Nehemiah 4 (BOGWICC)

1 Sanibalati atamva kuti tikumanganso khoma anapsa mtima nayamba kuseka ndi kunyogodola Ayuda kwambiri. 2 Ndipo anayankhula pamaso pa abale ake ndi asilikali a Samariya kuti, “Kodi Ayuda ofowokawa akuchita chiyani? Kodi iwo nʼkumanganso khoma? Kodi adzaperekanso nsembe? Kodi adzatsiriza ntchitoyi tsiku limodzi? Kodi adzachita kutenga miyala yakale ija ndi mmene inapseramo?” 3 Tobiya wa ku Amoni, amene anali naye anati, “Chimene akumangacho ngati nkhandwe itakwerapo, itha kugwetsa khoma lawolo!” 4 Tsono ndinayamba kupemphera kuti, “Timvereni, Inu Mulungu wathu, mmene akutinyozera. Mulole kuti mawu awo onyoza awabwerere, ndipo atengedwe ukapolo ku dziko lachilendo. 5 Musawakhululukire mphulupulu zawo kapena kufafaniza machimo awo pamaso panu popeza aputa ukali wanu pamaso pa anthu omanga khoma.” 6 Choncho ife tinamangabe khomalo kufikira lonse litafika theka la msinkhu wake, chifukwa chakuti anthu anagwira ntchitoyo ndi mtima wawo wonse. 7 Koma pamene Sanibalati, Tobiya, Aarabu, Aamoni ndi anthu a ku Asidodi anamva kuti ntchito yokonzanso makoma a Yerusalemu ikupitirirabe ndipo kuti mipata ikutsekedwa, anapsa mtima kwambiri. 8 Tsono onse anapangana za chiwembu kuti abwere ndi kudzathira nkhondo anthu a ku Yerusalemu ndi kuyambitsa mapokoso pakati pawo. 9 Koma ife tinapemphera kwa Mulungu wathu ndipo tinayika alonda otiteteza kwa adaniwo usiku ndi usana. 10 Pa nthawi yomweyi anthu a ku Yuda anati, “Mphamvu za anthu onyamula zinyalala zikutha ndipo pali zinyalala zambiri. Choncho ife sititha kumanga khomali.” 11 Adani athunso anati, “Iwo asanadziwe izi, kapena kutiona, tidzakhala tili pakati pawo ndipo tidzawapha ndi kuyimitsa ntchitoyo.” 12 Ndipo Ayuda amene ankhala pafupi ndi adani athuwo anabwera kakhumi konse kuchokera konse kumene ankakhala kudzatiwuza kuti tibwereko ku ntchito. 13 Choncho kumbuyo kwa khoma, cha mʼmunsi mwake komanso malo amene anali asanathe ndinayikamo anthu mʼmabanja atatenga malupanga, mikondo ndi mauta awo. 14 Popeza anthu ankachita mantha, tsono ndinawawuza anthu olemekezeka, akuluakulu ndiponso anthu onse kuti, “Musawaope. Kumbukirani kuti Ambuye ndi wamkulu ndipo ndi woopsa. Choncho menyerani nkhondo abale anu, ana aamuna ndi aakazi, akazi anu ndi nyumba zanu.” 15 Adani athu atamva kuti ife tadziwa za chiwembu chawo, anadziwanso kuti Yehova walepheretsa zimene ankafuna kutichita. Choncho tinabwerera aliyense ku ntchito yake yomanga khoma. 16 Kuyambira tsiku limenelo mpaka mʼtsogolo mwake, theka la antchito anga linkagwira ntchito, pamene theka linalo limatenga mikondo, zishango, mauta ndi kuvala malaya azitsulo. Akuluakulu ankalimbikitsa Ayuda onse 17 amene ankamanga khoma. Anthu onyamula zinyalala aja ankagwira ntchito ndi dzanja limodzi, dzanja linali atanyamula chida chankhondo. 18 Mʼmisiri aliyense ankamangirira lupanga lake mʼchiwuno mwake akamagwira ntchito. Koma munthu woyimba lipenga anali pambali panga nthawi zonse. 19 Ndipo ine ndinati kwa anthu olemekezeka ndi anthu ena onse, “Ntchitoyi ndi yayikulu ndipo ili padera lalikulu ndipo ifeyo takhala motayanatayana kwambiri pa khoma. 20 Tsono kulikonse kumene muliko, mukamva kulira kwa lipenga bwerani mudzasonkhane kumene kuli ine kuno. Mulungu wathu adzatimenyera nkhondo.” 21 Choncho enafe tinapitiriza kugwira ntchito, pamene theka lina linkanyamula mikondo kuyambira mʼbandakucha mpaka nyenyezi zitaoneka. 22 Pa nthawi imeneyo ndinawuzanso anthuwo kuti, “Aliyense pamodzi ndi wantchito wake agone mu Yerusalemu kuti tikhale ndi otilondera usiku ndi kuti masana tizigwira ntchito.” 23 Choncho ine, anzanga, antchito anga, ndi anthu otiteteza amene ankanditsata panalibe ndi mmodzi yemwe anavula zovala zake pogona. Aliyense anasunga chida chake chankhondo pambali pake.

In Other Versions

Nehemiah 4 in the ANGEFD

Nehemiah 4 in the ANTPNG2D

Nehemiah 4 in the AS21

Nehemiah 4 in the BAGH

Nehemiah 4 in the BBPNG

Nehemiah 4 in the BBT1E

Nehemiah 4 in the BDS

Nehemiah 4 in the BEV

Nehemiah 4 in the BHAD

Nehemiah 4 in the BIB

Nehemiah 4 in the BLPT

Nehemiah 4 in the BNT

Nehemiah 4 in the BNTABOOT

Nehemiah 4 in the BNTLV

Nehemiah 4 in the BOATCB

Nehemiah 4 in the BOATCB2

Nehemiah 4 in the BOBCV

Nehemiah 4 in the BOCNT

Nehemiah 4 in the BOECS

Nehemiah 4 in the BOHCB

Nehemiah 4 in the BOHCV

Nehemiah 4 in the BOHLNT

Nehemiah 4 in the BOHNTLTAL

Nehemiah 4 in the BOICB

Nehemiah 4 in the BOILNTAP

Nehemiah 4 in the BOITCV

Nehemiah 4 in the BOKCV

Nehemiah 4 in the BOKCV2

Nehemiah 4 in the BOKHWOG

Nehemiah 4 in the BOKSSV

Nehemiah 4 in the BOLCB

Nehemiah 4 in the BOLCB2

Nehemiah 4 in the BOMCV

Nehemiah 4 in the BONAV

Nehemiah 4 in the BONCB

Nehemiah 4 in the BONLT

Nehemiah 4 in the BONUT2

Nehemiah 4 in the BOPLNT

Nehemiah 4 in the BOSCB

Nehemiah 4 in the BOSNC

Nehemiah 4 in the BOTLNT

Nehemiah 4 in the BOVCB

Nehemiah 4 in the BOYCB

Nehemiah 4 in the BPBB

Nehemiah 4 in the BPH

Nehemiah 4 in the BSB

Nehemiah 4 in the CCB

Nehemiah 4 in the CUV

Nehemiah 4 in the CUVS

Nehemiah 4 in the DBT

Nehemiah 4 in the DGDNT

Nehemiah 4 in the DHNT

Nehemiah 4 in the DNT

Nehemiah 4 in the ELBE

Nehemiah 4 in the EMTV

Nehemiah 4 in the ESV

Nehemiah 4 in the FBV

Nehemiah 4 in the FEB

Nehemiah 4 in the GGMNT

Nehemiah 4 in the GNT

Nehemiah 4 in the HARY

Nehemiah 4 in the HNT

Nehemiah 4 in the IRVA

Nehemiah 4 in the IRVB

Nehemiah 4 in the IRVG

Nehemiah 4 in the IRVH

Nehemiah 4 in the IRVK

Nehemiah 4 in the IRVM

Nehemiah 4 in the IRVM2

Nehemiah 4 in the IRVO

Nehemiah 4 in the IRVP

Nehemiah 4 in the IRVT

Nehemiah 4 in the IRVT2

Nehemiah 4 in the IRVU

Nehemiah 4 in the ISVN

Nehemiah 4 in the JSNT

Nehemiah 4 in the KAPI

Nehemiah 4 in the KBT1ETNIK

Nehemiah 4 in the KBV

Nehemiah 4 in the KJV

Nehemiah 4 in the KNFD

Nehemiah 4 in the LBA

Nehemiah 4 in the LBLA

Nehemiah 4 in the LNT

Nehemiah 4 in the LSV

Nehemiah 4 in the MAAL

Nehemiah 4 in the MBV

Nehemiah 4 in the MBV2

Nehemiah 4 in the MHNT

Nehemiah 4 in the MKNFD

Nehemiah 4 in the MNG

Nehemiah 4 in the MNT

Nehemiah 4 in the MNT2

Nehemiah 4 in the MRS1T

Nehemiah 4 in the NAA

Nehemiah 4 in the NASB

Nehemiah 4 in the NBLA

Nehemiah 4 in the NBS

Nehemiah 4 in the NBVTP

Nehemiah 4 in the NET2

Nehemiah 4 in the NIV11

Nehemiah 4 in the NNT

Nehemiah 4 in the NNT2

Nehemiah 4 in the NNT3

Nehemiah 4 in the PDDPT

Nehemiah 4 in the PFNT

Nehemiah 4 in the RMNT

Nehemiah 4 in the SBIAS

Nehemiah 4 in the SBIBS

Nehemiah 4 in the SBIBS2

Nehemiah 4 in the SBICS

Nehemiah 4 in the SBIDS

Nehemiah 4 in the SBIGS

Nehemiah 4 in the SBIHS

Nehemiah 4 in the SBIIS

Nehemiah 4 in the SBIIS2

Nehemiah 4 in the SBIIS3

Nehemiah 4 in the SBIKS

Nehemiah 4 in the SBIKS2

Nehemiah 4 in the SBIMS

Nehemiah 4 in the SBIOS

Nehemiah 4 in the SBIPS

Nehemiah 4 in the SBISS

Nehemiah 4 in the SBITS

Nehemiah 4 in the SBITS2

Nehemiah 4 in the SBITS3

Nehemiah 4 in the SBITS4

Nehemiah 4 in the SBIUS

Nehemiah 4 in the SBIVS

Nehemiah 4 in the SBT

Nehemiah 4 in the SBT1E

Nehemiah 4 in the SCHL

Nehemiah 4 in the SNT

Nehemiah 4 in the SUSU

Nehemiah 4 in the SUSU2

Nehemiah 4 in the SYNO

Nehemiah 4 in the TBIAOTANT

Nehemiah 4 in the TBT1E

Nehemiah 4 in the TBT1E2

Nehemiah 4 in the TFTIP

Nehemiah 4 in the TFTU

Nehemiah 4 in the TGNTATF3T

Nehemiah 4 in the THAI

Nehemiah 4 in the TNFD

Nehemiah 4 in the TNT

Nehemiah 4 in the TNTIK

Nehemiah 4 in the TNTIL

Nehemiah 4 in the TNTIN

Nehemiah 4 in the TNTIP

Nehemiah 4 in the TNTIZ

Nehemiah 4 in the TOMA

Nehemiah 4 in the TTENT

Nehemiah 4 in the UBG

Nehemiah 4 in the UGV

Nehemiah 4 in the UGV2

Nehemiah 4 in the UGV3

Nehemiah 4 in the VBL

Nehemiah 4 in the VDCC

Nehemiah 4 in the YALU

Nehemiah 4 in the YAPE

Nehemiah 4 in the YBVTP

Nehemiah 4 in the ZBP