyangʼanana ndi chikweza chofikira ku nyumba yosungira zida za nkhondo pa ngodya. 20 Motsatana naye, Baruki mwana wa Zakai anakonzanso chigawo china kuchokera pa ngodya mpaka pa chitseko cha nyumba ya Eliyasibu mkulu wa ansembe. 21 Motsatana naye, Meremoti mwana wa Uriya, mwana wa Hakozi anakonzanso chigawo china kuchokera ku chitseko cha nyumba ya Eliyasibu mpaka kumapeto kwake. 22 Pambuyo pake ansembe okhala ku chidikha anakonzanso chigawo china. 23 Pambuyo pawo, Benjamini ndi Hasubu anakonza kutsogolo kwa nyumba zawo. Ndipo motsatana nawo, Azariya mwana wa Maaseya mwana wa Ananiya, anakonza chigawo choyangʼanana ndi nyumba zawo. 24 Motsatana naye, Binuyi mwana wa Henadadi anakonzanso chigawo china, kuchokera pa nyumba ya Azariya kukafika potsirizira pa ngodya. 25 Palali mwana Uzai anakonza chigawo china choyangʼanana ndi ngodya ndi nsanja yotuluka pa nyumba yapamwamba ya mfumu ku bwalo la alonda. Motsatana naye, Pedaya mwana wa Parosi, 26 ndi otumikira mʼNyumba ya Mulungu amene amakhala pa khoma la Ofeli anakonza chigawo china mpaka pa malo oyangʼanana ndi Chipata cha Madzi kuloza kummawa ndiponso nsanja yayitali ija. 27 Motsatana nawo, anthu a ku Tekowa anakonzanso chigawo china choyangʼanana ndi nsanja ija yayikulu ndi yayitali mpaka ku khoma la Ofeli. 28 Kuyambira ku Chipata cha Akavalo anakonza ndi ansembe ena ndipo aliyense amakonza khoma loyangʼanana ndi nyumba yake. 29 Motsatana nawo, Zadoki mwana wa Imeri anakonza chigawo china choyangʼanana ndi nyumba yake. Motsatana naye, Semeya mwana wa Sekaniya, mlonda wa Chipata cha Kummawa, anakonzanso khoma. 30 Hananiya mwana wa Selemiya ndiponso Hanuni mwana wachisanu ndi chimodzi wa Zalafi anakonza chigawo china. Motsatana naye, Mesulamu mwana wa Berekiya anakonza chigawo choyangʼanana ndi chipinda chake. 31 Motsatana naye, Malikiya mmodzi mwa amisiri a golide anakonza chigawo china mpaka ku nyumba ya atumiki a ku Nyumba ya Mulungu ndiponso ku nyumba ya anthu amalonda moyangʼanana ndi chipata cha Mifikade ndiponso mpaka pa chipinda chapamwamba chapangodya. 32 Ndipo pakati pa chipinda chapamwamba chapangodya ndi Chipata cha Nkhosa anakonza ndi amisiri a golide ndi anthu amalonda.

In Other Versions

Nehemiah 3 in the ANGEFD

Nehemiah 3 in the ANTPNG2D

Nehemiah 3 in the AS21

Nehemiah 3 in the BAGH

Nehemiah 3 in the BBPNG

Nehemiah 3 in the BBT1E

Nehemiah 3 in the BDS

Nehemiah 3 in the BEV

Nehemiah 3 in the BHAD

Nehemiah 3 in the BIB

Nehemiah 3 in the BLPT

Nehemiah 3 in the BNT

Nehemiah 3 in the BNTABOOT

Nehemiah 3 in the BNTLV

Nehemiah 3 in the BOATCB

Nehemiah 3 in the BOATCB2

Nehemiah 3 in the BOBCV

Nehemiah 3 in the BOCNT

Nehemiah 3 in the BOECS

Nehemiah 3 in the BOHCB

Nehemiah 3 in the BOHCV

Nehemiah 3 in the BOHLNT

Nehemiah 3 in the BOHNTLTAL

Nehemiah 3 in the BOICB

Nehemiah 3 in the BOILNTAP

Nehemiah 3 in the BOITCV

Nehemiah 3 in the BOKCV

Nehemiah 3 in the BOKCV2

Nehemiah 3 in the BOKHWOG

Nehemiah 3 in the BOKSSV

Nehemiah 3 in the BOLCB

Nehemiah 3 in the BOLCB2

Nehemiah 3 in the BOMCV

Nehemiah 3 in the BONAV

Nehemiah 3 in the BONCB

Nehemiah 3 in the BONLT

Nehemiah 3 in the BONUT2

Nehemiah 3 in the BOPLNT

Nehemiah 3 in the BOSCB

Nehemiah 3 in the BOSNC

Nehemiah 3 in the BOTLNT

Nehemiah 3 in the BOVCB

Nehemiah 3 in the BOYCB

Nehemiah 3 in the BPBB

Nehemiah 3 in the BPH

Nehemiah 3 in the BSB

Nehemiah 3 in the CCB

Nehemiah 3 in the CUV

Nehemiah 3 in the CUVS

Nehemiah 3 in the DBT

Nehemiah 3 in the DGDNT

Nehemiah 3 in the DHNT

Nehemiah 3 in the DNT

Nehemiah 3 in the ELBE

Nehemiah 3 in the EMTV

Nehemiah 3 in the ESV

Nehemiah 3 in the FBV

Nehemiah 3 in the FEB

Nehemiah 3 in the GGMNT

Nehemiah 3 in the GNT

Nehemiah 3 in the HARY

Nehemiah 3 in the HNT

Nehemiah 3 in the IRVA

Nehemiah 3 in the IRVB

Nehemiah 3 in the IRVG

Nehemiah 3 in the IRVH

Nehemiah 3 in the IRVK

Nehemiah 3 in the IRVM

Nehemiah 3 in the IRVM2

Nehemiah 3 in the IRVO

Nehemiah 3 in the IRVP

Nehemiah 3 in the IRVT

Nehemiah 3 in the IRVT2

Nehemiah 3 in the IRVU

Nehemiah 3 in the ISVN

Nehemiah 3 in the JSNT

Nehemiah 3 in the KAPI

Nehemiah 3 in the KBT1ETNIK

Nehemiah 3 in the KBV

Nehemiah 3 in the KJV

Nehemiah 3 in the KNFD

Nehemiah 3 in the LBA

Nehemiah 3 in the LBLA

Nehemiah 3 in the LNT

Nehemiah 3 in the LSV

Nehemiah 3 in the MAAL

Nehemiah 3 in the MBV

Nehemiah 3 in the MBV2

Nehemiah 3 in the MHNT

Nehemiah 3 in the MKNFD

Nehemiah 3 in the MNG

Nehemiah 3 in the MNT

Nehemiah 3 in the MNT2

Nehemiah 3 in the MRS1T

Nehemiah 3 in the NAA

Nehemiah 3 in the NASB

Nehemiah 3 in the NBLA

Nehemiah 3 in the NBS

Nehemiah 3 in the NBVTP

Nehemiah 3 in the NET2

Nehemiah 3 in the NIV11

Nehemiah 3 in the NNT

Nehemiah 3 in the NNT2

Nehemiah 3 in the NNT3

Nehemiah 3 in the PDDPT

Nehemiah 3 in the PFNT

Nehemiah 3 in the RMNT

Nehemiah 3 in the SBIAS

Nehemiah 3 in the SBIBS

Nehemiah 3 in the SBIBS2

Nehemiah 3 in the SBICS

Nehemiah 3 in the SBIDS

Nehemiah 3 in the SBIGS

Nehemiah 3 in the SBIHS

Nehemiah 3 in the SBIIS

Nehemiah 3 in the SBIIS2

Nehemiah 3 in the SBIIS3

Nehemiah 3 in the SBIKS

Nehemiah 3 in the SBIKS2

Nehemiah 3 in the SBIMS

Nehemiah 3 in the SBIOS

Nehemiah 3 in the SBIPS

Nehemiah 3 in the SBISS

Nehemiah 3 in the SBITS

Nehemiah 3 in the SBITS2

Nehemiah 3 in the SBITS3

Nehemiah 3 in the SBITS4

Nehemiah 3 in the SBIUS

Nehemiah 3 in the SBIVS

Nehemiah 3 in the SBT

Nehemiah 3 in the SBT1E

Nehemiah 3 in the SCHL

Nehemiah 3 in the SNT

Nehemiah 3 in the SUSU

Nehemiah 3 in the SUSU2

Nehemiah 3 in the SYNO

Nehemiah 3 in the TBIAOTANT

Nehemiah 3 in the TBT1E

Nehemiah 3 in the TBT1E2

Nehemiah 3 in the TFTIP

Nehemiah 3 in the TFTU

Nehemiah 3 in the TGNTATF3T

Nehemiah 3 in the THAI

Nehemiah 3 in the TNFD

Nehemiah 3 in the TNT

Nehemiah 3 in the TNTIK

Nehemiah 3 in the TNTIL

Nehemiah 3 in the TNTIN

Nehemiah 3 in the TNTIP

Nehemiah 3 in the TNTIZ

Nehemiah 3 in the TOMA

Nehemiah 3 in the TTENT

Nehemiah 3 in the UBG

Nehemiah 3 in the UGV

Nehemiah 3 in the UGV2

Nehemiah 3 in the UGV3

Nehemiah 3 in the VBL

Nehemiah 3 in the VDCC

Nehemiah 3 in the YALU

Nehemiah 3 in the YAPE

Nehemiah 3 in the YBVTP

Nehemiah 3 in the ZBP